Miyambo
30 Uwu ndi uthenga wamphamvu womwe Aguri mwana wa Yake analankhula ndi Itiyeli komanso Ukali.
2 Ine sindidziwa zambiri poyerekeza ndi anthu ena onse,+
Ndipo sinditha kumvetsa zinthu ngati mmene anthu ena amachitira.
3 Ine sindinaphunzire zinthu zanzeru,
Ndipo sindidziwa zinthu zimene Woyera Koposa amadziwa.
4 Ndi ndani amene anakwerapo kumwamba kenako nʼkutsika?+
Ndi ndani amene anasonkhanitsapo mphepo mʼmanja mwake?
Ndi ndani amene anamangapo madzi pachovala chake?+
Ndi ndani amene anaika malire a dziko lapansi?+
Dzina lake ndi ndani, nanga mwana wake dzina lake ndi ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.
5 Mawu onse a Mulungu ndi oyengeka.+
Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.+
7 Ndikukupemphani zinthu ziwiri.
Mundipatse zinthu zimenezi ndisanafe.
8 Zinthu zabodza komanso mawu onama muziike kutali ndi ine.+
Musandipatse umphawi kapena chuma.
Mungondipatsa chakudya chokwanira,+
9 Kuti ndisakhute kwambiri nʼkukukanani kuti: “Kodi Yehova ndi ndani?”+
Ndiponso kuti ndisasauke nʼkukaba ndi kuchititsa kuti dzina la Mulungu wanga linyozedwe.
10 Usanenere wantchito zoipa kwa bwana wake,
Kuti angakutemberere ndipo ungapezeke wolakwa.+
11 Pali mʼbadwo umene umatemberera bambo awo
Komanso umene sudalitsa mayi awo.+
13 Pali mʼbadwo umene maso ake ndi onyada
Ndiponso umene maso ake amayangʼana modzikweza.+
14 Pali mʼbadwo umene mano ake ndi malupanga
Ndiponso umene nsagwada zake ndi mipeni yophera nyama.
Mʼbadwowo umapondereza anthu ovutika apadziko lapansi
Komanso osauka pakati pa anthu.+
15 Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti, “Tipatseni! Tipatseni!”
Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta
Ndiponso zinthu 4 zimene sizinena kuti, “Ndakhuta!” Zinthu zake ndi izi:
17 Munthu amene amanyoza bambo ake ndiponso amene samvera mayi ake,+
Akhwangwala akuchigwa* adzakolowola diso lake
Ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.+
18 Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine,
Ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi:
19 Njira ya chiwombankhanga mumlengalenga,
Njira ya njoka pamwala,
Njira ya sitima pakatikati pa nyanja,
Ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.
20 Zimene mkazi wachigololo amachita ndi izi:
Iye amadya nʼkupukuta pakamwa pake
Kenako amanena kuti, “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+
21 Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansi
Ndiponso zinthu 4 zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthu zake ndi izi:
22 Kapolo akamalamulira monga mfumu,+
Munthu wopusa akamadya kwambiri,
23 Mkazi amene amadedwa* akakwatiwa,
Komanso mtsikana wantchito akatenga malo a abwana ake aakazi.+
24 Pali zinthu 4 zomwe zili mʼgulu la zinthu zingʼonozingʼono kwambiri padziko lapansi
25 Nyerere si zamphamvu,
Koma zimasonkhanitsa chakudya chawo mʼchilimwe.+
28 Nalimata+ amagwira zinthu ndi mapazi ake
Ndipo amalowa mʼnyumba yachifumu.
29 Pali zinthu zitatu zimene zimayenda mochititsa chidwi
Ndiponso zinthu 4 zimene zimasangalatsa zikamayenda. Zinthu zake ndi izi:
30 Mkango umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire
Ndiponso umene suopa chilichonse nʼkubwerera mʼmbuyo,+
31 Galu wosaka kapena mbuzi yamphongo,
Ndiponso mfumu imene ili limodzi ndi asilikali ake.
32 Ngati wachita zinthu zopusa nʼkudzikweza,+
Kapena ngati ukufuna kuchita zimenezo,
Gwira pakamwa pako.+
33 Chifukwa mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta,
Mphuno ukaifinya imatulutsa magazi,
Ndipo kukolezera mkwiyo kumayambitsa mkangano.+