Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.
131 Inu Yehova, mtima wanga si wodzikweza,
Maso anga si onyada.+
Sindilakalaka zinthu zapamwamba kwambiri,+
Kapena zinthu zimene sindingazikwanitse.
2 Koma ine ndatonthoza mtima wanga ndipo ndaukhazika mʼmalo+
Ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa, amene ali mʼmanja mwa mayi ake.
Ndine wokhutira ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa.
3 Isiraeli ayembekezere Yehova,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.