Salimo
Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Solomo.
127 Yehova akapanda kumanga nyumba,
Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+
Yehova akapanda kulondera mzinda,+
Alonda amakhala maso pachabe.
2 Mukudzuka mʼmawa pachabe,
Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,
Mumapeza chakudya movutikira,
Chifukwa Mulungu amapereka zinthu zofunika kwa anthu amene amawakonda komanso amawapatsa tulo tabwino.+
3 Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+
Chipatso cha mimba ndi mphoto yochokera kwa Mulungu.+
4 Ana a bambo wachinyamata,+
Ali ngati mivi mʼdzanja la mwamuna wamphamvu.
5 Wosangalala ndi mwamuna amene wadzaza kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.+
Abambo oterowo sadzachita manyazi,
Chifukwa ana awo adzalankhula ndi adani pageti la mzinda.