Salimo
Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kuphanga.+
142 Ndimafuulira Yehova kuti andithandize.+
Ndimachonderera Yehova kuti andikomere mtima.
2 Ndimakhuthula nkhawa zanga pamaso pake.
Ndimafotokoza mavuto anga pamaso pake+
3 Pamene mphamvu zanga zatha.*
Ndikatero, mumayangʼanitsitsa njira yanga.+
Adani anga anditchera msampha
Mʼnjira imene ndikuyenda.
Palibenso kulikonse kumene ndingathawire,+
Ndipo palibe amene akundidera nkhawa.
5 Ndikuitana inu Yehova kuti mundithandize.
Ndikunena kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako,+
Malo okhawo amene ndili nawo* mʼdziko la anthu amoyo.”
6 Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo,
Chifukwa ndavutika kwambiri.
Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+
Chifukwa iwo ndi amphamvu kuposa ine.
7 Nditulutseni mundende yamdima
Kuti nditamande dzina lanu.
Anthu olungama andizungulire
Chifukwa mumandichitira zabwino.