Miyambo
18 Munthu aliyense amene amadzipatula amangoganizira kuchita zimene amalakalaka.
Iye amakana* nzeru zonse zopindulitsa.
2 Munthu wopusa sasangalala ndi kumvetsa zinthu.
Iye amangokonda kuulula zimene zili mumtima mwake.+
3 Munthu woipa akabwera, pamabweranso kunyozeka,
Ndipo munthu akamachita zinthu zochititsa manyazi amanyozeka.+
4 Mawu amʼkamwa mwa munthu ali ngati madzi akuya.+
Kasupe wa nzeru ali ngati mtsinje wosefukira.
7 Pakamwa pa munthu wopusa mʼpamene pamamuchititsa kuti awonongedwe,+
Ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.
9 Munthu waulesi pa ntchito yake
Ndi mʼbale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+
10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+
Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.*+
11 Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.
Ndipo mʼmaganizo mwake chili ngati mpanda umene ukumuteteza.+
13 Munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse,
Kumakhala kupusa ndipo amachita manyazi.+
15 Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu,+
Ndipo khutu la munthu wanzeru limafunitsitsa kudziwa zinthu.
16 Mphatso ya munthu imamʼtsegulira njira,+
Ndipo imamuthandiza kuti akafike kwa anthu olemekezeka.
17 Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola,+
19 Kusangalatsa mʼbale amene walakwiridwa nʼkovuta kwambiri kuposa kulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba,+
Ndipo mikangano ingathe kulekanitsa anthu ngati mageti otseka a mzinda wolimba.+
20 Mimba ya munthu imakhuta zipatso za mawu otuluka pakamwa pake.+
Iye amakhuta zokolola za milomo yake.
21 Imfa ndiponso moyo zili mumphamvu ya lilime,+
Ndipo amene amakonda kuligwiritsa ntchito adzadya zipatso zake.+
23 Munthu wosauka akamalankhula amachita kuchonderera,
Koma munthu wolemera amayankha mwaukali.