Miyambo
9 Nzeru yeniyeni yamanga nyumba yake.
Yasema zipilala zake 7.
3 Yatuma antchito ake aakazi
Kuti apite pamalo okwera amumzinda kukaitana anthu kuti:+
4 “Aliyense wosadziwa zinthu abwere kuno.”
Aliyense wopanda nzeru, nzeru ikumuuza kuti:
5 “Bwera udzadye chakudya changa
Ndipo udzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.
6 Leka kukhala munthu wosadziwa zinthu kuti upitirize kukhala ndi moyo.+
Lola kuti kumvetsa zinthu kukutsogolere.”+
7 Amene amalangiza wonyoza amachititsidwa manyazi,+
Ndipo aliyense wodzudzula woipa adzavulazidwa.
8 Usadzudzule wonyoza chifukwa angadane nawe.+
Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+
9 Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+
Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.
10 Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru,+
Ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa,+ udzakhala womvetsa zinthu.
11 Chifukwa ine ndidzachulukitsa masiku a moyo wako,+
Ndipo ndidzawonjezera zaka za moyo wako.
12 Ukakhala wanzeru, iweyo ndi amene umapindula ndi nzeruzo,
Koma ngati ndiwe wonyoza, iweyo ndi amene udzavutike.
13 Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+
Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.
14 Amakhala pampando pakhomo la nyumba yake
Pamalo okwera amumzinda,+
15 Nʼkumaitana anthu odutsa
Amene akungodziyendera panjira kuti:
16 “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu abwere kuno.”
Aliyense wopanda nzeru, mkaziyo akumuuza kuti:+
17 “Madzi akuba amatsekemera,
Ndipo chakudya chodya mobisa chimakoma.”+