Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
64 Inu Mulungu, imvani mawu anga pamene ndikukuchondererani.+
Tetezani moyo wanga ku zinthu zoopsa zimene mdani akuchita.
2 Ndibiseni ku ziwembu zachinsinsi za anthu oipa,+
Kwa gulu la anthu ochita zoipa.
3 Iwo amanola lilime lawo ngati lupanga.
Amakonzekera kuponya mawu awo opweteka ngati mivi,
4 Kuti alase munthu wosalakwa atamubisalira.
Amamulasa modzidzimutsa ndiponso mopanda mantha.
5 Amaumirira kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa,*
Amakambirana zimene angachite kuti abise misampha yawo.
Iwo amanena kuti: “Angaione ndani?”+
6 Amafufuza njira zatsopano zochitira zinthu zoipa.
Mwachinsinsi amakonza njira zochitira ziwembu zawo mochenjera.+
Zimene munthu aliyense akuganiza mumtima mwake, nʼzovuta kuzimvetsa.
7 Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi.+
Adzavulazidwa ndi muvi modzidzimutsa.
8 Adzawonongedwa chifukwa cha zolankhula za lilime lawo lomwe,+
Onse amene adzaone zimenezi adzapukusa mitu yawo.
9 Ndiyeno anthu onse adzachita mantha,
Ndipo adzalengeza zimene Mulungu wachita,
Iwo adzamvetsa bwino zimene iye amachita.+