Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika Zimene Zili Mʼbuku la Maliro MALIRO ZIMENE ZILI MʼBUKULI 1 Yerusalemu anayerekezeredwa ndi mkazi wamasiye Yerusalemu anatsala yekhayekha wopanda munthu (1) Machimo aakulu a Ziyoni (8, 9) Ziyoni anakanidwa ndi Mulungu (12-15) Palibe aliyense amene akutonthoza Ziyoni (17) 2 Yehova anakwiyira Yerusalemu Sanamve chisoni (2) Yehova anakhala ngati mdani wake (5) Kulirira Ziyoni (11-13) Anthu odutsa mumsewu ananyoza mzinda umene poyamba unali wokongola (15) Adani anasangalala chifukwa cha kuwonongedwa kwa Ziyonil (17) 3 Yeremiya anasonyeza mmene akumvera komanso zimene ankayembekezera “Ndidzakhala ndi mtima wodikira” (21) Chifundo cha Mulungu chimakhala chatsopano mʼmawa uliwonse (22, 23) Mulungu ndi wabwino kwa anthu amene akumuyembekezera (25) Ndi bwino kuti munthu akumane ndi mavuto ali wamngʼono (27) Mulungu anadzitchinga ndi mtambo (43, 44) 4 Mavuto oopsa amene Yerusalemu anakumana nawo atazunguliridwa ndi adani Kusowa kwa chakudya (4, 5, 9) Azimayi anaphika ana awo (10) Yehova anakhuthula mkwiyo wake (11) 5 Pemphero la anthu lopempha kuti zinthu zibwerere mwakale ‘Kumbukirani zimene zatichitikira’ (1) ‘Tsoka kwa ife chifukwa tachimwa’ (16) ‘Inu Yehova, tibwezereni kwa inu’ (21) “Bwezeretsani zinthu zonse” (21)