Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Genesis 1:1-50:26
  • Genesis

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Genesis
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Genesis

GENESIS

1 Pachiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.+

2 Dziko lapansi linali lopanda chilichonse. Padzikoli panali madzi ambiri+ ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha. Mphamvu ya Mulungu+ inkayendayenda* pamwamba pa madziwo.+

3 Ndiyeno Mulungu anati: “Pakhale kuwala.” Ndipo kuwala+ kunakhalapo. 4 Zitatero, Mulungu anaona kuti kuwalako kunali kwabwino. Kenako Mulungu anayamba kulekanitsa kuwala ndi mdima. 5 Ndiyeno Mulungu anapatsa kuwalako dzina lakuti Masana, koma mdimawo anaupatsa dzina lakuti Usiku.+ Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku loyamba.

6 Kenako Mulungu ananena kuti: “Pakhale mlengalenga+ pakati pa madzi kuti madziwo+ alekane.” 7 Choncho Mulungu anapanga mlengalenga nʼkulekanitsa madzi kuti ena akhale pansi pa mlengalenga ndipo ena akhale pamwamba pa mlengalenga.+ Ndipo zinaterodi. 8 Mlengalengawo Mulungu anaupatsa dzina lakuti Kumwamba. Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku lachiwiri.

9 Kenako Mulungu anati: “Madzi apadziko lapansi akhale pamalo amodzi kuti mtunda uonekere.”+ Ndipo zinaterodi. 10 Mulungu anapatsa mtundawo dzina lakuti Dziko,+ koma madziwo anawapatsa dzina lakuti Nyanja.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.+ 11 Kenako Mulungu anati: “Padziko lapansi pamere udzu, zomera zobereka mbewu ndiponso mitengo yobereka zipatso zokhala ndi nthangala, monga mwa mitundu yake.” Ndipo zinaterodi. 12 Choncho dziko lapansi linayamba kumera udzu, zomera zobereka mbewu+ monga mwa mitundu yake komanso mitengo yobereka zipatso zokhala ndi nthangala monga mwa mitundu yake. Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino. 13 Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku lachitatu.

14 Kenako Mulungu anati: “Kumwamba kukhale zounikira+ kuti zilekanitse masana ndi usiku+ ndipo zidzakhala zizindikiro zosonyeza nyengo, masiku ndi zaka.+ 15 Zidzakhala zounikira zokhala mumlengalenga ndipo zizidzaunikira dziko lapansi.” Ndipo zinaterodi. 16 Choncho Mulungu anapanga zounikira ziwiri. Chounikira chowala kwambiri anachipanga kuti chiziwala* masana,+ ndipo chowala pangʼono kuti chiziwala* usiku, komanso anapanga nyenyezi.+ 17 Mulungu atatero, anaziika mumlengalenga kuti ziunikire dziko lapansi. 18 Anaziika kuti ziziwala masana ndi usiku, komanso kuti zizilekanitsa kuwala ndi mdima.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino. 19 Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 4.

20 Kenako Mulungu anati: “Mʼmadzi mukhale zamoyo zambirimbiri, ndiponso zolengedwa zouluka ziziuluka mumlengalenga mwa dziko lapansi.”+ 21 Mulungu analenga nyama zikuluzikulu zamʼnyanja ndi zamoyo zonse zokhala mʼmadzi mogwirizana ndi mitundu yake. Analenganso chamoyo chilichonse chouluka mogwirizana ndi mtundu wake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino. 22 Mulungu atatero, anazidalitsa ponena kuti: “Muswane ndipo muchulukane nʼkudzaza nyanja zonse.+ Ndipo zamoyo zouluka zichuluke padziko lapansi.” 23 Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 5.

24 Kenako Mulungu anati: “Dziko lapansi likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta, nyama zokwawa,* komanso nyama zakutchire monga mwa mitundu yake.”+ Ndipo zinaterodi. 25 Choncho Mulungu anapanga nyama zakutchire monga mwa mitundu yake komanso nyama zoweta monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.

26 Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu mʼchifaniziro+ chathu, kuti akhale wofanana nafe.+ Ayangʼanire nsomba zamʼnyanja, zamoyo zouluka mumlengalenga, nyama zoweta ndiponso nyama iliyonse yokwawa padziko lapansi. Komanso asamalire dziko lonse lapansi.”+ 27 Choncho Mulungu analenga munthu mʼchifaniziro chake, mʼchifaniziro cha Mulungu analenga munthu. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+ 28 Komanso, Mulungu anawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi+ ndipo muziliyangʼanira.+ Muyangʼanirenso+ nsomba zamʼnyanja ndi zamoyo zouluka mumlengalenga, komanso chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.”

29 Kenako Mulungu anati: “Ndakupatsani zomera zonse zimene zili padziko lapansi zobereka mbewu komanso mitengo yonse yobereka zipatso zokhala ndi nthangala kuti zikhale chakudya chanu.+ 30 Ndapereka zomera zonse kuti zikhale chakudya+ cha nyama iliyonse yamʼtchire padziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga komanso chokwawa chilichonse chapadziko lapansi chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinaterodi.

31 Pambuyo pa zimenezi Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.+ Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 6.

2 Choncho Mulungu anamaliza kulenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo.+ 2 Pofika tsiku la 7, Mulungu anali atamaliza ntchito imene ankagwira. Pa tsiku la 7 limeneli, iye anayamba kupuma pa ntchito yonse imene ankagwira.+ 3 Kenako Mulungu anadalitsa tsiku la 7 komanso ananena kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli wakhala akupuma pa ntchito yake yonse. Pamenepa Mulungu anali atamaliza kulenga zinthu zonse zimene ankafuna.

4 Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalili pa nthawi imene zinkalengedwa, pa tsiku limene Yehova* Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.+

5 Padziko lapansi panalibe tchire ndi zomera zina, chifukwa Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula padziko lapansi komanso panalibe munthu woti nʼkulima nthaka. 6 Koma nkhungu* inkakwera mʼmwamba kuchokera padziko lapansi, ndipo inkanyowetsa nthaka yonse.

7 Kenako Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kudothi,*+ ndipo anauzira mpweya wa moyo+ mumphuno mwake, munthuyo nʼkukhala wamoyo.+ 8 Zitatero Yehova Mulungu anadzala munda ku Edeni,+ chakumʼmawa, ndipo mʼmundamo anaikamo munthu amene anamuumba uja.+ 9 Choncho Yehova Mulungu anameretsa munthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino komanso wazipatso zabwino kudya. Anameretsanso mtengo wa moyo+ pakati pa mundawo komanso mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.+

10 Mu Edeni munali mtsinje umene unkathirira mundawo. Potuluka mʼmundawo, mtsinjewo unagawikana nʼkukhala mitsinje 4. 11 Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni. Mtsinjewu umazungulira dera lonse la Havila kumene kuli golide. 12 Golide wamʼdera limeneli ndi wabwino. Kulinso utomoni wonunkhira wa bedola ndi miyala yamtengo wapatali ya onekisi. 13 Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni. Mtsinje umenewu umazungulira dera lonse la Kusi. 14 Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidekeli.*+ Mtsinjewu umalowera kumʼmawa kwa Asuri.+ Ndipo mtsinje wa 4 ndi Firate.+

15 Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja nʼkumuika mʼmunda wa Edeni kuti aziulima komanso kuusamalira.+ 16 Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa mʼmundamu uzidya mmene ungafunire.+ 17 Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadye, udzafa ndithu.”+

18 Kenako Yehova Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu azikhala yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.”+ 19 Ndiyeno Yehova Mulungu anaumba ndi dothi nyama iliyonse yakutchire komanso chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga ndipo anazipititsa kwa munthuyo kuti azipatse mayina. Dzina lililonse limene munthuyo anapatsa chamoyo chilichonse linakhaladi dzina lake.+ 20 Munthuyo anapereka mayina kwa nyama zonse zoweta, ndiponso zamoyo zonse zouluka mumlengalenga, komanso nyama iliyonse yakutchire. Koma munthuyo analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera. 21 Choncho Yehova Mulungu anagonetsa munthuyo tulo tofa nato. Munthuyo ali mʼtulo, Mulungu anamuchotsa nthiti imodzi kenako nʼkutseka pamalopo. 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anapanga mkazi kuchokera kunthiti imene anaichotsa kwa mwamunayo. Atatero, anamupititsa kwa iye.+

23 Ndiyeno mwamunayo anati:

“Tsopano uyu ndi fupa la mafupa anga

Komanso mnofu wa mnofu wanga.

Ameneyu azitchedwa Mkazi,

Chifukwa anachokera kwa mwamuna.”+

24 Chifukwa cha zimenezi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake* ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.+ 25 Choncho onsewo, mwamuna ndi mkazi wakeyo, ankakhala maliseche+ koma sankachita manyazi.

3 Tsopano njoka+ inali yochenjera kwambiri kuposa nyama zonse zakutchire zimene Yehova Mulungu anapanga. Ndipo njokayo inafunsa mkaziyo kuti: “Eti nʼzoona kuti Mulungu ananena kuti musadye zipatso za mtengo uliwonse wamʼmundamu?”+ 2 Mkaziyo anayankha njokayo kuti: “Anatiuza kuti tingathe kudya zipatso za mitengo yamʼmundamu.+ 3 Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda,+ Mulungu ananena kuti: ‘Musadye zipatso zake, ndipo musayerekeze kuukhudza, chifukwa mukatero mudzafa.’” 4 Kenako njokayo inauza mkaziyo kuti: “Si zoona zimenezo, simudzafa ayi.+ 5 Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.”+

6 Mkaziyo atamva zimenezo, anayamba kuona kuti zipatso za mtengowo nʼzokoma kudya, zosiririka komanso zooneka bwino. Choncho anathyola chipatso cha mtengowo nʼkudya.+ Kenako anatenga zina nʼkukapatsa mwamuna wake pa nthawi imene anali limodzi, ndipo nayenso anadya.+ 7 Atatero onse maso awo anatseguka ndipo anazindikira kuti ali maliseche. Choncho anasoka masamba a mkuyu nʼkuwamangirira mʼchiuno mwawo.+

8 Pambuyo pake, iwo anamva mawu a Yehova Mulungu pamene iye ankayendayenda mʼmundamo pa nthawi imene kamphepo kayeziyezi kankaomba. Mwamuna ndi mkaziyo atamva, anabisala pakati pa mitengo ya mʼmundamo kuti Yehova Mulungu asawaone. 9 Koma Yehova Mulungu anapitiriza kuitana mwamunayo kuti: “Kodi uli kuti?” 10 Kenako mwamunayo anayankha kuti: “Ndinamva kuitana kwanu mʼmunda muno, koma ndinachita mantha poona kuti ndili maliseche. Choncho ndinabisala.” 11 Ndiyeno Mulungu anati: “Wakuuza ndi ndani kuti uli maliseche?+ Kodi wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti usadzadye uja?”+ 12 Mwamunayo anayankha kuti: “Mkazi amene munandipatsayu ndi amene wandipatsa chipatso cha mtengowo, ndipo ine ndadya.” 13 Ndiyeno Yehova Mulungu anafunsa mkaziyo kuti: “Ndiye chiyani wachitachi?” Mkaziyo anayankha kuti: “Njoka ndi imene yandipusitsa, ndipo ine ndadya.”+

14 Zitatero Yehova Mulungu anauza njokayo kuti:+ “Chifukwa cha zimene wachitazi, ukhala wotembereredwa pa nyama zonse zoweta ndi zakutchire. Udzakwawa ndi mimba yako ndipo udzadya fumbi masiku onse a moyo wako. 15 Ndidzaika chidani+ pakati pa iwe+ ndi mkaziyo,+ komanso pakati pa mbadwa* yako+ ndi mbadwa yake.+ Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako,+ ndipo iwe udzaivulaza chidendene.”+

16 Ndiyeno Mulungu anauza mkaziyo kuti: “Ndidzawonjezera kwambiri kuvutika kwako pa nthawi imene uli woyembekezera. Ndipo pobereka ana udzamva ululu. Uzidzafunitsitsa kukhala ndi mwamuna wako, ndipo iye azidzakulamulira.”

17 Kenako Mulungu anauza Adamu* kuti: “Popeza wamvera mawu a mkazi wako, ndipo wadya chipatso cha mtengo umene ndinakulamula kuti,+ ‘Usadzadye zipatso zake,’ nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha zimene wachitazi.+ Udzavutika kulima nthakayo masiku onse a moyo wako+ kuti upeze chakudya. 18 Minga ndi zitsamba zobaya zidzamera panthaka, ndipo chakudya chako chidzakhala zomera zamʼnthaka. 19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+

20 Pambuyo pa zimenezi, Adamu anapatsa mkazi wake dzina lakuti Hava,* chifukwa anali woti adzakhala mayi wa anthu onse.+ 21 Kenako Yehova Mulungu anapangira Adamu ndi mkazi wake zovala zazitali zachikopa, nʼkuwaveka.+ 22 Ndiyeno Yehova Mulungu anati: “Tsopano munthu wakhala ngati ife chifukwa wadziwa zabwino ndi zoipa.+ Choncho kuti asathyolenso ndi kudya chipatso cha mtengo wa moyo,+ nʼkukhala ndi moyo mpaka kalekale,—”* 23 Atatero Yehova Mulungu anatulutsa munthuyo mʼmunda wa Edeni,+ kuti akalime nthaka imene anatengedwako.+ 24 Choncho anathamangitsa munthuyo mʼmundamo, nʼkuika akerubi+ kumʼmawa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linkazungulira nthawi zonse, kutchinga njira yopita kumtengo wa moyo.

4 Kenako Adamu anagona ndi mkazi wake Hava ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera.+ Mkaziyo atabereka Kaini*+ ananena kuti: “Ndabereka mwana wamwamuna mothandizidwa ndi Yehova.” 2 Pambuyo pake, Hava anabereka Abele+ mʼbale wake wa Kaini.

Abele anali mʼbusa wa ziweto, koma Kaini anali mlimi. 3 Patapita nthawi, Kaini anabweretsa zina mwa zokolola zake zakumunda nʼkuzipereka nsembe kwa Yehova. 4 Koma Abele anabweretsa ana oyamba a ziweto zake+ nʼkuwapereka nsembe, ndipo anaperekanso nsembe mafuta a ziwetozo. Yehova anasangalala ndi Abele komanso nsembe yake.+ 5 Koma sanasangalale ndi Kaini komanso nsembe yake ngakhale pangʼono. Choncho Kaini anapsa mtima kwambiri ndipo nkhope yake inagwa chifukwa cha chisoni. 6 Ndiyeno Yehova anafunsa Kaini kuti: “Nʼchifukwa chiyani wapsa mtima choncho, komanso nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni? 7 Utasintha nʼkumachita zinthu zabwino, kodi sindingayambirenso kusangalala nawe? Koma ngati susintha nʼkumachita zinthu zabwino, uchimo wakubisalira pakhomo, ndipo ukufunitsitsa kukumbwandira. Kodi iweyo suyesetsa kuti uwugonjetse?”

8 Kenako Kaini anauza Abele mʼbale wake kuti: “Tiye tipite kunkhalango.” Ali kunkhalangoko, Kaini anamenya Abele mʼbale wake nʼkumupha.+ 9 Pambuyo pake, Yehova anafunsa Kaini kuti: “Kodi mʼbale wako Abele ali kuti?” Iye anayankha kuti: “Sindikudziwa. Kodi ndine mlonda wa mʼbale wangayo?” 10 Pamenepo Mulungu anati: “Nʼchiyani chimene wachitachi? Tamvetsera, magazi a mʼbale wako akundilirira munthaka.+ 11 Tsopano ndiwe wotembereredwa, ndipo ndikukuthamangitsa mʼdera limene nthaka yake yatsegula pakamwa nʼkulandira magazi a mʼbale wako, amene iwe wakhetsa ndi manja ako.+ 12 Uziti ukalima nthaka, suzikolola mokwanira. Udzakhala moyo woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi.” 13 Kaini atamva zimenezi anauza Yehova kuti: “Chilango cha kulakwa kwanga nʼchachikulu kwambiri moti sindingathe kuchipirira. 14 Lero mukundithamangitsa pamalo ano ndipo sindidzathanso kukuyandikirani. Ndidzakhala woyendayenda ndi wothawathawa padziko lapansi, ndipo aliyense wondipeza, ndithu adzandipha.” 15 Ndiyeno Yehova anauza Kaini kuti: “Chifukwa cha zimene wanenazi, aliyense amene adzaphe iweyo Kaini, adzalangidwa maulendo 7.”

Choncho Yehova anaikira Kaini chizindikiro* kuti aliyense womupeza asamuphe. 16 Kenako Kaini anachoka pamaso pa Yehova nʼkupita kukakhala kudera la Nodi,* kumʼmawa kwa Edeni.+

17 Patapita nthawi, Kaini anagona ndi mkazi wake+ ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nʼkubereka Inoki. Ndiyeno Kaini anayamba kumanga mzinda umene anaupatsa dzina la mwana wake lakuti Inoki. 18 Kenako Inoki anabereka Irade, Irade anabereka Mehuyaeli, Mehuyaeli anabereka Metusaeli, ndipo Metusaeli anabereka Lameki.

19 Lameki anakwatira akazi awiri. Woyamba anali Ada ndipo wachiwiri anali Zila. 20 Ada anabereka Yabala. Yabala anali munthu woyamba kukhala mʼmatenti nʼkumaweta ziweto. 21 Dzina la mʼbale wake wa Yabala linali Yubala. Yubala anali munthu woyamba pa anthu onse oimba zeze ndi chitoliro. 22 Komanso Zila anabereka Tubala-kaini, amene anali mmisiri wosula zipangizo zamtundu uliwonse zakopa ndi zachitsulo. Ndipo mlongo wake wa Tubala-kaini anali Naama. 23 Kenako Lameki ananena ndakatulo iyi kwa akazi ake, Ada ndi Zila:

“Tamverani mawu anga inu akazi a Lameki.

Tcherani khutu ku zonena zanga:

Ndapha munthu chifukwa chondivulaza,

Ndaphadi mnyamata chifukwa chondimenya.

24 Ngati wopha Kaini adzalangidwe+ maulendo 7,

Ndiye kuti wopha Lameki, adzalangidwa maulendo 77.”

25 Adamu anagonanso ndi mkazi wake Hava ndipo anabereka mwana wamwamuna. Hava anapatsa mwanayo dzina lakuti Seti*+ chifukwa atabadwa, Havayo ananena kuti: “Mulungu wandipatsa* mwana wina mʼmalo mwa Abele amene Kaini anamupha.”+ 26 Nayenso Seti anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Enosi.+ Pa nthawi imeneyi, anthu anayamba kuitanira pa dzina la Yehova.

5 Ili ndi buku la mbiri ya Adamu. Pa tsiku* limene Mulungu analenga Adamu, anamupanga mʼchifaniziro cha Mulungu.+ 2 Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Pa tsiku limene anawalengalo,+ anawadalitsa nʼkuwatchula dzina lakuti Anthu.*

3 Adamu ali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamʼpatsa dzina lakuti Seti.+ 4 Adamu atabereka Seti, anakhala ndi moyo zaka 800, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 5 Choncho zaka zonse zimene Adamu anakhala ndi moyo zinakwana 930, kenako anamwalira.+

6 Seti ali ndi zaka 105, anabereka Enosi.+ 7 Atabereka Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka 807, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 8 Choncho Seti anakhala ndi moyo zaka 912, kenako anamwalira.

9 Enosi ali ndi zaka 90, anabereka Kenani. 10 Atabereka Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka 815, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11 Choncho Enosi anakhala ndi moyo zaka 905, kenako anamwalira.

12 Kenani ali ndi zaka 70, anabereka Mahalalele.+ 13 Atabereka Mahalalele, Kenani anakhala ndi moyo zaka 840, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Choncho Kenani anakhala ndi moyo zaka 910, kenako anamwalira.

15 Mahalalele ali ndi zaka 65, anabereka Yaredi.+ 16 Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhala ndi moyo zaka 830, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17 Choncho Mahalalele anakhala ndi moyo zaka 895, kenako anamwalira.

18 Yaredi ali ndi zaka 162, anabereka Inoki.+ 19 Atabereka Inoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka 800, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Choncho Yaredi anakhala ndi moyo zaka 962, kenako anamwalira.

21 Inoki ali ndi zaka 65, anabereka Metusela.+ 22 Atabereka Metusela, Inoki anapitiriza kuyenda ndi Mulungu woona kwa zaka 300, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23 Choncho Inoki anakhala ndi moyo zaka 365. 24 Inoki anayendabe ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anamutenga.+

25 Metusela ali ndi zaka 187, anabereka Lameki.+ 26 Atabereka Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka 782. Ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27 Choncho Metusela anakhala ndi moyo zaka 969, kenako anamwalira.

28 Lameki ali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29 Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Nowa,*+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yovuta komanso yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+ 30 Atabereka Nowa, Lameki anakhala ndi moyo zaka 595, ndipo anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31 Choncho Lameki anakhala ndi moyo zaka 777, kenako anamwalira.

32 Nowa atakwanitsa zaka 500 anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+

6 Anthu atayamba kuchuluka padziko lapansi, kunabadwa ana ambiri aakazi. 2 Ndiyeno ana a Mulungu woona*+ anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola. Choncho anayamba kutenga akazi alionse amene ankawafuna nʼkuwakwatira. 3 Kenako Yehova anati: “Ine sindipitiriza* kulezera mtima anthu mpaka kalekale,+ chifukwa ndi ochimwa. Choncho adzangokhala ndi moyo zaka 120 zokha.”*+

4 Kuyambira masiku amenewo kupita mʼtsogolo, padziko lapansi panali Anefili.* Pa nthawi imeneyo, ana a Mulungu woona anapitiriza kugona ndi ana aakazi a anthu ndipo anawaberekera ana. Anawo anali zianthu zamphamvu zimene zinalipo kalelo, amuna otchuka.

5 Choncho Yehova anaona kuti anthu aipa kwambiri padziko lapansi. Anaona kuti maganizo a anthu komanso zofuna za mtima wawo zinali zoipa zokhazokha nthawi zonse.+ 6 Yehova anamva chisoni kuti anapanga anthu padziko lapansi, ndipo zinamupweteka kwambiri mumtima.+ 7 Choncho Yehova anati: “Ndidzaseseratu padziko lapansi anthu amene ndinawalenga. Ndidzaseseratu anthu, nyama zoweta, nyama zokwawa komanso zamoyo zouluka mumlengalenga, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndinazipanga.” 8 Koma Yehova ankasangalala ndi Nowa.

9 Iyi ndi mbiri ya Nowa.

Nowa anali munthu wolungama.+ Iye anali wopanda cholakwa pakati pa anthu a mʼnthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.+ 10 Patapita nthawi, Nowa anabereka ana aamuna atatu, Semu, Hamu ndi Yafeti.+ 11 Koma dziko lapansi linali litaipa pamaso pa Mulungu woona, ndipo linadzaza ndi chiwawa. 12 Mulungu anayangʼana dziko lapansi ndipo anaona kuti laipa.+ Anthu onse padziko lapansi ankachita zinthu zoipa.+

13 Pambuyo pake, Mulungu anauza Nowa kuti: “Ndaganiza zowononga anthu onse, chifukwa apangitsa kuti dziko lapansi lidzaze ndi chiwawa. Choncho ndiwawononga limodzi ndi zonse zimene zili padziko lapansi.+ 14 Upange chingalawa pogwiritsa ntchito matabwa a mtengo wa mnjale.+ Uchigawe zipindazipinda ndipo uchimate ndi phula+ mkati ndi kunja komwe. 15 Uchipange chonchi: Mulitali chikhale mamita 134,* mulifupi mamita 22, ndipo kutalika kwake kuyambira pansi mpaka pamwamba chikhale mamita 13. 16 Chingalawacho uchiikire windo* kuti mkatimo muziwala. Kuchokera kudenga kufika pamene pali windolo pakhale mpata wa masentimita 44 ndi hafu. Khomo la chingalawacho uliike mʼmbali mwake.+ Chikhale ndi zipinda zosanjikiza zitatu, chapansi, chapakati ndi chapamwamba.

17 Ine ndidzabweretsa chigumula+ padziko lapansi kuti chiwononge chamoyo chilichonse cha pansi pa thambo, chimene chili ndi mpweya wa moyo* mʼthupi lake. Chilichonse chimene chili padziko lapansi chidzawonongedwa.+ 18 Ndikuchita pangano ndi iwe. Iweyo udzalowe mʼchingalawacho limodzi ndi ana ako, mkazi wako ndi akazi a ana ako.+ 19 Mʼchingalawacho udzalowetsemo chamoyo cha mtundu uliwonse.+ Udzazilowetse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi,+ kuti zidzasungike zamoyo limodzi ndi iwe. 20 Udzalowe nazo ziwiriziwiri za mtundu uliwonse. Zolengedwa zouluka monga mwa mitundu yawo, nyama zoweta monga mwa mitundu yawo, nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yawo, kuti zidzasungike zamoyo.+ 21 Udzasonkhanitse chakudya+ cha mtundu uliwonse nʼkuchilowetsa mʼchingalawamo kuti chidzakhale chakudya chanu ndi cha zinyama.”

22 Ndipo Nowa anachita zonse mogwirizana ndi zimene Mulungu anamulamula. Anachitadi zomwezo.+

7 Kenako Yehova anauza Nowa kuti: “Lowa mʼchingalawacho, iwe ndi banja lako, chifukwa iwe ndi amene ndakuona kuti ndiwe wolungama pakati pa mʼbadwo uwu.+ 2 Pa nyama zosadetsedwa zamtundu uliwonse utengepo zokwanira 7,*+ yaimuna ndi yaikazi yake. Koma pa nyama zodetsedwa zilizonse utengepo ziwiri zokha, yaimuna ndi yaikazi yake. 3 Komanso pa zamoyo zilizonse zouluka mumlengalenga, utengepo zokwanira 7,* chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike padziko lonse lapansi.+ 4 Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula+ padziko lapansi kwa masiku 40, masana ndi usiku.+ Ndipo ndidzaseseratu padziko lapansi chamoyo chilichonse chimene ndinachipanga.”+ 5 Choncho Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamula.

6 Nowa anali ndi zaka 600 pamene chigumula chinachitika padziko lapansi.+ 7 Choncho chigumulacho chisanayambe, Nowa analowa mʼchingalawacho, limodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake.+ 8 Nyama zilizonse zosadetsedwa, nyama zilizonse zodetsedwa, zamoyo zilizonse zouluka komanso zilizonse zoyenda panthaka,+ 9 zinalowa ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa, yaimuna ndi yaikazi, monga mmene Mulungu analamulira Nowa. 10 Ndiyeno patapita masiku 7, kunayamba kugwa chimvula ndipo madzi anayamba kudzaza padziko lapansi.

11 Mʼchaka cha 600 cha moyo wa Nowa, mʼmwezi wachiwiri,* pa tsiku la 17 la mweziwo, pa tsiku limeneli madzi onse akumwamba anaphulika ndipo zitseko zotchingira madzi akumwamba zinatseguka.+ 12 Ndiyeno chimvula chinakhuthuka padziko lapansi kwa masiku 40 masana ndi usiku. 13 Pa tsiku limenelo Nowa analowa mʼchingalawacho. Analowa limodzi ndi ana ake Semu, Hamu ndi Yafeti,+ ndiponso mkazi wake ndi akazi atatu a ana akewo.+ 14 Iwo analowa limodzi ndi nyama zakutchire zamtundu uliwonse, nyama zoweta zamtundu uliwonse, nyama zokwawa* zapadziko lapansi zamtundu uliwonse, zamoyo zouluka zamtundu uliwonse, mbalame zilizonse ndiponso zamoyo zilizonse zamapiko. 15 Zamoyo zamtundu uliwonse zokhala ndi mpweya wa moyo* mʼthupi mwake, zinkapita ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa. 16 Choncho zamoyo zamtundu uliwonse, zazimuna ndi zazikazi, zinalowa mʼchingalawamo mogwirizana ndi mmene Mulungu analamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko.

17 Chimvulacho chinapitiriza kugwa padziko lapansi kwa masiku 40. Madziwo anachulukirachulukira ndipo anayamba kunyamula chingalawacho, moti chinkayandama pamwamba pa dziko lapansi. 18 Madziwo anapitiriza kuwonjezeka kwambiri padziko lapansi, ndipo chingalawacho chinkayandama pamwamba pa madzi. 19 Madziwo anawonjezeka kwambiri padziko lapansi moti mapiri onse ataliatali amene anali pansi pa thambo anamira.+ 20 Madziwo anakwera kwambiri kupitirira mapiriwo ndi mamita pafupifupi 6 ndi hafu.*

21 Choncho zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, monga zamoyo zouluka, nyama zoweta, nyama zakutchire, ndiponso tizilombo tonse tingʼonotingʼono toyenda mʼmagulu, zinafa+ pamodzi ndi anthu onse.+ 22 Chilichonse chapadziko lapansi chokhala ndi mpweya wa moyo mʼmphuno mwake, chinafa.+ 23 Choncho Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu, nyama, nyama zokwawa komanso zamoyo zouluka mumlengalenga. Zonsezi anazisesa padziko lapansi.+ Nowa yekha komanso amene anali naye limodzi mʼchingalawacho, anapulumuka.+ 24 Ndipo dziko lapansi linamirabe mʼmadzi kwa masiku 150.+

8 Koma Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakutchire ndiponso nyama zonse zoweta zimene anali nazo mʼchingalawa chija.+ Ndiyeno Mulungu anachititsa kuti chimphepo chiwombe padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kuchepa. 2 Madzi onse akumwamba anasiya kutuluka komanso zitseko zotchingira madziwo zinatsekeka, choncho chimvula chinasiya kugwa kuchokera kumwamba.+ 3 Kenako madzi anayamba kuchepa pangʼonopangʼono padziko lapansi. Pamene masiku 150 ankatha, madziwo anali atachepa ndithu. 4 Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 17 la mweziwo, chingalawacho chinaima pamapiri a Ararati. 5 Madzi anapitirizabe kuchepa mpaka mwezi wa 10. Mʼmwezi wa 10 umenewo, pa tsiku loyamba la mweziwo, nsonga za mapiri zinaonekera.+

6 Ndiyeno patatha masiku 40, Nowa anatsegula windo+ limene anaika pa chingalawacho 7 ndipo anatumiza khwangwala. Choncho khwangwalayo ankangouluka kunja nʼkumabwerera kuchingalawacho mpaka madzi ataphwa padziko lapansi.

8 Kenako, Nowa anatumiza njiwa kuti aone ngati madzi anaphwa padziko lapansi. 9 Koma njiwayo sinapeze malo alionse oti nʼkuterapo. Choncho, inabwerera kwa iye mʼchingalawamo chifukwa madzi anali asanaphwe padziko lonse lapansi.+ Itabwerera, iye anatulutsa dzanja lake, nʼkuitenga ndipo anailowetsa mʼchingalawamo. 10 Anadikirabe masiku ena 7, kenako anatumizanso njiwa ija kuchokera mʼchingalawamo. 11 Njiwayo itabwerera kwa iye chakumadzulo, anaona kuti ili ndi tsamba laliwisi kukamwa kwake. Tsambalo linali la mtengo wa maolivi longothyoledwa kumene. Nowa ataona zimenezi, anadziwa kuti madzi anali ataphwa padziko lapansi.+ 12 Anadikiranso masiku ena 7. Kenako anatumizanso njiwa ija koma sinabwererenso kwa iye.

13 Tsopano mʼchaka cha 601 cha Nowa,+ mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, madzi anali ataphwa padziko lapansi. Nowa anatsegula chibowo chimene chinali padenga la chingalawacho nʼkuyangʼana kunja ndipo anaona kuti nthaka yayamba kuuma. 14 Mʼmwezi wachiwiri, pa tsiku la 27 la mweziwo, nthaka inali itaumiratu.

15 Ndiyeno Mulungu anauza Nowa kuti: 16 “Tsopano tulukani mʼchingalawamo, iweyo, mkazi wako, ana ako ndi akazi a ana ako.+ 17 Utuluke limodzi ndi zamoyo zamtundu uliwonse+ zimene uli nazo. Utuluke limodzi ndi zamoyo zouluka, zinyama ndi zonse zokwawa padziko lapansi, kuti zichulukane padziko lapansi, ziberekane ndipo zikhale zambiri padziko lapansi.”+

18 Choncho Nowa anatuluka limodzi ndi ana ake,+ mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Komanso, zamoyo zilizonse, nyama zilizonse zokwawa, zamoyo zouluka zilizonse, chilichonse chimene chimayenda padziko lapansi, zinatuluka mʼchingalawamo monga mwa magulu awo.+ 20 Kenako Nowa anamangira Yehova guwa lansembe.+ Atatero, anatenga zina mwa nyama zonse zosadetsedwa, ndi zina mwa zouluka zonse zosadetsedwa,+ nʼkuzipereka nsembe yopsereza paguwapo.+ 21 Ndiyeno Yehova anayamba kumva fungo losangalatsa.* Choncho Yehova ananena mumtima mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira ali ana.+ Ndipo sindidzaphanso chamoyo chilichonse ngati mmene ndachitiramu.+ 22 Kuyambira pano mpaka mʼtsogolo, kudzala mbewu ndi kukolola sikudzatha padziko lapansi. Ndiponso nyengo yozizira ndi yotentha, chilimwe ndi chisanu, masana ndi usiku, zidzakhalapobe.”+

9 Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke ndipo mudzaze dziko lapansi.+ 2 Chamoyo chilichonse chapadziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga, chilichonse chokwawa padziko lapansi, ndi nsomba zonse zamʼnyanja, zidzapitiriza kukuopani. Tsopano ndapereka zonsezi mʼmanja mwanu.*+ 3 Mukhoza kudya chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.+ Monga mmene ndinakupatsirani zomera zonse kuti zikhale chakudya chanu, ndikukupatsaninso zonsezi.+ 4 Koma musadye+ nyama limodzi ndi magazi ake,+ chifukwa magaziwo ndi moyo wake. 5 Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene adzakupheni* ndidzamupatsa chilango. Ngati chamoyo chilichonse chapha munthu, chamoyocho chidzaphedwanso. Ndipo munthu aliyense wochotsa moyo wa mʼbale wake, ndidzamupatsa chilango.+ 6 Aliyense wopha munthu, nayenso adzaphedwa ndi munthu,*+ chifukwa Mulungu anapanga munthu mʼchifaniziro chake.+ 7 Koma inuyo muberekane ndi kuchuluka kwambiri, ndipo mudzaze padziko lonse lapansi.”+

8 Kenako Mulungu anauza Nowa ndi ana ake kuti: 9 “Tsopano ine ndikuchita pangano ndi inu+ komanso mibadwo yobwera pambuyo panu. 10 Ndikuchitanso panganoli ndi chamoyo chamtundu uliwonse chimene muli nacho limodzi, monga mbalame, zinyama komanso zamoyo zonse zapadziko lapansi, kutanthauza zonse zimene zinatuluka mʼchingalawa, kapena kuti chamoyo chilichonse chapadziko lapansi.+ 11 Pangano limene ndikuchita nanu ndi ili: Zamoyo zonse sizidzawonongedwanso ndi chigumula, ndipo chigumula sichidzachitikanso nʼkuwononga dziko lapansi.”+

12 Mulungu anawonjezera kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ndikuchita ndi inu komanso ndi chamoyo chilichonse chimene muli nacho, mpaka mibadwo yonse ya mʼtsogolo. 13 Ndaika utawaleza wanga mumtambo, ndipo ukhala chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi dziko lapansi. 14 Ndikabweretsa mtambo padziko lapansi, utawaleza udzaonekeranso mumtambowo. 15 Ndizikumbukira ndithu pangano limene ndachita ndi inu komanso ndi chamoyo cha mtundu uliwonse. Ndipo chigumula sichidzachitikanso nʼkuwononga zamoyo zonse.+ 16 Utawalezawo udzaonekera mumtambo, ndipo ndikauona ndizikumbukira pangano limene lidzakhale mpaka kalekale, pakati pa ine ndi chamoyo cha mtundu uliwonse chimene chili padziko lapansi.”

17 Mulungu anabwereza kuuza Nowa kuti: “Ichi ndi chizindikiro cha pangano limene ine ndikukhazikitsa ndi zamoyo zonse zimene zili padziko lapansi.”+

18 Ana a Nowa amene anatuluka mʼchingalawa anali Semu, Hamu ndi Yafeti.+ Patapita nthawi, Hamu anabereka Kanani.+ 19 Ana a Nowa anali atatu amenewa, ndipo anthu onse anachokera kwa iwowa nʼkufalikira padziko lonse lapansi.+

20 Tsopano Nowa anayamba ulimi, ndipo analima munda wa mpesa. 21 Tsiku lina Nowa anamwa vinyo nʼkuledzera, ndipo ali mutenti yake, anavula zovala zake. 22 Ndiyeno Hamu, bambo ake a Kanani, anaona maliseche a bambo ake. Atatero, anapita panja nʼkukauza abale ake awiri aja. 23 Atamva zimenezo, Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nʼkuchiika pamapewa awo ndipo anayenda chafutambuyo. Atalowa mutentimo, anafunditsa bambo awo nʼkuwabisa maliseche, iwo akuyangʼana kumbali moti sanaone maliseche a bambo awo.

24 Vinyo atamuthera mʼmutu mwake, Nowa anadzuka ndipo anamva zimene mwana wake wamngʼono anachita. 25 Ndiyeno iye anati:

“Kanani+ akhale wotembereredwa.

Akhale kapolo wotsika kwambiri wa abale ake.”+

26 Anawonjezera kuti:

“Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu,

Ndipo Kanani akhale kapolo wa Semu.+

27 Mulungu apereke malo aakulu kwa Yafeti,

Ndipo azikhala mʼmatenti a Semu.

Koma Kanani akhalenso kapolo wa Yafeti.”

28 Pambuyo pa Chigumula,+ Nowa anakhalabe ndi moyo zaka zina 350. 29 Choncho Nowa anakhala ndi moyo zaka 950, kenako anamwalira.

10 Iyi ndi mbiri ya ana a Nowa, omwe ndi Semu,+ Hamu ndi Yafeti.

Iwowa anabereka ana pambuyo pa Chigumula.+ 2 Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai, Yavani, Tubala,+ Meseki+ ndi Tirasi.+

3 Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati ndi Togarima.+

4 Ana a Yavani anali Elisha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.

5 Mwa anthu amenewa, munachokera anthu okhala mʼzilumba amene anafalikira mʼzilumbazo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.

6 Ana a Hamu anali Kusi, Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+

7 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka.

Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.

8 Kusi anabereka Nimurodi, amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi. 9 Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova. Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova.” 10 Ufumu wake unayambira ku* Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline mʼdziko la Sinara.+ 11 Atachoka mʼdzikolo analowera ku Asuri+ ndipo anamangako Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12 komanso Resene pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu ndi mzinda waukulu.*

13 Miziraimu anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14 Patirusimu,+ Kasiluhimu (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu) ndiponso Kafitorimu.+

15 Kanani anabereka Sidoni,+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16 Analinso kholo la Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17 Ahivi,+ Aariki, Asini, 18 Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19 Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ nʼkukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20 Amenewa ndi omwe anali ana a Hamu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo, mayiko awo komanso mitundu yawo.

21 Nayenso Semu anabereka ana ndipo anakhala kholo la ana onse a Ebere.+ Semu anali mngʼono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse.* 22 Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.+

23 Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi.

24 Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere.

25 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa mʼmasiku ake dziko lapansi linagawanika.* Mʼbale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+

26 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27 Hadoramu, Uzali, Dikila, 28 Obali, Abimaele, Sheba, 29 Ofiri,+ Havila ndi Yobabi. Onsewa anali ana a Yokitani.

30 Dziko limene ankakhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kumʼmawa.

31 Amenewa ndi ana a Semu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo komanso malinga ndi mayiko awo ndi mitundu yawo.+

32 Mabanja a ana a Nowa ndi amenewa malinga ndi mibadwo yawo komanso mitundu yawo. Kuchokera mwa anthu amenewa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa Chigumula.+

11 Tsopano dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi ndipo anthu ankagwiritsa ntchito mawu ofanana. 2 Pamene anthuwo ankalowera chakumʼmawa, anapeza chigwa mʼdera la Sinara+ ndipo anayamba kukhala kumeneko. 3 Kenako anauzana kuti: “Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche.” Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa mʼmalo mwa miyala, nʼkumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira. 4 Ndiyeno anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike mʼmwamba mwenimweni. Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo, ndipo sitimwazikana padziko lonse lapansi.”+

5 Kenako Yehova anapita kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anamanga. 6 Ndiyeno Yehova anati: “Taonani! Izi nʼzimene anthuwa ayamba kuchita, popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi.+ Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza. 7 Tiyeni+ tipite komweko nʼkukasokoneza chilankhulo chawo* kuti asamamvane polankhula.” 8 Choncho Yehova anawabalalitsa pamalopo moti anafalikira padziko lonse lapansi.+ Pangʼono ndi pangʼono iwo anasiya kumanga mzindawo. 9 Mzindawo unatchedwa Babele,*+ chifukwa kumeneko Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira anthuwo padziko lonse lapansi.

10 Iyi ndi mbiri ya Semu.+

Semu anali ndi zaka 100 pamene anabereka Aripakisadi,+ patatha zaka ziwiri chigumula chitachitika. 11 Atabereka Aripakisadi, Semu anakhalabe ndi moyo zaka zina 500. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.+

12 Aripakisadi ali ndi zaka 35, anabereka Shela.+ 13 Atabereka Shela, Aripakisadi anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

14 Shela ali ndi zaka 30, anabereka Ebere.+ 15 Atabereka Ebere, Shela anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

16 Ebere ali ndi zaka 34, anabereka Pelegi.+ 17 Atabereka Pelegi, Ebere anakhalabe ndi moyo zaka zina 430. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

18 Pelegi ali ndi zaka 30, anabereka Reu.+ 19 Atabereka Reu, Pelegi anakhalabe ndi moyo zaka zina 209. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

20 Reu ali ndi zaka 32, anabereka Serugi. 21 Atabereka Serugi, Reu anakhalabe ndi moyo zaka zina 207. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

22 Serugi ali ndi zaka 30, anabereka Nahori. 23 Atabereka Nahori, Serugi anakhalabe ndi moyo zaka zina 200. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

24 Nahori ali ndi zaka 29, anabereka Tera.+ 25 Atabereka Tera, Nahori anakhalabe ndi moyo zaka zina 119. Ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

26 Tera anakhala ndi moyo zaka 70, kenako anabereka Abulamu,+ Nahori+ ndi Harana.

27 Mbiri ya Tera ndi iyi.

Tera anabereka Abulamu, Nahori ndi Harana. Harana anabereka Loti.+ 28 Pambuyo pake, Harana anamwalira mumzinda wa Uri+ womwe ndi wa Akasidi,+ kumene anabadwira. Anamwalira bambo ake Tera ali ndi moyo. 29 Abulamu ndi Nahori anakwatira. Mkazi wa Abulamu anali Sarai,+ pamene mkazi wa Nahori anali Milika,+ mwana wa Harana. Harana analinso bambo ake a Yisika. 30 Koma Sarai anali wosabereka,+ ndipo analibe mwana.

31 Kenako Tera anatenga mwana wake Abulamu, mdzukulu+ wake Loti mwana wa Harana ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abulamu, nʼkuchoka mumzinda wa Uri womwe ndi wa Akasidi kupita kudziko la Kanani.+ Patapita nthawi anafika ku Harana+ ndipo anayamba kukhala kumeneko. 32 Choncho Tera anakhala ndi moyo zaka 205. Kenako anamwalira ku Harana.

12 Yehova anauza Abulamu kuti: “Samuka mʼdziko lako ndi kuchoka pakati pa abale ako ndipo usiye nyumba ya bambo ako. Upite kudziko limene ndidzakuonetse.+ 2 Ndidzakupangitsa kuti ukhale mtundu waukulu. Ndidzakudalitsa ndipo ndidzapangitsa kuti dzina lako litchuke. Komanso anthu ena adzadalitsidwa chifukwa cha iwe.+ 3 Odalitsa iwe ndidzawadalitsa, ndipo wotemberera iwe ndidzamutemberera.+ Mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa* kudzera mwa iwe.”+

4 Choncho Abulamu ananyamuka monga mmene Yehova anamuuzira, ndipo Loti ananyamuka naye limodzi. Pamene ankachoka ku Harana, Abulamu anali ndi zaka 75.+ 5 Abulamu anatenga mkazi wake Sarai,+ Loti mwana wa mʼbale+ wake ndi chuma chawo chonse+ komanso akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana. Iwo ananyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani.+ Atafika ku Kanani, 6 Abulamu anadutsa mʼdzikolo mpaka kukafika ku Sekemu,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More.+ Pa nthawiyo nʼkuti Akanani akukhala mʼdzikomo. 7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu nʼkumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbadwa* zako.”+ Choncho Abulamu anamanga guwa lansembe pamalo amene Yehova anaonekera kwa iye. 8 Patapita nthawi, anasamuka pamalopo nʼkupita kudera lamapiri, kumʼmawa kwa Beteli.+ Kumeneko iye anamanga tenti yake. Beteli anali kumadzulo kwake ndipo Ai+ anali kumʼmawa kwake. Kenako anamangira Yehova guwa lansembe+ nʼkuyamba kuitana pa dzina la Yehova.+ 9 Pambuyo pake Abulamu anasamutsa tenti yake kumeneko. Kuyambira pa nthawi imeneyi, iye ankangokhalira kumanga ndi kusamutsa msasa, kulowera ku Negebu.+

10 Tsopano mʼdzikolo munali njala, ndipo Abulamu ananyamuka kupita ku Iguputo kukakhala kumeneko kwa kanthawi,*+ chifukwa njalayo inafika poipa kwambiri mʼdzikolo.+ 11 Atatsala pangʼono kulowa mʼdziko la Iguputo anauza mkazi wake Sarai kuti: “Ndikudziwa kuti ndiwe mkazi wokongola.+ 12 Choncho Aiguputo akakuona, mosakayikira anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha koma iweyo akusiya wamoyo. 13 Ndiye chonde, unene kuti ndiwe mchemwali wanga kuti zindiyendere bwino. Ukatero upulumutsa moyo wanga.”+

14 Choncho Abulamu atangolowa mu Iguputo, Aiguputo anaonadi kuti mkaziyo ndi wokongola kwambiri. 15 Nawonso akalonga a Farao anamuona ndipo anakauza Farao kuti mkaziyo ndi wokongola. Choncho mkaziyo anatengedwa nʼkupita naye kunyumba kwa Farao. 16 Farao anamusamalira bwino Abulamu chifukwa cha mkazi wake, moti anamupatsa nkhosa, ngʼombe, abulu aamuna ndi aakazi, antchito aamuna ndi aakazi komanso ngamila.+ 17 Ndiyeno Yehova anagwetsera Farao ndi onse amʼbanja lake miliri yoopsa chifukwa cha Sarai, mkazi wa Abulamu.+ 18 Choncho Farao ataona zimenezi anaitana Abulamu nʼkumufunsa kuti: “Nʼchiyani wachitachi? Nʼchifukwa chiyani sunandiuze kuti ndi mkazi wako? 19 Nʼchifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mchemwali wanga,’+ moti ndinatsala pangʼono kumutenga kukhala mkazi wanga? Eko mkazi wako. Mutenge uzipita!” 20 Choncho Farao analamula anyamata ake kuti aperekeze Abulamu ndi mkazi wake, limodzi ndi zonse zimene anali nazo.+

13 Choncho Abulamu anachoka ku Iguputo nʼkulowera ku Negebu.+ Iye anachoka limodzi ndi mkazi wake ndi zonse zimene anali nazo komanso Loti. 2 Abulamu anali ndi chuma chambiri. Anali ndi ziweto, siliva ndi golide.+ 3 Abulamu atachoka ku Negebu, ankamanga misasa malo osiyanasiyana nʼkumasamuka mpaka anakafika ku Beteli, kumene kunali tenti yake poyamba, pakati pa Beteli ndi Ai.+ 4 Kumeneko nʼkumene anamangako guwa lansembe poyamba paja. Atafika kumeneko Abulamu anaitanira pa dzina la Yehova.

5 Nayenso Loti, amene ankayenda limodzi ndi Abulamu, anali ndi nkhosa, ngʼombe komanso matenti. 6 Chifukwa choti katundu wawo anachuluka kwambiri, malo anawachepera moti sakanathanso kukhala limodzi. 7 Zimenezi zinapangitsa kuti pabuke mkangano pakati pa abusa a Abulamu ndi abusa a Loti. (Pa nthawiyo nʼkuti Akanani ndi Aperezi akukhala mʼdzikomo.)+ 8 Choncho Abulamu anauza Loti+ kuti: “Chonde, pasakhale mkangano uliwonse pakati pa ine ndi iwe, komanso pakati pa abusa anga ndi abusa ako, pajatu ndife pachibale. 9 Tiye tisiyane. Ukhoza kusankha mbali iliyonse ya dzikoli. Iwe ukapita kumanzere, ine ndipita kumanja, koma ukapita kumanja, ine ndipita kumanzere.” 10 Choncho Loti anakweza maso ake nʼkuona chigawo chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali ndi madzi ambiri. (Pa nthawiyi nʼkuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.) Chinali ngati munda wa Yehova+ komanso ngati dziko la Iguputo. 11 Kenako Loti anasankha chigawo chonse cha Yorodano, ndipo anasamutsira msasa wake kumʼmawa. Choncho iwo anasiyana. 12 Abulamu anapitiriza kukhala mʼdziko la Kanani, koma Loti anakakhala pakati pa mizinda yamʼchigawocho.+ Kenako anakamanga tenti yake pafupi ndi Sodomu. 13 Koma anthu a ku Sodomu anali oipa ndiponso ochimwa kwambiri pamaso pa Yehova.+

14 Abulamu atasiyana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo. 15 Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa zako,* kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 16 Ndidzachulukitsa mbadwa zako* ngati mchenga wapadziko lapansi. Choncho ngati munthu angathe kuwerenga mchengawo, ndiye kuti mbadwa zako* zidzatha kuwerengedwa.+ 17 Nyamuka, uyendere dziko lonselo, mʼlitali ndi mʼlifupi mwake, chifukwa ndidzalipereka kwa iwe.” 18 Choncho Abulamu anapitiriza kukhala mʼmatenti. Patapita nthawi, anakakhala pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure,+ ku Heburoni.+ Kumeneko, anamangira Yehova guwa lansembe.+

14 Mʼmasiku a Amarafele mfumu ya ku Sinara,+ Arioki mfumu ya ku Elasara, Kedorelaomere+ mfumu ya ku Elamu+ ndi Tidala mfumu ya ku Goimu, 2 mafumuwa anachita nkhondo ndi mafumu otsatirawa: Bera mfumu ya ku Sodomu,+ Birisa mfumu ya ku Gomora,+ Sinabi mfumu ya ku Adima, Semebere mfumu ya ku Zeboyimu+ ndi mfumu ya ku Bela, kapena kuti ku Zowari. 3 Mafumu 5 onsewa anasonkhanitsa asilikali awo pamodzi ku chigwa cha Sidimu,+ kapena kuti Nyanja Yamchere.*+

4 Mafumuwa anatumikira Kedorelaomere kwa zaka 12, koma mʼchaka cha 13 anamupandukira. 5 Choncho mʼchaka cha 14, Kedorelaomere limodzi ndi mafumu omwe anali naye, anapita nʼkukagonjetsa Arefai ku Asiteroti-karanaimu, Azuzi ku Hamu, Aemi+ ku Save-kiriyataimu, 6 ndi Ahori+ kuphiri lawo la Seiri,+ mpaka kukafika ku Eli-parana, kuchipululu. 7 Kenako anabwerera nʼkulowera ku Eni-misipati, kumene ndi ku Kadesi,+ ndipo analanda dera lonse la Aamaleki,+ komanso anagonjetsa Aamori+ omwe ankakhala ku Hazazoni-tamara.+

8 Pa nthawi imeneyi, mfumu ya ku Sodomu, mfumu ya ku Gomora, mfumu ya ku Adima, mfumu ya ku Zeboyimu, ndi mfumu ya ku Bela, kapena kuti Zowari, ananyamuka nʼkupita ku chigwa cha Sidimu. Kumeneko, iwo anaima mwa dongosolo lomenyera nkhondo kuti amenyane ndi 9 Kedorelaomere mfumu ya ku Elamu, Tidala mfumu ya ku Goimu, Amarafele mfumu ya ku Sinara, ndi Arioki mfumu ya ku Elasara.+ Panali mafumu 4 amene anamenyana ndi mafumu 5. 10 Kenako mafumu a Sodomu ndi Gomora anayamba kuthawa. Koma chigwa cha Sidimu chinali ndi maenje aphula ambirimbiri, choncho iwo pothawa ankagwera mʼmaenje amenewo. Amene anatsala anathawira kudera lamapiri. 11 Ndiyeno amene anapambanawo anatenga katundu yense wa ku Sodomu ndi Gomora, limodzi ndi chakudya chawo chonse nʼkumapita.+ 12 Anatenganso Loti mwana wa mʼbale wake wa Abulamu, amene ankakhala ku Sodomu.+ Komanso anatenga katundu wake nʼkupitiriza ulendo wawo.

13 Kenako munthu wina amene anathawa anafika kwa Abulamu Mheberi. Pa nthawiyo nʼkuti Abulamu akukhala* pakati pa mitengo ikuluikulu imene mwiniwake anali Mamure, yemwe anali wa Chiamori.+ Ameneyu anali mʼbale wake wa Esikolo ndi Aneri.+ Iwowa anapanga ubale ndi Abulamu. 14 Choncho Abulamu anamva kuti mʼbale wake+ wagwidwa ndipo akupita naye kudziko lina. Atamva zimenezo iye anasonkhanitsa anyamata ake odziwa kumenya nkhondo. Anali atumiki ake okwanira 318, omwe anabadwira mʼnyumba yake. Iwo anatsatira adaniwo mpaka ku Dani.+ 15 Usiku iye anagawa mʼmagulu asilikali akewo, omwe anali atumiki ake, kuti amenyane ndi adaniwo. Ndipo anawagonjetsa, moti anawathamangitsa mpaka kukafika ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko. 16 Ndipo anapulumutsa katundu yense. Anapulumutsanso Loti mʼbale wake, katundu wake, akazi ndi anthu ena.

17 Abulamu akubwera kuchokera kumene anagonjetsa Kedorelaomere limodzi ndi mafumu amene anali naye, mfumu ya ku Sodomu inapita kukakumana naye kuchigwa cha Save, kapena kuti chigwa cha Mfumu.+ 18 Ndipo Melekizedeki,+ mfumu ya mzinda wa Salemu,+ anabweretsa mkate ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wamʼmwambamwamba.+

19 Kenako anadalitsa Abulamu kuti:

“Mulungu Wamʼmwambamwamba,

Iye amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, adalitse Abulamu.

20 Atamandike Mulungu Wamʼmwambamwamba,

Amene wapereka okupondereza mʼmanja mwako!”

Ndipo Abulamu anapatsa Melekizedeki chakhumi cha zinthu zonse+ zimene analanda adaniwo.

21 Kenako mfumu ya ku Sodomu inauza Abulamu kuti: “Mungondipatsa anthu okhawo, koma katunduyo mutenge.” 22 Koma Abulamu anauza mfumu ya ku Sodomuyo kuti: “Ndikukweza manja anga kulumbira kwa Yehova Mulungu Wamʼmwambamwamba, Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 23 Ndikulumbira kuti pa zinthu zako sinditengapo kanthu nʼkamodzi komwe, ngakhale kaulusi kapena kachingwe komangira nsapato, kuti usadzati, ‘Ndine ndinamulemeretsa Abulamu.’ 24 Sinditengapo chilichonse kupatulapo zokhazo zimene anyamata adya kale. Koma amene anapita nane, amene ndi Aneri, Esikolo ndi Mamure,+ aliyense akhoza kutenga gawo lake.”

15 Zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu mʼmasomphenya kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+ 2 Abulamu anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana ndipo Eliezere wa ku Damasiko ndi amene adzatenge katundu wanga yense monga cholowa chake.”+ 3 Abulamu ananenanso kuti: “Simunandipatse mwana*+ ndipo mtumiki wanga ndi amene adzatenge katundu wanga yense monga cholowa chake.” 4 Koma Yehova anamuyankha kuti: “Munthu ameneyu sadzatenga katundu wako monga cholowa chake, koma mwana wako ndi amene adzatenge kuti chikhale cholowa chake.”+

5 Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti atuluke panja nʼkumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.” Anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+ 6 Abulamu anakhulupirira zimene Yehova anamuuza,+ ndipo Mulunguyo anamuona kuti ndi wolungama.+ 7 Anamuuzanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndinakuchotsa ku Uri, mzinda wa Akasidi, kuti ndidzakupatse dzikoli likhale lako.”+ 8 Ndipo iye anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nditsimikiza bwanji kuti dzikoli ndidzalitengadi nʼkukhala langa?” 9 Iye anauza Abulamu kuti: “Utenge ngʼombe yazaka zitatu yomwe sinaberekepo, mbuzi yaikazi yazaka zitatu, nkhosa yamphongo yazaka zitatu, ndiponso njiwa yaingʼono ndi mwana wa nkhunda.” 10 Choncho iye anatenga zonsezi nʼkuzidula pakati ndipo anaika mbali iliyonse moyangʼanizana ndi inzake, koma mbalamezo sanazidule. 11 Kenako mbalame zodya nyama zinayamba kutera pa nyama zophedwazo. Koma Abulamu ankazithamangitsa.

12 Dzuwa litatsala pangʼono kulowa, Abulamu anagona tulo tofa nato. Kenako mdima wandiweyani komanso woopsa unafika pa iye. 13 Ndiyeno Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbadwa* zako zidzakhala alendo mʼdziko la eni ndipo anthu adzazisandutsa akapolo ndi kuzizunza kwa zaka 400.+ 14 Koma mtundu umene adzautumikirewo ndidzauweruza.+ Pambuyo pake, iwo adzachokako ndi katundu wambiri.+ 15 Pamene iweyo, udzamwalira mwamtendere* utakhala ndi moyo wabwino komanso wautali+ ndipo udzaikidwa mʼmanda. 16 Koma mʼbadwo wa 4 wa mbadwa zako ndi umene udzabwerere kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”*+

17 Dzuwa litalowa komanso mdima utayamba, ngʼanjo yofuka utsi inaonekera ndipo muuni wamoto unadutsa pakati pa nyama zodulidwazo. 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+ 19 Ndidzapereka kwa mbadwa zako dziko la Akeni,+ Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti,+ Aperezi,+ Arefai,+ 21 Aamori, Akanani, Agirigasi ndiponso la Ayebusi.”+

16 Sarai mkazi wa Abulamu, analibe ana.+ Koma iye anali ndi kapolo wake wa ku Iguputo, dzina lake Hagara.+ 2 Ndiye Sarai anauza Abulamu kuti: “Yehova wapangitsa kuti ndisabereke ana. Chonde gonani ndi kapolo wangayu. Mwina ndingapeze ana kuchokera kwa iye.”+ Choncho Abulamu anamvera mawu a Sarai. 3 Abulamu atakhala zaka 10 mʼdziko la Kanani, Sarai mkazi wake anapereka Hagara, kapolo wake wa ku Iguputo uja kwa mwamuna wake Abulamu kuti akhale mkazi wake. 4 Zitatero Abulamu anagona ndi Hagara ndipo iye anakhala woyembekezera. Hagara atazindikira kuti ndi woyembekezera, anayamba kuchitira mwano mbuye wake, Sarai.

5 Sarai ataona zimenezi anauza Abulamu kuti: “Mlandu wa zimene zikundichitikirazi ukhale pa inu. Ine ndinapereka kapolo wanga kwa inu kuti akhale mkazi wanu, koma iye ataona kuti ndi woyembekezera wayamba kundichitira mwano. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu.” 6 Abulamu anauza Sarai kuti: “Kapolo wakoyutu ali mʼmanja mwako. Chita chimene ukuchiona kuti nʼchabwino.” Ndiyeno Sarai anayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo anathawa.

7 Pambuyo pake, mngelo wa Yehova anakumana ndi Hagara mʼchipululu ali pakasupe wamadzi. Kasupeyo anali panjira yopita ku Shura.+ 8 Ndiyeno mngeloyo anati: “Hagara kapolo wa Sarai, kodi ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndikuthawa mbuye wanga, Sarai.” 9 Mngelo wa Yehovayo anauza Hagara kuti: “Bwerera kwa mbuye wako ndipo uzikamvera modzichepetsa zimene azikakuuza.” 10 Kenako mngelo wa Yehovayo anamuuzanso kuti: “Ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa* zako, moti zidzakhala zosawerengeka.”+ 11 Mngelo wa Yehovayo ananenanso kuti: “Taona, panopa ndiwe woyembekezera, ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamʼpatse dzina lakuti Isimaeli,* chifukwa Yehova wamva kulira kwako. 12 Mwanayo adzakhala ngati bulu wamʼtchire.* Dzanja lake lidzalimbana ndi aliyense, ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana naye. Iye adzakhala pafupi ndi abale ake onse.”*

13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?” 14 Nʼchifukwa chake chitsimecho anachipatsa dzina lakuti Beere-lahai-roi.* (Chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.) 15 Choncho Hagara anaberekera Abulamu mwana wamwamuna ndipo Abulamu anamʼpatsa mwanayo dzina lakuti Isimaeli.+ 16 Pamene Hagara anaberekera Abulamu Isimaeli, Abulamuyo nʼkuti ali ndi zaka 86.

17 Abulamu ali ndi zaka 99, Yehova anaonekera kwa iye nʼkumuuza kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse. Uziyenda mʼnjira zanga ndipo ukhale wopanda cholakwa. 2 Ndidzakhazikitsa pangano langa pakati pa ine ndi iwe+ ndipo ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zako.”+

3 Abulamu atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. Kenako Mulungu anapitiriza kulankhula naye kuti: 4 “Ine ndinachita pangano ndi iwe,+ ndipo iwe udzakhaladi tate wa mitundu yambiri.+ 5 Dzina lako silikhalanso Abulamu* koma likhala Abulahamu,* chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri. 6 Ndidzakupatsa mbadwa zambirimbiri, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu ndi mafumu.+

7 Ndidzasunga pangano limene ine ndachita ndi iwe+ komanso ndi mbadwa zako* mʼmibadwo yawo yonse. Lidzakhala pangano losatha kusonyeza kuti ndine Mulungu wako ndi wa mbadwa zako. 8 Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbadwa zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+

9 Mulungu anapitiriza kuuza Abulahamu kuti: “Koma iwe usunge pangano langa, iwe ndi mbadwa zako mʼmibadwo yawo yonse. 10 Ili ndi pangano la pakati pa ine ndi iwe, lakuti iwe ndi mbadwa zako muzilisunga: Mwamuna aliyense pakati panu azidulidwa.+ 11 Muzichita mdulidwe* kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.+ 12 Mwana aliyense wamwamuna amene wakwanitsa masiku 8 azidulidwa+ mʼmibadwo yanu yonse. Aliyense amene wabadwira mʼnyumba yanu komanso aliyense amene si mbadwa yanu koma munamugula ndi ndalama kwa mlendo azidulidwa. 13 Mwamuna aliyense wobadwira mʼnyumba mwanu komanso mwamuna aliyense amene mwamugula ndi ndalama zanu ayenera kudulidwa.+ Pangano langa, lomwe chizindikiro chake chili pathupi lanu, lidzakhala pangano losatha. 14 Mwamuna aliyense wosadulidwa akapanda kudulidwa, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake. Munthuyo waphwanya pangano langa.”

15 Kenako Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Mkazi wako Sarai,*+ usamamuitanenso kuti Sarai, chifukwa dzina lake tsopano likhala Sara.* 16 Ndidzamudalitsa ndipo adzakuberekera mwana wamwamuna.+ Iye ndidzamudalitsa moti adzakhala mayi wa mitundu yambiri ya anthu ndi wa mafumu a mitundu yambiri ya anthu.” 17 Abulahamu atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi, kenako anayamba kuseka nʼkunena mumtima mwake kuti:+ “Kodi mwamuna wa zaka 100 angabereke mwana zoona? Komanso Sara mkazi wa zaka 90, zoona angakhale ndi mwana?”+

18 Kenako Abulahamu anauza Mulungu woona kuti: “Ndikukupemphani kuti mudalitse Isimaeli.”+ 19 Ndiyeno Mulungu anati: “Ndithu Sara mkazi wako adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo udzamʼpatse dzina lakuti Isaki.*+ Ndidzakhazikitsa pangano ndi iye, kuti likhale pangano losatha kwa mbadwa zake.+ 20 Koma za Isimaeli ndamva pempho lako. Iye ndidzamudalitsa ndipo ndidzamupatsa ana ambiri, komanso ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa zake. Adzabereka ana 12 amene adzakhale atsogoleri a mafuko, ndipo ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.+ 21 Koma ndidzakhazikitsa pangano langa ndi Isaki,+ amene Sara adzakuberekera nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa.”+

22 Mulungu atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, anachoka. 23 Ndiyeno Abulahamu anatenga mwana wake Isimaeli ndi amuna onse obadwira mʼnyumba yake, ndi aliyense amene anamugula ndi ndalama zake. Anatenga amuna onse amʼnyumba yake ndipo anawadula tsiku lomwelo monga mmene Mulungu anamuuzira.+ 24 Abulahamu anadulidwa+ ali ndi zaka 99. 25 Ndipo mwana wake Isimaeli anadulidwa ali ndi zaka 13.+ 26 Choncho pa tsiku limenelo Abulahamu ndi mwana wake Isimaeli anadulidwa. 27 Amuna onse amʼnyumba yake, aliyense wobadwira mʼnyumba yake ndi aliyense wogulidwa ndi ndalama zake kwa mlendo, nawonso anadulidwa naye limodzi.

18 Kenako Yehova+ anaonekera kwa Abulahamu pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure.+ Pa nthawiyi nʼkuti Abulahamu atakhala pansi pakhomo la tenti yake masana dzuwa likuswa mtengo. 2 Atakweza maso, anaona amuna atatu ataima chapatali ndi iye.+ Atawaona, ananyamuka pakhomo la tentiyo nʼkuthamanga kukakumana nawo. Atafika, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. 3 Ndiyeno anati: “Yehova, ngati mungandikomere mtima, chonde, musangondipitirira ine mtumiki wanu. 4 Dikirani pangʼono tibweretse madzi kuti tikusambitseni mapazi.+ Kenako mupumeko pansi pa mtengo. 5 Popeza mwafika kwa mtumiki wanu, ndiloleni ndikubweretsereni kachakudya kuti mupezenso mphamvu. Kenako mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”

6 Choncho Abulahamu anathamangira kutenti kumene kunali Sara nʼkumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu,* uukande nʼkupanga mikate.” 7 Kenako Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, nʼkusankha ngʼombe yaingʼono yamphongo yabwino kwambiri. Atatero, anaipereka kwa mtumiki wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga. 8 Ndiyeno Abulahamu anatenga mafuta amumkaka, mkaka ndi ngʼombe yaingʼono yamphongo imene anakonza ija nʼkukaziika pamene panali alendowo. Atatero iye anaimirira chapafupi pa nthawi imene alendowo ankadya atakhala pansi pa mtengo.+

9 Alendowo anamufunsa kuti: “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Ali mutentimu.” 10 Ndiyeno mmodzi wa iwo anati: “Ndithu ndidzabweranso kwa iwe chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Pa nthawiyi nʼkuti Sara akumvetsera ali pakhomo la tenti imene inali kumbuyo kwa mlendoyo. 11 Abulahamu ndi Sara anali okalamba ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Sara anali atadutsa msinkhu woti nʼkubereka mwana.+ 12 Choncho Sara anayamba kuseka mumtima mwake nʼkunena kuti: “Kodi mmene ndatheramu komanso mmene mbuyanga wakalambiramu, zoona ndingakhaledi ndi mwayi wobereka mwana?”+ 13 Ndiyeno Yehova anafunsa Abulahamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani Sara waseka nʼkunena kuti, ‘Kodi nʼzoona kuti ineyo, mmene ndakalambiramu, ndingaberekedi mwana?’ 14 Kodi pali chosatheka ndi Yehova?+ Ndidzabweranso kwa iwe pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 15 Koma Sara anachita mantha nʼkukana kuti: “Sindinaseketu ine!” Koma mlendoyo anati: “Inde! Unaseka iwe.”

16 Amunawo ananyamuka kuti azipita ndipo Abulahamu anawaperekeza. Atafika pamalo ena amunawo anayangʼana ku Sodomu.+ 17 Kenako Yehova anati: “Bwanji ndimuuze Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+ 18 Pajatu Abulahamu adzakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse yapadziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iye.+ 19 Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake zonse* kuyenda mʼnjira ya Yehova. Azichita zimenezi pochita zabwino ndi zachilungamo+ kuti Yehova adzakwaniritse zimene ananena zokhudza Abulahamu.”

20 Kenako Yehova anati: “Ndamva madandaulo ambiri+ akuti machimo a anthu amene akukhala mʼmizinda ya Sodomu ndi Gomora ndi oipa kwambiri.+ 21 Ndiye ndipitako kuti ndikaone ngati akuchitadi zimene ndamvazo. Ndikufuna ndidziwe ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho.”+

22 Kenako amunawo anachoka pamalowo nʼkulowera ku Sodomu, koma Yehova+ anatsala ndi Abulahamu. 23 Zitatero Abulahamu anamuyandikira nʼkumufunsa kuti: “Kodi zoona muwonongadi olungama pamodzi ndi oipa?+ 24 Bwanji ngati mumzindamo mutapezeka anthu olungama 50? Kodi muwawonongabe, osakhululukira mzindawo chifukwa cha olungama 50 amenewo? 25 Simungachite zimenezo, simungaphe munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama alangidwe limodzi ndi woipa.+ Simungachite zimenezo.+ Ndinu Woweruza wa dziko lonse lapansi. Ndiye kodi simuchita chilungamo?”+ 26 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Ngati ndingapeze anthu olungama 50 mu Sodomu, ndikhululukira mzinda wonsewo chifukwa cha iwo.” 27 Koma Abulahamu anapitiriza kuti: “Pepanitu, musaone ngati ndatha mantha kulankhula ndi Yehova pamene ndine fumbi komanso phulusa. 28 Nanga bwanji pa olungama 50 aja pataperewera 5, kodi muwononga mzinda wonsewo chifukwa choti paperewera anthu 5?” Pamenepo iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo ndikapezamo olungama 45.”+

29 Koma iye anafunsabe kuti: “Nanga mutapezeka 40?” Iye anayankha kuti: “Sindingawononge chifukwa cha 40 amenewo.” 30 Iye anapitiriza kuti: “Chonde Yehova, musandipsere mtima,+ koma ndiloleni ndilankhulebe. Nanga atapezeka 30 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga ndikapezamo 30.” 31 Iye anapitirizabe kuti: “Pepani, musaone ngati ndatha mantha kulankhula ndi Yehova. Nanga mutapezeka 20 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 20 amenewo.” 32 Pomaliza anati: “Pepanitu Yehova, musandipsere mtima, ndiloleni ndilankhule komaliza kokha. Nanga mutapezeka 10 okha?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 10 amenewo.” 33 Yehova atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, ananyamuka nʼkumapita,+ ndipo Abulahamu anabwerera kwawo.

19 Angelo awiri aja anafika ku Sodomu madzulo. Loti anali atakhala pageti la mzinda wa Sodomu. Atawaona ananyamuka kukakumana nawo, ndipo anawagwadira nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 2 Ndiyeno anati: “Chonde ambuye anga, tiyeni kunyumba ya kapolo wanu. Tikakusambitseni mapazi ndiponso mukagone, kuti mawa mulawirire nʼkupitiriza ulendo wanu.” Koma iwo anati: “Ayi, ife tigona mʼbwalo lamumzindawu usiku wa lero.” 3 Ndiyeno Loti anawaumiriza kwambiri moti iwo anapita naye kunyumba kwake. Kumeneko anawakonzera phwando, nʼkuwaphikira mkate wopanda zofufumitsa, ndipo anadya.

4 Koma iwo asanagone, chigulu cha amuna a mumzinda wa Sodomu, chinafika nʼkuzungulira nyumba ya Loti. Pachigulupo panali anyamata komanso achikulire. 5 Iwo ankauza Loti mofuula kuti: “Kwanu kuno kwabwera amuna enaake usiku uno. Ali kuti amuna amenewo? Atulutse kuti tigone nawo.”+

6 Choncho Loti anatuluka mʼnyumbamo kuti alankhule nawo ndipo anatseka chitseko. 7 Ndiyeno iye anati: “Chonde abale anga, musachite zoipazi. 8 Paja ine ndili ndi ana aakazi awiri amene sanagonepo ndi mwamuna. Bwanji ndikutulutsireni amenewo kuti muchite nawo zimene mukufuna. Koma amuna okhawa musawachite chilichonse, chifukwa ndi alendo anga ndipo ndikuyenera kuwateteza.”+ 9 Koma iwo anati: “Choka apa!” Ananenanso kuti: “Iwe ndi wobwera kwathu kuno, ndipo ukukhala monga mlendo. Ndiye lero uzitiuza zochita? Tsopano iweyo tikuchita zoopsa kuposa iwowo.” Atatero iwo anamupanikiza kwambiri Loti, moti anatsala pangʼono kuthyola chitseko. 10 Kenako alendo aja anatulutsa manja ndi kumukokera Loti mʼnyumbamo, nʼkutseka chitseko. 11 Ndipo anachititsa khungu amuna amene anali pakhomo la nyumbayo, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, moti anthuwo anavutika kufufuza khomo.

12 Ndiyeno alendowo anafunsa Loti kuti: “Kodi uli ndi achibale alionse kuno? Uwatulutse mumzinda uno, kaya ndi akamwini ako, ana ako aamuna, ana ako aakazi kapena aliyense amene ndi mʼbale wako. 13 Malo ano tiwawononga chifukwa Yehova wamva madandaulo ambiri okhudza anthuwa,+ moti Yehova watituma kudzawononga mzindawu.” 14 Choncho Loti anatuluka nʼkupita kukalankhula ndi akamwini ake omwe ankayembekezera kukwatira ana ake. Iye anawauza mobwerezabwereza kuti: “Fulumirani! Tulukani mumzinda uno, chifukwa Yehova auwononga.” Koma akamwini akewo ankangoona ngati akunena zocheza.+

15 Kutatsala pangʼono kucha, angelowo anayamba kumuuza Loti kuti afulumire. Iwo anamuuza kuti: “Fulumira! Tenga mkazi wako ndi ana ako aakazi awiriwa, kuti musawonongedwe limodzi ndi mzindawu chifukwa cha kulakwa kwake.”+ 16 Iye ankazengereza koma popeza Yehova anamuchitira chifundo,+ alendowo anagwira dzanja la iyeyo, mkazi wake ndi ana ake aakazi awiriwo nʼkuwatulutsa kukawasiya kunja kwa mzinda.+ 17 Atafika nawo kunja kwa mzinda, anawauza kuti: “Thawani mupulumutse moyo wanu! Musayangʼane kumbuyo+ komanso musaime pamalo alionse mʼchigawochi.+ Thawirani kudera lakumapiri kuti musaphedwe!”

18 Koma Loti anawauza kuti: “Chonde Yehova, kumeneko ayi! 19 Mwandisonyeza kale chifundo ine mtumiki wanu komanso mwandisonyeza kukoma mtima kwakukulu* populumutsa moyo wanga.+ Koma sinditha kuthawira kudera lakumapiri chifukwa ndikuopa kuti tsoka likandigwera kumeneko nʼkufa.+ 20 Chonde, taonani pali tauni yaingʼono pafupipa ndipo ndingathe kuthawira kumeneko. Tauni imeneyi ndi yaingʼono. Chonde ndiloleni ndithawire mʼtauni imeneyi. Ndikatero, ndipulumutsa moyo wanga.” 21 Pamenepo iye anayankha Loti kuti: “Chabwino, ndavomera zimene wapempha.+ Sindiwononga tauni imene wanenayo.+ 22 Tiye, fulumira! Thawira kumeneko, ndipo sindichita chilichonse mpaka utakafika.”+ Nʼchifukwa chake anapatsa tauniyo dzina lakuti Zowari.*+

23 Pamene Loti ankafika ku Zowari nʼkuti dzuwa litatuluka. 24 Kenako Yehova anagwetsa sulufule ndi moto ngati mvula ku Sodomu ndi Gomora. Sulufule ndi motowo zinachokera kwa Yehova kumwamba.+ 25 Choncho anawononga mizindayi. Anawononga chigawo chonsecho, kuphatikizapo anthu onse okhala mʼmizindayi komanso zomera zapanthaka.+ 26 Koma mkazi wa Loti amene anali kumbuyo kwake, anayangʼana kumbuyo, ndipo anasanduka chipilala chamchere.+

27 Tsopano Abulahamu ananyamuka mʼmawa kwambiri nʼkupita pamalo amene anaimirira pamaso pa Yehova aja.+ 28 Atayangʼana kumunsi ku Sodomu ndi Gomora ndi kudera lonse la chigawocho, anaona zoopsa. Kumeneko chiutsi chinali tolo! Chinkafuka ngati chiutsi chochokera pa uvuni wa njerwa.+ 29 Koma Mulungu sanaiwale zimene anauza Abulahamu. Choncho pamene ankawononga mizinda ya mʼchigawocho, anatulutsa Loti mʼmizinda imeneyo. Imeneyi ndi mizinda imene Loti ankakhalako.+

30 Kenako Loti anachoka ku Zowari limodzi ndi ana ake aakazi awiri aja nʼkukakhala kudera lakumapiri,+ chifukwa ankachita mantha kukhala ku Zowari.+ Kumeneko, iye ndi ana ake awiriwo anayamba kukhala mʼphanga. 31 Ndiyeno mwana woyamba kubadwa anauza mngʼono wake kuti: “Bambo athuwatu akalamba, ndipo mʼdera lino mulibe mwamuna woti angatikwatire ngati mmene anthu amachitira. 32 Tiye tiwapatse vinyo bambowa kuti amwe, ndipo tigone nawo kuti tikhale ndi ana kuchokera kwa iwo.”

33 Choncho usiku umenewo iwo anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako mwana woyamba kubadwayo anapita nʼkukagona ndi bambo akewo. Koma kuyambira pamene mwanayo anapita kukagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse. 34 Tsiku lotsatira, mwana woyambayo anauza mngʼono wake kuti: “Ndinagona nawo bambo usiku. Leronso usiku tiwapatse vinyo kuti amwe. Ndiye iwenso upite ukagone nawo, kuti tikhale ndi ana kuchokera kwa iwo.” 35 Choncho usiku umenewonso anakhala akuwapatsa vinyo bambo awo kuti azimwa. Kenako, mwana wamngʼono uja anapita nʼkukagona nawo. Koma kuyambira pamene mwanayo anapita kukagona nawo mpaka pamene anachoka, bambowo sanadziwe chilichonse. 36 Choncho ana a Loti awiri onsewo anakhala oyembekezera atagona ndi bambo awo. 37 Mwana woyamba anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Mowabu.+ Iye ndi tate wa Amowabu amasiku ano.+ 38 Mwana wamngʼono nayenso anabereka mwana wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Beni-ami. Iye ndi tate wa Aamoni+ amasiku ano.

20 Tsopano Abulahamu anasamutsa msasa wake+ nʼkupita kudziko la Negebu ndipo anayamba kukhala pakati pa Kadesi+ ndi Shura.+ Pamene ankakhala* ku Gerari,+ 2 Abulahamu anabwerezanso kunena za Sara mkazi wake kuti: “Uyu ndi mchemwali wanga.”+ Choncho Abimeleki* mfumu ya ku Gerari atamva zimenezo, anatuma antchito ake kuti akamutenge Sara.+ 3 Pambuyo pake Mulungu anafikira Abimeleki usiku mʼmaloto nʼkumuuza kuti: “Ufatu iwe chifukwa mkazi amene watengayu+ ndi wokwatiwa.”+ 4 Koma Abimeleki anali asanagone ndi Sara. Choncho iye anati: “Yehova, kodi muwononga mtundu womwe ndi wosalakwa?* 5 Kodi mwamunayu sanandiuze yekha kuti, ‘Uyu ndi mchemwali wangaʼ? Ndipo kodi mkaziyunso sananene yekha kuti, ‘Uyu ndi mchimwene wangaʼ? Zimenezitu ndachita popanda mtima wanga kunditsutsa, komanso mosadziwa kuti ndikulakwa.” 6 Kenako Mulungu woona anamuuza mʼmalotomo kuti: “Inenso ndinadziwa kuti mtima wako sunakutsutse pochita zimenezi, ndipo ndinakutchinga kuti usandichimwire. Ndiye chifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze mkaziyu. 7 Tsopano bweza mkaziyo kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri,+ ndipo adzakupempherera+ moti udzakhala ndi moyo. Koma ukapanda kumubweza, udziwe kuti iweyo ndi anthu ako onse ndithu mufa.”

8 Abimeleki anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkuitana antchito ake onse ndipo anawauza zinthu zonsezi moti anthuwo anachita mantha kwambiri. 9 Kenako Abimeleki anaitana Abulahamu nʼkumufunsa kuti: “Nʼchiyani watichitirachi? Ndakuchimwira chiyani ine, kuti ubweretse tchimo lalikulu chonchi pa ine ndi ufumu wanga? Zimene wandichitirazi nʼzosayenera.” 10 Abimeleki anapitiriza kufunsa Abulahamu kuti: “Cholinga chako chinali chiyani makamaka pochita zimenezi?”+ 11 Abulahamu anayankha kuti: “Ndinachita zimenezi poganiza kuti, ‘Ndithu anthu akuno saopa Mulungu, andipha chifukwa cha mkazi wangayu.’+ 12 Komabe, ndi mchemwali wangadi ameneyu. Bambo athu ndi amodzi, tinangosiyana mayi, ndipo ndinamukwatira.+ 13 Mulungu atandiuza kuti ndichoke kunyumba ya bambo anga+ kuti ndiyambe kuyendayenda, ndinauza mkazi wangayu kuti: ‘Undisonyeze chikondi chokhulupirika pochita izi: Kulikonse kumene tizipita, uziuza anthu kuti: “Uyu ndi mchimwene wanga.”’”+

14 Ndiyeno Abimeleki anatenga nkhosa, ngʼombe ndiponso antchito aamuna ndi aakazi nʼkumupatsa Abulahamu. Anamubwezeranso Sara mkazi wake. 15 Abimeleki anamuuzanso kuti: “Dziko lonseli ndi langa. Ungathe kukhala kulikonse kumene ungakonde.” 16 Kenako Abimeleki anauza Sara kuti: “Ndalama zasiliva 1,000 izi ndikuzipereka kwa mchimwene wakoyu.+ Zikhale umboni wotsimikizira kwa onse amene muli nawo, ndi kwa wina aliyense, kuti ndiwe wosalakwa ndipo sukuyenera kuimbidwa mlandu.” 17 Kenako Abulahamu anayamba kumupempherera kwa Mulungu woona. Choncho Mulungu anachiritsa Abimeleki, mkazi wake komanso akapolo ake aakazi, moti iwo anayamba kubereka ana. 18 Zinatero chifukwa Yehova anachititsa kuti akazi onse amʼnyumba ya Abimeleki asabereke chifukwa cha Sara mkazi wa Abulahamu.+

21 Yehova anakumbukira Sara monga mmene ananenera, ndipo Yehova anachitira Sara mogwirizana ndi zimene analonjeza.+ 2 Choncho Sara anakhala woyembekezera+ ndipo anaberekera Abulahamu mwana, Abulahamuyo atakalamba. Izi zinachitika ndendende pa nthawi imene Mulungu analonjeza Abulahamu.+ 3 Abulahamu anapatsa mwana amene Sara anamuberekerayo dzina lakuti Isaki.+ 4 Isaki atakwanitsa masiku 8, Abulahamu anachita mdulidwe wa mwana wakeyo, monga mmene Mulungu anamulamulira.+ 5 Abulahamu anali ndi zaka 100 pamene mwana wake Isaki anabadwa. 6 Ndiyeno Sara anati: “Mulungu wandipatsa chifukwa chosangalalira. Tsopano aliyense akamva zimenezi asangalala nane limodzi.”* 7 Anapitiriza kunena kuti: “Ndi ndani akanauza Abulahamu kuti, ‘Sara adzayamwitsa mwanaʼ? Koma taonani, ndamuberekera mwana Abulahamu atakalamba.”

8 Ndiyeno mwanayo atakula anamusiyitsa kuyamwa. Pa tsiku limene Isaki anamusiyitsa kuyamwalo, Abulahamu anakonza phwando lalikulu. 9 Koma Sara ankaona mwana amene Hagara+ wa ku Iguputo anaberekera Abulahamu akuseka Isaki.+ 10 Choncho Sara anauza Abulahamu kuti: “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wanga Isaki.”+ 11 Koma zimene Sara ananenazi zokhudza Isimaeli, zinamuipira kwambiri Abulahamu.+ 12 Kenako Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Usaipidwe ndi zimene Sara akukuuza zokhudza mnyamatayo ndiponso kapolo wakoyo. Mumvere,* chifukwa mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.+ 13 Kunena za mwana wa kapoloyu,+ nayenso ndidzamupangitsa kukhala mtundu,+ chifukwa iyenso ndi mwana wako.”

14 Ndiyeno Abulahamu anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutenga mkate ndi thumba lachikopa la madzi, ndipo anaziika paphewa pa Hagara. Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Choncho Hagarayo ananyamuka nʼkumangoyendayenda mʼchipululu cha Beere-seba.+ 15 Potsirizira pake, madzi anamuthera mʼthumba lachikopa lija, ndipo iye anangomusiya mnyamata uja pachitsamba. 16 Ndiyeno iye anapita chapatali nʼkukakhala pansi payekhayekha pamtunda woti muvi woponya ndi uta ukhoza kufika. Anachita zimenezi chifukwa mumtima mwake anati: “Sindikufuna kuona mwana wanga akufa.” Choncho anakakhala pansi chapatali nʼkuyamba kulira mokweza.

17 Kenako Mulungu anamva mawu a mnyamatayo,+ ndipo mngelo wa Mulungu analankhula ndi Hagara kuchokera kumwamba kuti:+ “Kodi watani Hagara? Usaope, Mulungu wamva mawu a mnyamatayo pomwe wagonapo. 18 Nyamuka! Dzutsa mnyamatayo, ndipo umugwire kuti azitha kuyenda chifukwa ndidzamupangitsa kukhala mtundu waukulu.”+ 19 Ndiyeno Mulungu anamutsegula maso Hagara, moti anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita pachitsimecho nʼkutungira madziwo mʼthumba lachikopa lija, kenako anapatsa mnyamatayo kuti amwe. 20 Pamene Isimaeli+ ankakula, Mulungu anakhalabe naye. Mnyamata ameneyu ankakhala mʼchipululu ndipo anakhala katswiri woponya muvi pogwiritsa ntchito uta. 21 Iye anayamba kukhala mʼchipululu cha Parana,+ ndipo amayi ake anakamutengera mkazi kudziko la Iguputo.

22 Pa nthawi imeneyo, Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa gulu lake lankhondo, anauza Abulahamu kuti: “Mulungu ali ndi iwe pa zonse zomwe ukuchita.+ 23 Choncho panopa lumbira pamaso pa Mulungu kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine, kwa ana anga ndi kwa mbadwa zanga. Ndiponso kuti udzasonyeza chikondi chokhulupirika ngati chimene ine ndakusonyeza. Lumbira kuti udzasonyeza chikondi chimenechi kwa ineyo ndi anthu amʼdziko limene ukukhala.”+ 24 Abulahamu anayankha kuti: “Ndikulumbira.”

25 Koma Abulahamu anadandaulira Abimeleki za chitsime cha madzi chimene antchito a Abimeleki analanda mwachiwawa.+ 26 Abimeleki anayankha kuti: “Sindikudziwa amene anachita zimenezi, ndipo ngakhale iwe sunandiuze za nkhaniyi. Inetu sindinamve za nkhani imeneyi, moti ndikuimvera pompano.” 27 Ndiye Abulahamu anatenga nkhosa ndi ngʼombe nʼkuzipereka kwa Abimeleki. Ndipo awiriwo anachita pangano. 28 Kenako Abulahamu anapatula ana a nkhosa aakazi 7 pa gululo nʼkuwaika paokha. 29 Ndiyeno Abimeleki anafunsa Abulahamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani ana a nkhosa aakazi 7 amenewa wawaika paokha?” 30 Poyankha Abulahamu anati: “Mulandire ana a nkhosa aakazi 7 amene ndikukupatsaniwa, kuti akhale umboni wakuti ndinakumba chitsimechi ndine.” 31 Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Beere-seba,*+ chifukwa chakuti onse awiri analumbira pamalopo. 32 Choncho iwo anachita pangano+ pa Beere-sebapo, kenako Abimeleki limodzi ndi Fikolo mkulu wa asilikali ake, anabwerera kudziko la Afilisiti.+ 33 Zitatero, Abulahamu anadzala mtengo wa bwemba pa Beere-seba, ndipo kumeneko anaitanira pa dzina la Yehova,+ Mulungu yemwe adzakhalepo mpaka kalekale.+ 34 Ndipo Abulahamu anakhala* mʼdziko la Afilisiti kwa nthawi yaitali.*+

22 Pambuyo pa zimenezi, Mulungu woona anamuyesa+ Abulahamu ndipo anati: “Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!” 2 Kenako Mulungu anamuuza kuti: “Tenga Isaki+ mwana wako mmodzi yekhayo, mwana wako amene umamukonda kwambiriyo,+ ndipo mupite ku Moriya.+ Kumeneko ukamupereke nsembe yopsereza paphiri limene ndidzakuuza.”

3 Choncho Abulahamu anadzuka mʼmawa kwambiri, nʼkumanga chishalo pabulu wake ndipo anatenga atumiki ake awiri limodzi ndi mwana wake Isaki. Komanso anawaza nkhuni zokawotchera nsembe. Atatero ananyamuka ulendo wopita kumalo amene Mulungu woona anamuuza. 4 Pa tsiku lachitatu, Abulahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. 5 Kenako Abulahamu anauza atumiki akewo kuti: “Inu tsalani pano ndi buluyu, ine ndi mwana wangayu tikupita uko kukalambira, tikupezani.”

6 Choncho Abulahamu anatenga nkhuni zokawotchera nsembe zija nʼkumusenzetsa Isaki mwana wake ndipo iye ananyamula moto komanso mpeni.* Kenako anapitira limodzi. 7 Ndiyeno Isaki analankhula ndi Abulahamu bambo ake kuti: “Bambo!” Abulahamu anayankha kuti: “Lankhula mwana wanga.” Choncho iye anafunsa kuti: “Moto ndi nkhuni nʼzimenezi, nanga nkhosa yokapereka nsembe yopsereza ili kuti?” 8 Abulahamu anayankha kuti: “Mwana wanga, Mulungu apereka nkhosa yoti tipereke nsembe yopsereza.”+ Choncho awiriwo anapitiriza ulendo wawo.

9 Kenako iwo anafika pamalo amene Mulungu woona anamuuza Abulahamu. Atafika pamalowo, iye anamanga guwa lansembe nʼkuyala nkhuni zija paguwapo. Atatero, anamanga Isaki mwana wakeyo manja ndi miyendo nʼkumugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni.+ 10 Ndiyeno Abulahamu anatenga mpeni uja kuti aphe mwana wakeyo.+ 11 Koma mngelo wa Yehova anamuitana kuchokera kumwamba kuti: “Abulahamu! Abulahamu!” Iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga!” 12 Ndiyeno mngeloyo anati: “Usamuvulaze mwanayo ndipo usamuchite chilichonse. Tsopano ndadziwa kuti umaopa Mulungu, chifukwa sunakane kupereka kwa ine mwana wako mmodzi yekhayo.”+ 13 Zitatero Abulahamu anakweza maso ake nʼkuona nkhosa yamphongo chapoteropo, nyanga zake zitakodwa mʼziyangoyango. Ndiyeno Abulahamu anakaitenga nʼkuipereka nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abulahamu anatchula malowo dzina lakuti Yehova-yire.* Nʼchifukwa chake mpaka lero pali mawu akuti: “Mʼphiri lake Yehova adzapereka zinthu zofunikira.”+

15 Ndiyeno mngelo wa Yehova anaitana Abulahamu kachiwiri kuchokera kumwamba, 16 nʼkumuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndikulumbira pali dzina langa,+ kuti chifukwa cha zimene wachitazi, posakana kupereka mwana wako mmodzi yekhayo,+ 17 ndidzakudalitsa ndithu. Ndiponso ndidzachulukitsadi mbadwa* zako ngati nyenyezi zakumwamba komanso ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.+ Ndipo mbadwa yako idzalanda mzinda* wa adani ake.+ 18 Kudzera mwa mbadwa* yako,+ mitundu yonse yapadziko lapansi idzapeza madalitso chifukwa chakuti wamvera mawu anga.’”+

19 Kenako Abulahamu anabwerera kwa atumiki ake aja nʼkunyamuka nawo limodzi kubwerera ku Beere-seba.+ Ndipo Abulahamu anapitiriza kukhala ku Beere-sebako.

20 Pambuyo pa zimenezi, uthenga unafika kwa Abulahamu wonena kuti: “Nayenso Milika waberekera mchimwene wako Nahori ana aamuna.+ 21 Mwana wake woyamba ndi Uza, ndiye pali mchimwene wake Buza komanso Kemueli bambo ake a Aramu. 22 Palinso Kesede, Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betuele.”+ 23 Betuele anabereka Rabeka.+ Ana 8 amenewa ndi amene Milika anaberekera Nahori mchimwene wake wa Abulahamu. 24 Mdzakazi* wa Nahori, dzina lake Reuma anamuberekeranso ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.

23 Sara anakhala ndi moyo zaka 127. Zaka zimene Sara anakhala ndi moyo ndi zimenezi.+ 2 Sara anamwalirira ku Kiriyati-ariba,+ kapena kuti ku Heburoni,+ mʼdziko la Kanani.+ Ndiye Abulahamu anayamba kumulira Sara. 3 Kenako Abulahamu anachoka pamene panali mtembo wa mkazi wake nʼkupita kukalankhula ndi ana a Heti+ kuti: 4 “Ine ndinadzakhala kwanu kuno ngati mlendo.+ Choncho mundipatseko malo kuti ndikhale ndi manda angaanga, ndiikemo mkazi wanga.” 5 Ana a Heti anayankha Abulahamu kuti: 6 “Timvereni mbuyathu. Inu ndinu mtsogoleri wathu woikidwa ndi Mulungu.*+ Sankhani manda abwino kwambiri pa manda amene tili nawo kuti muikemo malemuwo. Palibe aliyense wa ife amene angakanize manda ake kuti muikemo malemuwo.”

7 Choncho Abulahamu anaimirira nʼkugwada pamaso pa eni dzikowo, ana a Heti.+ 8 Iye analankhula nawo kuti: “Ngati mukuvomera kuti ndiike mʼmanda malemu mkazi wanga kunoko, chonde mundipemphereko kwa Efuroni mwana wa Zohari 9 kuti andigulitse phanga lake la Makipela limene lili mʼmalire a malo ake. Andigulitse pa mtengo wake wonse+ inu mukuona, kuti ndikhale ndi manda.”+

10 Pa nthawiyi nʼkuti Efuroni atakhala pansi limodzi ndi ana a Heti. Choncho Efuroni Muhiti anayankha Abulahamu, ana a Hetiwo akumva limodzi ndi onse amene analowa pageti la mzinda+ wake kuti: 11 “Ayi mbuyanga! Ndimvereni. Malowo, pamodzi ndi phanga limene lili pamalopo, ndikukupatsani pamaso pa anthu a mtundu wangawa. Kaikeni malemuwo.” 12 Zitatero Abulahamu anagwada pamaso pa eni dzikowo. 13 Kenako iye anauza Efuroni pamaso pa eni dzikowo kuti: “Ndimvere chonde. Ine ndikupatsa ndalama zonse zimene ungandiuze zogulira malowo. Landira silivayu kuti ndikaike mkazi wanga kumeneko.”

14 Ndiyeno Efuroni anayankha Abulahamu kuti: 15 “Ndimvereni mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi siliva wolemera masekeli 400.* Koma ndalamazo si nkhani yaikulu pakati pa ine ndi inu. Kaikeni malemuwo.” 16 Abulahamu anamvera Efuroni, ndipo anamuyezera siliva wokwanira mtengo umene Efuroniyo ananena pamaso pa ana a Heti. Anamuyezera siliva wolemera masekeli 400,* mogwirizana ndi muyezo umene amalonda ankauvomereza.+ 17 Choncho Efuroni anagulitsa malo ake amene anali ku Makipela pafupi ndi Mamure. Anagulitsa malowo, phanga komanso mitengo yonse imene inali pamalopo, ndipo anatsimikizira 18 pamaso pa ana a Heti ndi onse amene analowa pageti la mzinda, kuti Abulahamu wagula malowo ndipo ndi ake. 19 Kenako Abulahamu anaika Sara mkazi wake mʼmanda kuphanga la Makipela, pafupi ndi Mamure, kapena kuti Heburoni, mʼdziko la Kanani. 20 Choncho ana a Heti anapereka kwa Abulahamu malowo ndi phanga limene linali pamenepo kuti akhale manda.+

24 Tsopano Abulahamu anali atakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Yehova anali atamudalitsa mʼchilichonse.+ 2 Ndiyeno Abulahamu anauza mtumiki wake, yemwe anali wamkulu kwambiri mʼnyumba yake komanso woyangʼanira zinthu zake zonse+ kuti: “Chonde, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. 3 Ndikufuna ulumbire pali Yehova, Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa dziko lapansi, kuti sutengera mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Akanani, amene ndikukhala mʼdziko lawo.+ 4 Mʼmalomwake, upite kudziko lakwathu kwa abale anga,+ ndipo kumeneko ukamutengere mkazi Isaki mwana wanga.”

5 Koma mtumikiyo anamufunsa kuti: “Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane kuno? Kodi ndidzatenge mwana wanuyu nʼkumubwezera kudziko limene munachokera?”+ 6 Pamenepo Abulahamu anayankha kuti: “Ayi, usadzatenge mwana wanga nʼkupita naye kumeneko.+ 7 Yehova Mulungu wakumwamba, amene ananditenga kunyumba kwa bambo anga ndi kudziko la abale anga,+ amenenso analankhula nane nʼkulumbira kwa ine+ kuti: ‘Ndidzapereka dziko+ ili kwa mbadwa* zako,’+ ameneyo atumiza mngelo wake kuti akutsogolere,+ ndipo ndithu ukamʼtengere mkazi mwana wanga kumeneko.+ 8 Koma ngati mkaziyo angakakane kubwera nawe, iweyo udzamasuka pa lumbiro limeneli. Koma sindikufuna kuti udzatenge mwana wanga nʼkupita naye kumeneko.” 9 Atatero, mtumikiyo anaika dzanja lake pansi pa ntchafu ya Abulahamu mbuye wake nʼkulumbira kwa iye pa nkhani imeneyi.+

10 Choncho mtumikiyo anatenga ngamila 10 pa ngamila za mbuye wake. Anatenganso zinthu zabwino zosiyanasiyana kwa mbuye wake. Kenako ananyamuka ulendo wopita ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori. 11 Atafika, anagwaditsa pansi ngamilazo pachitsime cha madzi chimene chinali kunja kwa mzindawo. Anafika chakumadzulo, nthawi imene akazi ankatuluka mumzindamo kukatunga madzi. 12 Ndiyeno mtumikiyo anati: “Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, chonde ndithandizeni kuti lero zinthu zindiyendere bwino, ndipo musonyeze chikondi chanu chokhulupirika kwa mbuye wanga Abulahamu. 13 Ndaima pano pakasupe wa madzi, ndipo ana aakazi amumzindawu akubwera kudzatunga madzi. 14 Zichitike kuti, mtsikana amene ndimuuze kuti, ‘Chonde tula pansi mtsuko wako wa madzi kuti ndimweko,’ ndipo iye nʼkundiyankha kuti, ‘Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe,’ ameneyo akhale amene mwasankhira mtumiki wanu Isaki. Mukachita zimenezo, ndidziwa kuti mwasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mbuye wanga.”

15 Asanamalize nʼkomwe kulankhula, anangoona Rabeka mwana wa Betuele+ akutuluka mumzindawo. Betuele anali mwana wa Milika,+ ndipo Milika anali mkazi wa Nahori,+ mchimwene wake wa Abulahamu. Rabekayo anali atanyamula mtsuko paphewa pake. 16 Mtsikanayo anali wokongola mochititsa kaso, ndipo anali namwali amene anali asanagonepo ndi mwamuna. Iye analowa mʼchitsimemo nʼkutungira madzi mumtsuko wake, kenako anatulukamo. 17 Nthawi yomweyo mtumiki wa Abulahamuyo anamuthamangira nʼkumuuza kuti: “Chonde ndipatse madzi amumtsuko wako ndimweko pangʼono.” 18 Rabekayo anayankha kuti: “Eni, imwani mbuyanga.” Atatero anatula mtsuko wake mwamsanga nʼkuupendeketsa kuti mtumikiyo amwe. 19 Atamaliza kupereka madzi akumwawo, anati: “Nditungiranso madzi ngamila zanu mpaka zitamwa mokwanira.” 20 Choncho, iye mwamsanga anakhuthulira madzi amene anali mumtsuko aja muchomweramo ziweto. Kenako anayamba kuthamanga mobwerezabwereza kukatunga madzi ena pachitsimepo mpaka ngamila zonse za mlendoyo zitamwa mokwanira. 21 Nthawi yonseyi nʼkuti munthu uja akungomuyangʼana modabwa osanena chilichonse, kuti aone ngati Yehova wapangitsadi kuti pa ulendo wakewo, zinthu ziyende bwino kapena ayi.

22 Ngamila zija zitamaliza kumwa, mlendoyo anatenga ndolo yagolide yovala pamphuno yolemera hafu ya sekeli,* ndi zibangili ziwiri zagolide zolemera masekeli 10 nʼkumupatsa Rabeka. 23 Kenako anamufunsa kuti: “Chonde ndiuze, kodi ndiwe mwana wa ndani? Kodi kunyumba kwa bambo ako kuli malo oti tikhoza kugonako?” 24 Iye anayankha kuti: “Ine ndine mwana wa Betuele.+ Bambo angawo mayi awo ndi Milika, bambo awo ndi Nahori.”+ 25 Ananenanso kuti: “Chakudya cha ziweto tili nacho chambiri, komanso malo ogona alipo.” 26 Kenako mwamunayo anagwada pansi nʼkuwerama pamaso pa Yehova 27 nʼkunena kuti: “Atamandike Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, chifukwa sanasiye kusonyeza mbuye wanga chikondi chokhulupirika komanso nthawi zonse amakwaniritsa zimene wamulonjeza. Yehova wanditsogolera kunyumba kwa abale a mbuye wanga.”

28 Ndiyeno mtsikanayo anathamangira kunyumba kwa mayi ake nʼkufotokozera onse zimenezi. 29 Rabeka anali ndi mchimwene wake dzina lake Labani.+ Choncho Labani anathamanga kupita kwa munthu uja, yemwe anali kuchitsime, kunja kwa mzinda. 30 Labani ataona ndolo ya pamphuno ndi zibangili pamikono ya mchemwali wake, ndiponso atamva mawu a mchemwali wake Rabeka akuti: “Munthuyo anandiuza zakutizakuti,” Labaniyo anapita kwa munthuyo ndipo anamupeza ataima pafupi ndi ngamila zija pachitsimepo. 31 Atangomuona anamuuza kuti: “Tabwerani, inu wodalitsika wa Yehova. Bwanji mwangoima kunja kuno? Inetu ndakonza kale malo kunyumbaku, a inu ndi a ngamilazi.” 32 Munthuyo atamva zimenezo, anapita nʼkukalowa mʼnyumbamo. Kenako Labani anamasula ngamila nʼkuzipatsa chakudya. Anatenganso madzi nʼkusambitsa mapazi a mlendoyo ndi mapazi a anyamata omwe anali nawo. 33 Kenako anamubweretsera chakudya, koma iye anati: “Sindidya pokhapokha nditanena chimene ndabwerera.” Choncho Labani anati: “Ndiye lankhulanitu!”

34 Iye anati: “Ine ndine mtumiki wa Abulahamu.+ 35 Yehova wamudalitsa kwambiri mbuye wanga ndipo wamupatsa chuma chambiri moti ali ndi nkhosa, ngʼombe, siliva, golide, antchito aamuna ndi aakazi komanso ngamila ndi abulu.+ 36 Ndiponso Sara mkazi wake anamuberekera mbuye wangayo mwana wamwamuna, Sarayo atakalamba.+ Mbuye wanga adzamupatsa mwanayo zonse zimene ali nazo.+ 37 Choncho mbuye wangayo anandilumbiritsa kuti, ‘Usatengere mwana wanga mkazi pakati pa ana aakazi a Chikananiwa amene ndikukhala mʼdziko lawo.+ 38 Usachite zimenezo, koma upite kubanja la bambo anga, kwa abale anga,+ ukamʼtengere mkazi mwana wanga.’+ 39 Koma ineyo ndinafunsa mbuye wanga kuti, ‘Bwanji ngati mkaziyo atakana kubwera nane?’+ 40 Iye anandiyankha kuti: ‘Yehova, amene ndakhala ndikuyenda pamaso pake+ movomerezeka, atumiza mngelo+ wake kuti apite nawe limodzi, ndipo akakuthandiza kuti zimene ukuyenderazo zikatheke. Kumeneko, ukamʼtengere mkazi mwana wanga, kwa abale anga, kubanja la bambo anga.+ 41 Udzamasuka ku lumbiro limene wachitali ngati utapita kwa abale anga koma iwo nʼkukana kukupatsa mkazi. Zikatero udzamasuka ku lumbiro limene wachitali.’+

42 Nditafika kuchitsime lero, ndinati: ‘Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu, ngati mundithandizedi kuti zimene ndayendera zitheke, pachitike zinthu izi: 43 Mtsikana+ amene abwere pachitsime ndaima pano kuchokera mumzindawu kudzatunga madzi, ine nʼkumuuza kuti, “Chonde, ndimweko pangʼono madzi amumtsuko wakowo,” 44 iye nʼkundiyankha kuti, “Imwani, ndiponso nditungira madzi ngamila zanu kuti zimwe.” Ameneyo akhale mkazi amene Yehova wasankhira mwana wa mbuye wanga.’+

45 Ndisanamalize nʼkomwe kulankhula mumtima mwanga, ndinangoona Rabeka akutuluka mumzindawu, atanyamula mtsuko wake paphewa. Iye analowa mʼchitsime nʼkuyamba kutunga madzi. Kenako ndinamupempha kuti, ‘Chonde undigaireko madzi ndimwe.’+ 46 Mwamsanga iye anatula mtsuko wake umene unali paphewa lake nʼkundiuza kuti: ‘Imwani,+ ndipo nditungiranso ngamila zanu kuti zimwe.’ Choncho ndinamwa madziwo, ndipo anatungiranso ngamila kuti zimwe. 47 Atachita zimenezi ndinamufunsa kuti, ‘Kodi ndiwe mwana wa ndani?’ Iye anandiyankha kuti, ‘Ine bambo anga ndi a Betuele. Bambo awo ndi a Nahori, ndipo mayi awo ndi a Milika.’ Ndiyeno ndinamuveka ndolo pamphuno ndi zibangili mʼmikono yake.+ 48 Kenako ndinagwada nʼkuwerama pamaso pa Yehova. Ndinatamanda Yehova, Mulungu wa mbuye wanga Abulahamu,+ amene wanditsogolera panjira yoyenera, kuti ndidzatengere mkazi mwana wa mbuye wanga kwa mʼbale wake. 49 Tsopano ndiuzeni ngati mukufuna kusonyeza mbuye wanga chikondi komanso kukhala okhulupirika kwa iye. Koma ngati simukufuna, mundiuzenso kuti ndikayangʼane kwina.”*+

50 Ndiyeno Labani ndi Betuele anamuyankha kuti: “Zimenezi zachokera kwa Yehova. Ife sitingathe kukuvomerani kapena kukukanizani.* 51 Rabeka ndi ameneyu. Mʼtengeni muzipita naye, ndipo akakhale mkazi wa mwana wa mbuye wanu mogwirizana ndi zimene Yehova wanena.” 52 Mtumiki wa Abulahamu atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Yehova. 53 Kenako mtumikiyo anayamba kutulutsa zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala nʼkupatsa Rabeka. Anaperekanso zinthu zamtengo wapatali kwa mchimwene wake wa Rabeka ndi kwa mayi ake. 54 Pambuyo pake, iye limodzi ndi anyamata ake anadya ndi kumwa, ndipo anagona komweko.

Atadzuka mʼmawa, mtumiki wa Abulahamu uja anati: “Ndiloleni ndizipita kwa mbuye wanga.” 55 Koma mchimwene wa mtsikanayo ndi mayi ake anati: “Bwanji mtsikanayu akhalebe nafe masiku 10 okha, kenako akhoza kupita.” 56 Iye anawauza kuti: “Musandichedwetse, chifukwa Yehova wandithandiza kukwaniritsa zimene ndayendera. Ndiloleni ndizipita kwa mbuye wanga.” 57 Choncho iwo anati: “Tiyeni timuitane mtsikanayo kuti timve maganizo ake.” 58 Ndiyeno anaitana Rabekayo nʼkumufunsa kuti: “Kodi upita naye limodzi munthuyu?” Iye anayankha kuti: “Eya ndipita.”

59 Choncho iwo analola kuti mchemwali wawo Rabeka+ ndi mlezi* wake,+ apite limodzi ndi mtumiki wa Abulahamuyo ndi anyamata ake. 60 Ndiyeno iwo anadalitsa Rabeka kuti: “Iwe mchemwali wathu, ukakhale mayi wa anthu masauzande kuchulukitsa ndi masauzande 10, ndipo mbadwa* zako zikalande mizinda ya adani awo.”+ 61 Kenako Rabeka ndi atumiki ake aakazi ananyamuka nʼkukwera ngamila kumapita limodzi ndi mtumiki wa Abulahamu uja. Choncho mtumikiyo anatenga Rabeka nʼkupita naye.

62 Isaki ankakhala mʼdziko la Negebu.+ Ndiye tsiku lina, akuyenda panjira yochokera ku Beere-lahai-roi,+ 63 analowa patchire madzulo kuti akasinkhesinkhe.+ Atakweza maso, anaona ngamila zikubwera poteropo! 64 Nayenso Rabeka atakweza maso anaona Isaki, ndipo mwamsanga anatsika pangamila. 65 Ndiye anafunsa mtumiki uja kuti: “Kodi munthu akubwera apoyo kuchokera mʼtchire kudzakumana nafe ndi ndani?” Mtumikiyo anayankha kuti: “Ameneyo ndi mbuye wanga.” Choncho iye anatenga nsalu yophimba kumutu nʼkudziphimba nayo. 66 Kenako mtumikiyo anafotokozera Isaki zonse zimene anachita. 67 Ndiyeno Isaki analowa ndi mkaziyo mutenti ya Sara, mayi ake.+ Choncho Isaki anatenga Rabeka kukhala mkazi wake. Iye anamʼkonda kwambiri,+ ndipo zimenezi zinamutonthoza pambuyo pa imfa ya mayi ake.+

25 Tsopano Abulahamu anatenganso mkazi wina, dzina lake Ketura. 2 Patapita nthawi, mkaziyo anamuberekera Zimirani, Yokesani, Medani, Midiyani,+ Isibaki ndi Shuwa.+

3 Yokesani anabereka Sheba ndi Dedani.

Ana a Dedani anali Asurimu, Letusimu ndi Leumimu.

4 Ana a Midiyani anali Efa, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.

Onsewa anali ana aamuna a Ketura.

5 Pambuyo pake, Abulahamu anapatsa Isaki zonse zimene anali nazo.+ 6 Koma Abulahamu anapereka mphatso kwa ana amene adzakazi ake anamuberekera. Kenako, iye adakali ndi moyo, anatumiza anawo Kumʼmawa, kutali ndi mwana wake Isaki.+ 7 Abulahamu anakhala ndi moyo zaka 175. 8 Kenako Abulahamu anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino, wautali komanso atakhutira ndi moyo wake ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.* 9 Ana ake, Isaki ndi Isimaeli, anamuika mʼmanda, mʼphanga la Makipela, pamalo a Efuroni mwana wa Zohari Mheti, pafupi ndi Mamure.+ 10 Malo amenewa ndi omwe Abulahamu anagula kwa ana a Heti. Abulahamu anaikidwa kumeneko ndipo nʼkomwenso Sara mkazi wake anaikidwa.+ 11 Abulahamu atamwalira, Mulungu anapitiriza kudalitsa Isaki+ mwana wake. Isakiyo ankakhala pafupi ndi Beere-lahai-roi.+

12 Iyi ndi mbiri ya Isimaeli+ mwana wa Abulahamu, amene Hagara+ wa ku Iguputo, kapolo wa Sara anaberekera Abulahamu.

13 Mayina a ana a Isimaeli, malinga ndi mabanja awo ndi awa: Nebayoti,+ mwana woyamba wa Isimaeli, Kedara,+ Adibeele, Mibisamu,+ 14 Misima, Duma, Maasa, 15 Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. 16 Amenewa ndi ana a Isimaeli, mayina awo ndi amenewa potengera midzi yawo komanso misasa yawo.* Anali atsogoleri okwanira 12 malinga ndi mafuko awo.+ 17 Isimaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Kenako anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake. 18 Mbadwa zake zinayamba kukhala ku Havila+ pafupi ndi Shura+ moyandikana ndi Iguputo, mpaka ku Asuri. Iwo anakhala pafupi ndi abale awo onse.*+

19 Mbiri ya Isaki mwana wa Abulahamu+ ndi iyi.

Abulahamu anabereka Isaki. 20 Isaki anali ndi zaka 40 pamene anakwatira Rabeka, mwana wa Betuele+ wa Chiaramu, wa ku Padani-aramu, amene anali mchemwali wake wa Labani wa Chiaramu. 21 Isaki ankachonderera Yehova mosalekeza zokhudza mkazi wake, chifukwa anali wosabereka. Choncho Yehova anamva pemphero lake, ndipo Rabeka mkazi wakeyo anakhala woyembekezera. 22 Ndiyeno ana amene anali mʼmimba mwake anayamba kulimbana,+ moti iye anati: “Ngati umu ndi mmene ndivutikire, kuli bwino ndingofa.” Choncho anafunsa Yehova kuti adziwe chifukwa chake. 23 Yehova anamuyankha kuti: “Mʼmimba mwako muli mitundu iwiri ya anthu+ ndipo mitundu iwiri imene idzatuluke mʼmimba mwako idzakhala kosiyana.+ Mtundu wina udzakhala wamphamvu kuposa mtundu winawo,+ ndipo wamkulu adzatumikira wamngʼono.”+

24 Nthawi yoti Rabeka abereke inakwana, ndipo mʼmimba mwake munali ana amapasa. 25 Woyamba kubadwa anali wofiira, ndipo thupi lake lonse linali ngati wavala chovala chaubweya.+ Choncho anamupatsa dzina lakuti Esau.*+ 26 Pambuyo pake, mʼbale wake anabadwa, ndipo dzanja lake linali litagwira chidendene cha Esau.+ Choncho Isaki anapatsa mwanayo dzina lakuti Yakobo.*+ Pamene Rabeka ankabereka anawa nʼkuti Isaki ali ndi zaka 60.

27 Anyamatawa atakula, Esau anakhala mlenje waluso,+ munthu wokonda kuyenda mʼtchire. Koma Yakobo ankakonda kukhala mʼmatenti+ ndipo anali munthu wosalakwa. 28 Isaki ankakonda kwambiri Esau chifukwa ankamuphera nyama, koma Rabeka ankakonda kwambiri Yakobo.+ 29 Tsiku lina Yakobo akuphika mphodza, Esau anafika kuchokera kutchire, ndipo anali atatopa. 30 Ndiyeno Esau anapempha Yakobo kuti: “Chonde, fulumira ndigawireko pangʼono mphodza zofiira zimene ukuphikazo,* ndatopatu ine!”* Nʼchifukwa chake anamupatsa dzina lakuti Edomu.*+ 31 Poyankha Yakobo ananena kuti: “Choyamba, undigulitse ukulu wako monga woyamba kubadwa.”+ 32 Ndiye Esau anati: “Ine pano ndikufuna kufa ndi njala, ndiye ukuluwo uli ndi ntchito yanji kwa ine?” 33 Ndiyeno Yakobo anati: “Uyambe kaye walumbira!” Ndipo iye analumbiradi kwa Yakobo nʼkumugulitsa ukulu wake monga woyamba kubadwa.+ 34 Atatero Yakobo anapatsa Esau mkate ndi mphodza, ndipo iye anadya nʼkumwa. Kenako, ananyamuka nʼkumapita. Umu ndi mmene Esau anasonyezera kuti ankaona kuti ukulu wake unali wopanda phindu.

26 Tsopano mʼdzikomo munagwa njala yaikulu ngati imene inagwa mʼmasiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari. 2 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa iye nʼkumuuza kuti, “Usapite ku Iguputo. Ukhale mʼdziko limene ndikusonyeze. 3 Ukhale ngati mlendo mʼdzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbira kwa bambo ako Abulahamu+ kuti: 4 ‘Ndidzachulukitsa mbadwa zako ngati nyenyezi zakumwamba,+ ndipo mayiko onsewa ndidzawapereka kwa mbadwa* zako.+ Mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa mbadwa zako.’+ 5 Ndidzachita zimenezi chifukwa Abulahamu anamvera mawu anga, ndipo ankachita zofuna zanga ndi kusunga malamulo anga onse.”+ 6 Choncho Isaki anapitiriza kukhala ku Gerari.+

7 Anthu akumeneko ankamufunsafunsa za mkazi wake, ndipo iye ankawayankha kuti, “Ndi mchemwali wanga ameneyu.”+ Ankaopa kunena kuti, “Ameneyu ndi mkazi wanga,” chifukwa anati: “Anthu a kuno akhoza kundipha chifukwa cha Rabeka,” pakuti mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso.+ 8 Patapita nthawi, Abimeleki mfumu ya Afilisiti ankayangʼana pawindo, ndipo anaona Isaki akucheza mwachikondi ndi mkazi wake* Rabeka.+ 9 Nthawi yomweyo Abimeleki anaitanitsa Isaki nʼkumufunsa kuti: “Ameneyu ndi mkazi wako eti? Nanga nʼchifukwa chiyani unanena kuti, ‘Ndi mchemwali wangaʼ?” Ndiyeno Isaki anayankha kuti: “Ndinanena choncho poopa kuti andipha chifukwa cha iye.”+ 10 Koma Abimeleki anapitiriza kuti: “Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi?+ Munthu wina akanatha kugona ndi mkazi wakoyu, ndipo ukanatipalamulitsa.”+ 11 Kenako Abimeleki analamula anthu ake onse kuti: “Aliyense amene angavutitse munthu uyu komanso mkazi wake, aphedwa.”

12 Zitatero, Isaki anayamba kudzala mbewu mʼdzikomo. Mʼchaka chimenechi anakolola zochuluka moti pa thumba limodzi lililonse la mbewu zimene anadzala anakolola matumba 100, chifukwa Yehova ankamudalitsa.+ 13 Isaki analemera, ndipo zinthu zinapitiriza kumuyendera bwino moti anali ndi chuma chambiri. 14 Iye anali ndi nkhosa komanso ngʼombe zankhaninkhani. Analinso ndi atumiki ochuluka kwambiri,+ moti Afilisitiwo anayamba kumʼchitira nsanje.

15 Choncho Afilisitiwo anatenga dothi nʼkukwirira zitsime zonse zimene atumiki a Abulahamu bambo ake anakumba, bambo akewo ali moyo.+ 16 Kenako Abimeleki anauza Isaki kuti: “Uchoke kwathu kuno, chifukwa wakhala munthu wamphamvu kwambiri kuposa ifeyo.” 17 Choncho Isaki anachoka kumeneko nʼkukamanga msasa wake mʼchigwa cha* Gerari+ nʼkuyamba kukhala kumeneko. 18 Ndiyeno Isaki anafukula zitsime zimene zinakumbidwa mʼmasiku a Abulahamu bambo ake. Afilisiti anakwirira zitsime zimenezi Abulahamu atamwalira,+ ndipo iye anazitchulanso mayina amene bambo ake anazipatsa.+

19 Pamene atumiki a Isaki ankakumba zitsime mʼchigwacho,* anapeza chitsime cha madzi abwino. 20 Koma abusa a ku Gerari anayamba kukangana ndi abusa a Isaki, kuti: “Ndi madzi athu amenewa!” Choncho iye anapatsa chitsimecho dzina lakuti Eseke,* chifukwa abusawo anakangana naye. 21 Kenako iwo anakumbanso chitsime china, koma anayambanso kukanganirana chitsimecho. Choncho anachipatsa dzina lakuti Sitina.* 22 Pambuyo pake anasamuka kumeneko, ndipo anakumbanso chitsime china. Koma sanakanganirane chitsime chimenechi. Choncho iye anachipatsa dzina lakuti Rehoboti* nʼkunena kuti: “Chifukwa chake nʼchakuti, tsopano Yehova watipatsa malo okwanira, ndipo watipangitsa kuti tichulukane mʼdziko lino.”+

23 Kenako iye anachokanso kumeneko nʼkupita ku Beere-seba.+ 24 Usiku umenewo, Yehova anaonekera kwa iye ndipo anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu wa bambo ako Abulahamu.+ Usaope,+ chifukwa ndili nawe. Ndidzakudalitsa ndi kuchulukitsa mbadwa* zako chifukwa cha Abulahamu mtumiki wanga.”+ 25 Kumeneko Isaki anamanga guwa lansembe nʼkuitanira pa dzina la Yehova.+ Anamanganso tenti yake,+ ndipo atumiki ake anakumba chitsime kumeneko.

26 Patapita nthawi, Abimeleki anafika kwa iye kuchokera ku Gerari limodzi ndi Ahuzati mlangizi wake komanso Fikolo mkulu wa asilikali ake.+ 27 Ndiyeno Isaki anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine? Si paja munadana nane ine nʼkundithamangitsa kwanu kuja?” 28 Koma iwo anayankha kuti: “Ife taona kuti Yehova ali ndi iwe.+ Choncho tinaganiza zokupempha kuti, ‘tilumbire kuti pakati pa iwe ndi ife pakhale mtendere ndipo tichite nawe pangano.+ 29 Tichite pangano kuti sudzatichitira choipa chilichonse, chifukwa ifenso sitinakuchitire choipa chilichonse. Tinakuchitira zabwino zokhazokha, chifukwa tinakuuza kuti uchoke kwathu kuja mwamtendere. Ndipo panopa Yehova wakudalitsa.’” 30 Kenako Isaki anawakonzera phwando, ndipo iwo anadya ndi kumwa. 31 Mʼmawa wake, analawirira kudzuka nʼkulumbiritsana.+ Kenako Isaki anatsanzikana nawo ndipo iwo anachoka mwamtendere.

32 Tsiku limenelo, atumiki a Isaki anapita kwa iye nʼkumuuza zokhudza chitsime chimene anakumba.+ Anamuuza kuti: “Ife tapeza madzi.” 33 Choncho chitsimecho anachipatsa dzina lakuti Siba.* Nʼchifukwa chake dzina la mzindawo ndi Beere-seba+ mpaka lero.

34 Esau atakwanitsa zaka 40, anakwatira Yuditi mwana wa Beeri, Muhiti. Anakwatiranso Basemati mwana wa Eloni, Muhiti.+ 35 Akaziwo anabweretsa chisoni kwa Isaki ndi Rabeka.+

27 Tsopano Isaki anakalamba moti maso ake anasiya kuona. Ndiyeno anaitana mwana wake wamkulu Esau+ nʼkumuuza kuti: “Mwana wanga!” Iye anayankha kuti: “Ine bambo!” 2 Isaki anapitiriza kuti: “Taona, ine tsopano ndakalamba. Tsiku lililonse ndikhoza kufa. 3 Choncho tenga zida zako pompano. Utenge uta ndi kachikwama kako koikamo mivi ndipo upite kutchire ukandisakire nyama.+ 4 Udzaikonze bwino ngati mmene ndimaikondera muja nʼkundibweretsera. Ndikufuna ndidye kenako ndikudalitse ndisanafe.”

5 Koma pamene Isaki ankalankhula ndi mwana wake Esau, Rabeka ankamvetsera. Ndiyeno Esau anapita kutchire kuti akaphe nyama nʼkubwera nayo.+ 6 Tsopano Rabeka anauza mwana wake Yakobo+ kuti: “Ndamva bambo ako akuuza mkulu wako Esau kuti, 7 ‘Ukandiphere nyama nʼkuiphika bwino. Ndiye udzandipatse kuti ndidye, kenako ndidzakudalitse pamaso pa Yehova ndisanafe.’+ 8 Tsopano mwana wanga, mvetsera mosamala ndipo uchite zimene ndikuuze.+ 9 Pita kuli ziwetoko ukatengeko ana a mbuzi awiri onenepa bwino. Ndikufuna ndiwakonzere bambo ako chakudya chokoma kwambiri chimene amakonda chija. 10 Ndiye ukapereke kwa bambo ako akadye, kuti akudalitse asanamwalire.”

11 Yakobo anayankha Rabeka mayi ake kuti: “Koma mʼbale wanga Esau ndi munthu wacheya,*+ pamene ine ndili ndi khungu losalala. 12 Nanga bambo akakandikhudza?+ Ndithu andiona ngati ndikungofuna kuwapusitsa ndipo ndidzibweretsera matemberero, osati madalitso.” 13 Koma mayi akewo anamuuza kuti: “Matemberero amenewo abwere kwa ine mʼmalo mwa iwe mwana wanga. Ingochita zimene ndakuuzazi. Pita ukanditengere ana a mbuziwo.”+ 14 Choncho iye anakawatenga nʼkubwera nawo kwa mayi ake. Mayi akewo anaphika nyamayo mopatsa mudyo mmene bambo ake ankaikondera. 15 Zitatero, Rabeka anatenga zovala zabwino kwambiri za mwana wake wamkulu Esau, zimene anali nazo mʼnyumba nʼkuveka mwana wake wamngʼono, Yakobo.+ 16 Anamuvekanso zikopa za ana a mbuzi aja, mʼmanja mwake ndi pakhosi pake pamene panalibe cheya.+ 17 Kenako anapatsa mwana wake Yakobo chakudya chokoma chimene anakonzacho, limodzi ndi mkate umene anaphika.+

18 Ndiyeno Yakobo anapita kumene kunali bambo ake nʼkunena kuti: “Bambo!” Ndipo Isaki anayankha kuti: “Ine pano! Ndiwe ndani kodi mwana wanga?” 19 Yakobo anauza bambo akewo kuti: “Ndine Esau, mwana wanu woyamba.+ Ndachita zonse zimene munandiuza. Dzukani, khalani pansi mudye nyama imene ndakupherani, kuti mundidalitse.”+ 20 Atamva zimenezi Isaki anafunsa mwana wake kuti: “Koma mwana wanga, waipeza bwanji mofulumira chonchi?” Iye anayankha kuti: “Yehova Mulungu wanu ndi amene waikusira kwa ine.” 21 Koma Isaki anauza Yakobo kuti: “Tayandikira ndikukhudze mwana wanga. Ndikufuna ndidziwe ngati ndiwedi mwana wanga Esau kapena ayi.”+ 22 Choncho Yakobo anafika pafupi ndi bambo ake Isaki. Atamukhudza ananena kuti: “Mawu akumveka kuti ndi a Yakobo, koma manja akumveka kuti ndi a Esau.”+ 23 Iye sanamuzindikire, chifukwa manja ake anali acheya ngati manja a Esau mʼbale wake. Choncho anamudalitsa.+

24 Kenako anamufunsanso kuti: “Koma ndiwedi mwana wanga Esau?” Iye anayankha kuti: “Eya ndi ineyo.” 25 Ndiyeno Isaki anati: “Mwana wanga, ndipatsire nyama imene wandipherayo kuti ndidye, kenako ndikudalitsa.” Choncho anamupatsira ndipo anadya. Anamupatsiranso vinyo ndipo iye anamwa. 26 Kenako bambo akewo anamuuza kuti: “Ndiyandikire mwana wanga, undikise.”*+ 27 Choncho anamuyandikira nʼkumukisa, ndipo anamva kafungo ka zovala zake.+ Kenako anamudalitsa kuti:

“Eya, kafungo ka mwana wanga kakununkhira ngati fungo labwino la munda umene Yehova waudalitsa. 28 Mulungu woona akupatse mame akumwamba,+ ndi nthaka yachonde ya dziko lapansi.+ Achulukitsenso zokolola zako ndi vinyo wako watsopano.+ 29 Mafuko akutumikire ndipo mitundu ya anthu ikugwadire. Ukhale mbuye wa abale ako, ndipo ana a mayi ako akugwadire.+ Aliyense wokutemberera atembereredwe, ndipo aliyense wokudalitsa adalitsidwe.”+

30 Isaki atangomaliza kudalitsa Yakobo, komanso Yakoboyo atangochoka kumene kunali Isaki bambo ake, Esau mʼbale wake anafika kuchokera kokasaka nyama.+ 31 Iyenso anakonzera bambo ake nyama ija mopatsa mudyo. Kenako anapita nayo kwa bambo ake nʼkuwauza kuti: “Bambo, dzukani mudye nyama imene ine mwana wanu ndakupherani, kuti mundidalitse.” 32 Ndiyeno Isaki, bambo ake, anati: “Nanga iwenso ndiwe ndani?” Iye anayankha kuti: “Ndine mwana wanu, mwana wanu woyamba Esau.”+ 33 Pamenepo Isaki anayamba kunjenjemera kwambiri, ndipo anati: “Nanga amene wandiphera nyama nʼkundibweretsera uja ndi ndani? Ine ndadya kale iwe usanabwere, moti ndamudalitsa. Ndipo adzalandiradi madalitso amenewa!”

34 Atamva mawu a bambo akewa, Esau anayamba kulira ndi kukuwa mogonthetsa mʼkhutu, komanso mowawidwa mtima kwambiri. Iye anachonderera bambo ake kuti: “Bambo ndidalitseni, ndidalitseni inenso chonde!”+ 35 Koma Isaki anamuuza kuti: “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo kuti adzalandire madalitso amene anali ako.” 36 Ndiyeno Esau anati: “Aka tsopano nʼkachiwiri akundichenjerera amene uja! Kodi si chifukwa chake dzina lake ndi Yakobo?*+ Ukulu wanga anatenga kale,+ apa tsopano watenganso madalitso anga!”+ Iye ananenanso kuti: “Kodi bambo, zoona palibiretu dalitso lililonse limene mwandisungirako?” 37 Koma Isaki anayankha Esau kuti: “Taona, iye uja ndamuika kukhala mbuye wako.+ Ndamupatsa abale ake onse kuti akhale atumiki ake. Komanso ndamudalitsa kuti akhale ndi zokolola zambiri ndiponso vinyo watsopano wambiri.+ Nanga chatsalanso nʼchiyani choti ndikuchitire mwana wanga?”

38 Esau anafunsa bambo ake kuti: “Bambo, ngakhale dalitso limodzi silinatsaleko? Bambo ndidalitseni, inenso ndidalitseni chonde!” Atatero Esau analira mofuula kwambiri, misozi ili mbwembwembwe.+ 39 Koma Isaki bambo ake anamuuza kuti:

“Taona, udzakhala kutali ndi nthaka yachonde, komanso kutali ndi mame akumwamba.+ 40 Pa nthawi yonse ya moyo wako uzidzadalira lupanga+ ndipo udzatumikira mʼbale wako.+ Koma ukadzatopa ndi goli lake, udzalithyola ndi kulichotsa mʼkhosi mwako.”+

41 Choncho, Esau anayamba kudana ndi Yakobo chifukwa cha madalitso amene bambo ake anamupatsa.+ Mumtima mwake ankanena kuti: “Masiku olira maliro a bambo anga ali pafupi.+ Pambuyo pake, ndidzamupha mʼbale wanga Yakobo.” 42 Rabeka atauzidwa zimene mwana wake wamkulu Esau ananena, nthawi yomweyo anaitanitsa mwana wake wamngʼono Yakobo nʼkumuuza kuti: “Mʼbale wako Esau akufuna akuphe pobwezera zimene unamuchitira.* 43 Choncho uchite zimene ndikuuze mwana wanga. Nyamuka, thawira kwa mchimwene wanga Labani, ku Harana.+ 44 Ukakhale naye kwa kanthawi, mpaka ukali wa mʼbale wako utatha. 45 Ukakhale kumeneko mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utaphwa komanso mpaka ataiwala zimene unamuchitira. Kenako ndidzatuma anthu kuti adzakutenge. Nanga nditaye ana awiri tsiku limodzi?”

46 Izi zitachitika, Rabeka ankauza Isaki nthawi ndi nthawi kuti: “Moyo wanga ndikunyansidwa nawo chifukwa cha akazi a Chihetiwa.+ Ngati Yakobo nayenso angatenge mkazi pakati pa akazi a Chiheti ngati amenewa, ndi bwino ndingofa!”+

28 Ndiyeno Isaki anaitana Yakobo nʼkumudalitsa ndipo anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+ 2 Upite ku Padani-aramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani+ mchimwene wa mayi ako. 3 Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+ 4 Adzakupatsa iwe ndi mbadwa* zako madalitso amene analonjeza Abulahamu,+ kuti dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli, limene Mulungu anapatsa Abulahamu, lidzakhale lako.”+

5 Choncho Isaki anatumiza Yakobo ndipo iye ananyamuka kupita ku Padani-aramu. Anapita kwa Labani mwana wa Betuele, wa Chiaramu.+ Labaniyo anali mchimwene wake wa Rabeka+ amene anali mayi ake a Yakobo ndi Esau.

6 Esau anaona kuti Isaki wadalitsa Yakobo ndiponso kuti wamʼtumiza ku Padani-aramu kukatenga mkazi kumeneko. Anaona kuti pomudalitsa anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.”+ 7 Anaonanso kuti Yakobo wamvera bambo ake ndi mayi ake ndipo wapita ku Padani-aramu.+ 8 Zitatero Esau anazindikira kuti Isaki bambo ake ankanyansidwa ndi ana aakazi a ku Kanani.+ 9 Choncho Esau anapita kwa Isimaeli* nʼkukatengako mkazi wina kuwonjezera pa akazi amene anali nawo. Mkaziyo dzina lake anali Mahalati ndipo anali mchemwali wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu.+

10 Yakobo anachoka ku Beere-seba nʼkupitiriza ulendo wake wopita ku Harana.+ 11 Atafika pamalo ena, anaganiza zogona pamenepo chifukwa dzuwa linali litalowa. Choncho anatenga mwala umodzi pamalopo ndipo anautsamira nʼkugona.+ 12 Kenako anayamba kulota. Mʼmalotowo anaona masitepe* ochokera padziko lapansi mpaka kumwamba, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pamasitepewo.+ 13 Pamwamba pa masitepewo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:

“Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ 14 Mbadwa zako ndithu zidzachuluka ngati mchenga wapadziko lapansi+ ndipo ana ako adzafalikira kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera. Komanso kudzera mwa iwe ndi mwa mbadwa zako, mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa ndithu.+ 15 Ine ndili ndi iwe. Ndikuyangʼanira kulikonse kumene ungapite ndipo ndidzakubwezera kudziko lino.+ Sindidzakusiya mpaka nditachita zimene ndakulonjeza.”+

16 Kenako Yakobo anadzuka nʼkunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo ano, koma ine sindinadziwe.” 17 Iye anachita mantha nʼkunenanso kuti: “Malo ano ndi oopsa! Ndithu malo ano ndi nyumba ya Mulungu,+ ndiponso ndi khomo lakumwamba.”+ 18 Choncho Yakobo anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutenga mwala umene anautsamira uja. Atatero anauimika monga mwala wachikumbutso ndipo anauthira mafuta pamwamba pake.+ 19 Kenako, malowo anawapatsa dzina lakuti Beteli.* Koma poyamba dzina la mzindawo linali Luzi.+

20 Yakobo analonjeza kuti: “Mulungu akapitiriza kukhala nane komanso kunditeteza pa ulendo wangawu, ndiponso akadzandipatsa chakudya ndi zovala, 21 komanso ndikadzabwerera mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga. 22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatse, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi.”

29 Kenako Yakobo anapitiriza ulendo wake wopita kudziko la anthu a Kumʼmawa. 2 Atafika pamalo enaake anaona chitsime, ndipo panali magulu atatu a nkhosa zitagona pansi, chifukwa mʼpamene anthu ankakonda kumwetserapo ziweto. Pachitsimepo panali potseka ndi mwala waukulu. 3 Nkhosa zonse zikafika pamalopo, abusa ankagubuduza mwala kuuchotsa pachitsimepo nʼkutunga madzi kuti nkhosazo zimwe. Akamaliza, ankabwezeretsa mwalawo pachitsimepo.

4 Ndiyeno Yakobo anawafunsa kuti: “Abale anga, kodi mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera ku Harana.”+ 5 Anawafunsanso kuti: “Kodi Labani+ mdzukulu wa Nahori+ mumamudziwa?” Iwo anati: “Eya timamudziwa.” 6 Kenako anawafunsa kuti: “Kodi ali bwino?” Iwo anayankha kuti: “Ali bwino. Komanso mwana wake Rakele,+ ndi uyo akubwera ndi nkhosa apoyo.” 7 Kenako Yakobo anawauza kuti: “Inotu si nthawi yosonkhanitsa ziweto, ndi masanatu ano. Zimwetseni madzi, kenako mupite nazo kubusa.” 8 Iwo anayankha kuti: “Sitiloledwa kuchita zimenezo mpaka magulu onse a nkhosa atafika. Zikatero timachotsa mwala wa pachitsimewu nʼkumwetsa nkhosa zathu.”

9 Akulankhula nawo choncho, Rakele anafika ndi nkhosa za bambo ake, chifukwa anali mʼbusa wamkazi. 10 Yakobo ataona Rakele mwana wa Labani, mchimwene wa mayi ake, ndiponso nkhosa za Labaniyo, nthawi yomweyo anapita pachitsime paja nʼkugubuduza mwalawo kuuchotsa pachitsimepo. Atatero anatungira madzi nkhosa za Labani, mchimwene wa mayi ake. 11 Ndiyeno Yakobo anakisa* Rakele, nʼkulira mofuula uku akugwetsa misozi. 12 Kenako anayamba kuuza Rakele kuti iye ndi wachibale wa bambo ake, ndiponso kuti ndi mwana wa Rabeka. Atamva zimenezi, Rakele anathamanga kukauza bambo ake.

13 Labani+ atangomva za Yakobo, mwana wa mchemwali wake, anathamanga kukakumana naye. Atafika, anamʼkumbatira ndi kumukisa nʼkupita naye kunyumba kwake. Ndipo Yakobo anafotokozera Labani zonse zimene zinamuchitikira. 14 Ndiyeno Labani anamuuza kuti: “Iwe ndiwedi mʼbale wanga weniweni.”* Choncho anakhala naye mwezi wathunthu.

15 Kenako Labani anafunsa Yakobo kuti: “Kodi ukufuna undigwirire ntchito yaulere chifukwa chakuti ndiwe wachibale wanga?+ Ndiuze, kodi ndidzakulipire chiyani?”+ 16 Labani anali ndi ana aakazi awiri, wamkulu dzina lake anali Leya, wamngʼono anali Rakele.+ 17 Leya anali ndi maso osaoneka bwino, pamene Rakele anali mtsikana wooneka bwino komanso wokongola kwambiri. 18 Koma Yakobo anakonda Rakele, ndiye anati: “Ndine wokonzeka kukugwirirani ntchito zaka 7, kuti mudzandipatse Rakele mwana wanu wamngʼonoyu.”+ 19 Labani anati: “Ndi bwino kuti Rakeleyu ndikupatse iweyo, kusiyana nʼkuti ndimupereke kwa munthu wina. Upitirize kukhala ndi ine.” 20 Yakobo anagwira ntchito zaka 7 kuti atenge Rakele.+ Koma zakazo anangoziona ngati masiku ochepa chabe, chifukwa anamʼkonda kwambiri mtsikanayo.

21 Kenako Yakobo anauza Labani kuti: “Ndipatseni mkazi wanga, chifukwa masiku anga akwana, kuti ndimukwatire.”* 22 Atatero Labani anasonkhanitsa anthu onse akumeneko nʼkuchita phwando. 23 Koma kutada, Labani anaganiza zotenga Leya mwana wake nʼkupita naye kwa Yakobo, kuti akagone naye. 24 Labani anaperekanso Zilipa kapolo wake kwa mwana wake Leya, kuti akhale kapolo wake.+ 25 Kutacha mʼmawa, Yakobo anadabwa kuona kuti ali ndi Leya. Ataona zimenezi anafunsa Labani kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? Ine ndakugwirirani ntchito kuti mundipatse Rakele. Nanga nʼchifukwa chiyani mwandipusitsa chonchi?”+ 26 Labani anayankha kuti: “Mogwirizana ndi mwambo wathu, nʼzosaloleka kukwatitsa wamngʼono mkulu wake asanakwatiwe. 27 Usangalale ndi mkaziyu mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako ndidzakupatsa mkazi winayu, komabe udzandigwirira ntchito zaka zina 7.”+ 28 Choncho Yakobo anasangalaladi ndi Leya mlungu wonse wokondwerera ukwati wake. Kenako Labani anamupatsa mwana wake Rakele kuti akhale mkazi wake. 29 Labani anaperekanso kapolo wake Biliha+ kwa mwana wake Rakele kuti akhale kapolo wake.+

30 Ndiyeno Yakobo anagonanso ndi Rakele ndipo anamʼkonda kwambiri kuposa Leya, moti anagwiriranso ntchito Labani zaka zina 7.+ 31 Yehova ataona kuti Leya sankakondedwa kwenikweni,* anamʼpatsa mphamvu zobereka,*+ koma Rakele anali wosabereka.+ 32 Choncho Leya anakhala woyembekezera ndipo anabereka mwana wamwamuna. Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Rubeni,*+ ndipo anati: “Chifukwa Yehova waona kusautsika kwanga,+ ndipo tsopano mwamuna wanga ayamba kundikonda.” 33 Leya anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Yehova wandipatsa mwana wina chifukwa wamva kudandaula kwanga kuti sindikukondedwa kwenikweni.” Choncho mwanayo anamupatsa dzina lakuti Simiyoni.*+ 34 Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Apa tsopano mwamuna wanga andikonda basi, chifukwa ndamuberekera ana aamuna atatu.” Choncho mwanayo anamupatsa dzina lakuti Levi.*+ 35 Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, ndipo anati: “Tsopano nditamanda Yehova.” Choncho Leya anamupatsa mwanayo dzina lakuti Yuda.*+ Atabereka mwana ameneyu, anasiya kaye kubereka.

30 Rakele ataona kuti sanaberekere Yakobo ana, anayamba kuchitira nsanje mchemwali wake. Iye anauza Yakobo kuti: “Mundipatse ana, apo ayi kuli bwino ndingofa.” 2 Pamenepo Yakobo anamupsera mtima kwambiri Rakele nʼkumuyankha kuti: “Kodi ine ndine Mulungu amene akukulepheretsa kuberekayo?” 3 Kenako Rakele anati: “Tengani kapolo wanga Biliha+ kuti mugone naye nʼcholinga choti andiberekere ana,* kuti inenso ndikhale ndi ana kudzera mwa iye.” 4 Choncho Rakele anapereka kapolo wake Biliha kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake, ndipo iye anagona naye.+ 5 Biliha anakhala woyembekezera ndipo patapita nthawi anamuberekera Yakobo mwana wamwamuna. 6 Ndiyeno Rakele anati: “Mulungu wakhala woweruza wanga komanso wamva mawu anga, ndipo wandipatsa mwana wamwamuna.” Nʼchifukwa chake Rakele anapatsa mwanayo dzina lakuti Dani.*+ 7 Biliha kapolo wa Rakele anakhalanso woyembekezera moti patapita nthawi anamuberekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 8 Ndiyeno Rakele anati: “Ndalimbana mwamphamvu ndi mchemwali wanga ndipo ndapambananso.” Choncho anapatsa mwanayo dzina lakuti Nafitali.*+

9 Leya ataona kuti wasiya kubereka, anapereka kapolo wake Zilipa kwa Yakobo kuti akhale mkazi wake.+ 10 Zilipa kapolo wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wamwamuna. 11 Zitatero Leya anati: “Ndachita mwayi!” Choncho anapatsa mwanayo dzina lakuti Gadi.*+ 12 Kenako Zilipa kapolo wa Leya, anaberekera Yakobo mwana wina wamwamuna. 13 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Ndasangalala kwambiri! Akazi adzanena kuti ndine wosangalala.”+ Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Aseri.*+

14 Pa nthawi yokolola tirigu, Rubeni+ anapita kutchire kukayenda. Kumeneko anapezako zipatso za mandereki,* ndipo anazitenga nʼkupita nazo kwa Leya mayi ake. Ndiyeno Rakele anapempha Leya kuti: “Chonde, undipatseko mandereki a mwana wakowa.” 15 Pamenepo, Leya anayankha Rakele kuti: “Kodi si zokwanira kuti unatenga mwamuna wanga?+ Ndiye pano ukufuna kutenganso mandereki a mwana wanga?” Choncho Rakele anati: “Chabwino, usiku walero mwamunayu agona ndi iwe kuti tisinthane ndi mandereki a mwana wakowa.”

16 Pamene Yakobo ankachokera kumunda madzulo, Leya anapita kukakumana naye nʼkumuuza kuti: “Lero mugona ndi ine, chifukwa ndapereka mandereki a mwana wanga kwa Rakele kuti mugone ndi ine.” Usiku umenewo Yakobo anagonadi ndi Leya. 17 Mulungu anamva pemphero la Leya ndipo anakhala woyembekezera. Patapita nthawi, Leya anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 5. 18 Mwanayo atabadwa, Leya anati: “Mulungu wandipatsa mphoto* chifukwa ndapereka kapolo wanga kwa mwamuna wanga.” Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Isakara.*+ 19 Leya anakhalanso woyembekezera, moti patapita nthawi anaberekera Yakobo mwana wamwamuna wa 6.+ 20 Ndiyeno Leya anati: “Mulungu wandipatsadi mphoto yabwino. Tsopano mwamuna wanga ayamba kukondwera nane,+ chifukwa ndamuberekera ana aamuna 6.”+ Choncho Leya anapatsa mwanayo dzina lakuti Zebuloni.*+ 21 Kenako, Leya anabereka mwana wamkazi ndipo anamupatsa dzina lakuti Dina.+

22 Potsirizira pake, Mulungu anakumbukira Rakele ndipo anamva pemphero lake nʼkumuthandiza kuti ayambe kubereka.*+ 23 Rakele anakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna. Ndiyeno iye anati: “Mulungu wachotsa kunyozeka kwanga.”+ 24 Choncho Rakele anapatsa mwanayo dzina lakuti Yosefe,*+ ndipo anati: “Yehova wandiwonjezera mwana wina wamwamuna.”

25 Rakele atabereka Yosefe, nthawi yomweyo Yakobo anauza Labani kuti: “Ndiloleni ndizipita kwathu, kudziko lakwathu.+ 26 Ndipatseni akazi anga ndi ana anga kuti ndizipita chifukwa ndinakupatsani kale malipiro pokugwirirani ntchito mwakhama, ndipo inunso mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani.”+ 27 Koma Labani anauza Yakobo kuti: “Ngati wandikomera mtima, uzikhala konkuno. Ndawombeza ndipo ndapeza kuti* Yehova akundidalitsa chifukwa cha iwe.” 28 Anamuuzanso kuti: “Ndiuze malipiro ako ndipo ndikupatsa.”+ 29 Yakobo anayankha Labani kuti: “Inuyo mukudziwa ntchito imene ndakugwirirani, ndiponso mmene ndasamalirira ziweto zanu.+ 30 Mukudziwa kuti ine ndisanabwere munali ndi ziweto zochepa, koma pano ziweto zanu zachuluka ndipo Yehova wakudalitsani kuchokera pamene ndinabwera kuno. Ndiye kodi ineyo ndidzayamba liti kugwirira ntchito banja langa?”+

31 Kenako Labani anati: “Ndikupatse chiyani?” Yakobo anayankha kuti: “Musandipatse kanthu. Koma mukachita zimene ndikupempheni pano, ndiyambiranso kuweta ziweto zanu, ndipo ndipitiriza kuziyangʼanira.+ 32 Ine ndipita kukayenda pakati pa ziweto zanu zonse lero. Inuyo mukapatule nkhosa iliyonse yamathothomathotho kapena yamawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaingʼono yamphongo yabulauni, ndi mbuzi iliyonse yaikazi yamawangamawanga kapena yamathothomathotho. Kuyambira panopa, ziweto zimene zizibadwa motere zizikhala malipiro anga.+ 33 Tsiku lililonse limene mudzabwere kudzaona malipiro anga, mudzaona chilungamo changa.* Mukadzapeza mbuzi iliyonse yaikazi yopanda mathothomathotho kapena mawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaingʼono yamphongo yomwe si yabulauni ili ndi ine, imeneyo ndiye kuti ndaba.”

34 Pamenepo Labani anati: “Chabwino, zikhale mmene waneneramo.”+ 35 Choncho tsiku limenelo, Labani anachotsa mbuzi zamphongo zamizeremizere ndi zamawangamawanga, ndiponso mbuzi zonse zazikazi zamathothomathotho ndi zamawangamawanga pakati pa ziweto zake. Anachotsanso iliyonse imene inali ndi banga loyera ndi nkhosa iliyonse yamphongo yaingʼono yabulauni, nʼkuzipereka kwa ana ake. 36 Atatero anapita ndi ziweto zakezo kumalo amene anali pamtunda woyenda masiku atatu kuchokera pamene panali Yakobo. Ndipo Yakobo anapitiriza kuweta ziweto zotsala za Labani.

37 Ndiyeno Yakobo anatenga timitengo tatiwisi ta mlanje, amondi ndi katungulume nʼkutisenda makungwa mwa apo ndi apo, mwakuti choyera chamkati mwake chinaonekera. 38 Kenako anaika timitengo timene anatisendasenda tija muzomwera madzi za ziweto. Anatiika mmenemo kuti ziweto zikabwera kudzamwa madzi, zazikazi zikaona timitengoto zizikonzekera kutenga bere.

39 Choncho ziweto zazikazi zikaona timitengoto zinkakonzekera kutenga bere. Zikatero, zinkaswa ana amizeremizere ndi amawangamawanga. 40 Kenako Yakobo anachotsapo nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono nʼkuziika pazokha. Atatero, anapatula nkhosa zonse zamizeremizere ndi zabulauni zimene zinali pakati pa ziweto za Labani. Kenako anatembenuza nkhosa zotsalazo kuti ziyangʼane zamizeremizere ndi zabulauni zija. Iye anaika ziweto zake pazokha, ndipo sanaziphatikize ndi ziweto za Labani. 41 Nthawi zonse ziweto zazikazi zamphamvu zikakonzekera kutenga bere, Yakobo ankaika timitengo tija mʼngalande momwera madzi kuti nkhosazo zitiyangʼane. 42 Koma nkhosazo zikakhala zofooka, iye sankaika timitengo tija momwera madzimo. Choncho nthawi zonse nkhosa zofooka zinkakhala za Labani koma zamphamvu zinkakhala za Yakobo.+

43 Yakobo anapeza chuma chambiri. Iye anali ndi ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna komanso ngamila ndi abulu.+

31 Patapita nthawi, Yakobo anamva zimene ana aamuna a Labani ankanena kuti: “Yakobo watenga zinthu zonse za bambo athu, ndipo chuma chonse chimene ali nachochi chachokera kwa bambo athu.”+ 2 Yakobo akayangʼana nkhope ya Labani ankaona kuti sakumuyangʼana ndi diso labwino ngati poyamba.+ 3 Kenako Yehova anauza Yakobo kuti: “Bwerera kudziko la makolo ako ndi kwa abale ako,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukuthandiza.” 4 Ndiyeno Yakobo anaitanitsa Rakele ndi Leya kuti abwere kubusa kumene iye anali ndi nkhosa zake. 5 Iye anawauza kuti:

“Ndikuona kuti bambo anu sakundiyangʼana ndi diso labwino ngati poyamba,+ koma Mulungu wa bambo anga sanandisiye.+ 6 Inunso mukudziwa bwino kuti bambo anu ndawagwirira ntchito ndi mphamvu zanga zonse.+ 7 Koma bambo anu akhala akundipusitsa, ndipo asintha malipiro anga maulendo 10. Ngakhale zili choncho, Mulungu sanawalole kuti andichitire zoipa. 8 Nthawi zonse akanena kuti, ‘Zamawangamawanga ndi zimene zidzakhale malipiro ako,’ ziweto zonse zinkabereka zamawangamawanga. Akanena kuti, ‘Zamizeremizere ndi zimene zidzakhale malipiro ako,’ ziweto zonse zinkabereka zamizeremizere.+ 9 Choncho Mulungu ankachotsa ziweto kwa bambo anu nʼkuzipereka kwa ine. 10 Pa nthawi imene ziweto zinali zokonzeka kutenga bere, ndinalota maloto ndipo ndinaona mbuzi zamphongo zikukwera zazikazi. Mbuzi zamphongozo zinali zamizeremizere, zamawangamawanga ndi zamathothomathotho.+ 11 Kenako, mngelo wa Mulungu woona anandiitana mʼmalotowo kuti, ‘Yakobo!’ Ine ndinayankha kuti, ‘Ine Ambuye.’ 12 Iye anapitiriza kuti, ‘Kweza maso ako ndipo uona kuti mbuzi zonse zamphongo zimene zikukwera zazikazizi ndi zamizeremizere, zamawangamawanga ndiponso zamathothomathotho. Ndachita zimenezi chifukwa ndaona zonse zimene Labani akukuchitira.+ 13 Ndine Mulungu woona wa ku Beteli+ kumene unadzoza mwala wachikumbutso kuja, kumenenso unachita lonjezo kwa ine.+ Tsopano nyamuka, uchoke kudziko lino, ubwerere kudziko limene unabadwira.’”+

14 Pamenepo Rakele ndi Leya anamuyankha kuti: “Kodi ifeyo tatsala ndi cholowa chilichonse mʼnyumba ya bambo athu ngati? 15 Kodi iwowa ife sakutiona ngati alendo? Bambowa anatigulitsa kwa inu ndipo akupitiriza kudya ndalama zimene inu munapereka.+ 16 Chuma chonse chimene Mulungu watenga kwa bambo athuwo ndi chathu ndi cha ana athu.+ Ndiye chilichonse chimene Mulungu wakuuzani, chitani.”+

17 Kenako Yakobo anakweza ana ake ndi akazi ake pangamila.+ 18 Atatero anayamba kutenga ziweto zake zonse ndi katundu wake yense amene anapeza+ ku Padani-aramu, nʼkunyamuka ulendo wopita kudziko la Kanani kwa Isaki bambo ake.+

19 Labani atapita kukameta ubweya wa nkhosa zake, Rakele anaba aterafi*+ a bambo akewo.+ 20 Yakobo anachita zinthu mochenjera chifukwa anachoka kwa Labani wa Chiaramu uja, osamuuza kuti akuchoka. 21 Yakobo anathawa nʼkuwoloka Mtsinje*+ limodzi ndi anthu komanso katundu amene anali naye. Atatero analowera kudera la mapiri la Giliyadi.+ 22 Pa tsiku lachitatu, Labani anauzidwa kuti Yakobo wathawa. 23 Atamva zimenezo, anatenga abale ake* nʼkuyamba kuthamangira Yakobo. Iwo anayenda ulendo wa masiku 7, ndipo anamupeza mʼdera la mapiri la Giliyadi. 24 Koma usiku mʼmaloto,+ Mulungu anafikira Labani wa Chiaramuyo+ nʼkumuuza kuti: “Usamale ndi zimene ukalankhule ndi Yakobo, kaya zabwino kapena zoipa.”+

25 Kenako Labani anapita kwa Yakobo. Pa nthawiyi nʼkuti Yakobo atamanga tenti yake mʼdera la mapiri la Giliyadi, ndipo Labani ndi abale ake anamanganso tenti yawo mʼdera lomwelo. 26 Ndiyeno Labani anafunsa Yakobo kuti: “Nʼchiyani wachitachi? Nʼchifukwa chiyani wandipusitsa nʼkutenga ana anga aakazi ngati akapolo ogwidwa kunkhondo? 27 Nʼchifukwa chiyani unachoka mozemba osandiuza? Ukanandiuza ndikanatsanzikana nawe mosangalala, tikuimba nyimbo, maseche ndi azeze. 28 Sunandipatse mpata woti ndikise* zidzukulu zanga* ndi ana anga. Zimene wachitazi nʼzopusa. 29 Ndikanatha kukuchitirani zoipa, koma Mulungu wa bambo anu analankhula nane usiku wapitawu kuti, ‘Usamale ndi zimene ukalankhule ndi Yakobo, kaya zabwino kapena zoipa.’+ 30 Wachoka chifukwa umafunitsitsa kubwerera kunyumba kwa bambo ako, koma nʼchifukwa chiyani waba milungu yanga?”+

31 Yakobo anayankha Labani kuti: “Ndinachoka mozemba chifukwa ndimaopa kuti mundilanda ana anuwa. 32 Aliyense amene mumʼpeze ndi milungu yanu aphedwe. Pamaso pa abale athuwa, fufuzani milungu yanuyo pakatundu amene ndili naye. Mukaipeza muitenge.” Koma Yakobo sanadziwe kuti Rakele anali ataba milunguyo. 33 Choncho Labani anakalowa mutenti ya Yakobo ndi mutenti ya Leya, ndiponso mutenti ya akapolo aakazi awiri aja,+ koma sanaipeze. Potsirizira pake, anatuluka mutenti ya Leya nʼkukalowa mutenti ya Rakele. 34 Rakele anali atatenga aterafi aja nʼkuwabisa mʼchishalo choika pangamila, nʼkuchikhalira. Labani anafunafuna mutenti monsemo koma sanawapeze aterafiwo. 35 Kenako Rakele anauza bambo ake kuti: “Musandikwiyire mbuyanga chifukwa sinditha kunyamuka pano. Kungoti sindili bwino malinga ndi chikhalidwe chathu akazife.”+ Labani anapitiriza kufunafuna mosamala koma sanawapeze aterafiwo.+

36 Ndiyeno Yakobo anapsa mtima nʼkuyamba kukalipira Labani. Iye anafunsa Labani kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani? Ndipo ndakuchimwirani chiyani kuti muchite kundilondola mokwiya chonchi? 37 Popeza mwafufuza katundu wanga yense, kodi mwapezapo chiyani chamʼnyumba mwanu? Chiikeni apa pamaso pa abale anga ndi abale anu kuti atiweruze. 38 Pa zaka 20 zonsezi zimene ndakhala nanu, nkhosa zanu ndi mbuzi zanu sizinaberekepo mwana wakufa.+ Ndiponso chiyambire sindinadyepo nkhosa yanu yamphongo ngakhale imodzi. 39 Sindinakubweretserenipo nyama iliyonse imene inaphedwa ndi chilombo+ koma ndinkaitenga kuti ikhale yanga. Nyama ikabedwa masana kapena usiku, munkandiuza kuti ndikulipireni. 40 Ndinkangokhalira kupsa ndi dzuwa masana komanso kuzizidwa ndi mphepo usiku, ndipo tulo sindinkationa.+ 41 Ndakhala mʼnyumba mwanu zaka 20. Ndakugwirirani ntchito zaka 14 kuti mundipatse ana anu aakazi awiriwa. Ndinagwiranso ntchito zaka zina 6 kuti mundipatse ziwetozi. Koma inu munkangosintha malipiro anga mpaka maulendo 10.+ 42 Mulungu wa bambo anga,+ Mulungu wa Abulahamu amenenso Isaki ankamuopa,+ akanapanda kukhala kumbali yanga, bwenzi mutandibweza kwathu chimanjamanja. Koma Mulungu waona kusautsika kwanga ndi ntchito zimene ndagwira molimbika, nʼchifukwa chake anakudzudzulani usiku wapitawu.”+

43 Ndiyeno Labani anamuyankha Yakobo kuti: “Akaziwa ndi ana anga, ana awo ndi ana anga, ziwetozi ndi ziweto zanga, ndipo chilichonse chimene ukuchiona ndi cha ine ndi ana anga aakaziwa. Ndiye kodi lero iwowa kapena ana awo amene anabereka, ndingawachitire choipa? 44 Tiye tichite pangano iwe ndi ine, kuti likhale umboni pakati pa ine ndi iwe.” 45 Choncho Yakobo anatenga mwala nʼkuuimika ngati mwala wachikumbutso.+ 46 Kenako Yakobo anauza abale ake kuti: “Tengani miyala!” Iwo anatenga miyala nʼkuiunjika mulu. Atatero, anadyera chakudya pamulu wamiyalawo. 47 Labani anatchula mulu wamiyalawo kuti Yegara-sahaduta,* koma Yakobo anautchula kuti Galeeda.*

48 Kenako Labani ananena kuti: “Mulu wamiyalawu ndi umboni wathu lero pakati pa ine ndi iwe.” Nʼchifukwa chake anaupatsa dzina lakuti Galeeda,+ 49 ndiponso lakuti Nsanja ya Mlonda, chifukwa Labani ananena kuti: “Yehova apitirize kuyangʼanira iwe ndi ine tikasiyana pano. 50 Ukamakazunza ana angawa ndiponso ukakatenga akazi ena kuwonjezera pa ana angawa, ngakhale kuti palibe munthu amene adzaone,* kumbukira kuti Mulungu ndi mboni pakati pa ine ndi iwe.” 51 Labani anauzanso Yakobo kuti: “Ona mulu wamiyala ndiponso mwala wachikumbutso umene ndaimika monga chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi iwe. 52 Muluwu ndiponso mwala wachikumbutsowu ndi umboni+ pakati pa ine ndi iwe, kuti wina sadzadutsa muluwu ndi mwala wachikumbutsowu kukachitira mnzake zoipa. 53 Mulungu wa Abulahamu+ ndi Mulungu wa Nahori, yemwe ndi Mulungu wa bambo awo, atiweruze.” Ndipo Yakobo analumbira mʼdzina la Mulungu amene bambo ake Isaki ankamuopa.+

54 Pambuyo pake, Yakobo anapereka nsembe mʼphirimo nʼkuitana abale ake kuti adye chakudya. Choncho iwo anadya chakudya nʼkugona mʼphirimo usiku umenewo. 55 Ndiyeno Labani anadzuka mʼmamawa nʼkukisa zidzukulu*+ zake ndi ana ake aakazi ndipo anawadalitsa.+ Atatero, ananyamuka nʼkubwerera kwawo.+

32 Kenako Yakobo ananyamuka, koma ali mʼnjira angelo a Mulungu anakumana naye. 2 Yakobo atangowaona anati: “Ilitu ndi gulu la Mulungu!” Choncho malowo anawatchula kuti Mahanaimu.*

3 Ndiyeno Yakobo anatuma anthu kuti apite kwa mchimwene wake Esau, kudziko la Seiri,+ mʼdera la Edomu.+ 4 Anawauza kuti: “Mbuyanga Esau mukamuuze kuti, ‘Kapolo wanu Yakobo wanena kuti: “Ndakhala ndi Labani* kwa nthawi yaitali.+ 5 Pano ndili ndi ngʼombe, abulu, nkhosa komanso antchito aamuna ndi aakazi.+ Ndatumiza uthengawu kwa inu mbuyanga kuti mundikomere mtima.”’”

6 Anthuwo atabwerako, anauza Yakobo kuti: “Takumana naye mchimwene wanu Esau, ndipo akubwera limodzi ndi amuna 400 kudzakumana nanu.”+ 7 Atamva zimenezi, Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.+ Choncho anagawa mʼmagulu awiri anthu amene anali nawo, nkhosa, mbuzi, ngʼombe ndi ngamila. 8 Kenako anati: “Ngati Esau angaukire gulu limodzi, gulu linalo lingathe kuthawa.”

9 Atatero, Yakobo anati: “Mulungu wa kholo langa Abulahamu, Mulungu wa bambo anga Isaki, inu Yehova munandiuza kuti, ‘Bwerera kudziko lakwanu kwa abale ako, ndipo ndidzakusamalira.’+ 10 Ine ndine wosayenerera chikondi chokhulupirika komanso kukoma mtima konseku, kumene mwandisonyeza ine mtumiki wanu.+ Ndinawoloka Yorodano ndilibe kanthu, koma ndodo yokha, ndipo pano ndili ndi magulu awiriwa.+ 11 Chonde ndipulumutseni+ mʼdzanja la mchimwene wanga, Esau. Ndikuchita naye mantha kuti akafika, akhoza kundivulaza+ komanso kuvulaza akaziwa limodzi ndi ana awo. 12 Pajatu munanena kuti: ‘Ndithu ndidzakusamalira, ndipo ndidzachulukitsa mbadwa* zako ngati mchenga wakunyanja, womwe ndi wosawerengeka.’”+

13 Tsiku limenelo Yakobo anagona pamalopo. Kenako anatenga zinthu zina pa chuma chake kuti akapatse mchimwene wake Esau ngati mphatso.+ 14 Anatenga mbuzi zazikazi 200, mbuzi zamphongo 20, nkhosa zazikazi 200, nkhosa zamphongo 20, 15 ngamila zoyamwitsa 30 ndi ana a ngamilazo, ngʼombe zazikazi 40, ngʼombe zamphongo 10, abulu aakazi 20 ndi abulu amphongo 10.+

16 Kenako anapatsa anyamata ake magulu a ziwetozo, gulu lililonse palokha nʼkuwauza kuti: “Tsogolani muwoloke mtsinje, ndipo muzisiya mpata pakati pa gulu lililonse la ziweto.” 17 Anauzanso mnyamata woyamba kuti: “Ngati mchimwene wanga Esau angakumane nawe nʼkukufunsa kuti, ‘Kodi mbuye wako ndi ndani? Ndipo ukupita kuti? Nanga ziweto zimene uli nazozi nʼzandani?’ 18 Ukayankhe kuti, ‘Mbuyanga ndi Yakobo kapolo wanu. Ziwetozi ndi mphatso imene iye watumiza kwa inu mbuyanga Esau.+ Iyeyo ali mʼmbuyo mwathumu.’” 19 Anauzanso mnyamata wachiwiri ndi wachitatu komanso ena onse amene anawapatsira ziwetozo kuti atsogole nazo, kuti: “Zimene ndanenazi mukauze Esau mukakakumana naye. 20 Mukamuuzenso kuti, ‘Ndiponso kapolo wanu Yakobo ali mʼmbuyo mwathumu.’” Popeza mumtima mwake anati: “Ngati angasangalale ndi mphatso imene ndatumizayi,+ ndiye kuti ndikakumana naye akhoza kundilandira bwino.” 21 Choncho atumiki akewo anatsogola ndi mphatsoyo, koma iye anagona pamsasapo usikuwo.

22 Usiku umenewo, iye anadzuka nʼkutenga akazi ake awiri aja,+ akapolo ake awiri aakazi aja+ ndi ana ake aamuna 11 nʼkuwoloka mtsinje wa Yaboki.+ 23 Atawawolotsa mtsinjewo,* anawolotsanso zonse zimene anali nazo.

24 Pomaliza, Yakobo anatsala yekhayekha. Kenako munthu winawake anayamba kulimbana naye mpaka mʼbandakucha.+ 25 Munthuyo ataona kuti Yakobo sakugonja, anamugwira pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno ndipo polumikizanapo panaguluka mmene ankalimbana naye.+ 26 Atatero anauza Yakobo kuti: “Ndisiye ndizipita, chifukwa kukucha tsopano.” Koma Yakobo anayankha kuti: “Sindikusiya mpaka utandidalitsa.”+ 27 Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Dzina lako ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Yakobo.” 28 Kenako munthuyo anati: “Dzina lako silikhalanso Yakobo, koma Isiraeli,*+ chifukwa walimbana ndi Mulungu+ komanso anthu, ndipo potsirizira pake wapambana.” 29 Nayenso Yakobo anamuuza kuti: “Iwenso undiuze dzina lako.” Koma iye anati: “Nʼchifukwa chiyani ukufuna kudziwa dzina langa?”+ Atatero, anamudalitsa pamalo amenewo. 30 Choncho Yakobo anatchula malowo dzina lakuti Penieli,*+ chifukwa iye anati, “Ndaonana ndi Mulungu pamasomʼpamaso, komabe ndapulumuka.”+

31 Dzuwa linali litatuluka pamene Yakobo ankachoka ku Penueli,* koma ankayenda motsimphina.+ 32 Nʼchifukwa chake mpaka pano, ana a Isiraeli sadya mtsempha wa pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno, chifukwa ndi umene munthu uja anagwira polimbana ndi Yakobo.

33 Tsopano Yakobo anakweza maso ake nʼkuona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400.+ Ataona choncho, anagawa ana ake nʼkuwapereka kwa Leya, kwa Rakele ndi kwa akapolo ake awiri aja.+ 2 Anaika akapolowo ndi ana awo patsogolo,+ Leya ndi ana ake anawaika pakati,+ ndipo Rakele+ ndi Yosefe anawaika pambuyo pawo. 3 Kenako iyeyo anapita kutsogolo kwawo nʼkuyamba kugwada ndipo anaweramitsa nkhope yake pansi mpaka maulendo 7. Anachita zimenezi mpaka kufika pafupi ndi mchimwene wakeyo.

4 Koma Esau anathamanga kukakumana naye ndipo anamukumbatira nʼkumukisa.* Atakumbatirana, onse awiri anagwetsa misozi kwambiri. 5 Kenako Esau anakweza maso ake nʼkuona akazi ndi ana. Ndiyeno anafunsa Yakobo kuti: “Nanga amene uli nawowa ndi ndani?” Iye anayankha kuti: “Amenewa ndi ana amene Mulungu wapatsa ine kapolo wanu.”+ 6 Pamenepo akapolo aja anafika pafupi limodzi ndi ana awo ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi. 7 Nayenso Leya anafika pafupi limodzi ndi ana ake ndipo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi. Kenako Yosefe anafika limodzi ndi Rakele ndipo nawonso anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+

8 Tsopano Esau anafunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani watumiza magulu onse amene ndakumana nawo aja?”+ Iye anayankha kuti: “Ndachita zimenezi kuti mundikomere mtima mbuyanga.”+ 9 Ndiyeno Esau anati: “Ziweto ndili nazo zambiri mʼbale wanga.+ Zimenezo ndi zako, usandipatse.” 10 Koma Yakobo anati: “Ayi chonde, musatero. Ngati mwandikomeradi mtima, landirani mphatso yangayi, chifukwa ndabweretsa mphatsoyi kuti ndidzaone nkhope yanu, ndipo ndaionadi. Zili ngati ndaona nkhope ya Mulungu, chifukwa mwandilandira ndi manja awiri.+ 11 Chonde landirani mphatso yangayi, yomwe ndabweretsa pokufunirani mafuno abwino,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Yakobo anapitiriza kumukakamiza mpaka analandira mphatsoyo.

12 Kenako Esau anati: “Tiye tinyamuke tizipita, ndipo ine nditsogola.” 13 Koma Yakobo anati: “Monga mukudziwa mbuyanga, anawa ndi osakhwima,+ komanso ndili ndi nkhosa ndi ngʼombe zoyamwitsa. Tikaziyendetsa mofulumira kwambiri kwa tsiku limodzi, ziweto zonse zifa. 14 Chonde mbuyanga, tsogolani ndipo ine kapolo wanu ndizibwera mʼmbuyo mwanu. Ndiziyenda pangʼonopangʼono mogwirizana ndi kuyenda kwa ziwetozi komanso anawa. Ndikakupezani ku Seiri,+ mbuyanga.” 15 Ndiyeno Esau anati: “Chabwino, ndiye ndikusiyireko ena mwa anyamata angawa kuti akuthandize.” Koma iye anati: “Ayi musachite kutero. Musavutike mbuyanga, ndikungosangalala kuti mwandirandira bwino.” 16 Choncho, Esau anabwerera ku Seiri tsiku lomwelo.

17 Kenako Yakobo ananyamuka ulendo wopita ku Sukoti.+ Kumeneko anamanga nyumba yake ndi makola a ziweto zake. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Sukoti.*

18 Atachoka ku Padani-aramu,+ Yakobo anafika bwino kumzinda wa Sekemu,+ mʼdziko la Kanani.+ Atafika, anamanga msasa pafupi ndi mzindawo. 19 Kenako anagula malo ndipo anamangapo tenti. Anawagula ndi ndalama zasiliva 100, kwa ana a Hamori, bambo ake a Sekemu.+ 20 Pamalopo anamangapo guwa lansembe nʼkulitchula kuti Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+

34 Dina, mwana wamkazi amene Leya anaberekera Yakobo,+ ankakonda kukacheza ndi* atsikana a mumzindawo.+ 2 Ndiyeno Sekemu mwana wamwamuna wa Hamori Mhivi,+ mmodzi wa atsogoleri amumzindawu ataona mtsikanayu, anamutenga nʼkumugwiririra. 3 Atatero, anayamba kulakalaka kwambiri Dina mwana wa Yakobo, ndipo anamukonda kwambiri mtsikanayu, moti ankalankhula naye momunyengerera. 4 Potsirizira pake, Sekemu anauza bambo ake Hamori+ kuti: “Mukanditengere mtsikana ameneyu kuti akhale mkazi wanga.”

5 Yakobo anamva kuti Sekemu wagwiririra mwana wake Dina. Pa nthawiyo nʼkuti ana ake aamuna ali koweta ziweto zake. Choncho Yakobo sananene kanthu kudikira kuti ana akewo abwere. 6 Kenako Hamori bambo ake a Sekemu, anapita kwa Yakobo kukakambirana naye. 7 Koma ana a Yakobo atamva za nkhaniyi, nthawi yomweyo anabwerako koweta ziweto kuja. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa, chifukwa Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chochititsa manyazi kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika ngakhale pangʼono.+

8 Ndiyeno Hamori anawauza kuti: “Mwana wanga Sekemu wamukonda mtsikana wanuyu ndi mtima wonse. Chonde, mupatseni kuti akhale mkazi wake. 9 Tiyeni tichite mgwirizano kuti tizikwatirana. Muzitipatsa ana anu aakazi, inunso muzitenga ana athu aakazi.+ 10 Muzikhala kwathu kuno ndipo dzikoli likhalanso lanu. Mukhazikike mumzinda uno ndipo muzichita malonda mwaufulu.” 11 Kenako Sekemu anauza bambo ake a Dina ndi alongo ake kuti: “Ndikomereni mtima, ndikupatsani chilichonse chimene mungafune. 12 Kwezani kwambiri ndalama za malowolo ndi mphatso zoti ndipereke.+ Ndine wokonzeka kupereka chilichonse chimene mungandiuze, bola mundipatse mtsikanayu kuti akhale mkazi wanga.”

13 Koma ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi bambo ake Hamori mowapusitsa chifukwa Sekemu anali atagwiririra mchemwali wawo Dina. 14 Iwo anawayankha kuti: “Sitingachite zimenezo. Sitingapereke mchemwali wathu kwa mwamuna wosadulidwa.+ Zimenezo nʼzochititsa manyazi kwa ife. 15 Tikulolani pokhapokha ngati mwamuna aliyense atadulidwa+ kuti mukhale ofanana ndi ife. 16 Mukatero tidzakupatsani ana athu aakazi ndipo ifenso tidzatenga ana anu aakazi. Tizidzakhala limodzi ndipo tidzakhala anthu amodzi. 17 Koma ngati simutsatira zimene tanenazi zakuti mudulidwe, mwana wathu wamkaziyo tikamutenga nʼkubwera naye.”

18 Zimene ananenazi zinasangalatsa Hamori+ ndi mwana wake Sekemu.+ 19 Choncho mnyamatayu sanachedwe kuchita zimene anauzidwazo+ chifukwa anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. Sekemu anali wolemekezeka kwambiri mʼnyumba yonse ya bambo ake.

20 Kenako Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita pageti la mzinda wawo nʼkuyamba kulankhula ndi amuna amumzindawo+ kuti: 21 “Anthu awa akufuna kuti tizikhala nawo mwamtendere. Ndiye aloleni akhale mʼdzikoli nʼkumachita malonda, popeza dzikoli ndi lalikulu moti atha kukhalamo. Tikhoza kukwatira ana awo aakazi ndiponso tikhoza kuwapatsa ana athu aakazi.+ 22 Koma pakufunika chinthu chimodzi kuti anthuwa alole kuti azikhala nafe nʼkukhala anthu amodzi ndi ife. Akufuna kuti mwamuna aliyense pakati pathu adulidwe ngati mmene iwowo alili.+ 23 Tikatero, kodi katundu wawo, chuma chawo ndi ziweto zawo zonse sizidzakhala zathu? Ndiye tiyeni tilolere zimene akufunazo kuti azikhala nafe.” 24 Choncho anthu onse otuluka pageti la mzindawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo amuna onse amumzinda wakewo anadulidwa.

25 Koma pa tsiku lachitatu, anthuwo akumvabe ululu, ana awiri a Yakobo, Simiyoni ndi Levi, alongo ake a Dina,+ aliyense anatenga lupanga lake nʼkukalowa mumzindawo anthuwo asakuyembekezera ndipo anapha mwamuna aliyense.+ 26 Anaphanso Hamori ndi mwana wake Sekemu ndi lupanga. Kenako anatenga Dina mʼnyumba ya Sekemu, nʼkumapita. 27 Ana ena a Yakobo anabwera mumzindawo amuna onse ataphedwa, nʼkutenga katundu yense wamumzindamo. Anatero chifukwa anthuwo anagwiririra mchemwali wawo.+ 28 Anatenga nkhosa zawo, abulu awo ndi ziweto zina komanso chilichonse chimene chinali mumzindawo ndi chimene chinali kunja kwa mzindawo. 29 Anatenganso chuma chawo chonse, ana awo onse angʼonoangʼono ndi akazi awo komanso zonse zimene zinali mʼnyumba zawo nʼkumapita.

30 Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira mavuto aakulu, ndipo mwandidanitsa ndi anthu amʼdziko lino, Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa. Iwowa ndithu asonkhana nʼkutiukira ndipo atitha tonse, ine ndi banja langa.” 31 Koma anawo anayankha kuti: “Kodi ndi bwino kuti munthu azitenga mchemwali wathu ngati hule?”

35 Zitatero, Mulungu anauza Yakobo kuti: “Nyamuka, pita ku Beteli+ ukakhale kumeneko. Ukandimangire guwa lansembe. Ndine Mulungu woona, amene anaonekera kwa iwe pamene unkathawa mchimwene wako Esau.”+

2 Ndiyeno Yakobo anauza anthu a mʼbanja lake ndi onse amene anali naye kuti: “Chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu.+ Dziyeretseni ndipo sinthani zovala zanu. 3 Mukatero, tinyamuke tipite ku Beteli. Kumeneko ndikamangira guwa lansembe Mulungu woona, amene anandiyankha pa tsiku la kusautsika kwanga, ndipo wakhala nane kulikonse kumene ndapita.”+ 4 Choncho anthuwo anapereka kwa Yakobo milungu yachilendo yonse imene anali nayo, ndi ndolo zimene anavala mʼmakutu. Kenako Yakobo anakwirira* zinthuzo pansi pa mtengo waukulu umene unali pafupi ndi ku Sekemu.

5 Atanyamuka, Mulungu anachititsa kuti anthu amʼmizinda yowazungulira agwidwe ndi mantha, moti sanatsatire ana a Yakobo kuti amenyane nawo. 6 Kenako Yakobo anafika ku Luzi,+ komwe ndi ku Beteli, mʼdziko la Kanani. Iye anafika kumeneko limodzi ndi anthu onse amene anali naye. 7 Anamanga guwa lansembe kumeneko nʼkutchula malowo kuti Eli-beteli.* Malowo anawapatsa dzinali chifukwa Mulungu woona anaonekera kwa iye kumeneko pamene ankathawa mʼbale wake.+ 8 Pambuyo pake Debora,+ mlezi* wa Rabeka anamwalira, ndipo anamuika ku Beteli mʼmunsi mwa phiri, pansi pa mtengo waukulu. Choncho mtengowo anautchula kuti Aloni-bakuti.*

9 Mulungu anaonekeranso kwa Yakobo pamene ankabwerera kwawo kuchokera ku Padani-aramu, ndipo anamudalitsa. 10 Mulungu anamuuza kuti: “Dzina lako ndi Yakobo.+ Kuyambira lero, dzina lako silikhalanso Yakobo, koma likhala Isiraeli.” Choncho anayamba kumutchula kuti Isiraeli.+ 11 Mulungu anamuuzanso kuti: “Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse.+ Ubereke ndipo ukhale ndi ana ambiri. Mitundu ndi mafuko ambiri adzatuluka mwa iwe,+ ndipo zina mwa mbadwa zako zidzakhala* mafumu.+ 12 Dziko limene ndinalipereka kwa Abulahamu ndi Isaki, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.”+ 13 Kenako Mulungu anachoka pamalo amene ankalankhula ndi Yakobo.

14 Zitatero, Yakobo anaimika mwala wachikumbutso pamalo amene ankalankhula nayepo, kenako pamwalawo anathirapo nsembe yachakumwa ndi mafuta.+ 15 Ndiyeno Yakobo anatchulanso malo amene Mulungu analankhula nayewo kuti Beteli.+

16 Kenako anachoka ku Beteliko. Kutatsala mtunda wautali kuti afike ku Efurata, nthawi yoti Rakele abereke inakwana, koma poberekapo anavutika kwambiri. 17 Pamene ankavutika kwambiri kuti abereke, mzamba* anamuuza kuti: “Usaope, chifukwa ubereka mwana wina wamwamuna.”+ 18 Pa nthawi imene moyo wake unkachoka (chifukwa anali akumwalira), anapereka dzina kwa mwanayo lakuti Beni-oni.* Koma bambo ake anamupatsa dzina lakuti Benjamini.*+ 19 Choncho Rakele anamwalira, ndipo anamuika mʼmanda mʼmbali mwa njira yopita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+ 20 Yakobo anaika mwala pamandapo. Mwala umenewo ulipobe mpaka lero pamanda a Rakele.

21 Kenako Isiraeli ananyamuka nʼkukamanga tenti yake patsogolo pa nsanja ya Ederi. 22 Nthawi ina Isiraeli akukhala mʼdziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamngʼono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+

Yakobo anali ndi ana aamuna 12. 23 Ana aamuna amene Leya anaberekera Yakobo anali Rubeni+ mwana wake woyamba, kenako Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara ndi Zebuloni. 24 Ana amene Rakele anaberekera Yakobo anali Yosefe ndi Benjamini. 25 Ana amene Biliha kapolo wa Rakele anaberekera Yakobo anali Dani ndi Nafitali. 26 Ana amene Zilipa kapolo wa Leya anaberekera Yakobo anali Gadi ndi Aseri. Ana aamuna amene Yakobo anabereka ku Padani-aramu ndi amenewa.

27 Pamapeto pake Yakobo anafika kwa bambo ake Isaki ku Mamure,+ mʼdera la Kiriyati-ariba, komwe ndi ku Heburoni. Uku nʼkumenenso Abulahamu ndi Isaki anakhalako monga alendo.+ 28 Isaki anakhala ndi moyo zaka 180.+ 29 Kenako Isaki anamwalira, ndipo anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.* Anamwalira atakhala ndi moyo wautali komanso atakhutira ndi masiku a moyo wake ndipo ana ake, Esau ndi Yakobo, anamuika mʼmanda.+

36 Mbiri ya Esau, kapena kuti Edomu,+ ndi iyi:

2 Esau anakwatira ana aakazi a ku Kanani. Anakwatira Ada,+ mwana wamkazi wa Eloni, Muhiti.+ Anakwatiranso Oholibama,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Ana komanso anali mdzukulu wa Zibeoni, Mhivi. 3 Anakwatiranso Basemati,+ yemwe anali mwana wamkazi wa Isimaeli komanso anali mchemwali wake wa Nebayoti.+

4 Ada anaberekera Esau mwana dzina lake Elifazi, ndipo Basemati anamuberekera Reueli.

5 Ana amene Oholibama anaberekera Esau anali Yeusi, Yalamu ndi Kora.+

Amenewa anali ana a Esau amene anabereka mʼdziko la Kanani. 6 Pambuyo pake, Esau anatenga akazi ake, ana ake aamuna ndi aakazi komanso ena onse amʼnyumba yake, ziweto zake zonse ndi chuma chake chonse chimene anachipeza+ mʼdziko la Kanani nʼkupita kudziko lina, kutali ndi Yakobo mchimwene wake.+ 7 Iye anachoka chifukwa chuma chawo chinali chitachuluka kwambiri, moti sakanathanso kukhala limodzi. Mʼdziko limene ankakhalalo* malo anali ochepa chifukwa ziweto zawo zinali zambiri. 8 Choncho Esau anakakhazikika kudera lamapiri ku Seiri.+ Dzina lina la Esau linali Edomu.+

9 Imeneyi ndi mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu, amene ankakhala kudera lamapiri la Seiri.+

10 Mayina a ana a Esau ndi awa: Elifazi, mwana wamwamuna amene Ada mkazi wake wa Esau anabereka, komanso Reueli, mwana wamwamuna amene Basemati mkazi wake wa Esau anabereka.+

11 Ana a Elifazi anali Temani,+ Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi.+ 12 Timina anali mkazi wamngʼono wa Elifazi mwana wa Esau. Patapita nthawi, Timina anaberekera Elifazi mwana wamwamuna dzina lake Amaleki.+ Ana a Ada mkazi wa Esau anali amenewa.

13 Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Shama ndi Miza. Ana a Basemati+ mkazi wa Esau anali amenewa.

14 Oholibama, mkazi wake wa Esau, anaberekera Esau ana aamuna awa: Yeusi, Yalamu ndi Kora. Oholibamayu anali mwana wa Ana komanso mdzukulu wa Zibeoni.

15 Mafumu a mafuko a ana a Esau ndi awa:+ Ana a Elifazi, mwana woyamba wa Esau anali: Mfumu Temani, Mfumu Omari, Mfumu Zefo, Mfumu Kenazi,+ 16 Mfumu Kora, Mfumu Gatamu ndi Mfumu Amaleki. Awa ndi amene anali mafumu akubanja la Elifazi+ mʼdziko la Edomu. Amenewa ndi ana a Ada.

17 Ana a Reueli, mwana wamwamuna wa Esau ndi awa: Mfumu Nahati, Mfumu Zera, Mfumu Shama ndi Mfumu Miza. Amenewa ndi amene anali mafumu akubanja la Reueli mʼdziko la Edomu.+ Amenewa anali ana a Basemati mkazi wa Esau.

18 Potsiriza, ana a Oholibama mkazi wa Esau ndi awa: Mfumu Yeusi, Mfumu Yalamu ndi Mfumu Kora. Amenewa ndi amene anali mafumu akubanja la Oholibama mkazi wa Esau, amenenso anali mwana wa Ana.

19 Amenewa anali ana a Esau kapena kuti Edomu+ ndi mafumu awo.

20 Ana a Seiri Mhori, nzika za dzikolo+ ndi awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana,+ 21 Disoni, Ezeri ndi Disani.+ Amenewa anali ana a Seiri, mafumu a fuko la Ahori, mʼdziko la Edomu.

22 Ana a Lotani anali Hori ndi Hemamu, ndipo Lotani anali ndi mchemwali wake dzina lake Timina.+

23 Ana a Sobala anali Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.

24 Ana a Zibeoni+ anali Aya ndi Ana. Uyu ndi Ana amene anapeza akasupe a madzi otentha mʼchipululu pa nthawi imene ankadyetsa abulu a Zibeoni bambo ake.

25 Ana anabereka ana awa: Disoni ndi Oholibama mwana wamkazi wa Ana.

26 Ana a Disoni anali Hemadani, Esibani, Itirani ndi Kerana.+

27 Ana a Ezeri anali Bilihani, Zavani ndi Ekani.

28 Ana a Disani anali Uzi ndi Arani.+

29 Mafumu a fuko la Ahori ndi awa: Mfumu Lotani, Mfumu Sobala, Mfumu Zibeoni, Mfumu Ana, 30 Mfumu Disoni, Mfumu Ezeri ndi Mfumu Disani.+ Amenewa ndi amene anali mafumu a fuko la Ahori mogwirizana ndi ufumu wawo mʼdziko la Seiri.

31 Mafumu amene analamulira dziko la Edomu,+ Aisiraeli* asanayambe kulamulidwa ndi mfumu ina iliyonse,+ ndi awa: 32 Bela mwana wa Beori analamulira Edomu, ndipo dzina la mzinda wake linali Dinihaba. 33 Bela atamwalira, Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozira, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 34 Yobabi atamwalira, Husamu wa ku Temani, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 35 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi amene anagonjetsa Amidiyani+ mʼdera la Mowabu, anayamba kulamulira mʼmalo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Aviti. 36 Hadadi atamwalira, Samila wa ku Masereka anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 37 Samila atamwalira, Shauli wamumzinda wa Rehoboti, womwe unali mʼmbali mwa Mtsinje,* anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 38 Shauli atamwalira, Baala-hanani mwana wa Akibori, anayamba kulamulira mʼmalo mwake. 39 Baala-hanani mwana wa Akibori atamwalira, Hadari anayamba kulamulira mʼmalo mwake, ndipo dzina la mzinda wake linali Pau. Mkazi wake dzina lake anali Mehetabele, mwana wa Matiredi. Matiredi anali mwana wamkazi wa Mezahabu.

40 Mayina a mafumu a Esau mogwirizana ndi mabanja awo komanso madera awo ndi awa: Mfumu Timina, Mfumu Aliva, Mfumu Yeteti,+ 41 Mfumu Oholibama, Mfumu Ela, Mfumu Pinoni, 42 Mfumu Kenazi, Mfumu Temani, Mfumu Mibezari, 43 Mfumu Magidieli ndi Mfumu Iramu. Amenewa ndi amene anali mafumu a Edomu mogwirizana ndi madera awo mʼdziko lawo.+ Mibadwo ya Esau, kholo la Aedomu+ ndi imeneyi.

37 Yakobo anapitiriza kukhala mʼdziko la Kanani, kumene bambo ake anakhalako ngati mlendo.+

2 Iyi ndi mbiri ya Yakobo.

Yosefe+ ali ndi zaka 17, anapita kokadyetsa nkhosa+ limodzi ndi ana a Biliha+ ndi ana a Zilipa,+ omwe anali akazi a bambo ake. Ndiyeno Yosefe anakauza bambo ake zoipa zimene abale akewo ankachita. 3 Isiraeli ankamukonda kwambiri Yosefe kuposa ana ake onse,+ chifukwa anali mwana amene anamʼbereka atakalamba. Choncho anamusoketsera mkanjo wokongola. 4 Abale ake ataona kuti bambo awo ankakonda kwambiri Yosefe kuposa abale ake onse, anayamba kudana naye, moti sankalankhula naye mwamtendere.

5 Kenako Yosefe analota maloto ndipo anauza abale ake+ moti iwo anapeza chifukwa china chowapangitsa kuti azidana naye. 6 Iye anawauza kuti: “Tamvetserani maloto amene ine ndinalota. 7 Ndinalota tikumanga mitolo ya tirigu pakati pa munda. Mtolo wanga unadzuka nʼkuima chilili. Mitolo yanunso inadzuka nʼkuzungulira mtolo wanga ndipo inayamba kuuweramira.”+ 8 Abale akewo anamufunsa kuti: “Kodi zoona iweyo ukuganiza kuti ungadzakhale mfumu yathu nʼkumatilamulira?”+ Choncho maloto amenewa komanso zimene ananena zinapangitsa kuti abale akewo apeze chifukwa chinanso choti azidana naye.

9 Tsiku linanso analota maloto ena, ndipo anauza abale akewo kuti: “Leronso ndinalota maloto ena. Ndinalota dzuwa ndi mwezi ndiponso nyenyezi zokwana 11 zikundigwadira.”+ 10 Kenako anafotokozeranso bambo ake ndi abale ake malotowo. Koma bambo ake anamʼdzudzula kuti: “Kodi maloto akowa akutanthauza chiyani? Kodi zoona ineyo ndi mayi akowa, komanso abale akowa tidzagwada pansi pamaso pa iwe?” 11 Abale akewo anamuchitira nsanje,+ koma bambo ake anasunga mawuwo mumtima.

12 Ndiyeno abale ake aja anapita kokadyetsa ziweto za bambo awo kufupi ndi ku Sekemu.+ 13 Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Kodi abale ako sakudyetsa ziweto pafupi ndi ku Sekemu? Tabwera ndikutume kwa iwo.” Iye anati: “Chabwino bambo.” 14 Ndiyeno Isiraeli anati: “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino. Ukaonenso ngati ziweto zili bwino ndipo udzandiuze.” Choncho anamuuza kuti anyamuke kuchigwa cha Heburoni+ ndipo ananyamuka nʼkulowera ku Sekemu. 15 Kenako Yosefe akungoyendayenda kutchireko, munthu wina anakumana naye. Ndiyeno munthuyo anamufunsa kuti: “Kodi ukufufuza chiyani?” 16 Iye anayankha kuti: “Ndikufufuza abale anga. Tandiuzani chonde, kodi iwo akudyetsera kuti ziweto?” 17 Munthuyo anati: “Amenewo achoka kuno chifukwa ndinawamva akunena kuti, ‘Tiyeni tipite ku Dotani.’” Choncho Yosefe anawalondola abale akewo mpaka anakawapeza ku Dotani.

18 Abale akewo anamuonera patali akubwera, koma asanafike anayamba kukonza chiwembu kuti amuphe. 19 Ndiye anayamba kukambirana kuti: “Tamuonani wolota uja.+ Uyo akubwera apoyo! 20 Tiyeni timuphe nʼkumuponya muchitsime chopanda madzi, ndipo tikanene kuti chilombo cholusa chamudya. Tidzaone kuti chidzachitike nʼchiyani ndi maloto ake aja.” 21 Rubeni+ atamva zimenezo anayesa kumupulumutsa. Iye anati: “Ayi, tisamuphe.”+ 22 Rubeni anawauza kuti: “Musakhetse magazi.+ Muponyeni mʼchitsime chopanda madzichi kutchire kuno, koma musamuvulaze.”+ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo nʼkumubwezera kwa bambo ake.

23 Choncho Yosefe atangofika kwa abale akewo, anamuvula mkanjo wake wokongola uja, womwe anavala.+ 24 Atatero, anamutenga nʼkumuponya mʼchitsime chomwe pa nthawiyo chinali chopanda madzi.

25 Ndiyeno abale akewo anakhala pansi kuti adye chakudya. Koma atayangʼana, anaona gulu la Aisimaeli+ amene ankachokera ku Giliyadi. Ngamila zawo zinali zitanyamula zinthu zonunkhira monga labidanamu, basamu komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Iwo anali pa ulendo wopita ku Iguputo. 26 Yuda atawaona, anauza abale ake kuti: “Tipindulapo chiyani tikapha mʼbale wathu ndi kubisa imfa yake?+ 27 Tiyeni timugulitse+ kwa Aisimaeliwa, tisamuvulaze. Ndipotu ndi mʼbale wathu ameneyu, magazi amodzi.”* Choncho iwo anamvera zimene mʼbale wawoyo ananena. 28 Pamene amalonda a Chimidiyani+ aja ankadutsa, abale a Yosefe anamutulutsa mʼchitsimemo nʼkumugulitsa kwa Aisimaeliwo. Anamugulitsa ndalama zasiliva 20,+ ndipo amalondawo anapita naye ku Iguputo.

29 Rubeni atabwerera kuchitsime kuja nʼkupeza kuti Yosefe mulibe mʼchitsimemo, anangʼamba zovala zake. 30 Atabwerera kwa abale ake aja, anafuula kuti: “Mwana ujatu kulibe! Mayo ine, nditani ine?”

31 Ndiyeno iwo anapha mbuzi yamphongo nʼkutenga mkanjo wa Yosefe uja nʼkuuviika mʼmagazi a mbuziyo. 32 Kenako, iwo anatumiza mkanjo uja kwa bambo awo ndipo bambowo anauzidwa kuti: “Tapeza mkanjo uwu. Chonde, uonetsetseni kuti muone ngati uli mkanjo wa mwana wanu kapena ayi.”+ 33 Bambowo anayangʼanitsitsa mkanjowo nʼkufuula kuti: “Mayo ine! Mkanjowu ndi wa mwana wanga! Chilombo cholusa chamudya mwana wanga. Wakhadzulidwa ndithu mwana wanga Yosefe!” 34 Atatero Yakobo anangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli mʼchiuno mwake, ndipo anamulira mwana wake masiku ambiri. 35 Ana ake onse aamuna ndi aakazi ankapita kukamutonthoza, koma iye ankakana kutonthozedwa. Ankanena kuti: “Ayi! Ndidzalira mpaka kutsikira ku Manda*+ kumene kuli mwana wanga.” Ndipo bambo akewo anapitiriza kumulira.

36 Amidiyani aja anakamugulitsa Yosefe ku Iguputo kwa Potifara. Potifara anali nduna yapanyumba ya Farao,+ ndiponso anali mkulu wa asilikali olondera mfumu.+

38 Pa nthawi imeneyi, Yuda anasiyana ndi abale ake, ndipo anakamanga tenti yake pafupi ndi munthu wina wa Chiadulamu, dzina lake Hira. 2 Kumeneko Yuda anaona mwana wamkazi wa munthu wina wa Chikanani+ ndipo anamukwatira. Munthuyo dzina lake anali Sua. 3 Mkaziyo anakhala woyembekezera. Kenako, anabereka mwana wamwamuna, ndipo Yuda anamupatsa dzina lakuti Ere.+ 4 Anakhalanso woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna ndipo anamupatsa dzina lakuti Onani. 5 Anaberekanso mwana wina wamwamuna nʼkumupatsa dzina lakuti Shela. Pa nthawi imene mwanayu ankabadwa, Yuda anali ku Akizibu.+

6 Patapita nthawi, Yuda anatengera mkazi Ere, mwana wake woyamba. Mkaziyo dzina lake anali Tamara.+ 7 Koma makhalidwe a Ere, mwana woyamba wa Yuda, sanasangalatse Yehova ndipo Yehova anamupha. 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa mchimwene wako ndipo ulowe chokolo,* kuti umuberekere ana mchimwene wako.”+ 9 Koma Onani anadziwa kuti anawo sadzakhala ake.+ Choncho, nthawi zonse akagona ndi mkazi wa mʼbale wakeyo, ankataya pansi umuna wake kuti asamuberekere ana mʼbale wakeyo.+ 10 Zimene ankachitazo zinali zoipa pamaso pa Yehova, choncho nayenso anamupha.+ 11 Yuda anauza Tamara mpongozi wake kuti: “Pita kunyumba kwa bambo ako, ukakhale kumeneko monga mkazi wamasiye kufikira Shela mwana wanga wamwamuna atakula.” Anatero chifukwa mumtima mwake anati: “Nayenso Shela angamwalire ngati abale ake aja.”+ Choncho Tamara anapita kukakhala kunyumba kwa bambo ake.

12 Patapita nthawi, mkazi wa Yuda, yemwe anali mwana wa Sua,+ anamwalira. Nthawi yolira maliro itatha Yuda anapita ku Timuna,+ kumene anyamata ake ankameta ubweya wa nkhosa zake. Anapita ndi mnzake Hira wa Chiadulamu uja.+ 13 Ndiye munthu wina anauza Tamara kuti: “Apongozi ako akupita ku Timuna kukameta nkhosa zawo.” 14 Tamara atamva zimenezo, anavula zovala zake zaumasiye nʼkufunda nsalu. Kenako anaphimba nkhope yake ndi nsalu ina. Atatero anakakhala pansi pachipata cha Enaimu mʼmbali mwa msewu wopita ku Timuna. Tamara anachita zimenezi poona kuti Shela wakula, koma apongozi ake sakudzamutenga kuti akakhale mkazi wa Shelayo.+

15 Yuda atamuona mkaziyo, anaganiza kuti ndi hule chifukwa anali ataphimba nkhope yake. 16 Choncho Yuda anapatuka nʼkupita pamene panali mkaziyo mʼmbali mwa msewu nʼkumuuza kuti: “Ndikufuna ndigone nawe.” Anamuuza zimenezi chifukwa sankadziwa kuti anali mpongozi wake.+ Koma mkaziyo anayankha kuti: “Mundipatsa chiyani kuti mugone nane?” 17 Iye anayankha kuti: “Ndidzakutumizira mwana wa mbuzi.” Koma mkaziyo anati: “Mundipatse chikole choti ndisunge kufikira pamene mudzaitumize.” 18 Iye anati: “Ukufuna ndikupatse chikole chotani?” Mkaziyo anapitiriza kuti: “Mundipatse mphete ya udindo+ wanuyo ndi chingwe chake, ndiponso ndodo yanuyo.” Pamenepo iye anapereka zinthuzo kwa mkaziyo, nʼkugona naye ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera. 19 Atagona naye, mkaziyo ananyamuka nʼkubwerera kwawo. Atafika anavula nsalu imene anadziphimba nayo ija nʼkuvala zovala zake zaumasiye.

20 Yuda anatumiza mwana wa mbuzi kudzera mwa mnzake wa Chiadulamu uja+ nʼcholinga choti akamutengere chikole chake kwa mkazi uja, koma sanakamupeze. 21 Kenako anafunsa amuna akuderalo kuti: “Kodi hule lapakachisi lija, limene limaima mʼmbali mwa msewu kuno ku Enaimu lili kuti?” Koma amunawo anayankha kuti: “Kunotu sikunakhalepo hule lapakachisi.” 22 Pamapeto pake, mnzakeyo anabwerera kwa Yuda nʼkumuuza kuti: “Mkazi ujatu sindinamupeze. Ndiponso amuna akumeneko anena kuti, ‘Kunotu sikunakhalepo hule lapakachisi.’” 23 Choncho Yuda anati: “Mulekeni atenge zinthuzo zikhale zake, kuopera kuti anthu angatiseke. Ndipotu mwana wa mbuziyo ndinatumiza ndithu, koma mkaziyo sunakamupeze.”

24 Patapita miyezi itatu, Yuda anauzidwa kuti: “Tamara mpongozi wako wayamba uhule, ndipo ndi woyembekezera.” Yuda atamva zimenezo anati: “Mutulutseni ndipo mumuphe kenako mumuotche.”+ 25 Pamene ankamutulutsa, Tamarayo anatumiza uthenga kwa apongozi ake kuti: “Mwiniwake wa zinthu izi ndi amene anandipatsa mimbayi.” Ananenanso kuti: “Chonde ziyangʼanitsitseni, muone kuti mpheteyo ndi chingwe chake komanso ndodoyo nʼzandani.”+ 26 Ndiyeno Yuda atayangʼanitsitsa zinthuzo, ananena kuti: “Mkaziyu ndi wolungama koposa ine, chifukwa sindinamupereke kwa mwana wanga Shela.”+ Zitatero, Yuda sanagonenso naye.

27 Nthawi yoti Tamara abereke itakwana, anapezeka kuti ali ndi mapasa mʼmimba mwake. 28 Pamene ankabereka, mwana mmodzi anatulutsa dzanja lake. Nthawi yomweyo mzamba anatenga kachingwe kofiira nʼkumanga dzanjalo, ndipo ananena kuti: “Uyu ndi amene wayamba kubadwa.” 29 Koma mwanayo anabweza dzanja lake. Nthawi yomweyo mchimwene wake anatuluka, moti mzambayo anafuula kuti: “Bwanji ukuchita kungʼamba njira?” Nʼchifukwa chake anamupatsa dzina lakuti Perezi.*+ 30 Pambuyo pake, mʼbale wake yemwe anali ndi kachingwe kofiira padzanja lake uja anatuluka, ndipo anamupatsa dzina lakuti Zera.+

39 Kenako Aisimaeli+ aja anapita naye Yosefe ku Iguputo+ ndipo anakamugulitsa kwa munthu wina wa ku Iguputo dzina lake Potifara.+ Potifara anali nduna yapanyumba ya Farao, komanso mkulu wa asilikali olondera mfumu. 2 Koma Yehova anali ndi Yosefe,+ moti chilichonse chimene ankachita chinkamuyendera bwino. Ndipo anaikidwa kuti aziyangʼanira nyumba ya munthu wa ku Iguputo uja, amene anali mbuye wake. 3 Mbuye wakeyo anaona kuti Yehova anali ndi mnyamatayo komanso kuti Yehova ankathandiza mnyamatayo kuti chilichonse chimene ankachita chiziyenda bwino.

4 Potifara anapitiriza kumukonda Yosefe ndipo anakhala mtumiki amene ankamudalira. Choncho anamusankha kuti akhale woyangʼanira nyumba yake komanso zinthu zonse zimene anali nazo. 5 Kuyambira pamene Potifara anasankha Yosefe kukhala woyangʼanira nyumba yake ndi zinthu zake zonse, Yehova anapitiriza kudalitsa nyumba ya munthu wa ku Iguputoyo chifukwa cha Yosefe. Yehova anadalitsa zonse zamʼnyumba ya Potifara ndi zakumunda zomwe.+ 6 Kenako Potifara anasiya zinthu zake zonse mʼmanja mwa Yosefe, moti sankadera nkhawa chilichonse kupatulapo kusankha chakudya choti adye. Komanso Yosefe anali wooneka bwino ndiponso wa thupi loumbika bwino.

7 Kenako, mkazi wa mbuye wake anayamba kuyangʼana Yosefe momusirira, moti ankamuuza kuti: “Ugone nane.” 8 Koma Yosefe ankakana ndipo ankauza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Mbuye wanga sadera nkhawa chilichonse mʼnyumba muno chifukwa cha ine, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachisiya mʼmanja mwanga. 9 Mʼnyumba muno mulibe woyangʼanira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse mʼmanja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?”+

10 Mkaziyo ankalankhula ndi Yosefe tsiku ndi tsiku, koma iye sanamvere zoti agone pambali pake kapena kuti agone naye. 11 Tsiku lina Yosefe analowa mʼnyumba kuti akagwire ntchito yake, ndipo mʼnyumbamo munalibe antchito ena. 12 Choncho mkaziyo anagwira malaya a mnyamatayo nʼkumuuza kuti: “Ugone nane basi!” Koma mnyamatayo anangovula malayawo nʼkuwasiya mʼmanja mwa mkaziyo nʼkuthawira panja. 13 Mkaziyo ataona kuti mnyamatayo wasiya malaya ake mʼmanja mwake nʼkuthawira panja, 14 anayamba kufuulira antchito ena amʼnyumbamo, kuti: “Taonani! Anatibweretsera mwamuna wa Chiheberiyu kuti adzatichite chipongwe anthu nʼkutiseka. Iye anabwera kwa ine kuti adzandigwiririre, koma ndinakuwa mwamphamvu. 15 Ndiye ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa nʼkuthawira panja.” 16 Atatero, anasunga malaya a mnyamatayo pambali pake mpaka mwamuna wake atabwera kunyumbako.

17 Mwamuna wake atafika, mkaziyo anamuuzanso mawu omwe aja akuti: “Wantchito wa Chiheberi amene munatibweretsera uja, anabwera kwa ine kuti andichite zachipongwe. 18 Koma ataona kuti ndayamba kukuwa, anasiya malaya ake pambali pangapa nʼkuthawira panja.” 19 Mbuye wa mnyamatayo atamva zimene mkazi wake anamuuza zakuti: “Wantchito wanu anachita zakutizakuti,” anapsa mtima kwambiri. 20 Zitatero, mbuye wake wa Yosefe anamutenga nʼkukamusiya kundende ya akaidi a mfumu kuti akamutsekere, ndipo Yosefe anakhala kumeneko.+

21 Koma Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe nʼkumamusonyeza chikondi chokhulupirika ndipo anachititsa kuti mkulu wa ndende azimukonda.+ 22 Choncho, mkulu wa ndendeyo anasankha Yosefe kuti aziyangʼanira akaidi onse mʼndendemo, ndi chilichonse chimene chinkachitika mmenemo.+ 23 Mkulu wa ndendeyo sankayangʼaniranso chilichonse chimene chinali mʼmanja mwa Yosefe. Zinali choncho chifukwa Yehova anali ndi Yosefe, ndipo Yehova ankamuthandiza kuti chilichonse chimene iye ankachita chiziyenda bwino.+

40 Pambuyo pa zimenezi, mkulu wa operekera zakumwa+ wa Farao mfumu ya ku Iguputo ndi mkulu wa ophika mkate anachimwira mbuye wawo, mfumu ya ku Iguputo. 2 Choncho Farao anawakwiyira kwambiri atumiki ake awiriwo, mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika mkate.+ 3 Ndipo anawaika mʼndende yakunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu,+ kumene Yosefe anali mkaidi.+ 4 Kenako, mkulu wa asilikali olondera mfumu anauza Yosefe kuti azikhala nawo nʼkumawasamalira,+ ndipo iwo anakhala mʼndendemo kwa nthawi yayitali.

5 Usiku wina, woperekera zakumwa kwa mfumu ya Iguputo komanso wophika mkate, omwe anali mʼndende aja, aliyense analota maloto ndipo malotowo anali ndi matanthauzo osiyana. 6 Yosefe atabwera kudzawaona mʼmawa, anadabwa poona kuti ankaoneka achisoni. 7 Choncho anafunsa atumiki a Farao aja, omwe anali naye mʼndende yakunyumba kwa mbuye wakeyo kuti: “Nʼchifukwa chiyani nkhope zanu zili zachisoni lero?” 8 Iwo anamuyankha kuti: “Talota maloto, koma palibe woti atimasulire malotowo.” Yosefe anawauza kuti: “Kodi Mulungu si amene amamasulira?+ Ndifotokozereni malotowo.”

9 Choncho mkulu wa operekera zakumwa anafotokozera Yosefe maloto ake kuti: “Mʼmaloto anga, ndinaona mtengo wa mpesa uli patsogolo panga. 10 Mtengo wa mpesawo unali ndi nthambi zitatu, ndipo unatulutsa mphukira. Kenako unamasula maluwa nʼkubereka mphesa ndipo zinapsa. 11 Mʼmanja mwanga ndinali ndi chikho cha Farao, ndipo ndinatenga mphesazo nʼkuzifinyira mʼchikho cha Faraocho. Nditatero, ndinapereka chikhocho kwa Farao.” 12 Ndiyeno Yosefe anamuuza kuti: “Kumasulira kwake ndi uku: Nthambi zitatuzo zikuimira masiku atatu. 13 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa.* Adzakubwezera ndithu pa ntchito yako yakale,+ yoperekera zakumwa kwa mfumu ngati mmene unkachitira poyamba.+ 14 Koma usadzandiiwale zinthu zikadzakuyendera bwino. Chonde, udzandisonyeze chikondi chokhulupirika pomuuza Farao za ine, nʼcholinga choti ndidzatuluke mʼndende muno. 15 Kuti ndipezeke kuno anachita kundiba kudziko la Aheberi,+ ndipo palibe chilichonse chimene ndinalakwa choti andiikire mʼndende* muno.”+

16 Mkulu wa ophika mkate ataona kuti Yosefe wamasulira zabwino, nayenso anati: “Inenso ndinalota maloto. Ndinalota nditasenza pamutu pangapa mabasiketi atatu a mikate yoyera. 17 Mubasiketi yapamwamba munali mikate yosiyanasiyana ya Farao, ndipo mbalame zimadya mikate imene inali mʼbasiketimo pamutu panga.” 18 Ndiyeno Yosefe anati: “Kumasulira kwake ndi uku: Mabasiketi atatuwo akuimira masiku atatu. 19 Pakapita masiku atatu, Farao akutulutsa nʼkukudula mutu.* Adzakupachika pamtengo, ndipo mbalame zidzadya nyama yako.”+

20 Tsiku lachitatulo linali tsiku lokumbukira kubadwa+ kwa Farao. Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa mʼndende* mkulu wa operekera zakumwa ndi mkulu wa ophika mkate, nʼkuwaimiritsa pamaso pa antchito ake onse. 21 Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera zakumwa uja, moti anapitiriza ntchito yake yoperekera zakumwa kwa Farao. 22 Koma mkulu wa ophika mkate anamupachika, mogwirizana ndi zimene Yosefe anawauza pomasulira maloto aja.+ 23 Komabe, mkulu wa operekera zakumwa uja sanamʼkumbukire Yosefe, anamuiwala.+

41 Patatha zaka ziwiri zathunthu, Farao analota+ ataimirira mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo. 2 Iye anaona ngʼombe 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailo. Ngʼombezo zinali zooneka bwino komanso zonenepa, ndipo zinkadya udzu wamʼmbali mwa mtsinjewo.+ 3 Pambuyo pake anaonanso ngʼombe zina 7 zikutuluka mumtsinje wa Nailowo. Zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda, ndipo zinaima pambali pa zonenepazo mʼmbali mwa mtsinjewo. 4 Ndiye ngʼombe zonyansa ndi zowondazo zinayamba kudya ngʼombe 7 zooneka bwino ndi zonenepa zija. Kenako Farao anadzidzimuka.

5 Ndiyeno Farao anagonanso nʼkulota maloto ena. Mʼmalotowa anaona ngala za tirigu 7 zikutuluka paphesi limodzi. Ngalazo zinali zokhwima ndi zazikulu bwino.+ 6 Pambuyo pake anaonanso ngala zina 7 zikutuluka. Ngalazo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa. 7 Ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zokhwima ndi zazikulu bwinozo. Kenako Farao anadzidzimuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.

8 Mʼmawa kutacha, Farao anavutika kwambiri maganizo. Choncho anaitanitsa ansembe onse amatsenga ndi amuna anzeru onse a mu Iguputo, nʼkuwafotokozera malotowo. Koma palibe amene anatha kumumasulira Farao maloto akewo.

9 Kenako mkulu wa operekera zakumwa uja anauza Farao kuti: “Lero ndiulule machimo anga. 10 Inuyo Farao munatikwiyira kwambiri ife atumiki anu. Ineyo ndi mkulu wa ophika mkate munatitsekera mʼndende yakunyumba kwa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ 11 Kundendeko tonse awiri tinalota maloto usiku umodzi. Aliyense analota maloto ndipo malotowo anali ndi matanthauzo osiyana.+ 12 Tinalinso ndi mnyamata wina wa Chiheberi kumeneko. Iyeyo anali wantchito wa mkulu wa asilikali olondera mfumu.+ Titamufotokozera maloto athu,+ anatimasulira matanthauzo ake. Aliyense anamumasulira mogwirizana ndi maloto amene analota. 13 Zimene anamasulira nʼzomwedi zinachitika. Ineyo ndinabwezeretsedwa pa ntchito, koma mnzangayo anapachikidwa.”+

14 Choncho Farao anatuma anthu kukatenga Yosefe+ kundendeko,* ndipo anabwera naye mofulumira.+ Yosefe anameta bwinobwino, kenako anasintha zovala nʼkukaonekera pamaso pa Farao. 15 Ndiyeno Farao anauza Yosefe kuti: “Ine ndalota maloto, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kuwamasulira. Koma ndamva kuti iweyo ukamva maloto umatha kumasulira.”+ 16 Yosefe anayankha Farao kuti: “Mulungu ndi amene anene nkhani yabwino yokhudza inu Farao, osati ine.”+

17 Farao anafotokozera Yosefe kuti: “Ndinalota nditaima mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo. 18 Ndiyeno ndinaona ngʼombe 7 zonenepa ndi zooneka bwino zikutuluka mumtsinje wa Nailo, ndipo zinayamba kudya udzu wa mʼmbali mwa mtsinjewo.+ 19 Pambuyo pake ndinaonanso ngʼombe zina 7 zikutuluka mumtsinjewo. Ngʼombe zimenezi zinali zonyansa ndi zowonda. Sindinaonepo ngʼombe zonyansa ngati zimenezo mʼdziko lonse la Iguputo. 20 Ngʼombe zowonda ndi zonyansazo zinayamba kudya ngʼombe 7 zonenepa zija. 21 Koma ngakhale zinadya zinzakezo, palibe akanadziwa chifukwa ngʼombezo zimaonekabe zowonda ngati poyamba. Kenako ndinadzidzimuka.

22 Ndiyeno ndinalotanso maloto ena. Ndinalota ngala 7 za tirigu, zokhwima ndi zooneka bwino, zikutuluka paphesi limodzi.+ 23 Pambuyo pake ndinaonanso ngala zina 7 zikutuluka ndipo zinali zonyala komanso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa. 24 Ndiyeno ngala zonyalazo zinayamba kumeza ngala 7 zooneka bwinozo. Ndinafotokozera malotowa ansembe amatsenga,+ koma palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kumasulira.”+

25 Pamenepo Yosefe anauza Farao kuti: “Maloto anu awiriwa tanthauzo lake ndi limodzi. Mulungu woona wakudziwitsani inu Farao zimene adzachite.+ 26 Ngʼombe 7 zonenepazo zikuimira zaka 7. Komanso ngala 7 zooneka bwinozo zikuimira zaka 7. Malotowa tanthauzo lake ndi limodzi. 27 Ngʼombe 7 zowonda ndi zonyansazo, zimene zinatuluka pambuyo pa zoyamba zija, zikuimira zaka 7. Komanso ngala 7 zopanda kanthu ndiponso zowauka ndi mphepo yakumʼmawa, zidzakhala zaka 7 za njala. 28 Choncho, monga ndakuuzirani inu Farao, Mulungu woona wakuonetsani zimene adzachite.

29 Kukubwera zaka 7 zimene kudzakhala chakudya chochuluka mʼdziko lonse la Iguputo. 30 Koma pambuyo pa zaka zimenezo, padzabwera zaka 7 za njala. Chakudya chonse chochuluka cha mʼdziko la Iguputo chija chidzaiwalika, ndipo njalayo idzawononga dziko lonse.+ 31 Sizidzadziwika kuti mʼdzikoli pa nthawi ina munali chakudya chambiri, chifukwa njalayo idzakhala yoopsa kwambiri. 32 Inu Farao mwalota kawiri malotowa chifukwa Mulungu woona watsimikiza mtima kuchita zimenezi, ndipo Mulungu woona azichita posachedwapa.

33 Choncho inu Farao mufufuze munthu wozindikira ndi wanzeru, ndipo mumuike kuti akhale woyangʼanira dziko la Iguputo. 34 Inu Farao muike anthu oyangʼanira mʼdziko lino, ndipo muzitenga gawo limodzi mwa magawo 5 a chakudya cha dziko la Iguputo pa zaka 7 zimene kudzakhale zokolola zochuluka.+ 35 Mʼzaka zimene kudzakhale chakudya chambiri, oyangʼanirawo azidzasonkhanitsa tirigu yense nʼkumusunga bwino mʼmizinda ndipo adzakhale wa inu Farao.+ 36 Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha dzikoli pa zaka 7 zimene mʼdziko la Iguputo mudzakhale njala, kuti anthu ndi ziweto asadzafe ndi njalayo.”+

37 Zimene Yosefe ananena zinasangalatsa Farao ndi antchito ake onse. 38 Ndiyeno Farao anafunsa antchito ake kuti: “Kodi pangapezekenso munthu wina ngati uyu, amene ali ndi mzimu wa Mulungu?” 39 Kenako Farao anauza Yosefe kuti: “Popeza kuti Mulungu wakudziwitsa zonsezi, palibenso munthu wina wozindikira ndi wanzeru ngati iwe. 40 Iweyo ukhala woyangʼanira nyumba yanga, ndipo anthu anga onse azimvera chilichonse chimene iweyo ungawauze.+ Koma ine ndekha ndikhala wamkulu kwa iwe chifukwa ndine mfumu.” 41 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Tsopano ndikukuika kukhala woyangʼanira dziko lonse la Iguputo.”+ 42 Atatero, Farao anavula mphete yake yachifumu kudzanja lake nʼkuveka Yosefe. Anamuvekanso zovala zokongola komanso tcheni chagolide mʼkhosi mwake. 43 Ndiponso anamukweza pagaleta lina la Farao,* ndipo anthu ankafuula patsogolo pake kuti, “A·vrékh!”* Choncho Farao anamupatsa udindo woyangʼanira dziko lonse la Iguputo.

44 Farao anauzanso Yosefe kuti: “Farao ndine, koma popanda chilolezo chako, palibe wina aliyense amene angachite* chilichonse mʼdziko lonse la Iguputo.”+ 45 Kenako Farao anapatsa Yosefe dzina lakuti Zafenati-panea.* Anamʼpatsanso mkazi dzina lake Asenati+ yemwe anali mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.* Ndipo Yosefe anayamba kuyangʼanira* dziko la Iguputo.+ 46 Yosefe anali ndi zaka 30+ pamene anayamba kutumikira* Farao, mfumu ya Iguputo.

Kenako anachoka pamaso pa Farao nʼkuyamba kuyendera dziko lonse la Iguputo. 47 Pa zaka zonse 7 zimene dzikolo linabereka chakudya chochuluka, mʼdzikolo munali chakudya chamwanaalirenji. 48 Pa zaka 7 zimenezo, Yosefe anasonkhanitsa chakudya chonse chimene anakolola mʼdziko lonse la Iguputo nʼkuchisunga mʼmizinda. Mumzinda uliwonse, ankasunga chakudya chochokera mʼminda yozungulira mzindawo. 49 Yosefe anapitiriza kusunga tirigu, mpaka anachuluka kwambiri ngati mchenga wakunyanja moti anasiya kumuyeza chifukwa sakanathanso kumuyeza chifukwa anali wambiri.

50 Chaka choyamba cha njala chisanafike, Yosefe anakhala ndi ana aamuna awiri,+ amene anamʼberekera mkazi wake Asenati, mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni. 51 Mwana woyambayo, Yosefe anamupatsa dzina lakuti Manase*+ chifukwa anati, “Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse ndi nyumba yonse ya bambo anga.” 52 Wachiwiriyo anamupatsa dzina lakuti Efuraimu*+ chifukwa anati, “Mulungu wandipatsa ana mʼdziko la masautso anga.”+

53 Kenako zaka 7 zimene mʼdziko la Iguputo munali chakudya chochuluka zinatha.+ 54 Ndipo zaka 7 za njala zinayamba, mogwirizana ndi zimene Yosefe ananena.+ Njalayo inali mʼmayiko onse, koma dziko lonse la Iguputo linali ndi chakudya.+ 55 Kenako njala ija inafika mʼdziko lonse la Iguputo, ndipo anthu anayamba kulirira Farao kuti awapatse chakudya.+ Koma Farao anauza Aiguputo onse kuti: “Pitani kwa Yosefe, ndipo mukachite chilichonse chimene akakuuzeni.”+ 56 Njala ija inapitirizabe padziko lonse lapansi.+ Zitatero, Yosefe anayamba kutsegula nkhokwe zonse zimene zinali pakati pawo nʼkuyamba kugulitsa chakudya kwa Aiguputo,+ chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri mʼdziko la Iguputo. 57 Komanso, anthu padziko lonse lapansi anayamba kubwera ku Iguputo kudzagula chakudya kwa Yosefe, chifukwa njalayo inali itafika poipa kwambiri padziko lonse lapansi.+

42 Yakobo atamva kuti ku Iguputo kuli tirigu,+ anafunsa ana ake kuti: “Kodi muzingoyangʼanana?” 2 Anapitiriza kuti: “Ine ndamva kuti ku Iguputo kuli tirigu. Pitani mukatigulire kuti tikhalebe ndi moyo, tisafe ndi njala.”+ 3 Choncho abale ake a Yosefe 10+ anapita ku Iguputo kuti akagule tirigu. 4 Koma Yakobo sanalole kuti Benjamini,+ mʼbale wake wa Yosefe, apite limodzi ndi abale akewo chifukwa anati: “Mwina ngozi yoopsa ingamuchitikire nʼkufa.”+

5 Ndiyeno ana a Isiraeliwo anafika ku Iguputo limodzi ndi anthu ena okagula tirigu, chifukwa mʼdziko la Kanani munali njala.+ 6 Yosefe ndi amene anali wolamulira mʼdzikomo+ ndipo ndi amene ankagulitsa tirigu kwa anthu onse ochokera kumayiko ena onse.+ Choncho abale a Yosefe anafika kwa iye ndipo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 7 Yosefe ataona abale akewo, nthawi yomweyo anawazindikira, koma iye anayesetsa kuti asamuzindikire.+ Choncho analankhula nawo mwaukali nʼkuwafunsa kuti: “Mwachokera kuti?” Iwo anayankha kuti: “Tachokera kudziko la Kanani, ndipo tabwera kudzagula chakudya.”+

8 Ngakhale kuti Yosefe anawazindikira abale akewo, iwo sanamʼzindikire. 9 Nthawi yomweyo Yosefe anakumbukira maloto ake aja okhudza abale akewo.+ Choncho anawauza kuti: “Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka!” 10 Koma iwo anakana kuti: “Ayi mbuyathu, akapolo anufe tabwera kudzagula chakudya. 11 Tonsefe ndife ana a munthu mmodzi, ndipo ndife anthu achilungamo. Akapolo anufe sitichita zaukazitape.” 12 Koma iye anawauza kuti: “Mukunama! Mwabwera kuno kudzafufuza malo ofooka a dziko lathu.” 13 Iwo anati: “Akapolo anufe ndife pachibale ndipo tinalipo 12.+ Ndife ana a munthu mmodzi+ wa ku Kanani. Wamngʼono kwambiri watsala ndi bambo athu,+ koma mmodzi kulibenso.”+

14 Komabe Yosefe anawauza kuti: “Ndiye kuti zimene ndanena zija ndi zoona kuti, ‘Anthu inu ndi akazitape!’ 15 Ndiye ndikuyesani kuti ndione ngati mukunena zoona: Pali Farao wamoyo, ndithu simuchoka kuno mpaka mngʼono wanuyo atabwera.+ 16 Tumani mmodzi wa inu kuti apite kukatenga mngʼono wanuyo. Enanu ndikutsekerani mʼndende. Ndikufuna ndione ngati mukunena zoona. Ndipo ngati si zoona, pali Farao wamoyo, ndiye kuti ndinu akazitape basi.” 17 Atatero, anawatsekera mʼndende onse pamodzi kwa masiku atatu.

18 Pa tsiku lachitatu, Yosefe anawauza kuti: “Chitani izi kuti mukhale ndi moyo, chifukwa ndimaopa Mulungu. 19 Ngati mulidi achilungamo, mmodzi wa inu atsale mʼndendemu. Ena nonsenu mukhoza kumapita kuti mukapereke tirigu kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 20 Ndiyeno mukabweretse mngʼono wanuyo kwa ine. Mukatero, ndidzatsimikiza kuti mukunena zoona, moti simudzaphedwa.” Iwo anachitadi zomwezo.

21 Kenako iwo anayamba kukambirana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira mʼbale wathu uja.+ Pajatu tinaona mmene ankamvetsera chisoni pamene ankatichonderera kuti timuchitire chifundo, koma ife sitinamumvere. Nʼchifukwa chaketu takumana ndi tsoka limeneli.” 22 Ndiyeno Rubeni anayankha kuti: “Kodi ine sindinakuuzeni kuti, ‘Mwanayu musamuchitire zoipaʼ?* Koma inu simunamvere.+ Si izi nanga, magazi ake akufunidwatu kwa ife.”+ 23 Iwo sanadziwe kuti Yosefe akumva zimene ankanenazo, chifukwa ankalankhula nawo kudzera mwa womasulira. 24 Ndiyeno Yosefe anapita kwayekha kukalira.+ Kenako anabwerako nʼkuyambiranso kulankhula nawo, ndipo anatenga Simiyoni+ nʼkumumanga iwo akuona.+ 25 Atatero Yosefe analamula anyamata ake kuti awathirire tirigu mʼmatumba awo mpaka kudzaza komanso kuti aliyense amubwezere ndalama zake pomuikira mʼthumba lake. Anawalamulanso kuti awapatse chakudya cha pa ulendo. Anyamatawo anawachitiradi zimenezo.

26 Choncho iwo ananyamulitsa abulu awo tiriguyo nʼkuyamba ulendo wawo. 27 Atafika pamalo oti agone, mmodzi wa iwo anamasula thumba lake kuti atengemo chakudya choti apatse bulu wake. Atamasula, anangoona kuti ndalama zake zili pakamwa pa thumbalo. 28 Iye anauza abale akewo kuti: “Taonani! Ndalama zanga andibwezera, izi zili mʼthumbazi!” Choncho mitima yawo inangoti myuu! ndipo anayamba kunjenjemera nʼkuyamba kufunsana kuti: “Kodi Mulungu akutichitira chiyani ife?”

29 Atafika kwa bambo awo Yakobo mʼdziko la Kanani, anawafotokozera zonse zimene zinawachitikira kuti: 30 “Nduna yaikulu ya dzikolo inalankhula nafe mwaukali,+ chifukwa inationa ngati akazitape okafufuza dzikolo. 31 Koma tinaiuza kuti, ‘Ndife anthu achilungamo, si ife akazitape.+ 32 Ndife ana a bambo mmodzi ndipo tinalipo ana aamuna 12.+ Koma mmodzi kulibenso,+ ndipo wamngʼono ali ndi bambo athu kudziko la Kanani.’+ 33 Ndiye nduna yaikulu ya dzikolo inatiuza kuti, ‘Ngati mulidi achilungamo muchite izi: Mmodzi wa inu atsale ndi ine kuno.+ Koma enanu tengani chakudya, mupite nacho kunyumba zanu chifukwa kuli njala.+ 34 Mukabweretse mʼbale wanu wamngʼonoyo kwa ine kuti ndidzatsimikize kuti si inu akazitape koma anthu achilungamo. Mukatero, ndidzakubwezerani mʼbale wanuyu, ndipo mudzatha kuchita malonda mʼdziko lino.’”

35 Pamene ankakhuthula matumba awo, aliyense anapeza kachikwama ka ndalama zake mʼthumba lake. Iwo limodzi ndi bambo awo ataona ndalamazo, anachita mantha. 36 Yakobo bambo awo anadandaula kuti: “Inetu mwandisandutsa namfedwa!+ Yosefe anapita,+ Simiyoni kulibenso.+ Tsopano mukufuna kutenga Benjamini! Nʼchifukwa chiyani zonsezi zikundichitikira?” 37 Koma Rubeni anauza bambo ake kuti: “Ngati Benjamini sindidzabwera naye kwa inu, mudzaphe ana anga aamuna awiri.+ Mumupereke mʼmanja mwanga, ndipo ndidzamʼbwezera kwa inu.”+ 38 Koma bambowo anati: “Zoti mwana wanga apite nanu, izo ndiye ndakana, chifukwa mʼbale wake anafa, ndipo iye anatsala yekha.+ Ngati ngozi yoopsa itamuchitikira panjira nʼkufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda*+ imvi zanga chifukwa cha chisoni.”+

43 Tsopano njala ija inakula kwambiri mʼdzikomo.+ 2 Tirigu amene anabweretsa kuchokera ku Iguputo+ uja atatha, bambo awo anawauza kuti: “Pitaninso mukatigulireko kachakudya pangʼono.” 3 Koma Yuda anauza bambo ake kuti: “Munthu ujatu anatichenjeza momveka bwino kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine* pokhapokha mʼbale wanuyo mutabwera naye.’+ 4 Mukalola kuti mʼbale wathuyu timutenge, tipita ku Iguputo kuti tikakugulireni chakudya. 5 Koma ngati simutilola kupita naye, sitipitako, chifukwa munthu uja anatiuza kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine pokhapokha mʼbale wanuyo mutabwera naye.’”+ 6 Ndiyeno Isiraeliyo+ anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandiputira mavuto pomuuza munthuyo kuti muli ndi mʼbale wanu wina?” 7 Koma iwo anayankha kuti: “Munthuyo anachita kufunsa zokhudza ife ndi banja lathu kuti, ‘Kodi bambo anu adakali ndi moyo? Kodi muli ndi mʼbale wanu wina?’ Ndipo ife tinamuuza zoona.+ Nanga tikanadziwa bwanji zoti anena kuti, ‘Mukabwere naye kuno mʼbale wanuyoʼ?”+

8 Kenako Yuda anauza Isiraeli bambo ake kuti: “Ndiloleni ndimutenge mnyamatayu+ kuti tinyamuke tizipita kuti tikhalebe ndi moyo tisafe,+ inuyo ndi ife, limodzi ndi ana athuwa.+ 9 Moyo wa mnyamatayu ukhale mʼmanja mwanga.*+ Ngati chinachake chitamuchitikira mudzandilange. Ndikadzapanda kubwera naye ndi kumʼpereka kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu moyo wanga wonse. 10 Ndipotu tikanapanda kuzengereza, bwenzi pano titapita nʼkubwerako maulendo awiri.”

11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Ngati ndi choncho, chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali zamʼdziko lino mʼmatumba anu, mukamʼpatse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pangʼono, uchi pangʼono, labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho ndi zipatso za amondi. 12 Mutengenso ndalama kuchulukitsa kawiri zoyamba zija. Komanso mutenge ndalama zimene anakubwezerani zija, zomwe munazipeza pakamwa pa matumba anu,+ mukazibweze. Mwina anangosokoneza. 13 Mutenge mʼbale wanuyu ndipo mupitenso kwa munthuyo. 14 Mulungu Wamphamvuyonse apangitse munthuyo kukuchitirani chifundo, kuti akamasule mʼbale wanu uja, ndipo mukabwere naye limodzi ndi Benjamini. Koma ngati ndingataye ana angawa, chabwino, zikhale choncho!”+

15 Ndiyeno amunawo anatenga mphatso zija, ndalama kuchulukitsa kawiri ndiponso Benjamini, nʼkunyamuka kupita ku Iguputo. Kumeneko anakaonananso ndi Yosefe.+ 16 Yosefe atangoona Benjamini ali ndi abale akewo, anauza mwamuna amene ankayangʼanira nyumba yake kuti: “Pita nawo kunyumba anthuwa ndipo ukaphe nyama ndi kukonza chakudya, chifukwa anthuwa adya ndi ine masana ano.” 17 Nthawi yomweyo mwamuna uja anachita zimene Yosefe ananena.+ Anatenga anthu aja nʼkupita nawo kunyumba kwa Yosefe. 18 Koma amunawo atapita nawo kunyumba kwa Yosefe, anachita mantha ndipo anati: “Atibweretsa kuno chifukwa cha ndalama zimene anatibwezera mʼmatumba athu pa ulendo woyamba uja. Anthu amenewa atiukira nʼkutigwira kuti tikhale akapolo ndipo atilanda abulu athu!”+

19 Choncho iwo anapita kwa munthu woyangʼanira nyumba ya Yosefe uja nʼkulankhula naye pakhomo lolowera mʼnyumbamo. 20 Iwo anati: “Pepani mbuyathu! Ifetu tinabwera kuno kudzagula chakudya ulendo woyamba.+ 21 Koma pobwerera, titafika pamalo oti tigone, tinamasula matumba athu ndipo tinangoona kuti ndalama za aliyense zili pakamwa pa thumba lake, zonse mogwirizana ndi kulemera kwake.+ Choncho tabwera nazo kuti tizibweze tokha. 22 Tabwera ndi ndalama zina zogulira chakudya. Koma sitikudziwa kuti ndi ndani amene anatiikira ndalama mʼmatumba athu.”+ 23 Pamenepo mwamunayo anati: “Musachite mantha, simunalakwe chilichonse. Mulungu wanu, Mulungu wa bambo anu ndi amene anaika chumacho mʼmatumba mwanu. Ndalama zanu ndinalandira kale.” Atatero mwamunayo anamasula Simiyoni nʼkumupititsa kwa iwo.+

24 Kenako munthuyo analowetsa amunawo mʼnyumba ya Yosefe. Anawapatsa madzi kuti asambe mapazi awo nʼkuwapatsanso chakudya choti adyetse abulu awo. 25 Amunawo anakonzeratu mphatso+ zimene anabwera nazo zija kuti apatse Yosefe masanawo, popeza anali atamva kuti adya nawo limodzi chakudya kumeneko.+ 26 Ndiyeno Yosefe atafika nʼkulowa mʼnyumbamo, iwo anapereka mphatsozo kwa iye. Ndipo anamugwadira nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 27 Kenako Yosefe anawafunsa za moyo wawo. Anawafunsanso kuti: “Kodi bambo anu okalamba amene munkanena aja ali bwanji? Kodi adakali ndi moyo?”+ 28 Iwo anayankha kuti: “Kapolo wanu bambo athu ali bwino. Adakali ndi moyo.” Atatero anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+

29 Yosefe atakweza maso ake nʼkuona mngʼono wake Benjamini, mʼbale wake wa mimba imodzi,+ anati: “Kodi uyu ndi mngʼono wanu amene munkanena uja?”+ Ananenanso kuti: “Mulungu akukomere mtima mwana wanga.” 30 Ndiyeno Yosefe anachokapo mofulumira chifukwa anagwidwa chifundo ataona mʼbale wakeyo. Anafunafuna malo oti akalirireko, ndiye analowa mʼchipinda chimene munalibe anthu nʼkugwetsa misozi.+ 31 Kenako, anasamba kumaso nʼkutuluka ndipo anadzilimbitsa nʼkunena kuti: “Ikani chakudya.” 32 Iwo anamuikira Yosefe chakudya payekha. Abale akewo anawaikiranso paokha. Nawonso Aiguputo amene ankadya mʼnyumba mwake anawaikira paokha. Aiguputo sankadya limodzi ndi Aheberi, chifukwa chinali chinthu chonyansa kwa iwo.+

33 Abale akewo anawauza kuti akhale pansi pamaso pake, kuyambira wamkulu kwambiri*+ mpaka wamngʼono kwambiri. Iwo ankangoyangʼanana modabwa. 34 Yosefe ankatapa chakudya patebulo pake nʼkumapatsa operekera chakudya kuti aziwonjezera pachakudya cha abale akewo. Koma chakudya chimene ankapatsa Benjamini ankachichulukitsa maulendo 5 kuposa cha ena onsewo.+ Choncho iwo anapitiriza kudya ndi kumwa naye limodzi mosangalala mpaka kukhuta.

44 Kenako Yosefe analamula woyangʼanira nyumba yake uja kuti: “Udzazitse chakudya mʼmatumba a anthuwa chimene angakwanitse kunyamula. Aliyense umubwezere ndalama zake ndipo uziike pakamwa pa thumba lake.+ 2 Koma uike kapu yanga yasiliva ija pakamwa pa thumba la wamngʼonoyo limodzi ndi ndalama zake zogulira tirigu.” Choncho woyangʼanira nyumba yakeyo anachita zimene Yosefe anamuuzazo.

3 Mʼmawa kutacha, abale ake a Yosefe aja anawalola kuti azipita pamodzi ndi abulu awo. 4 Iwo asanapite patali kuchokera mumzindawo, Yosefe anauza woyangʼanira nyumba yake kuti: “Nyamuka, athamangire anthu aja. Ukawapeza uwafunse kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwabwezera zoipa pa zabwino? 5 Nʼchifukwa chiyani mwaba kapu yomwera mbuye wanga, imenenso amaombezera pofuna kudziwa zinthu? Mwachita chinthu choipa kwambiri.’”

6 Choncho munthu uja atawapeza, anawafunsa zimenezo. 7 Koma iwo anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula choncho mbuyathu? Nʼzosatheka kuti akapolo anufe tichite zinthu ngati zimenezo. 8 Pajatu ndalama zimene tinazipeza pakamwa pa matumba athu kudziko la Kanani tinazibweza kwa inu.+ Ndiye zingatheke bwanji kuti tibe siliva ndi golide mʼnyumba ya mbuye wanu? 9 Amene apezeke ndi kapuyo mwa akapolo anufe aphedwe, ndipo enafe tikhale akapolo anu mbuyathu.” 10 Ndiyeno iye anati: “Chabwino, zichitike mmene mwaneneramo. Amene ati apezeke nayo akhala kapolo wanga, koma enanu mukhala opanda mlandu.” 11 Zitatero, aliyense anatsitsa pansi thumba lake mwamsanga nʼkulimasula. 12 Munthu uja anafufuza mosamala mʼmatumba awo, kuyambira la wamkulu kumalizira ndi la wamngʼono. Pamapeto pake, kapuyo inapezeka mʼthumba la Benjamini.+

13 Zitatero, iwo anangʼamba zovala zawo. Kenako aliyense anakwezanso thumba lake pabulu wake nʼkubwerera kumzinda kuja. 14 Yuda+ ndi abale ake atalowa mʼnyumba ya Yosefe, anamupeza adakali mʼnyumbamo, ndipo iwo anagwada nʼkumuweramira mpaka nkhope zawo pansi.+ 15 Yosefe anati: “Ndiye chiyani mwachitachi? Kodi inu simukudziwa kuti munthu ngati ine ndingathe kudziwa zinthu poombeza maula?”+ 16 Ndiyeno Yuda anayankha kuti: “Kodi tinganene chiyani kwa inu mbuyathu? Tilankhule kuti chiyani? Titani kuti muone kuti sitinalakwe? Pamenepa Mulungu woona ndi amene wapeza cholakwa mwa ife akapolo anu.+ Basi, titengeni ndife akapolo anu mbuyathu, ifeyo limodzi ndi amene mwamʼpeza ndi kapuyo.” 17 Koma Yosefe anati: “Sindingachite zimenezo! Amene wapezeka ndi kapu yangayo ndi amene akhale kapolo wanga.+ Enanu mupite kwa bambo anu mwamtendere.”

18 Tsopano Yuda anayandikira kwa Yosefe nʼkunena kuti: “Chonde mbuyanga, ndikukupemphani. Ndiloleni kapolo wanune kuti ndinene mawu amodzi okha. Chonde musandipsere mtima, chifukwa inu muli ngati Farao yemwe.+ 19 Pajatu inu mbuyanga munatifunsa akapolo anufe kuti: ‘Kodi muli ndi bambo kapena mʼbale wanu wina?’ 20 Ife tinakuyankhani mbuyanga kuti, ‘Bambo tili nawo koma ndi okalamba. Ali ndi mwana amene anabereka atakalamba, yemwe ndi wamngʼono kwa tonsefe.+ Mʼbale wake wa mimba imodzi anamwalira,+ moti anatsala yekha+ ndipo bambo amamukonda kwambiri.’ 21 Kenako inu munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Mukabwere naye kuno kuti ndidzamuone.’+ 22 Koma ife tinakuuzani inu mbuyanga kuti, ‘Mwanayo sangachoke kwa bambo ake. Atati achoke, ndithu bambo akewo akhoza kufa.’+ 23 Ndiyeno munatiuza ife akapolo anu kuti, ‘Musadzabwerenso kwa ine* pokhapokha ngati mʼbale wanuyo mutabwera naye.’+

24 Choncho ife tinapita kwa kapolo wanu, bambo athu, ndipo tinawauza zimene munanena mbuyanga. 25 Patapita nthawi bambo athu anatiuza kuti, ‘Pitaninso mukatigulireko kachakudya pangʼono.’+ 26 Koma ife tinati, ‘Sitingathe kupitanso. Ngati mungatilole kutenga mngʼono wathuyu tipitako, chifukwa sitingathe kukaonananso ndi munthuyo pokhapokha ngati mngʼono wathuyu titapita naye.’+ 27 Ndiyeno kapolo wanu bambo athuwo anatiuza kuti, ‘Inuyo mukudziwa bwino kuti mkazi wanga anandiberekera ana awiri okha.+ 28 Koma mmodzi wa awiriwo anandisiya, ndipo ndinafuula kuti: “Mayo ine! Wakhadzulidwa ndithu mwana wanga!”+ moti sindinamuonenso mpaka lero. 29 Ndiye ngati uyunso mungapite naye, ngozi yoopsa nʼkumuchitikira panjira nʼkufa, ndithu mudzatsitsira ku Manda*+ imvi zanga chifukwa cha chisoni.’+

30 Bambo amamʼkonda kwambiri mwanayu ngati mmene amakondera moyo wawo. Choncho ndikakangofika kwa kapolo wanu bambo anga ndilibe mwanayu, 31 iwo nʼkuona kuti mwanayu palibe, basi akafa. Ndithu, akapolo anufe tidzatsitsira ku Manda* imvi za kapolo wanu bambo athu chifukwa cha chisoni. 32 Ine kapolo wanu ndinalonjeza bambo anga kuti moyo wa mwanayu udzakhala mʼmanja mwanga. Ndinalonjeza kuti, ‘Ndikadzalephera kubwera naye kwa inu, ndidzakhale wochimwa kwa inu bambo anga moyo wanga wonse.’+ 33 Ndiye chonde mbuyanga, tengani ineyo ndikhale kapolo wanu mʼmalo mwa mwanayu, kuti iye apite ndi abale akewa. 34 Ndingathe bwanji kupita kwa bambo anga ndilibe mwanayu? Ayi, sindikufuna kukaona bambo anga akuzunzika.”

45 Zitatero Yosefe analephera kudzigwira pamaso pa atumiki ake onse.+ Ndiyeno anafuula kuti: “Aliyense atuluke muno!” Choncho panalibe aliyense amene anali naye pamene Yosefe ankadziulula kwa abale ake.+

2 Atatero, anayamba kulira mokweza mawu mpaka Aiguputo ndiponso anthu akunyumba ya Farao anamva. 3 Kenako Yosefe anauza abale akewo kuti: “Ndine Yosefe! Kodi bambo anga adakali ndi moyo?” Koma abale akewo sanathe kumuyankha chifukwa anali atawasokoneza maganizo. 4 Ndiyeno Yosefe anauza abale akewo kuti: “Sunthirani pafupi ndi ine.” Ndipo anasunthiradi pafupi ndi iye.

Kenako Yosefe anati: “Ndine mʼbale wanu uja Yosefe, amene munamugulitsa ku Iguputo.+ 5 Koma musadzimvere chisoni kapena kuimbana mlandu kuti munandigulitsa kuno, chifukwa Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti tikhalebe ndi moyo.+ 6 Chino ndi chaka chachiwiri cha njala padziko pano.+ Kutsogoloku kukubwera zaka zina 5 zimene anthu sadzalima kapena kukolola. 7 Koma Mulungu ananditumiza kuno, kuti anthu inu musatheretu+ padziko lapansi,* komanso kuti mukhalebe ndi moyo pokupulumutsani modabwitsa. 8 Choncho si inu amene munanditumiza kuno, koma ndi Mulungu woona. Anachita zimenezi kuti andiike kukhala nduna yaikulu ya* Farao, mbuye wa nyumba yake yonse ndiponso wolamulira wa dziko lonse la Iguputo.+

9 Bwererani kwa bambo anga msanga, ndipo mukawauze kuti, ‘Mwana wanu Yosefe wanena kuti: “Mulungu wandiika ine kukhala mbuye wa dziko lonse la Iguputo.+ Bwerani kuno kwa ine, musachedwe.+ 10 Mudzakhala mʼdziko la Goseni+ kuti mudzakhale pafupi ndi ine. Mubwere inuyo, ana anu, adzukulu anu, nkhosa zanu, ngʼombe zanu ndi zonse zimene muli nazo. 11 Kumeneko ndizidzakupatsani chakudya chifukwa kwatsala zaka 5 za njala.+ Mukapanda kuchita zimenezi, inuyo ndi amʼnyumba yanu komanso zonse zimene muli nazo muvutika ndi njala.”’ 12 Inuyo ndi mʼbale wangayu Benjamini, mukuona ndi maso anu kuti ndine amene ndikulankhula nanu.+ 13 Choncho, mukauze bambo anga za ulemerero wanga wonse ku Iguputo kuno ndi zonse zimene mwaona. Ndiye fulumirani mukatenge bambo anga nʼkubwera nawo kuno.”

14 Yosefe atatero, anakumbatira Benjamini mʼbale wake nʼkuyamba kulira. Nayenso Benjamini analira atakumbatira mʼbale wakeyo.+ 15 Kenako Yosefe anakisa abale ake onsewo nʼkumalira akuwakumbatira. Pambuyo pake, abale akewo analankhula naye.

16 Uthenga unafika kunyumba kwa Farao wakuti: “Abale ake a Yosefe abwera!” Farao ndi atumiki ake anasangalala atamva zimenezo. 17 Choncho Farao anauza Yosefe kuti: “Abale akowa uwauze kuti, ‘Chitani izi: Kwezani katundu panyama zanu, mupite kudziko la Kanani. 18 Mukatenge bambo anu ndi mabanja anu nʼkubwera nawo kuno kwa ine. Ndidzakupatsani zabwino zamʼdziko la Iguputo, ndipo mudzadya zinthu zochokera munthaka yachonde yamʼdzikoli.’+ 19 Uwauzenso kuti:+ ‘Chitani izi: Mutenge ngolo+ kuno ku Iguputo zoti mukatengeremo ana anu ndi akazi anu. Ngolo ina mukatengeremo bambo anu nʼkubwera kuno.+ 20 Musadandaule za katundu wanu,+ chifukwa zabwino za dziko lonse la Iguputo ndi zanu.’”

21 Ana a Isiraeli aja anachitadi zimenezo. Yosefe anawapatsa ngolo monga momwe Farao analamulira. Anawapatsanso chakudya cha pa ulendo. 22 Aliyense wa iwo anamupatsa chovala chatsopano, koma Benjamini anamupatsa zovala zatsopano 5, ndi ndalama zasiliva 300.+ 23 Kwa bambo ake anatumizako abulu 10 onyamula zinthu zabwino zochokera ku Iguputo, abulu aakazi 10 onyamula tirigu ndi chakudya chawo cha pa ulendo. 24 Atatero, anauza abale akewo kuti anyamuke. Pamene ankanyamuka anawauza kuti: “Musakanganetu mʼnjira.”+

25 Iwo anachoka ku Iguputo kuja nʼkukafika kudziko la Kanani, kwa Yakobo bambo awo. 26 Atafika, anauza bambo awo kuti: “Yosefe uja ali moyo, ndipo ndi wolamulira wa dziko lonse la Iguputo!”+ Koma Yakobo atamva zimenezo sanawayankhe chifukwa sanawakhulupirire.+ 27 Koma atamufotokozera zonse zimene Yosefe ananena, ndiponso ataona ngolo zimene Yosefe anatumiza kuti zidzamutenge, Yakobo bambo awo anayamba kusangalala. 28 Kenako Isiraeli anafuula kuti: “Basi, tsopano ndakhulupirira! Yosefe mwana wanga adakali ndi moyo! Ndipita ndikamuone ndisanafe!”+

46 Choncho Isiraeli anatenga banja lake komanso zinthu zonse zimene anali nazo nʼkunyamuka. Atafika ku Beere-seba+ anapereka nsembe kwa Mulungu wa bambo ake Isaki.+ 2 Ndiyeno Mulungu analankhula ndi Isiraeli mʼmasomphenya usiku kuti: “Yakobo, Yakobo!” Ndipo Yakobo anayankha kuti: “Ine mbuyanga!” 3 Mulungu anamuuza kuti: “Ine ndine Mulungu woona, Mulungu wa bambo ako.+ Usaope kupita ku Iguputo, chifukwa kumeneko ndidzakupangitsa kukhala mtundu waukulu.+ 4 Ineyo ndipita nawe ku Iguputo, ndiponso ine ndi amene ndidzabwere nawe mʼdziko lino kuchokera kumeneko.+ Ndipo Yosefe ndi amene adzakutseke maso pa imfa yako.”+

5 Kenako Yakobo ananyamuka ku Beere-sebako. Ana a Isiraeliwo anatenga Yakobo bambo awo, limodzi ndi ana awo komanso akazi awo. Anawatengera mʼngolo zimene Farao anatumiza. 6 Anatenganso ziweto zawo zonse ndi katundu wawo yense amene anapeza mʼdziko la Kanani. Kenako Yakobo ndi ana ake onse anafika ku Iguputo. 7 Anafika limodzi ndi ana ake aamuna ndi aakazi limodzinso ndi zidzukulu zake. Anafika ndi banja lake lonse.

8 Awa ndi mayina a ana a Isiraeli, kapena kuti ana a Yakobo, omwe anapita nawo ku Iguputo:+ Mwana woyamba wa Yakobo anali Rubeni.+

9 Ana a Rubeni anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+

10 Ana a Simiyoni+ anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli+ mwana wa mkazi wa Chikanani.

11 Ana a Levi+ anali Gerisoni, Kohati ndi Merari.+

12 Ana a Yuda+ anali Ere, Onani, Shela,+ Perezi+ ndi Zera.+ Koma Ere ndi Onani anafera kudziko la Kanani.+

Ana a Perezi anali Hezironi ndi Hamuli.+

13 Ana a Isakara anali Tola, Puva, Yabi ndi Simironi.+

14 Ana a Zebuloni+ anali Seredi, Eloni ndi Yahaleeli.+

15 Amenewa ndi ana a Leya, amene anaberekera Yakobo ku Padani-aramu, kuphatikizapo Dina+ mwana wamkazi wa Yakobo. Ana onse aamuna ndi aakazi komanso zidzukulu zake analipo 33.

16 Ana a Gadi+ anali Zifioni, Hagi, Suni, Eziboni, Eri, Arodi ndi Areli.+

17 Ana a Aseri+ anali Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya ndipo mchemwali wawo anali Sera.

Ana a Beriya anali Hiberi ndi Malikieli.+

18 Amenewa ndi ana a Zilipa,+ yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Leya. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 16.

19 Ana a Rakele, mkazi wa Yakobo, anali Yosefe+ ndi Benjamini.+

20 Yosefe anabereka Manase+ ndi Efuraimu+ ku Iguputo. Anabereka anawa ndi mkazi wake Asenati+ mwana wa Potifera, wansembe wa mzinda wa Oni.*

21 Ana a Benjamini+ anali Bela, Bekeri, Asibeli, Gera,+ Namani, Ehi, Rosi, Mupimu, Hupimu+ ndi Aridi.+

22 Amenewa ndi ana amene Rakele anaberekera Yakobo. Onse pamodzi analipo 14.

23 Mwana wa* Dani+ anali Husimu.+

24 Ana a Nafitali+ anali Yahazeeli, Guni, Yezera ndi Silemu.+

25 Amenewa ndi ana a Biliha, yemwe Labani anamupereka kwa mwana wake wamkazi Rakele. Iye anaberekera Yakobo ana amenewa. Onse pamodzi analipo 7.

26 Mbadwa zonse za Yakobo zimene anapita nazo ku Iguputo zinalipo 66,+ osawerengera akazi a ana ake. 27 Ana amene Yosefe anabereka ku Iguputo analipo awiri. Anthu onse amʼnyumba ya Yakobo amene anali nawo ku Iguputo analipo 70.+

28 Yakobo anatumiza Yuda+ kuti atsogole kupita kwa Yosefe kukamudziwitsa kuti akubwera ku Goseni. Iwo atafika ku Goseni,+ 29 Yosefe anauza anthu kuti amukonzere galeta lake, kenako ananyamuka kuti akakumane ndi Isiraeli bambo ake ku Goseni. Atangofika kwa bambo akewo, nthawi yomweyo anawakumbatira nʼkulira kwa kanthawi.* 30 Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Tsopano ndingathe kufa mwamtendere. Ndaona nkhope yako ndipo ndadziwa kuti udakali moyo.”

31 Ndiyeno Yosefe anauza abale ake ndi amʼnyumba ya bambo ake kuti: “Ndipite kwa Farao+ ndikamudziwitse kuti, ‘Abale anga ndi amʼnyumba ya bambo anga amene anali mʼdziko la Kanani, abwera kuno kwa ine.+ 32 Anthuwa ndi abusa+ ndipo amaweta ziweto.+ Abwera ndi nkhosa, ngʼombe ndi zinthu zonse zimene ali nazo.’+ 33 Farao akakuitanani nʼkukufunsani kuti, ‘Kodi mumagwira ntchito yanji?’ 34 Inu mukayankhe kuti: ‘Akapolo anufe takhala tikuweta ziweto kuyambira tili ana kufikira lero, ifeyo ndi makolo athu omwe.’+ Mukayankhe choncho kuti mukhale ku Goseni+ kuno, chifukwa aliyense woweta nkhosa Aiguputo amanyansidwa naye.”+

47 Choncho Yosefe anapita kwa Farao nʼkukamuuza kuti:+ “Bambo anga ndi abale anga abwera kuchokera ku Kanani. Abwera ndi nkhosa zawo, ngʼombe zawo ndi zonse zimene ali nazo, ndipo afikira ku Goseni.”+ 2 Pa abale akewo, Yosefe anatengapo 5 nʼkukamuonetsa Farao.+

3 Farao anafunsa abale ake a Yosefe aja kuti: “Kodi mumagwira ntchito yanji?” Iwo anayankha Farao kuti: “Akapolo anufe timaweta nkhosa ngati mmene ankachitira makolo athu.”+ 4 Kenako anauza Farao kuti: “Tabwera kuno kudzakhala monga alendo,+ chifukwa akapolo anufe tilibe chakudya chopatsa ziwetozi, popeza njala yafika poipa kwambiri ku Kanani.+ Ndiye chonde, tiloleni ife akapolo anu tikhale ku Goseni.”+ 5 Zitatero Farao anauza Yosefe kuti: “Bambo ako ndi abale akowa abwera kuno kwa iwe. 6 Dziko la Iguputo lili mʼmanja mwako, choncho uwapatse malo abwino kwambiri.+ Uwauze kuti akhale ku Goseni, ndipo ngati ukudziwapo amuna olimbikira ntchito, uwaike kuti akhale oyangʼanira ziweto zanga.”

7 Kenako Yosefe anabweretsa bambo ake Yakobo nʼkuwasonyeza kwa Farao, ndipo Yakobo anadalitsa Farao. 8 Ndiyeno Farao anafunsa Yakobo kuti: “Kodi muli ndi zaka zingati?” 9 Yakobo anayankha Farao kuti: “Ndili ndi zaka 130 ndipo pa zaka zimenezi ndakhala ndikuyendayenda* mʼmalo osiyanasiyana. Ndakhala ndi moyo zaka zowerengeka komanso zosautsa,+ ndipo si zambiri poyerekezera ndi zaka zimene makolo anga akhala akuyendayenda mʼmalo osiyanasiyana.”+ 10 Atatero, Yakobo anadalitsa Farao nʼkuchoka pamaso pake.

11 Choncho Yosefe anauza bambo ake ndi abale akewo kuti azikhala ku Iguputo. Anawapatsa malo abwino kwambiri adzikolo ku Ramese*+ monga mmene Farao analamulira. 12 Kumeneko, Yosefe ankapatsa chakudya bambo ake, abale ake ndi banja lonse la bambo ake, mogwirizana ndi kuchuluka kwa ana awo.

13 Chakudya chinatheratu mʼdziko lonselo ndipo njala inafika poipa kwambiri. Anthu onse a ku Iguputo ndi a ku Kanani anali ofooka chifukwa cha njalayo.+ 14 Yosefe anasonkhanitsa ndalama zonse zimene zinali mʼdziko la Iguputo ndi la Kanani, zomwe anthu ankagulira chakudya.+ Iye ankatenga ndalamazo nʼkuzipititsa kunyumba kwa Farao. 15 Pamapeto pake, ndalama zonse zamʼdziko la Iguputo ndi dziko la Kanani zinatha. Choncho anthu onse a ku Iguputo anayamba kufika kwa Yosefe nʼkunena kuti: “Tipatseni chakudya! Kodi tikufereni mukuona chifukwa choti ndalama zatithera?” 16 Ndiye Yosefe anati: “Ngati ndalama zakutherani, bweretsani ziweto zanu tidzasinthane ndi chakudya.” 17 Choncho anthuwo anayamba kubweretsa ziweto zawo kwa Yosefe. Yosefeyo ankawapatsa chakudya posinthanitsa ndi mahatchi awo, nkhosa, ngʼombe ndi abulu. Mʼchaka chonsecho, Yosefe ankawapatsa chakudya posinthanitsa ndi ziweto zawo.

18 Chakacho chitatha, anthu anayamba kupita kwa iye chaka chotsatira. Iwo ankanena kuti: “Tisakubisireni mbuyathu, ndalama zathu ndi ziweto zonse zatha chifukwa tinazipereka kwa inu. Tilibenso chilichonse choti tikupatseni kupatulapo matupi athuwa komanso minda yathu. 19 Tiferenji ife inu mukuona, ndipo minda yathu ikhalirenji yogonera? Mutigule limodzi ndi minda yathu potipatsa chakudya kuti tikhale akapolo a Farao. Mutipatse tirigu kuti tikhale ndi moyo tisafe, komanso kuti minda yathu isagonere.” 20 Choncho Yosefe anagulira Farao minda yonse ya Aiguputo, chifukwa munthu aliyense wa mu Iguputo anagulitsa munda wake. Anachita zimenezi chifukwa njala inali itafika poopsa, moti minda yonse inakhala ya Farao.

21 Kenako Yosefe anasamutsira anthuwo mʼmizinda, kuchokera kumalire a dziko la Iguputo mpaka kumalire ena.+ 22 Malo a ansembe okha ndi amene sanawagule,+ chifukwa chakudya chimene ansembe ankadya chinkachokera kwa Farao. Nʼchifukwa chake ansembewo sanagulitse malo awo. 23 Ndiyeno Yosefe anauza anthuwo kuti: “Onani, ndakugulani inu lero limodzi ndi minda yanu kuti mukhale a Farao. Tengani mbewu iyi, mukadzale mʼmindamo. 24 Nthawi yokolola ikakwana, muzipereka kwa Farao gawo limodzi mwa magawo 5 a zokololazo.+ Magawo 4 otsalawo muzigwiritsa ntchito monga mbewu yodzala mʼmindamo, chakudya chanu ndi cha anthu amʼnyumba zanu komanso cha ana anu.” 25 Iwo anayankha kuti: “Mwapulumutsa miyoyo yathu.+ Mwatikomera mtima mbuyathu, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.”+ 26 Choncho Yosefe anakhazikitsa lamulo limene lilipobe mpaka lero lakuti, Farao azilandira gawo limodzi mwa magawo 5 a zokolola za minda yonse ya mu Iguputo. Koma malo a ansembe okha sanakhale a Farao.+

27 Aisiraeliwo anakhazikika mʼdziko la Iguputo, mʼdera la Goseni.+ Kumeneko anaberekana nʼkuchulukana kwambiri.+ 28 Ndipo Yakobo anakhalabe ndi moyo mʼdziko la Iguputo kwa zaka 17. Choncho Yakobo anakhala ndi moyo zaka 147.+

29 Tsopano nthawi yakuti Isiraeli amwalire inayandikira.+ Ndiye anaitana mwana wake Yosefe nʼkumuuza kuti: “Ngati ungandikomere mtima, ika dzanja lako pansi pa ntchafu yanga. Ulumbire kuti udzandisonyeza chikondi chokhulupirika komanso kuti udzakhala wokhulupirika kwa ine. Chonde, usadzandiike mʼmanda ku Iguputo kuno.+ 30 Ndikadzamwalira,* udzandinyamule kuchoka ku Iguputo kuno nʼkukandiika mʼmanda a makolo anga.”+ Yosefe anayankha kuti: “Ndidzachitadi mogwirizana ndi zimene mwanena.” 31 Ndiyeno Yakobo anati: “Lumbira kwa ine.” Yosefe analumbira kwa iye.+ Zitatero Isiraeli anawerama nʼkutsamira kumutu kwa bedi lake.+

48 Patapita nthawi Yosefe anauzidwa kuti: “Bambo anutu afooka.” Ndiyeno Yosefe anatenga ana ake awiri, Manase ndi Efuraimu nʼkupita kwa bambo akewo.+ 2 Kenako Yakobo anauzidwa kuti: “Mwana wanu Yosefe wabwera.” Choncho Isiraeli anadzuka modzilimbitsa nʼkukhala tsonga pabedi. 3 Yakobo anauza Yosefe kuti:

“Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine ku Luzi mʼdziko la Kanani nʼkundidalitsa.+ 4 Iye anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana, ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+ 5 Kuyambira lero ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, akhala anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga ngati mmene alili Rubeni ndi Simiyoni.+ 6 Koma ana amene udzabereke pambuyo pa anawa, amenewo adzakhala ako. Iwo adzalandira mbali ya malo amene abale awo adzalandire ngati cholowa.+ 7 Kunena za ine, pamene ndinkachokera ku Padani, mayi ako Rakele anandifera+ panjira mʼdziko la Kanani, patatsala mtunda ndithu kuti tifike ku Efurata.+ Zitatero, ndinawaika mʼmanda panjira yopita ku Efurata, kapena kuti Betelehemu.”+

8 Ndiyeno Isiraeli ataona ana a Yosefe, anafunsa kuti: “Kodi awa ndi ndani?” 9 Yosefe anayankha bambo akewo kuti: “Ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kunoko.”+ Ndiyeno bambo akewo anati: “Tawabweretse kuno chonde, ndiwadalitse.”+ 10 Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba, moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anakisa anawo nʼkuwakumbatira. 11 Ndiyeno Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Sindinkayembekezera kuti ndingadzaonenso nkhope yako,+ koma pano Mulungu wandilola kuti ndionenso ana ako.” 12 Atatero, Yosefe anachotsa anawo pamawondo a Isiraeli. Kenako, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.

13 Ndiyeno Yosefe anatenga ana ake awiriwo. Efuraimu+ anamuika kudzanja lake lamanja, kumanzere kwa Isiraeli. Ndipo Manase+ anamuika kudzanja lake lamanzere, kudzanja lamanja la Isiraeli. Atatero, anawabweretsa pafupi ndi bambo ake. 14 Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja nʼkuliika pamutu pa Efuraimu, ngakhale kuti ndi amene anali wamngʼono. Anatambasulanso dzanja lake lamanzere nʼkuliika pamutu pa Manase. Anasemphanitsa dala manja ake chifukwa Manase ndi amene anali mwana woyamba.+ 15 Kenako anadalitsa Yosefe kuti:+

“Mulungu woona amene makolo anga Abulahamu ndi Isaki anayenda pamaso pake,+

Mulungu woona amene wakhala mʼbusa wanga moyo wanga wonse mpaka lero,+

16 Mngelo amene wakhala akundiwombola ku masoka anga onse,+ adalitse anyamatawa.+

Anawa azidziwika ndi dzina langa komanso mayina a makolo anga, Abulahamu ndi Isaki,

Anawa adzachulukane nʼkukhala gulu la anthu ambiri padziko lapansi.”+

17 Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse. Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu nʼkuliika pamutu pa Manase. 18 Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba+ ndi uyu. Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19 Koma bambo akewo anapitiriza kukana nʼkunena kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu. Koma mngʼono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri nʼkupanga mitundu ya anthu.”+ 20 Iye anapitiriza kuwadalitsa pa tsikulo+ kuti:

“Aisiraeli akamadalitsana azidzatchula dzina lako kuti,

‘Mulungu akudalitse ngati mmene anadalitsira Efuraimu ndi Manase.’”

Choncho Isiraeli anapitiriza kuika Efuraimu patsogolo pa Manase.

21 Kenako Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Taona, inetu ndikufa.+ Koma Mulungu adzakhalabe nanu ndithu anthu inu, ndipo adzakubwezerani kudziko la makolo anu.+ 22 Koma ine ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako, limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa komanso uta wanga.”

49 Kenako Yakobo anaitana ana ake nʼkuwauza kuti: “Sonkhanani pamodzi kuti ndikuuzeni zimene zidzachitike kwa inu mʼtsogolo.* 2 Bwerani nonse kuti mumvetsere, inu ana a Yakobo. Bwerani mumvetsere kwa Isiraeli bambo anu.

3 Rubeni,+ iwe ndi mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka. Unayenera kukhala ndi ulemu waukulu ndi mphamvu zochuluka. 4 Koma sudzakhala wapamwamba kuposa abale ako, chifukwa mofanana ndi madzi osefukira unalephera kudziletsa, ndipo unakwera pogona pa bambo ako.+ Pa nthawiyo unadetsa* bedi langa. Anagonapo ndithu ameneyu!

5 Simiyoni ndi Levi mʼpachibale.+ Malupanga awo ndi zida zochitira zachiwawa.+ 6 Iwe moyo wanga, usakhale nawo pagulu lawo. Iwe mtima wanga,* usagwirizane ndi mpingo wawo, chifukwa atakwiya anapha anthu,+ ndipo anapundula* ngʼombe zamphongo pofuna kusangalala. 7 Mkwiyo wawo ukhale wotembereredwa chifukwa ndi wankhanza, komanso ukali wawo chifukwa umachita zinthu mwachiwawa.+ Ndidzawamwaza mwa Yakobo, ndipo ndidzawabalalitsa mwa Isiraeli.+

8 Koma iwe Yuda,+ abale ako adzakutamanda.+ Dzanja lako lidzakhala pakhosi la adani ako.+ Ana a bambo ako adzakuweramira.+ 9 Yuda ndi mwana wa mkango.+ Mwana wanga, ukadzadya nyama imene wapha udzachokapo. Iye wapinda mawondo ake nʼkudziwongola ngati mkango umene wagona pansi. Ndipo mofanana ndi mkango, ndi ndani amene angamudzutse? 10 Ndodo yachifumu sidzachoka kwa Yuda,+ ndiponso chibonga cha wolamulira sichidzachoka pakati pa mapazi ake, mpaka Silo* atabwera.+ Ndipo mitundu ya anthu idzamumvera.+ 11 Atamanga bulu wake pamtengo wa mpesa ndi kamwana ka bulu wake pamtengo wa mpesa wabwino, adzachapa zovala zake muvinyo komanso malaya ake mʼmadzi ofiira a mphesa. 12 Maso ake ndi ofiira chifukwa cha vinyo, ndipo mano ake ndi oyera chifukwa cha mkaka.

13 Zebuloni+ adzakhala mʼmbali mwa nyanja, adzakhala pafupi ndi doko pamene pamaima sitima.+ Malire ake akutali adzakhala cha ku Sidoni.+

14 Isakara+ ndi bulu wa mafupa olimba. Amagona pansi kuti apume, atanyamula matumba awiri a katundu. 15 Adzaona kuti malo opumirawo ndi abwino, komanso kuti dzikolo ndi losangalatsa. Adzaweramitsa phewa lake kuti anyamule katundu, ndipo adzalolera kugwira ntchito mokakamizidwa.

16 Dani+ adzaweruza anthu a mtundu wake ngati mmodzi wa mafuko a Isiraeli.+ 17 Dani adzakhala njoka yobisala mʼmbali mwa msewu, njoka yokhala ndi tinyanga yobisala mʼmphepete mwa njira, imene imaluma zidendene za hatchi ndipo wokwerapo amagwa chagada.+ 18 Ndidzayembekezera chipulumutso kuchokera kwa inu, Yehova.

19 Kunena za Gadi,+ gulu la achifwamba lidzamuukira, koma iye adzalimbana nawo, ndipo achifwambawo pothawa adzawamenya koopsa.+

20 Chakudya cha Aseri+ chidzakhala chochuluka, ndipo adzapereka chakudya choyenera mfumu.+

21 Nafitali+ ndi mbawala yaikazi yopepuka miyendo, ndipo amalankhula mawu osangalatsa.+

22 Yosefe+ ndi mphukira yamtengo wobala zipatso. Iye ndi mtengo wobala zipatso pakasupe, umene nthambi zake zimafika pamwamba pa khoma la mpanda. 23 Koma oponya mivi ndi uta sanaleke kumuzunza, kumulasa ndi kumusungira chidani.+ 24 Koma uta wake unakhalabe pamalo ake,+ ndipo manja ake anakhalabe amphamvu ndi ochenjera.+ Zimenezi zinachokera mʼmanja mwa wamphamvu wa Yakobo, zinachokera kwa mʼbusa, mwala wa Isiraeli. 25 Iye* ndi wochokera kwa Mulungu wa bambo ako ndipo adzakuthandiza. Iye ali ndi Wamphamvuyonse, ndipo Mulunguyo adzakudalitsa pokupatsa madzi ochokera kumwamba ndi pansi pa nthaka.+ Adzakudalitsa pokupatsa ana ndi ziweto zambiri.* 26 Madalitso a bambo ako adzaposa madalitso a mapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale. Adzaposanso zinthu zosiririka za zitunda zosatha.+ Madalitsowo adzapitiriza kukhala pamutu pa Yosefe, paliwombo pa wosankhidwa pakati pa abale ake.+

27 Benjamini+ adzapitiriza kukhadzula ngati mmbulu.+ Mʼmawa adzadya nyama imene wagwira, ndipo madzulo adzagawa zinthu zimene watenga atagonjetsa adani ake.”+

28 Onsewa ndi mafuko 12 a Isiraeli, ndipo zimenezi ndi zimene bambo awo anawauza pamene ankawadalitsa. Aliyense anamupatsa madalitso omuyenerera.+

29 Atatero anawalamula kuti: “Ine uno ndi ulendo wopita kumene kunapita makolo anga.*+ Mukandiike limodzi ndi makolo anga, mʼphanga limene lili mʼmunda wa Efuroni, Muhiti.+ 30 Ndithu mukandiike mʼphanga limene lili mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure, mʼdziko la Kanani. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda. 31 Kumeneko nʼkumene anaika Abulahamu ndi mkazi wake Sara.+ Nʼkumene anaika Isaki+ ndi mkazi wake Rabeka, ndipo nʼkumenenso ndinaika Leya. 32 Mundawo ndiponso phanga limene lili mmenemo, anagula kwa ana a Heti.”+

33 Yakobo atamaliza kupereka malangizo kwa ana akewo, anabwezeranso miyendo yake pabedi, nʼkumwalira. Kenako anaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake.*+

50 Choncho Yosefe anakumbatira bambo ake+ ndipo analira kwambiri nʼkuwakisa.* 2 Kenako Yosefe analamula atumiki ake omwe anali madokotala, kuti akonze mtembo wa bambo ake ndi mankhwala kuti usawonongeke.+ Choncho madokotalawo anakonza mtembo wa Isiraeli. 3 Anatenga masiku 40 akukonza thupi lake, chifukwa kukonza mtembo kunkatenga masiku ochuluka choncho. Aiguputowo anapitiriza kumulira Isiraeli kwa masiku 70.

4 Masiku olira maliro a Yakobo atatha, Yosefe anauza nduna* za Farao kuti: “Ngati mungandikomere mtima, chonde mukandiperekere uthenga uwu kwa Farao: 5 ‘Bambo anga anandilumbiritsa+ kuti: “Inetu ndikufa.+ Ukandiike mʼmanda amene ndinakonza+ mʼphanga kudziko la Kanani.”+ Ndiye chonde, ndiloleni ndipite ndikaike bambo anga, pambuyo pake ndikabweranso.’” 6 Farao anayankha kuti: “Pita ukaike bambo ako mogwirizana ndi mmene anakulumbiritsira.”+

7 Choncho Yosefe anapita kukaika bambo ake. Atumiki onse a Farao, akuluakulu+ amʼnyumba yake ndi akuluakulu onse amʼdziko la Iguputo anamuperekeza. 8 Anthu onse amʼnyumba ya Yosefe, abale ake, ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake, anapita naye limodzi.+ Ku Goseni kunangotsala ana awo aangʼono, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zawo. 9 Anatenganso magaleta+ ndi anthu okwera mahatchi, moti gululo linali lalikulu kwambiri. 10 Kenako anafika pamalo opunthira mbewu a Atadi mʼchigawo cha Yorodano. Kumeneko, anthuwo analira mokweza kwambiri, ndipo Yosefe analira maliro a bambo ake kwa masiku 7. 11 Akanani amene ankakhala mʼdzikolo anaona anthuwo akulira pamalo opunthira mbewu a Atadi, ndipo anati: “Aiguputowa ali pa chisoni chachikulu kwambiri!” Nʼchifukwa chake malowo anawatchula kuti Abele-miziraimu,* ndipo ali mʼchigawo cha Yorodano.

12 Choncho ana a Yakobowo anamuchitira zonse zimene iye anawalamula.+ 13 Ana akewo anamunyamula nʼkupita naye kudziko la Kanani ndipo anakamuika mʼphanga mʼmunda wa Makipela, umene uli moyangʼanizana ndi munda wa Mamure. Mundawo ndi umene Abulahamu anagula kwa Efuroni, Muhiti, kuti akhale manda.+ 14 Yosefe ataika bambo ake mʼmanda, anabwerera ku Iguputo limodzi ndi abale ake ndi onse amene anamuperekeza pokaika bambo akewo.

15 Abale ake a Yosefe ataona kuti bambo awo amwalira, ananena kuti: “Mwina Yosefe anatisungira chidani, ndipo atibwezera zoipa zonse zimene tinamuchitira.”+ 16 Choncho iwo anatumiza uthenga kwa Yosefe wakuti: “Bambo anu asanamwalire anatisiyira mawu. Anatiuza kuti: 17 ‘Mukamuuze Yosefe kuti: “Mwana wanga, zimene abale ako anakuchitira si zabwino. Koma ndikukupempha kuti uwakhululukire zonse zimene anakuchitira.”’ Ndiye chonde, tikhululukireni ife akapolo a Mulungu wa bambo anu.” Atamuuza zimenezi, Yosefe analira kwambiri. 18 Kenako abale akewonso anafika nʼkudzigwetsa pansi pamaso pake, ndipo ananena kuti: “Tikudzipereka kwa inu ngati akapolo anu.”+ 19 Yosefe anawauza kuti: “Musaope. Kodi ine ndatenga malo a Mulungu? 20 Ngakhale kuti munali ndi cholinga chondichitira zoipa,+ Mulungu anali ndi cholinga chabwino, kuti apulumutse miyoyo ya anthu ambiri ngati mmene akuchitira panomu.+ 21 Ndiye musachite mantha. Ine ndipitiriza kukupatsani chakudya limodzi ndi ana anu.”+ Choncho anawalimbikitsa komanso kuwatsimikizira zimenezi.

22 Yosefe anapitiriza kukhala ku Iguputo limodzi ndi anthu amʼnyumba ya bambo ake, ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka 110. 23 Yosefe anakhalabe ndi moyo mpaka kuona ana a Efuraimu+ amʼbadwo wachitatu. Anaonanso ana a Makiri+ mwana wa Manase. Onsewo anabadwira pamawondo a Yosefe.* 24 Potsirizira pake, Yosefe anauza abale ake kuti: “Ine ndikufa, koma Mulungu adzakuthandizani+ ndipo adzakutulutsani ndithu mʼdziko lino. Adzakupititsani kudziko limene analumbira kuti adzalipereka kwa Abulahamu, kwa Isaki ndi kwa Yakobo.”+ 25 Tsopano Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeliwo kuti: “Ndithu Mulungu adzakuthandizani. Choncho mudzatenge mafupa anga pochoka kuno.”+ 26 Yosefe anamwalira ali ndi zaka 110. Thupi lake analikonza ndi mankhwala kuti lisawonongeke,+ ndipo analiika mʼbokosi ku Iguputo.

Kapena kuti, “Mzimu wa Mulungu unkayendayenda.”

Kapena kuti, “chizilamulira.”

Kapena kuti, “chizilamulira.”

Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “nyama zokwawa” amatanthauza zamoyo zimene zimayenda chokwawa monga nyama zingʼonozingʼono, mbewa, abuluzi, njoka, ndi tizilombo tina tingʼonotingʼono.

Malo oyamba kupezeka dzina lenileni la Mulungu, יהוה (YHWH). Onani Zakumapeto A4.

Zikuoneka kuti madzi ankasanduka nthunzi nʼkukwera mʼmwamba ndipo zikatero nthunziyo inkasandukanso madzi omwe ankanyowetsa nthaka.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera kufumbi.”

Kapena kuti, “Tigirisi.”

Kapena kuti, “nʼkukhalabe ndi mkazi wake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.” Mawuwa mʼChiheberi angatanthauze mbewu zambiri kapena imodzi.

Kutanthauza kuti “Munthu Wochokera Kufumbi; Mtundu wa Anthu.”

Dzina limeneli limatanthauza “Wamoyo.”

Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.

Kutanthauza kuti, “Woberekedwa.”

Nʼkutheka kuti chizindikiro chimenechi linali lamulo lochenjeza anthu.

Mawu akuti, “kudera la Nodi” amatanthauza kuti kudera la anthu othawa kwawo.

Kutanthauza, “Wosankhidwa; Kuika; Kukhazikitsa.”

Kapena kuti, “Mulungu wandisankhira.”

MʼBaibulo mawu akuti tsiku amanena za nthawi yotalika mosiyanasiyana, osati ya maola 24 yokha.

Kapena kuti, “mtundu wa anthu.”

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza kuti “Mpumulo; Kutonthoza.”

Mawu okuluwika a Chiheberi amene akunena za angelo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga supitiriza.”

Zaka 120 zimenezi zinkaimira zaka zimene zinatsala kuti anthu oipa awonongedwe ndi chigumula.

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Ogwetsa” kutanthauza amene amagwetsa anthu ena. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 300.” Onani Zakumapeto B14.

Mawu a Chiheberi ndi “tsoʹhar.” Anthu ena amaona kuti mawuwa akutanthauza denga lokhala ndi mpata wa masentimita 44 ndi hafu, osati bowo kapena windo loti kuwala kuzilowa.

Kapena kuti, “mzimu wa moyo.”

Mabaibulo ena amati, “utengepo 7 zazimuna komanso 7 zazikazi.”

Mabaibulo ena amati, “utengepo 7 zazimuna komanso 7 zazikazi.”

“Mwezi wachiwiri” umene ukutchulidwa mʼvesili unadzakhala mwezi wa 8 pakalendala yopatulika imene Yehova anapatsa Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo. Mwezi umenewu, wotchedwa Buli, unkayambira chapakati pa October nʼkutha chapakati pa November. Onani Zakumapeto B15.

Onani mawu amʼmunsi pa Ge 1:24.

Kapena kuti, “mzimu wa moyo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 15.” Onani zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “fungo lokhazika mtima pansi.”

Kapena kuti, “ndakupatsani kuti muzizilamulira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense amene adzakhetse magazi anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu.”

Kapena kuti, “Mizinda yoyambirira ya ufumu wake inali.”

Zikuoneka kuti mizinda ya Nineve, Rehoboti-iri, Kala komanso Resene, yonse pamodzi ankaiona kuti ndi mzinda umodzi waukulu.

Mawu a Chiheberi amasonyeza kuti nʼkutheka kuti Semu ndi amene anali wamkulu kwa Yafeti.

Dzina lakuti “Pelegi” limatanthauza “Kugawika.”

Kapena kuti, “anthu okhala padziko lapansi anagawanika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tiyeni titsikire kumeneko ndi kukasokoneza chilankhulo chawo.”

Kutanthauza kuti, “Chisokonezo.”

Kapena kuti, “adzapeza madalitso.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “kukakhala kumeneko ngati mlendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”

Yomwe ndi Nyanja Yakufa.

Kapena kuti, “akukhala mʼmatenti.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzapita kwa makolo ako.”

Kapena kuti, “chifukwa tchimo la Aamori silinafike poti alangidwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kutanthauza kuti, “Mulungu Amamva.”

Anthu ena amaganiza kuti bulu wamʼtchireyu anali mbidzi mwina chifukwa chakuti imakonda kuchita zinthu payokha osati limodzi ndi nyama zina.

Mabaibulo ena amati, “azidzachitira nkhanza abale ake onse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anaitanira pa dzina la Yehova.”

Kutanthauza kuti, “Chitsime cha Wamoyo Amene Amatha Kundiona.”

Kutanthauza kuti, “Atate Ndi Wapamwamba (Ndi Wokwezeka).”

Kutanthauza kuti, “Tate wa Anthu Ambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.” MʼChiheberi mawu akuti “mbadwa zako” akunena za mbadwa imodzi koma angaimirenso gulu la anthu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Muzichita mdulidwe wa khungu lanu lakunsonga.”

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Wolongolola.”

Kutanthauza kuti, “Mfumukazi.”

Kutanthauza kuti, “Kuseka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “muyezo wa seya.” Muyezo wa seya unali wokwana malita 7.33. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “onse a mʼnyumba yake.”

Kapena kuti, “chikondi chokhulupirika.”

Kutanthauza kuti, “Kuchepa.”

Kapena kuti, “Pamene ankakhala monga mlendo.”

Mwina limeneli linali dzina laudindo.

Kapena kuti, “wolungama.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “aseka limodzi ndi ine.” Mabaibulo ena amati, “andiseka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mvera mawu ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Chitsime cha Lumbiro” kapena “Chitsime cha 7.”

Kapena kuti, “anakhala monga mlendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”

Kapena kuti, “mpeni wophera nyama.”

Kutanthauza kuti, “Yehova Adzapereka,” kapena kuti, “Yehova Adziwa Chochita.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “geti la mzinda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mabaibulo ena amati, “mtsogoleri wamkulu.”

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti nditembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.”

Kapena kuti, “sitingathe kulankhula zoipa kapena zabwino kwa inu.”

Mlezi ndi wantchito wamkazi amene amalera mwana. Choncho mlezi wa Rabekayu anamulera ali mwana, ndipo atakula mleziyu anakhala mtumiki wake.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo anagona limodzi ndi makolo ake.”

Kapena kuti, “misasa yawo yokhala ndi mpanda.”

Mabaibulo ena amati, “Ankachitira nkhanza abale awo onse.”

Kutanthauza kuti, “Wacheya.”

Kutanthauza kuti, “Wogwira Chidendene; Wochenjerera Ena.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chofiiracho, icho chofiiracho.”

Kapena kuti, “ndili ndi njalatu ine.”

Kutanthauza, “Wofiira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “akukumbatira mkazi wake.”

Kapena kuti, “mʼkhwawa la.”

Kapena kuti, “mʼkhwawamo.”

Kutanthauza, “Mkangano.”

Kutanthauza, “Kuimba Mlandu.”

Kutanthauza, “Malo Aakulu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kutanthauza, “Lumbiro” kapena “7.”

“Cheya” ndi ubweya wa pathupi la munthu.

Kapena kuti, “undipsompsone.”

Kutanthauza, “Wogwira Chidendene; Wochenjerera Ena.”

Kapena kuti, “Mʼbale wako Esau akudzilimbitsa mtima ndi maganizo ofuna kukupha.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Pavesili, mawu akuti “Isimaeli” akutanthauza “Aisimaeli.” Pa nthawiyi Isimaeli anali atamwalira kale ndipo Esau anali ndi zaka pafupifupi 77. Onani Ge 25:17, 26.

Kapena kuti, “makwerero.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kutanthauza, “Nyumba ya Mulungu.”

Kapena kuti, “anapsompsona.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “fupa langa ndi mnofu wanga.”

Kapena kuti, “kuti ndigone naye.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ankadedwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anatsegula mimba yake.”

Kutanthauza, “Onani, ndi Mwana Wamwamuna!”

Kutanthauza, “Wandimvera.”

Kutanthauza, “Kuphatikizana; Kulumikizana.”

Kutanthauza, “Kutamandidwa; Wotamandika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “aberekere pamawondo anga.”

Kutanthauza, “Woweruza.”

Kutanthauza, “Ndalimbana Nazo.”

Kutanthauza, “Mwayi.”

Kutanthauza, “Kusangalala; Chisangalalo.”

“Mandereki” ndi chomera cha mʼgulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso ndipo azimayi ankadya zipatso zimenezi chifukwa ankakhulupirira kuti akadya ziwathandiza kuti akhale oyembekezera.

Kapena kuti, “malipiro a munthu waganyu.”

Kutanthauza, “Iye Ndi Malipiro.”

Kutanthauza, “Kulolera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkutsegula mimba yake.”

Chidule cha dzina lakuti Yosifiya limene limatanthauza kuti “Ya Awonjezere (Achulukitse).”

Kapena kuti, “Ndapeza umboni wosonyeza kuti.”

Kapena kuti, “kuona mtima kwanga.”

Kapena kuti, “milungu ya banja ya; mafano.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “achibale ake.”

Kapena kuti, “ndipsompsone.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga aamuna.”

Mawu a Chiaramu otanthauza, “Mulu wa Umboni.”

Mawu a Chiheberi otanthauza, “Mulu wa Umboni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale kuti palibe munthu pano.”

Kutanthauza, “ana aamuna.”

Kutanthauza, “Magulu Awiri.”

Kapena kuti, “Ndakhala ndi Labani ngati mlendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “chigwacho; khwawalo.”

Kutanthauza, “Wolimbana ndi Mulungu” kapena “Mulungu Walimbana Naye.”

Kutanthauza, “Nkhope ya Mulungu.”

Kapena kuti, “Penieli.”

Kapena kuti, “kumupsompsona.”

Kutanthauza, “Makola; Makola Adenga.”

Kapena kuti, “kukaona.”

Kapena kuti, “anabisa.”

Kutanthauza, “Mulungu wa ku Beteli.”

Mlezi ndi wantchito wamkazi amene amalera mwana.

Kutanthauza, “Mtengo Waukulu Wolirirapo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana amene adzatuluke mʼchiuno mwako adzakhala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

“Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutchula kuti “namwino.”

Kutanthauza, “Mwana wa Chisoni Changa.”

Kutanthauza, “Mwana wa Dzanja Langa Lamanja.”

“Mkazi wamngʼono” ameneyu anali kapolo wa Rakele.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”

Kapena kuti, “ankakhalamo monga alendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Mʼchilankhulo choyambirira, “thupi limodzi.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kutanthauza “Kungʼamba,” mwina kutanthauza kungʼambika kwa njira yotulukira mwana pobadwa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “atukula mutu wako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchitsime; mʼdzenje.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuzula mutu wako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anatukula mutu wa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchitsimemo; mʼdzenjemo.”

Galeta limeneli linali la munthu amene anali wachiwiri kwa Farao.

Zikuoneka kuti mawuwa ndi ouza anthu kuti apereke ulemu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene anganyamule dzanja lake kapena phazi lake.”

Zikuoneka kuti mʼChiheberi, dzinali limatanthauza “Woulula Zinthu Zobisika.”

Amene ndi Heliyopolisi.

Kapena kuti, “kuyendera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene anaima pamaso pa.”

Kutanthauza, “Wochititsa Kuiwala; Woiwalitsa.”

Kutanthauza, “Kubereka Kawiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “musamuchimwire.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musadzaonenso nkhope yanga.”

Kapena kuti, “Ndikhala chikole cha moyo wake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “woyamba kubadwa mogwirizana ndi ukulu wake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musadzaonenso nkhope yanga.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “nʼcholinga choti pakhale otsalira a anthu inu padziko lapansi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “tate wa.”

Amene ndi Heliyopolisi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana a.” Nʼkutheka kuti panali ana ena aamuna amene mayina awo sanatchulidwe.

Kapena kuti, “nʼkulira mobwerezabwereza.”

Kapena kuti, “ndakhala ngati mlendo.”

Zikuoneka kuti Ramese chinali chigawo cha mʼdera la Goseni kapena linali dzina lina la Goseni.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndikadzagona ndi makolo anga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumapeto kwa masiku.”

Kapena kuti, “unaipitsa.”

Kapena kuti, “Iwe ulemu wanga.”

Ankazipundula podula mtsempha wakuseri kwa mwendo wamʼmbuyo.

Kutanthauza, “Amene Chili Chake; Mwini Wake.”

Kutanthauza Yosefe.

Mʼchilankhulo choyambirira, “madalitso a mabere ndi mimba.”

Awa ndi mawu okuluwika otanthauza imfa.

Awa ndi mawu okuluwika otanthauza imfa.

Kapena kuti, “nʼkuwapsompsona.”

Kapena kuti, “anthu amʼnyumba ya Farao.”

Kutanthauza, “Kulira Maliro kwa Aiguputo.”

Kutanthauza kuti, ankawaona ngati ana ake ndipo ankawakonda mwapadera.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani