Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Nehemiah 1:1-13:31
  • Nehemiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nehemiya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nehemiya

NEHEMIYA

1 Awa ndi mawu a Nehemiya*+ mwana wa Hakaliya. Mʼmwezi wa Kisilevi,* mʼchaka cha 20, ine ndinali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*+ 2 Pa nthawiyo Haneni,+ mmodzi wa abale anga, anabwera limodzi ndi amuna ena kuchokera ku Yuda. Ndinawafunsa mmene zinthu zinalili kwa Ayuda amene anathawa ku ukapolo+ komanso za Yerusalemu. 3 Iwo anandiyankha kuti: “Anthu amene anatsala mʼchigawo,* omwe anapulumuka ku ukapolo, ali pamavuto aakulu ndipo akunyozedwa.+ Nawonso mpanda wa Yerusalemu unagwa+ ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto.”+

4 Nditangomva mawu amenewa, ndinakhala pansi nʼkuyamba kulira ndipo ndinalira kwa masiku angapo, kusala kudya+ komanso kupemphera kwa Mulungu wakumwamba. 5 Ndinati: “Inu Yehova Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha. Inu mumakwaniritsa pangano lanu ndipo mumasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.+ 6 Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu limene ndikupemphera kwa inu lero. Masana ndi usiku+ ndikumapempherera atumiki anu, Aisiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza machimo a Aisiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine limodzi ndi nyumba ya bambo anga.+ 7 Tachita zinthu zolakwika pamaso panu+ ndipo sitinasunge malamulo, malangizo ndi ziweruzo zimene munapatsa mtumiki wanu Mose.+

8 Chonde, kumbukirani mawu amene munauza* mtumiki wanu Mose kuti, ‘Mukadzachita zinthu mosakhulupirika, ndidzakumwazani pakati pa anthu a mitundu ina.+ 9 Koma mukadzabwerera kwa ine nʼkumatsatira malamulo anga, ngakhale anthu a mtundu wanu atamwazikira kumalekezero akumwamba, ndidzawasonkhanitsa+ kuchokera kumeneko nʼkuwabweretsa kumalo amene ndasankha kuti kukhale dzina langa.’+ 10 Iwo ndi atumiki anu komanso anthu anu amene munawawombola ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11 Inu Yehova, chonde mvetserani pemphero la ine mtumiki wanu ndiponso pemphero la atumiki anu amene amaopa dzina lanu ndi mtima wonse. Chonde, ndithandizeni ine mtumiki wanu kuti zinthu zindiyendere bwino lero ndipo munthuyu andichitire chifundo.”+

Pa nthawiyi ndinali woperekera zakumwa kwa mfumu.+

2 Mʼmwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 20+ cha mfumu Aritasasita,+ mfumuyo inkafuna vinyo choncho ndinatenga vinyoyo nʼkukapereka kwa mfumu ngati mmene ndinkachitira nthawi zonse.+ Koma ndinali ndisanakhalepo wachisoni pamaso pake. 2 Choncho mfumu inati: “Nʼchifukwa chiyani ukuoneka wachisoni pamene sukudwala? Payenera kuti pali chinachake chimene chikukuvutitsa mumtima.” Atanena zimenezi ndinachita mantha kwambiri.

3 Kenako ndinayankha mfumuyo kuti: “Mfumu mukhale ndi moyo wautali! Ndilekerenji kuoneka wachisoni pamene mzinda umene makolo anga anaikidwako uli bwinja ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto?”+ 4 Mfumuyo inandifunsa kuti: “Ndiye ukufuna chiyani?” Nthawi yomweyo ndinapemphera kwa Mulungu wakumwamba.+ 5 Kenako ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima ine mtumiki wanu, munditumize ku Yuda, kumzinda umene makolo anga anaikidwako kuti ndikaumangenso.”+ 6 Mfumu inandiyankha kuti: “Ulendo wako udzatenga masiku angati, ndipo udzabwera liti?” Pa nthawiyi, mkazi wamkulu wa mfumu anali atakhala pambali pake. Choncho mfumu inandilola kupita+ nditaiuza nthawi.+

7 Ndiyeno ndinauza mfumu kuti: “Ngati zili bwino ndi inu mfumu, lolani kuti ndipatsidwe makalata okasonyeza kwa abwanamkubwa a tsidya lina la Mtsinje,*+ kuti akandilole kudutsa mpaka ndikafike ku Yuda. 8 Komanso andipatse kalata yopita kwa Asafu amene akuyangʼanira Nkhalango ya Mfumu, kuti akandipatse mitengo yokakonzera mageti a Nyumba ya Chitetezo Champhamvu+ yakukachisi, mpanda wa mzindawo+ ndiponso nyumba imene ndizikakhalamo.” Choncho mfumu inandipatsa makalatawo+ chifukwa Mulungu anandikomera mtima.+

9 Kenako ndinafika kwa abwanamkubwa akutsidya lina la Mtsinje nʼkuwapatsa makalata a mfumu aja. Mfumu inandipatsanso akuluakulu a asilikali komanso asilikali okwera pamahatchi* kuti andiperekeze. 10 Sanibalati wa ku Beti-horoni+ ndi Tobia,+ mtumiki wa Chiamoni,+ anakwiya kwambiri atamva zimenezi komanso ataona kuti kwabwera munthu wodzachitira Aisiraeli zinthu zabwino.

11 Patapita nthawi, ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Ndinadzuka usiku limodzi ndi amuna angapo amene ndinali nawo. Sindinauze aliyense zimene Mulungu wanga anaika mumtima mwanga zoti ndichitire Yerusalemu. Pa nthawiyo ndinalibe chiweto chilichonse kupatulapo chiweto chimene ndinakwerapo. 13 Usikuwo ndinatulukira pa Geti ya Kuchigwa+ nʼkukadutsa kutsogolo kwa Kasupe wa Chinjoka Chachikulu* mpaka ndinakafika ku Geti ya Milu ya Phulusa.+ Pa nthawiyi, ndinkaona mmene mpanda wa Yerusalemu unawonongekera ndiponso mmene moto unawonongera mageti ake.+ 14 Ndinayendabe mpaka kukafika ku Geti la Kukasupe+ ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma kunalibe njira yoti chiweto chimene ndinakwerapo chidutse. 15 Koma usikuwo ndinayendabe mʼchigwamo+ molowera kumtunda ndipo ndinapitiriza kuona mpandawo. Kenako ndinabwerera nʼkukalowanso pa Geti ya Kuchigwa.

16 Atsogoleri+ sanadziwe kumene ndinapita komanso zomwe ndinkachita chifukwa sindinanene chilichonse kwa Ayuda, ansembe, anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu ena onse ogwira ntchito. 17 Kenako ndinawauza kuti: “Inu mukuona vuto lalikulu limene tili nalo. Yerusalemu ndi bwinja ndipo mageti ake anatenthedwa ndi moto. Tiyeni timangenso mpanda wa Yerusalemu kuti anthu asiye kutinyoza.” 18 Ndinawauzanso mmene dzanja la Mulungu wanga landithandizira+ ndiponso mawu amene mfumu inandiuza.+ Pamenepo iwo anati: “Tiyeni timange mpandawo.” Choncho anadzilimbitsa* kuti agwire ntchito yabwinoyi.+

19 Ndiyeno Sanibalati wa ku Beti-horoni, Tobia+ mtumiki wa Chiamoni+ ndi Gesemu Mluya+ atamva zimenezi anayamba kutiseka ndi kutinyoza.+ Iwo anati: “Nʼchiyani chimene mukuchitachi? Kodi mukugalukira mfumu?”+ 20 Koma ine ndinawayankha kuti: “Mulungu wakumwamba ndi amene adzatithandize kuti zinthu zitiyendere bwino,+ ndipo ife atumiki ake tipitiriza kumanga mpandawu. Inuyo sizikukukhudzani komanso mulibe ufulu kapena choti nʼkukukumbukirani nacho mu Yerusalemu.”+

3 Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Geti la Nkhosa+ ndipo analiyeretsa+ nʼkuika zitseko zake. Anayeretsa chigawo chonse mpaka ku Nsanja ya Meya+ nʼkukafika ku Nsanja ya Hananeli.+ 2 Amuna a ku Yeriko+ anamanga kuyambira pamene Eliyasibu ndi abale ake analekezera. Ndipo Zakuri mwana wa Imiri, anapitiriza kuyambira pamene amuna a ku Yeriko analekezera.

3 Ana a Haseneya anamanga Geti la Nsomba.+ Iwo analipangira felemu lamatabwa+ nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. 4 Meremoti+ mwana wa Uliya, mwana wa Hakozi, anakonza mpandawo kuchokera pamene ana a Haseneya analekezera. Mesulamu+ mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele, anapitiriza kuchokera pamene Meremoti analekezera. Ndipo Zadoki mwana wa Baana, anapitiriza kuchokera pamene Mesulamu analekezera. 5 Atekowa+ anapitiriza kuchokera pamene Zadoki analekezera. Koma anthu otchuka pakati pa Atekowa sanadzichepetse nʼkugwira nawo ntchito ya atsogoleri awo.

6 Yoyada mwana wa Paseya, komanso Mesulamu mwana wa Besodeya, anakonza Geti la Mzinda Wakale.+ Iwo analipangira felemu lamatabwa nʼkuika zitseko, anamphatika* ndi mipiringidzo. 7 Kenako Melatiya wa ku Gibiyoni+ ndi Yadoni wa ku Meronoti anapitiriza kuchokera pamene Yoyada ndi Mesulamu analekezera. Amenewa anali amuna a ku Gibiyoni ndi Mizipa+ amene anali pansi pa ulamuliro wa bwanamkubwa wakutsidya la Mtsinje.*+ 8 Kenako Uziyeli mwana wa Harihaya, mmodzi wa osula golide, anakonza mpandawo kuchokera pamene analekezera. Hananiya mmodzi wa opanga mafuta onunkhira, anapitiriza kuchokera pamene Uziyeli analekezera. Iwo anayala miyala mu Yerusalemu mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 9 Refaya mwana wa Hura, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anapitiriza kuchokera pamene Hananiya analekezera. 10 Yedaya mwana wa Harumafi anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake kuchokera pamene Refaya analekezera. Kenako Hatusi mwana wa Hasabineya anapitiriza kuchokera pamene Yedaya analekezera.

11 Malikiya mwana wa Harimu+ komanso Hasubu mwana wa Pahati-mowabu,+ anakonza gawo lina la mpandawo ndi Nsanja ya Mauvuni.+ 12 Kenako Salumu mwana wa Halohesi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anapitiriza kukonza mpandawo limodzi ndi ana ake aakazi kuchokera pamene enawo anasiyira.

13 Hanuni ndi anthu a ku Zanowa+ anakonza Geti la Kuchigwa.+ Iwo analikonza nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. Anakonzanso mpandawo mikono 1,000* mpaka kukafika ku Geti la Milu ya Phulusa.+ 14 Malikiya mwana wa Rekabu, kalonga wa chigawo cha Beti-hakeremu,+ anakonza Geti la Milu ya Phulusa. Analikonza nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo.

15 Saluni mwana wa Kolihoze, kalonga wa chigawo cha Mizipa,+ anakonza Geti la Kukasupe+ nʼkukhoma denga lake. Anaikanso zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. Anamanganso mpanda wa Dziwe+ la Ngalande kukafika ku Munda wa Mfumu+ ndi ku Masitepe+ ochokera mu Mzinda wa Davide.+

16 Nehemiya mwana wa Azibuki, kalonga wa hafu ya chigawo cha Beti-zuri,+ anapitiriza kuchokera pamene Saluni analekezera. Anakafika patsogolo pa Manda Achifumu a Davide+ mpaka kudziwe+ lochita kukumba komanso ku Nyumba ya Anthu Amphamvu.

17 Alevi, moyangʼaniridwa ndi Rehumu mwana wa Bani, anakonza mpandawo kuchokera pamene Nehemiya analekezera. Hasabiya, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila,+ anakonza mpandawo mʼchigawo chake kuchokera pamene Alevi analekezera. 18 Kuchokera pamenepo, abale awo anakonza mpandawo moyangʼaniridwa ndi Bavai mwana wa Henadadi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila.

19 Ezeri mwana wa Yesuwa,+ kalonga wa Mizipa, anakonza gawo lina la mpandawo pafupi ndi chitunda chimene anthu ankadutsa popita Kosungira Zida pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe.+

20 Baruki mwana wa Zabai,+ anagwira ntchito mwachangu kwambiri moti anakonza gawo lina la mpandawo, kuchokera pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe kukafika pageti la nyumba ya Eliyasibu+ mkulu wa ansembe.

21 Meremoti+ mwana wa Uliya, mwana wa Hakozi, anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera pageti la nyumba ya Eliyasibu mpaka pamene nyumbayo inathera.

22 Ansembe, amuna amʼchigawo cha Yorodano*+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. 23 Benjamini ndi Hasubu anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yawo kuchokera pamene ansembe analekezera. Azariya mwana wa Maaseya, mwana wa Ananiya, anakonza mpandawo pafupi ndi nyumba yake kuchokera pamene Benjamini ndi Hasubu analekezera. 24 Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera panyumba ya Azariya kukafika pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe+ mpaka pakona ya mpanda wa mzindawo.

25 Palali mwana wa Uzai, anakonza mpandawo kutsogolo kwa khoma lothandizira kuti mpanda usagwe. Anakonzanso nsanja yochokera pa Nyumba ya Mfumu+ imene ili kumtunda mʼBwalo la Alonda.+ Pedaya mwana wa Parosi, anapitiriza kuchokera pamene Palali+ analekezera.

26 Atumiki apakachisi*+ omwe ankakhala ku Ofeli+ anakonza mpandawo mpaka patsogolo pa Geti la Kumadzi,+ kumʼmawa. Iwo anakonzanso nsanja yomwe inatulukira kunja kwa mpanda.

27 Atekowa+ anakonza chigawo chinanso cha mpandawo, kuchokera patsogolo pa nsanja yomwe inatulukira kunja kwa mpanda kukafika kumpanda wa Ofeli.

28 Ansembe anakonza mpandawo kuyambira kumtunda kwa Geti ya Hatchi,+ ndipo aliyense ankakonza patsogolo pa nyumba yake.

29 Zadoki+ mwana wa Imeri anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake.

Semaya mwana wa Sekaniya, woyangʼanira Geti ya Kumʼmawa,+ anapitiriza kuchokera pamene Zadoki analekezera.

30 Hananiya mwana wa Selemiya ndi Hanuni mwana wa 6 wa Zalafi, anakonzanso chigawo china cha mpanda.

Mesulamu+ mwana wa Berekiya, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake kuchokera pamene Hananiya analekezera.

31 Malikiya amene anali mʼgulu la osula golide, anakonza mpandawo kukafika kunyumba ya atumiki apakachisi*+ ndi amalonda, kutsogolo kwa Geti la Kufufuza mpaka pachipinda chapadenga chapakona.

32 Osula golide ndi amalonda anakonza mpandawo kuyambira pachipinda chapadenga chapakona kukafika pa Geti la Nkhosa.+

4 Sanibalati+ atangomva kuti tikumanganso mpanda, anakwiya ndiponso anapsa mtima kwambiri moti anapitiriza kunyoza Ayuda. 2 Iye anauza abale ake komanso asilikali a ku Samariya kuti: “Kodi Ayuda ofookawa akuchita chiyani? Kodi akuona ngati angaikwanitse ntchito imeneyi? Kodi adzapereka nsembe? Kodi amaliza kumangako tsiku limodzi? Kodi afukula miyala imene inatenthedwa nʼkukwiririka ndi dothi kuti aigwiritsenso ntchito?”+

3 Tobia+ Muamoni,+ yemwe anaima pambali pake anati: “Ngakhaletu nkhandwe itakwera pampanda wamiyala umene akumangawo ikhoza kuugwetsa.”

4 Nehemiya anati: “Inu Mulungu wathu, onani mmene akutinyozera.+ Abwezereni chipongwe chawo+ ndipo lolani kuti atengedwe ngati katundu kupita ku ukapolo. 5 Musanyalanyaze zolakwa zawo+ kapena kufufuta machimo awo chifukwa anyoza anthu omanga mpanda.”

6 Choncho tinapitiriza kumanga mpandawo moti khoma lonse linalumikizana ndipo linafika hafu kupita mʼmwamba. Anthu anapitiriza kugwira ntchitoyo ndi mtima wonse.

7 Sanibalati, Tobia,+ Aluya,+ Aamoni ndi Aasidodi+ atamva kuti ntchito yokonza mpanda wa Yerusalemu ikuyenda bwino ndipo malo ogumuka ayamba kutsekedwa, anakwiya kwambiri. 8 Choncho anakonza chiwembu kuti abwere kudzamenyana ndi Yerusalemu nʼkusokoneza ntchito yathu. 9 Koma ife tinapemphera kwa Mulungu wathu ndipo tinaika alonda kuti azititeteza masana ndi usiku.

10 Koma anthu a ku Yuda anayamba kunena kuti: “Mphamvu za anthu ogwira ntchito zatha, koma pali zinthu zambiri zofunika kuchotsa, ndipo sitingathe kumanga mpandawu.”

11 Adani athu ankanena kuti: “Adzangozindikira tafika ndipo tidzawapha nʼkuimitsa ntchito yomangayo.”

12 Ayuda okhala pafupi ndi adaniwo anabwera nʼkutiuza mobwerezabwereza* kuti: “Adaniwo adzatiukira kuchokera kumbali zonse.”

13 Choncho ndinaika amuna kuseri kwa mpanda pamalo otsika omwe anali poonekera. Ndinawaika mogwirizana ndi mabanja awo atanyamula malupanga, mikondo ingʼonoingʼono ndi mauta. 14 Nditaona kuti akuchita mantha, nthawi yomweyo ndinanyamuka nʼkuuza anthu olemekezeka,+ atsogoleri ndiponso anthu onse kuti: “Musachite nawo mantha.+ Kumbukirani Yehova yemwe ndi Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha.+ Menyani nkhondo kuti muteteze abale anu, ana anu aamuna, ana anu aakazi, akazi anu komanso nyumba zanu.”

15 Adani athuwo atamva zoti tadziwa za chiwembu chawo ndipo Mulungu woona wasokoneza mapulani awo, tonse tinayambiranso kumanga mpanda. 16 Kungochokera tsiku limenelo, hafu ya anyamata anga ankagwira ntchito+ ndipo hafu inayo ankanyamula mikondo ingʼonoingʼono, zishango, mauta ndipo ankavala zovala za mamba achitsulo. Akalonga ankathandiza*+ anthu onse amʼnyumba ya Yuda 17 amene ankamanga mpandawo. Anthu amene ankanyamula zinthu ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi ndipo kudzanja linalo ankanyamula chida. 18 Aliyense amene ankamanga, anali atamangirira lupanga mʼchiuno ndipo woliza lipenga la nyanga+ ya nkhosa anaima pafupi ndi ine.

19 Kenako ndinauza anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu ena onse kuti: “Ntchitoyi ndi yaikulu ndipo tikumakhala motalikirana kuzungulira mpandawu. 20 Ndiye mukamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, muzibwera kumene tili ndipo Mulungu wathu atimenyera nkhondo.”+

21 Choncho tinkagwira ntchito uku hafu ina itanyamula mikondo ingʼonoingʼono, kuyambira mʼbandakucha mpaka usiku nyenyezi zitatuluka. 22 Pa nthawiyo ndinauza anthu kuti: “Mwamuna aliyense limodzi ndi wantchito wake azigona mu Yerusalemu ndipo usiku azikhala alonda athu koma masana azigwira ntchito.” 23 Choncho ine, abale anga, atumiki anga+ ndi alonda amene ankanditsatira, sitinkasintha zovala ndipo aliyense ankanyamula mkondo mʼdzanja lake lamanja.

5 Koma panali amuna ena pamodzi ndi akazi awo amene anayamba kuwadandaula kwambiri Ayuda anzawo.+ 2 Ena ankanena kuti: “Ife ndi ana athu aamuna komanso aakazi tilipo ambiri. Tiyenera kupeza chakudya kuti tikhale ndi moyo.” 3 Ndipo ena ankanena kuti: “Nthawi ya njala, tikumapereka minda yathu ya tirigu, minda yathu ya mpesa ndi nyumba zathu monga chikole kuti tipeze chakudya.” 4 Enanso ankanena kuti: “Ife takongola ndalama kuti tikhome msonkho kwa mfumu wa minda yathu ya tirigu ndi ya mpesa.+ 5 Komatu ife ndi anzathuwo ndife pachibale ndipo ana athu nʼchimodzimodzi ndi ana awo, koma ife tikufunika kusandutsa ana athu aamuna ndi aakazi kukhala akapolo. Ndipo ana athu ena aakazi tawasandutsa kale akapolo.+ Tilibe mphamvu zoti nʼkuletsa zimenezi chifukwa minda yathu ya tirigu ndi ya mpesa ili mʼmanja mwa anthu ena.”

6 Nditamva kudandaula kwawo komanso mawu awowa, ndinakwiya kwambiri. 7 Choncho ndinayamba kuganizira zimenezi mumtima mwanga ndipo ndinapeza kuti anthu olemekezeka ndi atsogoleri anali olakwa. Ndiyeno ndinawauza kuti: “Nonsenu mukuumiriza abale anu kuti akupatseni chiwongoladzanja.”+

Komanso ndinaitanitsa msonkhano waukulu chifukwa cha iwowa. 8 Ndipo ndinawauza kuti: “Ife tayesetsa kuwombola abale athu a Chiyuda amene anagulitsidwa kwa anthu a mitundu ina. Ndiye inu mukugulitsa abale anu+ ndipo mufuna kuti ife tiwawombole?” Atamva zimenezi anangokhala chete, kusowa chonena. 9 Ndiyeno ndinati: “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi simuyenera kuyenda moopa Mulungu+ kuti adani athu, anthu a mitundu ina, asamatinyoze? 10 Ndiponso ine, abale anga ndi atumiki anga, tikuwakongoza abale athu ndalama ndi chakudya. Chonde, tiyeni tisiye kulandira chiwongoladzanja tikakongoza zinthu.+ 11 Chonde, lero abwezereni minda yawo+ ya tirigu, ya mpesa, ya maolivi, nyumba zawo ndiponso gawo limodzi pa magawo 100 a ndalama, tirigu, vinyo watsopano komanso mafuta zimene munawauza kuti azikupatsani ngati chiwongoladzanja.”

12 Atamva zimenezi anati: “Tiwabwezera ndipo sitiwauzanso kuti atipatse kenakake. Tichita ndendende mmene mwanenera.” Choncho ndinaitana ansembe nʼkulumbiritsa anthuwo kuti achite zimene alonjeza. 13 Komanso ndinakutumula zovala zanga nʼkunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Mulungu woona akutumule munthu amene sachita zimene walonjeza nʼkumuchotsa mʼnyumba yake ndi pa zinthu zake zonse. Akutumulidwe chonchi nʼkukhala wopanda kanthu.” Ndiyeno gulu lonse la anthulo linati: “Ame!”* Anthuwo anatamanda Yehova ndipo anachita zimene analonjezazo.

14 Komanso kwa zaka 12, kuchokera tsiku limene ndinaikidwa kukhala bwanamkubwa wawo+ mʼdziko la Yuda, kuyambira chaka cha 20+ mpaka chaka cha 32+ cha mfumu Aritasasita,+ ine ndi abale anga sitinadye chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa.+ 15 Abwanamkubwa amene analipo ine ndisanakhale, ankalemetsa anthu ndipo tsiku lililonse ankalandira masekeli* 40 asiliva ogulira chakudya ndi vinyo. Komanso atumiki awo ankapondereza anthu. Koma ine sindinachite zimenezo+ chifukwa choopa Mulungu.+

16 Kuwonjezera pamenepo, ndinagwira nawo ntchito yomanga mpandawo ndipo sitinakhale ndi minda.+ Atumiki anga onse anasonkhana kumeneko kuti agwire ntchito. 17 Panali Ayuda ndi atsogoleri okwana 150 amene ankadya nane limodzi komanso anthu a mitundu ina amene anabwera. 18 Ndinauza anthu kuti tsiku lililonse azipha ngʼombe imodzi yamphongo, nkhosa zabwino kwambiri zokwana 6 ndiponso mbalame, ndipo pakatha masiku 10 tinkakhala ndi vinyo wambiri wamtundu uliwonse. Koma sindinapemphe kuti andipatse chakudya choyenera kuperekedwa kwa bwanamkubwa chifukwa anthuwa ankagwira kale ntchito yolemetsa. 19 Mulungu wanga, mundikumbukire pa zonse* zimene ndachitira anthuwa.+

6 Ndiyeno Sanibalati,+ Tobia, Gesemu Muluya+ komanso adani athu onse atangouzidwa kuti ndamanganso mpanda,+ ndipo ndatseka mipata yonse (ngakhale kuti pa nthawiyo ndinali ndisanaike zitseko mʼmageti),+ 2 nthawi yomweyo Sanibalati ndi Gesemu ananditumizira uthenga wakuti: “Bwera tidzapangane nthawi yoti tikakumane mʼmudzi wina mʼchigwa cha Ono.”+ Koma ankandikonzera chiwembu. 3 Choncho ndinatumiza anthu kuti akawauze kuti: “Ntchito imene ndikugwirayi ndi yaikulu ndipo sindingathe kubwera. Kodi ntchitoyi iime chifukwa chakuti ine ndabwera kumeneko?” 4 Koma iwo ananditumizira uthenga womwewo maulendo 4, ndipo ine ndinkawayankha chimodzimodzi.

5 Kenako Sanibalati ananditumizira uthenga womwewo ulendo wa 5 kudzera mwa mtumiki wake. Mtumikiyo anali ndi kalata yosatseka mʼmanja mwake. 6 Mʼkalatayo analembamo kuti: “Pali mphekesera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo Gesemu+ akunenanso zomwezo, kuti iwe ndi Ayuda mukufuna kupanduka.+ Nʼchifukwa chake ukumanga mpandawo ndipo mogwirizana ndi zimene anthu akunenazi, iweyo ukufuna kukhala mfumu yawo. 7 Komanso waika aneneri kuti azilengeza za iwe mu Yerusalemu monse kuti, ‘Dziko la Yuda lili ndi mfumu!’ Mfumu ikhoza kumva mphekesera zimenezi. Choncho bwera tidzakambirane.”

8 Koma ine ndinamutumizira uthenga wakuti: “Palibe amene wachita zimene ukunenazi, koma wangozipeka mumtima mwako.” 9 Onsewo ankangofuna kutichititsa mantha, ndipo ankanena kuti: “Manja awo afooka ndipo asiya kugwira ntchitoyi, moti siitha.”+ Inu Mulungu wanga, limbitsani manja anga.+

10 Kenako ndinapita kunyumba kwa Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene anali atadzitsekera mʼnyumba. Iye anandiuza kuti: “Tiye tigwirizane nthawi yoti tikakumane kunyumba ya Mulungu woona, mʼkachisi ndipo tikatseke zitseko za kachisiyo. Chifukwa akubwera kudzakupha, akubwera kudzakupha usiku.” 11 Koma ndinamuyankha kuti: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe? Kodi munthu ngati ine angalowe mʼkachisi nʼkukhala ndi moyo?+ Ine sindikalowamo!” 12 Kenako ndinazindikira kuti sanatumidwe ndi Mulungu, koma Tobia ndi Sanibalati+ ndi amene anamulemba ganyu kuti andinamize ndi ulosi wabodzawu. 13 Iwo anamulemba ganyu kuti andiopseze komanso kuti ndichite tchimo nʼcholinga choti apeze zifukwa zondiipitsira mbiri kuti azindinyoza.

14 Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobia+ ndi Sanibalati komanso zimene anachitazi. Mukumbukirenso Nowadiya mneneri wamkazi ndi aneneri onse amene ankafuna kundiopseza.

15 Choncho ntchito yomanga mpanda inatha pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli* ndipo inatenga masiku 52.

16 Adani athu onse atangomva zimenezi komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi kwambiri+ ndipo anazindikira kuti ntchitoyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu. 17 Mʼmasiku amenewo, anthu olemekezeka+ a mu Yuda ankalemba makalata ambiri opita kwa Tobia ndipo Tobiayo ankawayankha. 18 Anthu ambiri mu Yuda anamulumbirira kuti akhala kumbali yake chifukwa anali mkamwini wa Sekaniya, mwana wa Ara.+ Ndipo Yehohanani mwana wa Tobia anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu,+ mwana wa Berekiya. 19 Komanso anthu amenewa nthawi zonse ankandiuza zinthu zabwino za Tobia. Kenako ankatenga zimene ine ndanena nʼkukamuuza Tobiayo ndipo iye ankanditumizira makalata ondiopseza.+

7 Mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika pa udindo alonda amʼmageti,+ oimba+ ndi Alevi.+ 2 Kenako ndinaika Haneni mʼbale wanga+ ndi Hananiya, mkulu wa mʼNyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyangʼanira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika ndiponso woopa Mulungu woona+ kuposa anthu ena ambiri. 3 Choncho ndinawauza kuti: “Mageti a Yerusalemu sayenera kutsegulidwa mpaka dzuwa litakwera. Alonda amʼmageti aime pafupi ndipo atseke zitseko nʼkuzikhoma ndi anamphatika. Muikenso alonda a anthu a ku Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.” 4 Mzindawo unali wotakasuka ndiponso waukulu. Munali anthu ochepa+ ndipo nyumba zinali zisanamangidwenso.

5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina motsatira mndandanda wa makolo awo.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti mʼbukumo analembamo izi:

6 Awa ndi anthu amʼchigawo amene anachoka ku ukapolo, anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatenga nʼkupita nawo ku ukapolo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense mumzinda wakwawo.+ 7 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Moredikayi, Bilisani, Misiperete, Bigivai, Nehumu ndi Bana.

Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+ 8 Ana a Parosi, 2,172. 9 Ana a Sefatiya, 372. 10 Ana a Ara,+ 652. 11 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818. 12 Ana a Elamu,+ 1,254. 13 Ana a Zatu, 845. 14 Ana a Zakai, 760. 15 Ana a Binui, 648. 16 Ana a Bebai, 628. 17 Ana a Azigadi, 2,322. 18 Ana a Adonikamu, 667. 19 Ana a Bigivai, 2,067. 20 Ana a Adini, 655. 21 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 22 Ana a Hasumu, 328. 23 Ana a Bezai, 324. 24 Ana a Harifi, 112. 25 Ana a Gibiyoni,+ 95. 26 Amuna a ku Betelehemu ndi ku Netofa, 188. 27 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 28 Amuna a ku Beti-azimaveti, 42. 29 Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira ndi ku Beeroti,+ 743. 30 Amuna a ku Rama ndi ku Geba,+ 621. 31 Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 32 Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123. 33 Amuna a ku Nebo wina, 52. 34 Ana a Elamu wina, 1,254. 35 Ana a Harimu, 320. 36 Ana a Yeriko, 345. 37 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono,+ 721. 38 Ana a Senaya, 3,930.

39 Ansembe:+ Ana a Yedaya, a mʼbanja la Yesuwa, 973. 40 Ana a Imeri, 1,052. 41 Ana a Pasuri,+ 1,247. 42 Ana a Harimu,+ 1,017.

43 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva, 74. 44 Oimba:+ ana a Asafu,+ 148. 45 Alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni, ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, 138.

46 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 47 ana a Kerosi, ana a Siya, ana a Padoni, 48 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai, 49 ana a Hanani, ana a Gideli, ana a Gahara, 50 ana a Reyaya, ana a Rezini, ana a Nekoda, 51 ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya, 52 ana a Besai, ana a Meyuni, ana a Nefusesimu, 53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 54 ana a Baziliti, ana a Mehida, ana a Harisa, 55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 56 ana a Neziya komanso ana a Hatifa.

57 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida, 58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Amoni. 60 Atumiki apakachisi*+ onse ndiponso ana a atumiki a Solomo analipo 392.

61 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi,+ ndi awa: 62 Ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 642. 63 Ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ndiponso ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 64 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 65 Bwanamkubwa*+ anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+

66 Anthu onse analipo 42,360.+ 67 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi akapolo awo aakazi+ amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi 245.+ 68 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245. 69 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.

70 Atsogoleri ena a nyumba za makolo anapereka zinthu zothandizira pa ntchito.+ Bwanamkubwa* anapereka kumalo osungira chuma ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zolowa 50 ndi mikanjo ya ansembe 530.+ 71 Panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000 ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200. 72 Ndipo anthu ena onse anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67.

73 Ndiyeno ansembe, Alevi, alonda apageti, oimba,+ anthu ena, atumiki apakachisi* ndiponso Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7,+ Aisiraeli anali atakhala mʼmizinda yawo.+

8 Anthu onse anasonkhana mogwirizana mʼbwalo lalikulu kutsogolo kwa Geti la Kumadzi.+ Anthuwo anauza Ezara+ wokopera Malemba* kuti abweretse buku la Chilamulo cha Mose+ chimene Yehova analamula Aisiraeli kuti azitsatira.+ 2 Choncho Ezara wansembe anapititsa buku la Chilamulo kugulu la anthuwo.+ Panali amuna, akazi komanso aliyense amene akanatha kumvetsa zimene zikunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+ 3 Ezara anawerenga mokweza bukulo+ mʼbwalo lalikulu limene linali kutsogolo kwa Geti la Kumadzi, kuyambira mʼmawa mpaka masana. Anawerenga bukuli pamaso pa amuna, akazi ndiponso aliyense amene akanatha kumvetsa zimene zikunenedwa. Ndipo anthu ankamvetsera mwatcheru+ zimene zinali mʼbuku la Chilamuloli. 4 Ezara wokopera Malembayo,* anaima pansanja yamatabwa imene anaimanga chifukwa cha mwambowu. Kumanja kwake kunaima Matitiya, Sema, Anaya, Uriya, Hilikiya ndi Maaseya. Kumanzere kwake kunali Pedaya, Misayeli, Malikiya,+ Hasumu, Hasi-badana, Zekariya ndi Mesulamu.

5 Ezara anatsegula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza anaima pamalo okwera kusiyana ndi anthu onse. Pamene ankatsegula bukulo, anthu onse anaimirira. 6 Kenako Ezara anatamanda Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu. Atatero anthu onse ananena kuti, “Ame! Ame!”*+ ndipo anakweza manja awo mʼmwamba. Ndiyeno anthuwo anagwada nʼkuwerama pamaso pa Yehova mpaka nkhope zawo kufika pansi. 7 Yesuwa, Bani, Serebiya,+ Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseya, Kelita, Azariya, Yozabadi,+ Hanani ndi Pelaya, omwe anali Alevi, ankafotokozera anthu Chilamulocho,+ anthuwo ataimirira. 8 Iwo anapitiriza kuwerenga bukulo mokweza. Anapitiriza kuwerenga Chilamulo cha Mulungu woona, kuchifotokoza momveka bwino ndi kumveketsa tanthauzo lake. Choncho anathandiza anthuwo kumvetsa tanthauzo la zimene ankawerenga.+

9 Ndiyeno Nehemiya, yemwe pa nthawiyo anali bwanamkubwa,* Ezara+ wansembe ndi wokopera Malemba,* komanso Alevi amene ankapereka malangizo kwa anthu, anauza anthuwo kuti: “Lero ndi tsiku lopatulika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musakhale achisoni ndipo musalire.” Ananena zimenezi chifukwa anthu onse ankalira pamene ankamvetsera mawu a mʼChilamulocho. 10 Nehemiya anati: “Pitani mukadye zinthu zabwino kwambiri,* mukamwe zokoma ndiponso mukagawire chakudya+ anthu amene alibe, chifukwa lero ndi tsiku lopatulika kwa Ambuye wathu. Musadzimvere chisoni, chifukwa chimwemwe chimene Yehova amapereka ndi malo anu achitetezo.”* 11 Alevi ankauza anthu onse kuti asachite phokoso. Ankanena kuti: “Khalani chete chifukwa lero ndi tsiku lopatulika, choncho musadzimvere chisoni.” 12 Ndiyeno anthu onse anapita kukadya, kukamwa, kukagawira ena chakudya ndiponso kukasangalala kwambiri+ chifukwa anamvetsa bwino mawu amene anawafotokozera.+

13 Pa tsiku lachiwiri, atsogoleri a mabanja a anthu onse, ansembe ndiponso Alevi, anasonkhana pamodzi pamaso pa Ezara wokopera Malemba,* kuti amvetse bwino mawu a mʼChilamulo. 14 Ndiyeno anapeza kuti mʼChilamulo chimene Yehova anawapatsa kudzera mwa Mose analembamo kuti Aisiraeli azikhala mʼmisasa pa nthawi yachikondwerero mʼmwezi wa 7.+ 15 Analembamonso kuti azilengeza mofuula+ mʼmizinda yonse ndi ku Yerusalemu konse kuti: “Pitani kumapiri mukatenge nthambi za mitengo ya maolivi, nthambi za mitengo ya paini, nthambi za mitengo ya mchisu, mitengo ya kanjedza ndi nthambi za masamba ambiri za mitengo ina kuti mudzamangire misasa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.”

16 Choncho anthu anapita nʼkukatenga zinthu zimenezi ndipo anamangira misasa. Aliyense anamanga msasa pamwamba pa nyumba yake, mʼmabwalo awo, mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu woona,+ mʼbwalo lalikulu la Geti la Kumadzi+ ndiponso mʼbwalo lalikulu la Geti la Efuraimu.+ 17 Choncho gulu lonse la anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo anamanga misasa nʼkukhala mʼmisasayo. Anthu anasangalala kwambiri+ chifukwa Aisiraeli anali asanachitepo zimenezi kuchokera mu nthawi ya Yoswa+ mwana wa Nuni, mpaka nthawi imeneyi. 18 Ndiyeno tsiku lililonse, kuyambira tsiku loyamba mpaka lomaliza, ankawerenga mokweza buku la Chilamulo cha Mulungu woona.+ Anachita chikondwererochi masiku 7 ndipo pa tsiku la 8 anachita msonkhano wapadera mogwirizana ndi Chilamulo.+

9 Pa tsiku la 24 la mwezi umenewu Aisiraeli anasonkhana pamodzi ndipo anasala kudya atavala ziguduli komanso atadzithira dothi kumutu.+ 2 Aisiraeli anadzipatula kwa anthu onse omwe sanali Aisiraeli+ ndipo anaimirira nʼkuyamba kuulula machimo awo komanso zolakwa za makolo awo.+ 3 Iwo anaimirirabe ndipo anawerenga mokweza buku la Chilamulo+ cha Yehova Mulungu wawo kwa maola atatu. Kwa maola enanso atatu anaulula machimo awo ndiponso kugwadira Yehova Mulungu wawo.

4 Ndiyeno Yesuwa, Bani, Kadimiyeli, Sebaniya, Buni, Serebiya,+ Bani ndi Kenani anakwera pansanja+ ya Alevi nʼkuyamba kufuula kwa Yehova Mulungu wawo. 5 Ndipo Yesuwa, Kadimiyeli, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya, omwe anali Alevi, anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu mpaka kalekale.*+ Inu Mulungu wathu, anthuwa atamande dzina lanu laulemerero, lomwe ndi lalikulu kuposa dalitso ndiponso chitamando chilichonse.

6 Inu nokha ndinu Yehova.+ Munapanga kumwamba, ngakhalenso kumwamba kwa kumwamba ndi magulu ake onse. Munapanganso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo komanso nyanja ndi zonse zomwe zili mmenemo. Mumasunga zinthu zamoyo ndipo magulu akumwamba amakugwadirani. 7 Inu ndinu Yehova Mulungu woona, amene munasankha Abulamu+ nʼkumutulutsa mumzinda wa Uri+ wa Akasidi ndipo munamupatsa dzina lakuti Abulahamu.+ 8 Munamuona kuti anali ndi mtima wokhulupirika,+ choncho munachita naye pangano kuti mudzamʼpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ayebusi ndi Agirigasi. Munalonjeza kuti mudzapereka dziko limeneli kwa mbadwa*+ zake ndipo munakwaniritsadi zimene munalonjeza chifukwa ndinu wolungama.

9 Choncho munaona mavuto amene makolo athu ankakumana nawo ku Iguputo+ ndipo munamva kulira kwawo pa Nyanja Yofiira. 10 Ndiyeno munakhaulitsa Farao, atumiki ake onse ndiponso anthu onse amʼdziko lake powaonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa.+ Munachita zimenezi chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepa munadzipangira dzina lomwe lilipobe mpaka lero.+ 11 Munagawa nyanja pamaso pawo ndipo anadutsa panthaka youma.+ Anthu amene ankawathamangitsa munawaponya pansi pa nyanja ngati mwala woponyedwa mʼmafunde amphamvu.+ 12 Masana munkawatsogolera ndi chipilala cha mtambo ndipo usiku munkawatsogolera ndi chipilala cha moto kuti uziwaunikira njira imene ankayenera kudutsa.+ 13 Ndiyeno munatsikira paphiri la Sinai+ nʼkulankhula nawo muli kumwamba+ ndipo munawapatsa ziweruzo zolungama, malamulo a choonadi* ndiponso mfundo ndi malangizo abwino.+ 14 Munawauza za Sabata+ lanu lopatulika ndipo munawapatsa malangizo, mfundo ndi malamulo kudzera mwa Mose mtumiki wanu. 15 Pamene anali ndi njala munawapatsa chakudya chochokera kumwamba+ ndipo pamene anali ndi ludzu munatulutsa madzi pathanthwe.+ Munawauza kuti alowe nʼkutenga dziko limene munalumbira* kuti mudzawapatsa.

16 Koma makolo athuwo anachita zinthu modzikuza+ moti anaumitsa khosi+ ndipo sankatsatira malamulo anu. 17 Iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire zinthu zodabwitsa zimene munawachitira. Mʼmalomwake anaumitsa khosi ndipo anasankha munthu woti awatsogolere pobwereranso ku ukapolo ku Iguputo.+ Koma inu ndinu Mulungu wokonzeka kukhululuka, wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika*+ chochuluka, choncho simunawasiye.+ 18 Ngakhale pamene anapanga chifaniziro chachitsulo cha mwana wa ngʼombe nʼkuyamba kunena kuti, ‘Uyu ndiye Mulungu wanu amene anakutulutsani ku Iguputo,’+ ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani, 19 inu simunawasiye mʼchipululu, chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ Chipilala cha mtambo sichinawachokere masana ndipo chinkawatsogolera, komanso chipilala cha moto sichinawachokere usiku ndipo chinkawaunikira njira yoyenera kudutsa.+ 20 Munawapatsa mzimu wanu wabwino kuti akhale anzeru.+ Simunawamane mana+ ndipo pamene anali ndi ludzu munawapatsa madzi.+ 21 Kwa zaka 40 munawapatsa chakudya mʼchipululu+ moti sanasowe kanthu. Zovala zawo sizinathe+ ndipo mapazi awo sanatupe.

22 Munawapatsa maufumu ndi mitundu ya anthu ndipo munawagawira dzikolo mʼzigawozigawo.+ Iwo anatenga dziko la Sihoni,+ lomwe ndi dziko la mfumu ya Hesiboni+ komanso dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. 23 Ndipo munachulukitsa ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Kenako munawalowetsa mʼdziko limene munalonjeza makolo awo kuti adzalowamo nʼkulitenga kukhala lawo.+ 24 Choncho ana awo analowa nʼkutenga dzikolo.+ Munagonjetsa Akanani,+ anthu amʼdzikolo ndipo munawapereka mʼmanja mwawo. Munaperekanso mafumu a Akananiwo ndi anthu amʼdzikolo kwa Aisiraeli kuti awachitire zimene akufuna. 25 Iwo analanda mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ ndi dziko la nthaka yachonde.+ Ndipo anatenga zitsime zokumba kale, nyumba zodzaza ndi zinthu zabwino, minda ya mpesa, minda ya maolivi+ ndiponso mitengo yokhala ndi zipatso zambiri. Choncho ankadya nʼkukhuta moti ananenepa ndipo ankasangalala ndi ubwino wanu waukulu.

26 Koma iwo anali osamvera ndipo anakugalukirani.+ Anasiya kutsatira Chilamulo chanu, anapha aneneri anu amene ankawachenjeza kuti abwerere kwa inu ndipo anachita zinthu zikuluzikulu zosakulemekezani.+ 27 Chifukwa cha zimenezi, munawapereka mʼmanja mwa adani awo+ amene ankawazunza.+ Koma akakumana ndi mavuto ankakulirirani ndipo inu munkamva muli kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, munkawapatsa anthu oti awapulumutse mʼmanja mwa adani awo.+

28 Koma akangokhala pamtendere ankachitanso zoipa pamaso panu+ ndipo munkawapereka mʼmanja mwa adani awo amene ankawapondereza.+ Zikatero, ankabwereranso kwa inu nʼkupempha thandizo+ ndipo inu munkamva muli kumwambako nʼkuwapulumutsa mobwerezabwereza chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 29 Ngakhale kuti munkawachenjeza kuti ayambenso kutsatira Chilamulo chanu, iwo ankadzikuza ndipo ankakana malamulo anu.+ Iwo anachimwa chifukwa sankatsatira ziweruzo zanu zimene munthu akamazitsatira amakhala ndi moyo.+ Anatseka makutu awo ndi kuumitsa makosi awo ndipo anakana kumvera. 30 Munawalezera mtima+ kwa zaka zambiri ndipo munapitiriza kuwachenjeza pogwiritsa ntchito mzimu wanu kudzera mwa aneneri anu, koma anakana kumvera. Kenako munawapereka mʼmanja mwa anthu amʼdzikolo.+ 31 Ndipo chifukwa cha chifundo chanu chachikulu simunawafafanize+ kapena kuwasiya, popeza ndinu Mulungu wachisomo ndi wachifundo.+

32 Tsopano inu Mulungu wathu, Mulungu wamkulu, wamphamvu, wochititsa mantha, wosunga pangano komanso wachikondi chokhulupirika,+ musachepetse mavuto amene tikukumana nawo ifeyo, mafumu athu, akalonga athu,+ ansembe athu,+ aneneri athu,+ makolo athu ndi anthu anu onse kuyambira mu nthawi ya mafumu a Asuri+ mpaka pano. 33 Inu mwachita zinthu molungama pa zonse zimene zatichitikira. Mwachita zinthu mokhulupirika koma ife ndi amene tachita zinthu zoipa.+ 34 Mafumu athu, akalonga athu, ansembe athu ndi makolo athu sanatsatire Chilamulo chanu ndipo sanamvere malamulo anu kapena zikumbutso zanu zowachenjeza. 35 Ngakhale pamene ankalamuliridwa ndi mafumu awo ndipo ankadalitsidwa kwambiri komanso ankakhala mʼdziko lalikulu ndi lachonde limene munawapatsa, iwo sankakutumikirani+ ndipo sanasiye kuchita zoipa. 36 Pano ndife akapolo.+ Ndife akapolo mʼdziko limene munapatsa makolo athu kuti adye zipatso zake ndi zinthu zake zabwino. 37 Mafumu amene mwalola kuti azitilamulira chifukwa cha machimo athu+ ndi amene akusangalala ndi zokolola zochuluka zamʼdzikoli. Iwo akulamulira matupi athu komanso ziweto zathu mmene akufunira, ndipo tili pamavuto aakulu.

38 Choncho chifukwa cha zimenezi, tikuchita pangano lodalirika+ lochita kulemba ndipo akalonga athu, Alevi athu ndi ansembe athu atsimikizira panganoli ndi chidindo chawo.”+

10 Amene anatsimikizira panganoli ndi chidindo chawo+ anali awa:

Nehemiya amene anali bwanamkubwa,* mwana wa Hakaliya,

Zedekiya, 2 Seraya, Azariya, Yeremiya, 3 Pasuri, Amariya, Malikiya, 4 Hatusi, Sebaniya, Maluki, 5 Harimu,+ Meremoti, Obadiya, 6 Danieli,+ Ginetoni, Baruki, 7 Mesulamu, Abiya, Miyamini, 8 Maaziya, Biligai ndi Semaya. Amenewa anali ansembe.

9 Panalinso Alevi awa: Yesuwa, mwana wamwamuna wa Azaniya, Binui wochokera kwa ana a Henadadi, Kadimiyeli+ 10 ndi abale awo awa, Sebaniya, Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani, 11 Mika, Rehobu, Hasabiya, 12 Zakuri, Serebiya,+ Sebaniya, 13 Hodiya, Bani ndiponso Beninu.

14 Panalinso atsogoleri awa: Parosi, Pahati-mowabu,+ Elamu, Zatu, Bani, 15 Buni, Azigadi, Bebai, 16 Adoniya, Bigivai, Adini, 17 Ateri, Hezekiya, Azuri, 18 Hodiya, Hasumu, Bezai, 19 Harifi, Anatoti, Nebai, 20 Magipiasi, Mesulamu, Heziri, 21 Mesezabele, Zadoki, Yaduwa, 22 Pelatiya, Hanani, Anaya, 23 Hoshiya, Hananiya, Hasubu, 24 Halohesi, Pila, Sobeki, 25 Rehumu, Hasabina, Maaseya, 26 Ahiya, Hanani, Anane, 27 Maluki, Harimu ndiponso Bana.

28 Anthu ena onse, ansembe, Alevi, alonda apageti, oimba, atumiki apakachisi* ndiponso aliyense amene anadzipatula kwa anthu amʼmayikowo kuti asunge Chilamulo cha Mulungu woona,+ akazi awo, ana awo aamuna ndi aakazi ndiponso aliyense wodziwa zinthu komanso woti akhoza kumvetsa zimene zikunenedwa, 29 anagwirizana ndi abale awo, anthu otchuka. Iwo analumbira* kuti azitsatira Chilamulo cha Mulungu woona chimene chinaperekedwa kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu woona komanso kuti azitsatira mosamala malamulo onse, ziweruzo ndi mfundo za Yehova Ambuye wathu. 30 Komanso kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa anthu amʼdzikoli ndiponso sitidzatenga ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana athu aamuna.+

31 Tinalumbira kuti anthu amʼdzikolo akabwera kudzagulitsa katundu ndi mbewu zamtundu uliwonse* pa tsiku la Sabata,+ sitidzawagula chilichonse pa Sabata kapena pa tsiku lililonse lopatulika.+ Tinalumbiranso kuti sitizilima minda yathu mʼchaka cha 7+ ndipo tizikhululuka ngongole zonse.+

32 Kuwonjezera pamenepo, tinalonjeza kuti chaka chilichonse aliyense azipereka ndalama zasiliva zolemera magalamu 4* kuti akazigwiritse ntchito pa utumiki wapanyumba* ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsenso ntchito pokonza mkate wosanjikiza,*+ nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse, nsembe yopsereza yoperekedwa nthawi zonse pa Masabata+ ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka,+ madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika, nsembe yamachimo+ yophimba machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu wathu.

34 Komanso tinachita maere okhudza nkhuni zimene ansembe, Alevi ndi anthu ankayenera kubweretsa kunyumba ya Mulungu wathu, mogwirizana ndi nyumba za makolo athu. Ankayenera kuzibweretsa pa nthawi zoikidwiratu, chaka chilichonse kuti aziziyatsa paguwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo.+ 35 Tinalonjezanso kuti chaka chilichonse tizibweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyambirira kupsa zamʼdziko lathu komanso za mtengo uliwonse.+ 36 Tizibweretsanso ana athu aamuna oyamba kubadwa ndiponso a ziweto zathu+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo. Tizibweretsa ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi nkhosa zathu. Tizibweretsa zimenezi kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene amatumikira mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tizibweretsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu, zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano ndi mafuta+ kwa ansembe mʼzipinda zosungira katundu* mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Tifunikanso kubweretsa chakhumi kwa Alevi pa zinthu zochokera mʼdziko lathu+ chifukwa Aleviwo ndi amene amatolera chakhumi kuchokera mʼmizinda yathu yonse ya zaulimi.

38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akutolera chakhumi. Aleviwo azipereka gawo limodzi pa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu wathu+ kuzipinda* za nyumba yosungira katundu. 39 Chifukwa Aisiraeli ndi Alevi ayenera kubweretsa zopereka+ zambewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ kuzipinda zosungira katundu.* Kumeneku nʼkumene kuli ziwiya zakumalo opatulika, ansembe amene amatumikira, alonda apageti ndiponso oimba. Sitidzanyalanyaza nyumba ya Mulungu wathu.+

11 Akalonga a anthuwo ankakhala ku Yerusalemu.+ Anthu ena onse anachita maere+ kuti apeze munthu mmodzi pa anthu 10 alionse woti akakhale ku Yerusalemu, mzinda woyera, ndipo anthu 9 otsalawo ankakhala mʼmizinda ina. 2 Komanso anthu anadalitsa amuna onse amene anadzipereka kukakhala ku Yerusalemu.

3 Otsatirawa ndi atsogoleri a chigawo cha Yuda amene ankakhala ku Yerusalemu, (Aisiraeli ena onse, ansembe, Alevi, atumiki apakachisi*+ ndiponso ana a atumiki a Solomo+ ankakhala mʼmizinda ina ya Yuda. Aliyense ankakhala pamalo ake mumzinda wake.+

4 Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a fuko la Yuda ndi la Benjamini.) Anthu a fuko la Yudawo anali Ataya mwana wa Uziya. Uziyayo anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Sefatiya, Sefatiya anali mwana wa Mahalalele wochokera mʼbanja la Perezi.+ 5 Panalinso Maaseya mwana wa Baruki amene anali mwana wa Kolihoze. Kolihoze anali mwana wa Hazaya, Hazaya anali mwana wa Adaya, Adaya anali mwana wa Yoyaribi, Yoyaribi anali mwana wa Zekariya mbadwa ya Shela. 6 Ana onse a Perezi amene ankakhala ku Yerusalemu anali amuna amphamvu okwana 468.

7 Anthu a fuko la Benjamini anali awa: Salelu+ mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Yoedi, Yoedi anali mwana wa Pedaya, Pedaya anali mwana wa Kolaya, Kolaya anali mwana wa Maaseya, Maaseya anali mwana wa Itiyeli ndipo Itiyeli anali mwana wa Yesaiya. 8 Pambuyo pa Salelu panali Gabai ndi Salai ndipo onse pamodzi analipo 928. 9 Yoweli mwana wa Zikiri anali woyangʼanira wawo ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali wachiwiri kwa woyangʼanira mzinda.

10 Pagulu la ansembe panali awa: Yedaya mwana wa Yoyaribi, Yakini,+ 11 Seraya mwana wa Hilikiya. Hilikiya anali mwana wa Mesulamu, Mesulamu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Merayoti, Merayoti anali mwana wa Ahitubu,+ mtsogoleri wa panyumba* ya Mulungu woona. 12 Abale awo omwe ankagwira ntchito panyumbapo analipo 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu. Yerohamu anali mwana wa Pelaliya, Pelaliya anali mwana wa Amuzi, Amuzi anali mwana wa Zekariya, Zekariya anali mwana wa Pasuri+ ndipo Pasuri anali mwana wa Malikiya. 13 Abale ake a Adaya, atsogoleri a nyumba za makolo awo, analipo 242. Ndiyeno panalinso Amasisai mwana wa Azareli. Azareli anali mwana wa Azai, Azai anali mwana wa Mesilemoti amene anali mwana wa Imeri. 14 Amasisai pamodzi ndi abale ake, amuna amphamvu ndiponso olimba mtima, analipo okwana 128. Iwowa mtsogoleri wawo anali Zabidiyeli wochokera mʼbanja lotchuka.

15 Pagulu la Alevi panali awa: Semaya+ mwana wa Hasubu. Hasubu anali mwana wa Azirikamu, Azirikamu anali mwana wa Hasabiya ndipo Hasabiya anali mwana wa Buni. 16 Panalinso Sabetai+ ndi Yozabadi,+ omwe anali mʼgulu la atsogoleri a Alevi. Amenewa ankayangʼanira ntchito yapanja pa nyumba ya Mulungu woona. 17 Komanso panali Mataniya+ mwana wa Mika ndipo Mika anali mwana wa Zabidi. Zabidi anali mwana wa Asafu,+ yemwe anali mtsogoleri wa nyimbo zotamanda Mulungu. Iye ankatsogolera potamanda Mulungu pa nthawi ya pemphero.+ Bakibukiya anali wachiwiri wake poyangʼanira abale ake. Panalinso Abada mwana wa Samuwa, Samuwa anali mwana wa Galali ndipo Galali anali mwana wa Yedutuni.+ 18 Alevi onse amene ankakhala mumzinda woyera analipo 284.

19 Alonda apageti anali Akubu, Talimoni+ ndi abale awo amene ankalondera mʼmageti. Onse pamodzi analipo 172.

20 Aisiraeli ena onse komanso ansembe ndi Alevi ena onse, anali mʼmizinda ina ya Yuda, aliyense pacholowa chake. 21 Atumiki apakachisi*+ ankakhala ku Ofeli+ ndipo Ziha ndi Gisipa ankayangʼanira atumiki apakachisiwo.

22 Woyangʼanira Alevi ku Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani. Bani anali mwana wa Hasabiya, Hasabiya anali mwana wa Mataniya,+ Mataniya anali mwana wa Mika wa mʼbanja la Asafu ndipo a mʼbanja la Asafu anali oimba. Uzi ankayangʼanira ntchito yapanyumba ya Mulungu woona 23 Mfumu inapereka lamulo lokhudza oimba,+ ndipo panali dongosolo loti aziwapatsa thandizo tsiku lililonse mogwirizana ndi zofunikira za tsikulo. 24 Petahiya mwana wa Mesezabele, wa mʼbanja la Zera mwana wa Yuda, anali mlangizi wa mfumu pa nkhani zonse zokhudza anthu.

25 Ayuda ena ankakhala mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira midziyo. Ena ankakhala ku Kiriyati-ariba+ ndi midzi yake yozungulira, ku Diboni ndi midzi yake yozungulira, ku Yekabizeeli+ ndi midzi yake yozungulira, 26 ku Yesuwa, ku Molada,+ ku Beti-peleti,+ 27 ku Hazara-suali,+ ku Beere-seba ndi midzi yake yozungulira, 28 ku Zikilaga,+ ku Mekona ndi midzi yake yozungulira, 29 ku Eni-rimoni,+ ku Zora,+ ku Yarimuti, 30 ku Zanowa,+ ku Adulamu ndi midzi yake yozungulira, ku Lakisi+ ndi madera ake ozungulira ndiponso ku Azeka+ ndi midzi yake yozungulira. Iwo anakhala* kuyambira ku Beere-seba mpaka kuchigwa cha Hinomu.+

31 Anthu a fuko la Benjamini anakhala ku Geba,+ ku Mikimasi, ku Aiya, ku Beteli+ ndi midzi yake yozungulira, 32 ku Anatoti,+ ku Nobu,+ ku Ananiya, 33 ku Hazori, ku Rama,+ ku Gitaimu, 34 ku Hadidi, ku Zeboyimu, ku Nebalati, 35 ku Lodi ndiponso ku Ono,+ chigwa cha amisiri. 36 Ndipo Alevi ena ochokera ku Yuda anapatsidwa malo ku Benjamini.

12 Ansembe ndi Alevi amene anapita ndi Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi Yesuwa+ ndi awa: Seraya, Yeremiya, Ezara, 2 Amariya, Maluki, Hatusi, 3 Sekaniya, Rehumu, Meremoti, 4 Ido, Ginetoi, Abiya, 5 Miyamini, Maadiya, Biliga, 6 Semaya, Yoyaribi, Yedaya, 7 Salelu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya. Amenewa anali atsogoleri a ansembe komanso a abale awo mʼmasiku a Yesuwa.

8 Ndiyeno panali Alevi awa: Yesuwa, Binui, Kadimiyeli,+ Serebiya, Yuda ndiponso Mataniya,+ amene ankatsogolera nyimbo zotamanda Mulungu limodzi ndi abale ake. 9 Ndipo abale awo, Bakibukiya ndi Uni, ankaima moyangʼanizana nawo nʼkumagwira ntchito ya ulonda.* 10 Yesuwa anabereka Yoyakimu, Yoyakimu anabereka Eliyasibu,+ Eliyasibu anabereka Yoyada.+ 11 Yoyada anabereka Yonatani ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.

12 Mʼmasiku a Yoyakimu anthu awa ndi amene anali ansembe, atsogoleri a nyumba za makolo: Woimira nyumba ya Seraya+ anali Meraya, woimira nyumba ya Yeremiya anali Hananiya. 13 Woimira nyumba ya Ezara+ anali Mesulamu, woimira nyumba ya Amariya anali Yehohanani. 14 Woimira nyumba ya Maluka anali Yonatani, woimira nyumba ya Sebaniya anali Yosefe. 15 Woimira nyumba ya Harimu+ anali Adena, woimira nyumba ya Merayoti anali Helikai. 16 Woimira nyumba ya Ido anali Zekariya, woimira nyumba ya Ginetoni anali Mesulamu. 17 Woimira nyumba ya Abiya+ anali Zikiri, woimira nyumba ya Miniyamini anali . . . ,* woimira nyumba ya Moadiya anali Pilitai. 18 Woimira nyumba ya Biliga+ anali Samuwa, woimira nyumba ya Semaya anali Yehonatani. 19 Woimira nyumba ya Yoyaribi anali Matenai, woimira nyumba ya Yedaya+ anali Uzi. 20 Woimira nyumba ya Salai anali Kalai, woimira nyumba ya Amoki anali Ebere. 21 Woimira nyumba ya Hilikiya anali Hasabiya ndipo woimira nyumba ya Yedaya anali Netaneli.

22 Mʼmasiku a Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa,+ mayina a atsogoleri a nyumba za makolo za Alevi, ankawalemba ngati mmene ankachitira ndi ansembe mpaka kudzafika mʼnthawi ya ufumu wa Dariyo wa ku Perisiya.

23 Alevi amene anali atsogoleri a nyumba za makolo ankalembedwa mʼbuku la zochitika za pa nthawi imeneyo mpaka kudzafika mʼmasiku a Yohanani, mwana wa Eliyasibu. 24 Atsogoleri a Alevi anali Hasabiya, Serebiya ndi Yesuwa+ mwana wa Kadimiyeli.+ Ndipo abale awo ankaima moyangʼanizana nawo nʼkumatamanda ndi kuyamika Mulungu mogwirizana ndi malangizo a Davide,+ munthu wa Mulungu woona. Gulu lililonse la alonda linaima moyandikana ndi gulu lina la alonda. 25 Mataniya,+ Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu+ ankalondera mageti.+ Iwo ankalondera zipinda zosungira zinthu zomwe zinali pafupi ndi mageti. 26 Anthu amenewa ankatumikira mʼmasiku a Yoyakimu mwana wa Yesuwa+ amene anali mwana wa Yozadaki, komanso mʼmasiku a Nehemiya amene anali bwanamkubwa, ndi Ezara+ amene anali wansembe komanso wokopera Malemba.

27 Ndiyeno mwambo wotsegulira mpanda wa Yerusalemu uli pafupi, anthu anafunafuna Alevi mʼmadera onse amene ankakhala nʼkubwera nawo ku Yerusalemu. Anachita izi kuti potsegulira mpandawo pakhale kusangalala, kuimba nyimbo zoyamika Mulungu+ ndiponso kuimba pogwiritsa ntchito zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze. 28 Ana a oimbawo* anasonkhana pamodzi kuchokera mʼchigawo,* mʼmadera onse ozungulira Yerusalemu komanso mʼmidzi yonse kumene Anetofa ankakhala.+ 29 Ena anachokera ku Beti-giligala+ komanso mʼmadera a ku Geba+ ndi ku Azimaveti,+ chifukwa oimbawo anamanga midzi yawo kuzungulira Yerusalemu yense. 30 Ndiyeno ansembe ndi Alevi anadziyeretsa nʼkuyeretsanso anthu,+ mageti+ ndi mpandawo.+

31 Kenako ndinabwera ndi akalonga a Yuda pamwamba pa mpandawo. Ndinaikanso magulu akuluakulu awiri oimba nyimbo zoyamika Mulungu ndiponso magulu ena oti aziwatsatira pambuyo. Gulu lina la oimba linkayenda pampandawo mbali yakumanja kulowera ku Geti la Milu ya Phulusa.+ 32 Hoshaya ndi hafu ya akalonga a Yuda ankayenda pambuyo pa oimbawo 33 pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu, 34 Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya. 35 Analinso ndi ena mwa ana a ansembe oimba malipenga:+ Zekariya mwana wa Yonatani. Yonatani anali mwana wa Semaya, Semaya anali mwana wa Mataniya, Mataniya anali mwana wa Mikaya, Mikaya anali mwana wa Zakuri ndipo Zakuri anali mwana wa Asafu.+ 36 Panalinso Semaya, Azareli, Milalai, Gilelai, Maai, Netaneli, Yuda ndi Haneni, abale ake a Zekariya. Anali ndi zipangizo zoimbira za Davide,+ munthu wa Mulungu woona, ndipo amene ankawatsogolera anali Ezara+ wokopera Malemba.* 37 Oimbawo atafika pa Geti la Kukasupe,+ gulu lowatsatira lija lili pambuyo pawo, anayenda pamalo okwera a mpandawo kudutsa pamasitepe+ ochokera ku Mzinda wa Davide+ mpaka kukafika kumtunda kwa Nyumba ya Davide.+ Kenako anafika ku Geti la Kumadzi, chakumʼmawa.

38 Gulu lina loimba nyimbo zoyamika Mulungu linkayenda kumanzere, ndipo ine ndi hafu ya anthuwo tinkabwera pambuyo pawo. Oimbawo ankayenda pampandawo, kudutsa pamwamba pa Nsanja ya Mauvuni+ mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 39 Anadutsanso pamwamba pa Geti la Efuraimu,+ Geti la Mzinda Wakale,+ Geti la Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya ndi ku Geti la Nkhosa,+ ndipo anaima pa Geti la Alonda.

40 Kenako magulu awiri oimba nyimbo zoyamikawo anaima panyumba ya Mulungu woona ndipo ine ndi atsogoleri amene ndinali nawo tinaimanso pomwepo. 41 Panafikanso ansembe otsatirawa okhala ndi malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, Hananiya, 42 Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Malikiya, Elamu ndi Ezeri. Oimbawo anaimba mokweza ndipo amene ankawatsogolera anali Izirahiya.

43 Pa tsiku limenelo anapereka nsembe zambiri ndipo anasangalala+ chifukwa Mulungu woona anawachititsa kuti asangalale kwambiri. Akazi ndi ana nawonso anasangalala+ moti phokoso lachisangalalo ku Yerusalemu linamveka kutali.+

44 Pa tsikuli anasankha amuna kuti aziyangʼanira nyumba zosungiramo+ zopereka,+ mbewu zoyambirira kucha+ ndiponso chakhumi.+ Anawapatsa udindo woti azitutira mʼnyumbamo magawo oyenera kuperekedwa kwa ansembe ndi Alevi+ mogwirizana ndi Chilamulo,+ kuchokera mʼminda yonse yamʼmizinda yawo. Popeza anthu a ku Yuda anasangalala chifukwa cha ansembe ndi Alevi amene ankatumikira. 45 Ansembe ndi Alevi anayamba kugwira ntchito ya Mulungu wawo ndiponso kusunga lamulo lakuti azikhala oyera, ngati mmene ankachitira oimba ndi alonda apageti, mogwirizana ndi malangizo a Davide ndi mwana wake Solomo. 46 Kalelo mʼmasiku a Davide ndi Asafu, kunali atsogoleri a anthu oimba ndiponso a nyimbo zotamanda ndi kuyamika Mulungu.+ 47 Mʼmasiku a Zerubabele+ komanso a Nehemiya, Aisiraeli onse ankapereka magawo a chakudya kwa oimba+ ndi alonda apageti+ mogwirizana ndi zimene ankafunikira tsiku lililonse. Ankaikanso padera gawo lina la Alevi+ ndipo Aleviwo ankaikanso padera gawo la mbadwa za Aroni.

13 Pa tsiku limenelo buku la Mose linawerengedwa anthu onse akumva.+ Iwo anapeza kuti mʼbukumo analembamo kuti mbadwa iliyonse ya Amoni ndi ya Mowabu+ isamaloledwe kukhala mʼgulu la anthu a Mulungu woona,+ 2 chifukwa iwowa sanapatse Aisiraeli chakudya ndi madzi. Mʼmalomwake, analemba ganyu Balamu kuti awatemberere.+ Koma Mulungu wathu anasintha temberero limenelo kukhala dalitso.+ 3 Choncho atangomva Chilamulocho, anayamba kuchotsa anthu a mitundu ina pakati pa Aisiraeli.+

4 Zimenezi zisanachitike, wansembe amene ankayangʼanira zipinda zosungira katundu* mʼnyumba* ya Mulungu wathu+ anali Eliyasibu,+ ndipo anali wachibale wa Tobia.+ 5 Eliyasibu anapatsa Tobia chipinda chachikulu chosungira katundu.* Poyamba mʼchipindachi ankaikamo nsembe yambewu, lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda apageti ankayenera kulandira, komanso zimene ankapereka kwa ansembe.+

6 Nthawi yonseyi ine sindinali ku Yerusalemu, chifukwa mʼchaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Ndiyeno patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke kwakanthawi. 7 Kenako ndinafika ku Yerusalemu ndipo ndinaona zoipa zimene Eliyasibu+ anachita popatsa Tobia+ chipinda mʼbwalo la nyumba ya Mulungu woona. 8 Zimenezi zinandinyansa kwambiri. Choncho ndinataira panja katundu yense wa Tobia amene anali mʼchipinda chosungiramo zinthu.* 9 Zitatero ndinalamula kuti ayeretse zipinda zosungira katundu.* Kenako ndinabwezera pamalo pake ziwiya za mʼnyumba ya Mulungu+ woona komanso zopereka zambewu ndi lubani.+

10 Ndinazindikiranso kuti Alevi sankapatsidwa magawo awo, moti Alevi+ ndiponso oimba amene ankatumikira anachoka,+ ndipo aliyense anapita kumunda wake.+ 11 Choncho ndinadzudzula atsogoleriwo+ ndipo ndinawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani nyumba ya Mulungu woona yasiyidwa chonchi?”+ Kenako ndinawasonkhanitsa nʼkuwabwezera pa ntchito zawo. 12 Ayuda onse anabweretsa chakhumi+ cha mbewu, vinyo watsopano ndiponso mafuta kuzipinda zosungira katundu.+ 13 Ndiyeno ndinaika Selemiya wansembe, Zadoki wokopera Malemba* ndi Pedaya Mlevi, kuti aziyangʼanira zipinda zosungira katundu. Ndipo Hanani mwana wa Zakuri amene anali mwana wa Mataniya, anali wachiwiri wawo chifukwa anthuwa ankaonedwa kuti ndi okhulupirika. Iwowa anapatsidwa udindo wogawa zinthu kwa abale awo.

14 Mundikumbukire,+ inu Mulungu wanga, chifukwa cha zinthu zimenezi ndiponso chikondi chokhulupirika chimene ndinasonyeza chifukwa cha nyumba ya Mulungu wanga ndi zonse zochitika kumeneko.+

15 Masiku amenewo ndinaona anthu ku Yuda akuponda moponderamo mphesa pa tsiku la Sabata.+ Ankabweretsa mbewu ndipo ankazikweza pa abulu. Ankabweretsanso vinyo, mphesa, nkhuyu ndi katundu wosiyanasiyana ku Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+ Choncho ndinawadzudzula pa nkhani yogulitsa zinthu pa tsiku limenelo.* 16 Anthu a ku Turo amene ankakhala mumzindawu ankabweretsa nsomba ndi zinthu zosiyanasiyana nʼkumagulitsa kwa anthu a ku Yuda ndiponso mu Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+ 17 Choncho ndinadzudzula anthu olemekezeka a ku Yuda nʼkuwauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zoipa mpaka kufika poipitsa tsiku la Sabata? 18 Kodi izi si zimene makolo anu anachita, moti Mulungu wathu anabweretsa tsoka lonseli pa ife ndi mzindawu? Ndiye inu mukuchititsa kuti akwiyire kwambiri Aisiraeli poipitsa Sabata?”+

19 Ndiyeno mthunzi utafika pamageti a Yerusalemu, Sabata lisanayambe, ndinalamula kuti zitseko zitsekedwe. Ndinalamulanso kuti asatsegule zitsekozo mpaka Sabata litatha. Ndipo ndinaika mʼmageti atumiki anga ena kuti katundu aliyense asalowe pa tsiku la Sabata. 20 Choncho amalonda osiyanasiyana anagona panja pa Yerusalemu, mwinanso kawiri konse. 21 Kenako ndinawachenjeza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukugona kunja kwa mpanda? Mukachitanso zimenezi, ndidzachita kukuthamangitsani.” Kuyambira nthawi imeneyo sanabwerenso pa tsiku la Sabata.

22 Ndiyeno ndinauza Alevi kuti azidziyeretsa nthawi zonse komanso azibwera kudzalondera mageti a mzinda kuti tsiku la Sabata likhale loyera.+ Inu Mulungu wanga, mundikumbukirenso pa zimenezi ndipo mundichitire chifundo mogwirizana ndi kuchuluka kwa chikondi chanu chokhulupirika.+

23 Pa nthawi imeneyo ndinaonanso kuti Ayuda ena anali atakwatira akazi+ a Chiasidodi,+ a Chiamoni ndi a Chimowabu.+ 24 Hafu ya ana awo aamuna ankalankhula Chiasidodi ndipo hafu ina inkalankhula zilankhulo za anthu a mitundu ina koma panalibe amene ankatha kulankhula chilankhulo cha Ayuda. 25 Choncho ndinawadzudzula ndiponso kuwatemberera. Ena mwa amunawa ndinawamenya+ komanso kuwazula tsitsi ndipo ndinawalumbiritsa pamaso pa Mulungu kuti: “Musapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, ndipo musalole kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna kapenanso inuyo.+ 26 Kodi si akazi amenewa amene anachimwitsa Solomo mfumu ya Isiraeli? Pa mitundu yonse ya anthu panalibe mfumu yofanana ndi iye.+ Iye ankakondedwa ndi Mulungu wake,+ moti anamuika kukhala mfumu ya Aisiraeli onse. Koma akazi a mitundu ina anamuchimwitsa.+ 27 Nʼzodabwitsa kuti inunso mukuchita choipa chachikulu chimenechi, ndipo mukukwatira akazi a mitundu ina, zomwe nʼkusakhulupirika kwa Mulungu wathu.”+

28 Mmodzi mwa ana aamuna a Yoyada,+ mwana wa Eliyasibu,+ mkulu wa ansembe anali mkamwini wa Sanibalati+ wa ku Beti-horoni. Choncho ndinamuthamangitsa.

29 Inu Mulungu wanga, akumbukireni amenewa chifukwa anaipitsa unsembe+ ndiponso pangano limene munachita ndi ansembe ndi Alevi.+

30 Ndiyeno ndinawayeretsa ku zinthu zonse zodetsa za anthu a mitundu ina. Komanso ndinapereka ntchito kwa ansembe ndi Alevi, aliyense ndinamʼpatsa ntchito yake.+ 31 Ndinakonzanso zoti ena azibweretsa nkhuni+ pa nthawi zoikidwiratu ndiponso mbewu zoyamba kucha.

Inu Mulungu wanga, mundikumbukire pa zabwino zimene ndinachita.+

Dzinali limatanthauza “Ya Amatonthoza.”

Onani Zakumapeto B15.

Kapena kuti, “Susa.”

Nʼkutheka kuti chinali chigawo cha Yuda.

Kapena kuti, “amene munamuchenjeza.”

Onani Zakumapeto B15.

Kapena kuti, “a chakumtsinje wa Firate.”

Ena amati “mahosi.”

Mwina amenewa anali malo amene ankatchedwanso “Chitsime cha Eni-rogeli.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “analimbitsa manja awo.”

Ena amati “kabali” kapena “kapichi.”

Kapena kuti, “wa chakumtsinje wa Firate.”

Pafupifupi mamita 445. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “amʼchigawo chapafupi.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “maulendo 10.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ankaima kumbuyo.”

Kapena kuti, “Zikhale momwemo!”

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “pa zabwino.”

Onani Zakumapeto B15.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”

Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

“Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.

“Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “Zikhale momwemo!”

Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

Kapena kuti, “mlembi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zonona.”

Kapena kuti, “chimakupatsani mphamvu.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “kuyambira kalekale mpaka kalekale.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “malamulo odalirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “munalumbira mutakweza dzanja.”

Kapena kuti, “kukoma mtima kosatha.”

Kapena kuti, “Tirisata,” dzina la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Lumbiroli linkachititsa kuti munthu atembereredwe akapanda kulikwaniritsa.

Mbewu zimenezi mwina zinali tirigu kapena balere.

Mʼchilankhulo choyambirira, “gawo limodzi pa magawo atatu a sekeli.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “wapakachisi.”

Umenewu unali mkate wachionetsero.

Kapena kuti, “mʼzipinda zodyera.”

Kapena kuti, “zipinda zodyera.”

Kapena kuti, “zipinda zodyera.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “wapakachisi.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “anamanga misasa.”

Mabaibulo ena amati, “akamachita utumiki wawo.”

Zikuoneka kuti mʼMalemba a Chiheberi sanamutchule dzina.

Kapena kuti, “Ana a oimba ochita kuphunzitsidwawo.”

Chimenechi chinali chigawo cha Yorodano.

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “zipinda zodyera.”

Kapena kuti, “mʼkachisi.”

Kapena kuti, “chipinda chachikulu chodyera.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mʼchipinda chodyera.”

Kapena kuti, “zipinda zodyera.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Mabaibulo ena amati, “ndinawadzudzula pa tsiku limenelo pa nkhani yogulitsa zinthu.”

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani