Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Proverbs 1:1-31:31
  • Miyambo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Miyambo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Miyambo

MIYAMBO

1 Miyambi ya Solomo+ mwana wa Davide,+ mfumu ya Isiraeli:+

 2 Yothandiza munthu kuti apeze* nzeru+ ndi malangizo.*

Kuti amvetse mawu anzeru.

 3 Kuti apeze malangizo+ amene amathandiza munthu kuti akhale wozindikira,

Wachilungamo,+ wochita zinthu mwanzeru*+ komanso woona mtima.

 4 Yothandiza munthu wosadziwa zinthu kuti akhale wozindikira.+

Yothandiza wachinyamata kuti akhale wodziwa zinthu komanso kuti aziganiza bwino.+

 5 Munthu wanzeru amamvetsera ndipo amaphunzira zinthu zambiri.+

Munthu womvetsa zinthu amapeza malangizo anzeru+

 6 Omuthandiza kumvetsa mwambi komanso mawu ovuta kuwamvetsa,*

Mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko yawo.+

 7 Kuopa Yehova ndi chiyambi cha kudziwa zinthu.+

Zitsiru zokha ndi zimene zimanyoza nzeru komanso malangizo.+

 8 Mwana wanga, uzimvera malangizo a bambo ako,+

Ndipo usasiye kutsatira malangizo* a mayi ako.+

 9 Malangizowa ali ngati nkhata ya maluwa yokongola pamutu pako+

Komanso mkanda wokongola mʼkhosi mwako.+

10 Mwana wanga, anthu ochimwa akayesa kukunyengerera, usavomere.+

11 Akanena kuti: “Tiye tipitire limodzi.

Tiye tikabisalire anthu kuti tikakhetse magazi.

Tikabisale nʼkumadikirira anthu osalakwa kuti tiwaphe popanda chifukwa.

12 Tikawameza amoyo ngati mmene Manda* amachitira,

Tikawameza athunthu ngati amene akupita kudzenje.

13 Tiye tikawalande zinthu zawo zonse zamtengo wapatali.

Tidzaza nyumba zathu ndi zinthu zimene talanda anthu.

14 Tiye tipitire limodzi.*

Ndipo zinthu zimene tikabe, tidzagawana mofanana.”*

15 Mwana wanga, usawatsatire.

Mapazi ako asayende panjira yawo,+

16 Chifukwa mapazi awo amathamangira kukachita zoipa,

Amapita mofulumira kukakhetsa magazi.+

17 Ndithudi, kutchera ukonde mbalame ikuona nʼkopanda phindu.

18 Nʼchifukwa chake anthu ochimwawa amabisala kuti akhetse magazi a anthu.

Amabisala kuti achotse miyoyo ya anthu ena.

19 Izi ndi zimene anthu ofuna kupeza phindu mwachinyengo amachita,

Ndipo phindu limene apezalo lidzachotsa moyo wawo.+

20 Nzeru yeniyeni+ ikufuula mumsewu.+

Ikufuula mokweza mawu mʼmabwalo a mzinda.+

21 Ikufuula pamphambano ya* misewu yodutsa anthu ambiri.

Pamageti olowera mumzinda, ikunena kuti:+

22 “Inu anthu osadziwa zinthu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa zinthu mpaka liti?

Inu anthu onyoza, kodi mupitiriza kusangalala ndi kunyoza anthu mpaka liti?

Ndipo anthu opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+

23 Mverani kudzudzula kwanga.*+

Mukatero ndidzakukhuthulirani mzimu wanga.

Ndidzachititsa kuti mudziwe mawu anga.+

24 Chifukwa ine ndinaitana, koma inu munapitiriza kukana,

Ndinatambasula dzanja langa, koma palibe amene anafuna kuti ndimuthandize.+

25 Munapitiriza kunyalanyaza malangizo anga onse,

Komanso nditakudzudzulani munakana kusintha.

26 Inenso ndidzaseka tsoka likadzakugwerani.

Ndidzakunyogodolani zimene mumaopa zikadzabwera,+

27 Zimene mumaopa zikadzabwera ngati mvula yamkuntho,

Tsoka likadzafika ngati mphepo yamkuntho,

Ndiponso masautso ndi mavuto zikadzakugwerani.

28 Pa nthawi imeneyo azidzangondiitana koma sindidzayankha.

Adzayesetsa kundifunafuna koma sadzandipeza,+

29 Chifukwa chakuti anadana ndi kudziwa zinthu,+

Ndipo sanasankhe kuopa Yehova.+

30 Anakana malangizo anga.

Sanalemekeze mawu anga onse pamene ndinawadzudzula.

31 Choncho adzakumana ndi zotsatira* za zochita zawo,+

Ndipo mapulani awo adzawabweretsera* mavuto ambiri.

32 Chifukwa kupanduka kwa anthu osadziwa zinthu kudzawaphetsa,

Ndipo mphwayi za anthu opusa zidzawawonongetsa.

33 Koma munthu wondimvera adzakhala motetezeka+

Ndipo sadzasokonezeka chifukwa choopa tsoka.”+

2 Mwana wanga, ukamvera mawu anga

Ndi kusunga malamulo anga+ ngati chuma chamtengo wapatali,

 2 Potchera khutu lako kuti umvetsere mawu anzeru+

Ndiponso kutsegula mtima wako kuti ukhale wozindikira,+

 3 Komanso ukapempha kuti ukhale womvetsa zinthu+

Ndi kuchonderera kuti ukhale wozindikira,+

 4 Ukapitiriza kuzifunafuna ngati siliva,+

Ndi kuzifufuza ngati chuma chobisika,+

 5 Udzamvetsa tanthauzo la kuopa Yehova+

Ndipo udzamudziwadi Mulungu.+

 6 Chifukwa Yehova ndi amene amapereka nzeru.+

Kudziwa zinthu komanso kuzindikira zimatuluka mʼkamwa mwake.

 7 Anthu owongoka mtima, amawasungira nzeru zopindulitsa.

Iye ndi chishango kwa anthu amene amachita zinthu mokhulupirika.+

 8 Amayangʼanira njira za anthu amene amachita zachilungamo,

Ndipo adzateteza njira ya anthu ake okhulupirika.+

 9 Ukachita zimenezi udzamvetsa zinthu zolungama, zolondola komanso zabwino.

Udzamvetsa njira yabwino yoyenera kuyendamo.+

10 Nzeru zikalowa mumtima mwako,+

Ndipo kudziwa zinthu kukakhala kosangalatsa kwa iwe,+

11 Kuganiza bwino kudzakuyangʼanira,+

Ndipo kuzindikira kudzakuteteza,

12 Kuti zikupulumutse kunjira yoipa,

Komanso kwa munthu wolankhula zinthu zopotoka,+

13 Kwa anthu amene amasiya njira zowongoka

Kuti ayende mʼnjira zamdima.+

14 Zidzakupulumutsanso kwa anthu amene amasangalala akamachita zoipa,

Amene amakondwera ndi zinthu zoipa komanso zachinyengo,

15 Amene njira zawo ndi zokhota

Ndiponso amene zochita zawo zonse ndi zachinyengo.

16 Nzeru zidzakupulumutsa kwa mkazi wamakhalidwe oipa.*

Zidzakupulumutsa ku mawu okopa a mkazi wachiwerewere,*+

17 Amene amasiya mnzake wapamtima* wapachitsikana chake+

Ndiponso amene amaiwala pangano limene anachita ndi Mulungu wake.

18 Chifukwa kupita kunyumba yake kuli ngati kupita kokafa,

Ndipo njira yopita kunyumba yake ndi njira yakumanda.+

19 Onse ogona naye* sadzabwerera

Ndipo sadzapezanso njira zopita kumoyo.+

20 Choncho uziyenda mʼnjira za anthu abwino

Ndipo upitirize kuyenda mʼnjira za anthu olungama,+

21 Chifukwa owongoka mtima okha ndi amene adzakhale padziko lapansi,

Ndipo opanda cholakwa* ndi amene adzatsalemo.+

22 Koma anthu oipa adzachotsedwa padziko lapansi+

Ndipo achinyengo adzazulidwamo.+

3 Mwana wanga, usaiwale zimene ndimakuphunzitsa,*

Ndipo mtima wako uzisunga malamulo anga.

 2 Ukamachita zimenezi, udzakhala ndi masiku ochuluka

Komanso moyo wazaka zambiri ndi mtendere.+

 3 Usalole kuti chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika* zichoke mwa iwe.+

Uzimange mʼkhosi mwako

Ndi kuzilemba pamtima pako.+

 4 Ukachita zimenezi, Mulungu ndi anthu+

Adzakukomera mtima ndipo adzakuona kuti ndiwe wozindikira.

 5 Uzikhulupirira Yehova+ ndi mtima wako wonse,

Ndipo usamadalire* luso lako lomvetsa zinthu.+

 6 Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse,+

Ndipo iye adzawongola njira zako.+

 7 Usamadzione kuti ndiwe wanzeru.+

Uziopa Yehova ndi kupatuka pa choipa.

 8 Zimenezi zidzachiritsa thupi lako*

Ndi kutsitsimutsa mafupa ako.

 9 Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali+

Ndiponso ndi zipatso zako zonse zoyambirira.*+

10 Ukatero nyumba zako zosungiramo zinthu zidzadzaza kwambiri,+

Ndipo zoponderamo mphesa zako zidzasefukira ndi vinyo watsopano.

11 Mwana wanga, usakane malangizo* a Yehova+

Ndipo usanyansidwe ndi kudzudzula kwake,+

12 Chifukwa Yehova amadzudzula munthu amene amamukonda,+

Ngati mmene bambo amadzudzulira mwana amene amasangalala naye.+

13 Wosangalala ndi munthu amene amapeza nzeru,+

Ndiponso munthu amene amaphunzira zinthu zimene zingamuthandize kukhala wozindikira.

14 Chifukwa kupeza nzeru nʼkwabwino kuposa kupeza siliva,

Ndipo kukhala nazo monga phindu nʼkwabwino kuposa kukhala ndi golide.+

15 Nʼzamtengo wapatali kuposa miyala ya korali,*

Palibe chimene umalakalaka chimene chingafanane nazo.

16 Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali.

Mʼdzanja lake lamanzere muli chuma ndi ulemerero.

17 Kuyenda mʼnjira zake kumasangalatsa,

Ndipo kuyenda mʼmisewu yake kumabweretsa mtendere.+

18 Munthu akagwiritsitsa nzeru, zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye,

Ndipo anthu amene amazigwiritsitsa adzatchedwa osangalala.+

19 Yehova anayala maziko a dziko lapansi mwanzeru.+

Anakhazikitsa kumwamba mozindikira.+

20 Chifukwa chakuti iye amadziwa zinthu, anagawa madzi akuya

Ndipo kumwamba kwa mitambo kunagwetsa mame.+

21 Mwana wanga, zimenezi* zisachoke pamaso pako.

Uteteze nzeru zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.

22 Zidzakupatsa moyo

Komanso zidzakhala zokongoletsera mʼkhosi mwako.

23 Ukatero udzayenda panjira yako popanda chokuopseza,

Ndipo phazi lako silidzapunthwa.*+

24 Ukagona sudzaopa chilichonse.+

Udzagona ndithu, ndipo tulo tako tidzakhala tokoma.+

25 Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi,+

Kapena mphepo yamkuntho imene ikubwera pa oipa.+

26 Chifukwa uzidzadalira kwambiri Yehova,+

Ndipo adzateteza phazi lako kuti lisakodwe.+

27 Usalephere kuchitira zabwino anthu amene ukuyenera kuwachitira* zabwinozo,+

Ngati ungathe kuwathandiza.*+

28 Mnzako usamuuze kuti, “Pita, ukabwerenso mawa ndipo ndidzakupatsa,”

Ngati ungathe kumupatsa nthawi yomweyo.

29 Usakonze zochitira mnzako zoipa+

Pamene iye akuona kuti akukhala nawe mwamtendere.

30 Usakangane ndi munthu popanda chifukwa+

Ngati sanakuchitire choipa chilichonse.+

31 Usasirire munthu wachiwawa+

Kapena kusankha kuyenda mʼnjira yake iliyonse,

32 Chifukwa Yehova amanyansidwa ndi munthu wachiphamaso,+

Koma anthu owongoka mtima amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.+

33 Yehova amatemberera banja la munthu woipa,+

Koma iye amadalitsa nyumba ya munthu wolungama.+

34 Onyoza, iye amawanyoza,+

Koma ofatsa amawakomera mtima.+

35 Anzeru adzalandira ulemu,

Koma opusa amalemekeza zinthu zimene zidzawachititse manyazi.+

4 Ana anga, mverani malangizo* a bambo anu.+

Mvetserani kuti mupeze luso lomvetsa zinthu,

 2 Chifukwa ndidzakupatsani malangizo abwino.

Musasiye kutsatira zimene ndimakuphunzitsani.*+

 3 Ndinali mwana wabwino kwambiri kwa bambo anga+

Ndipo mayi anga ankandikonda kwambiri.+

 4 Bambo anga ankandiphunzitsa kuti: “Mtima wako ugwire mwamphamvu mawu anga.+

Uzisunga malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+

 5 Upeze nzeru, upezenso luso lomvetsa zinthu.+

Usaiwale ndipo usapatuke pa zimene ndimakuuza.

 6 Nzeruzo usazisiye ndipo zidzakuteteza.

Uzikonde ndipo zidzakuteteza.

 7 Nzeru ndi chinthu chofunika kwambiri,+ choncho upeze nzeru,

Ndipo pa zinthu zonse zimene upeze, upezenso luso lomvetsa zinthu.+

 8 Uzilemekeze kwambiri ndipo zidzakukweza.+

Zidzakulemekeza chifukwa chakuti wazikumbatira.+

 9 Zidzaika nkhata yamaluwa yokongola kumutu kwako.

Zidzakuveka chisoti chachifumu chokongola.”

10 Tamvera mwana wanga, ndipo utsatire mawu anga.

Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka.+

11 Ndidzakutsogolera mʼnjira ya nzeru.+

Ndidzakutsogolera mʼnjira zowongoka.+

12 Ukamayenda, mapazi ako sadzapanikizika.

Ndipo ngati ukuthamanga sudzapunthwa.

13 Gwira mwamphamvu malangizo ndipo usawasiye.+

Uwasunge bwino chifukwa iwo ndi moyo wako.+

14 Usatengere zochita za anthu oipa,

Ndipo usayende panjira ya anthu oipa.+

15 Uipewe, usayende mʼnjirayo.+

Upatukepo ndipo uilambalale.+

16 Chifukwa iwo sangagone mpaka atachita zoipa.

Tulo sitiwabwerera mpaka atachititsa kuti wina agwe.

17 Amadya chakudya chimene achipeza chifukwa chochita zoipa,

Ndipo amamwa vinyo amene amupeza chifukwa chochita chiwawa.

18 Koma njira ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kwa mʼmawa

Kumene kumawonjezereka mpaka kunja kutawala kwambiri.+

19 Njira ya oipa ili ngati mdima.

Iwo sadziwa chimene chimawapunthwitsa.

20 Mwana wanga, tchera khutu ku mawu anga.

Mvetsera mosamala* zonena zanga.

21 Zisachoke pamaso pako.

Uzisunge mkati mwa mtima wako.+

22 Chifukwa amene amazipeza adzakhala ndi moyo+

Ndipo thupi lawo lonse lidzakhala lathanzi.

23 Uteteze mtima wako kuposa zinthu zonse zimene umaziteteza,+

Chifukwa mumtimamo ndi mmene muli akasupe a moyo.

24 Usamalankhule mawu abodza,+

Ndipo usamanene zinthu zimene si zoona.

25 Maso ako aziyangʼana patsogolo.

Inde, uziyangʼanitsitsa* zinthu zimene zili patsogolo pako.+

26 Salaza* njira imene phazi lako likuyenda,+

Ndipo njira zako zonse zidzakhala zotetezeka.

27 Usakhotere kudzanja lamanja kapena lamanzere.+

Phazi lako lipatuke pa zinthu zoipa.

5 Mwana wanga, tchera makutu ako ku mawu anga anzeru.

Mvetsera mosamala zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kukhala wozindikira,+

 2 Kuti uteteze luso lako loganiza bwino,

Ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+

 3 Chifukwa milomo ya mkazi wamakhalidwe oipa* imakha uchi ngati chisa cha njuchi,+

Ndipo mʼkamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+

 4 Koma pamapeto pake amawawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+

Ndipo amakhala wakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+

 5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.

Miyendo yake imalowera ku Manda.*

 6 Iye saganizira zimene zingamuthandize kukapeza moyo.

Amangoyendayenda, osadziwa kumene akulowera.

 7 Tsopano mwana wanga,* ndimvere,

Ndipo usapatuke pa zimene ndikukuuza.

 8 Ukhale kutali kwambiri ndi iye.

Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+

 9 Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+

Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+

10 Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+

Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo.

11 Ukapanda kumvera, udzabuula kumapeto kwa moyo wako,

Mphamvu zako zikadzatha komanso ukadzawonda kwambiri.+

12 Ndipo udzanena kuti: “Ndinkadana ndi malangizo* ine!

Ndipo mtima wanga sunkamvera, ena akandidzudzula.

13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,

Kapena kutchera khutu kwa aphunzitsi anga.

14 Ndangotsala pangʼono kutheratu

Pakati pa mpingo wonse.”*+

15 Imwa madzi ochokera mʼchitsime chako,

Komanso madzi oyenderera kuchokera pakasupe wako.+

16 Kodi akasupe ako amwazike panja?

Ndipo kodi mitsinje yako ya madzi imwazike mʼmabwalo amumzinda?+

17 Zimenezi zikhale zako zokha

osati uzigawana ndi anthu achilendo.+

18 Kasupe wako akhale wodalitsidwa,*

Ndipo uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.+

19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yachikondi komanso ngati kamwana ka mbuzi zamʼmapiri kokongola.+

Mabere ake azikukhutiritsa* nthawi zonse.

Chikondi chake chizikusangalatsa kwambiri nthawi zonse.+

20 Ndiye mwana wanga, kodi pali chifukwa chilichonse choti uzisangalalira ndi mkazi wamakhalidwe oipa,*

Kapena choti uzikumbatirira chifuwa cha mkazi wachiwerewere?*+

21 Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,

Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+

22 Woipa amakodwa ndi zolakwa zake zomwe,

Ndipo adzamangidwa ndi zingwe za tchimo lake lomwe.+

23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,

Ndipo adzasochera chifukwa cha kuchuluka kwa uchitsiru wake.

6 Mwana wanga, ngati walonjeza kuti udzapereka ngongole ya mnzako iye akadzalephera kubweza,+

Ngati wagwirana dzanja ndi mlendo pochita mgwirizano,+

 2 Ngati wakodwa ndi lonjezo limene unapanga,

Ngati wagwidwa ndi mawu amʼkamwa mwako,+

 3 Uchite izi mwana wanga kuti udzipulumutse,

Chifukwa uli mʼmanja mwa mnzako:

Pita ukadzichepetse ndipo ukamuchonderere kwambiri mnzakoyo.+

 4 Usalole kuti maso ako agone,

Kapena kuti zikope zako ziwodzere.

 5 Dzipulumutse ngati insa mʼmanja mwa wosaka,

Ndiponso ngati mbalame mʼmanja mwa wosaka mbalame.

 6 Pita kwa nyerere waulesi iwe,+

Ukaone mmene imachitira zinthu kuti ukhale wanzeru.

 7 Ngakhale kuti ilibe mtsogoleri, kapitawo, kapena wolamulira,

 8 Imakonza chakudya chake mʼchilimwe,+

Ndipo imasonkhanitsa chakudya chake pa nthawi yokolola.

 9 Kodi waulesi iwe, ugona pamenepo mpaka liti?

Kodi udzuka nthawi yanji kutulo tako?

10 Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,

Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,+

11 Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,

Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

12 Munthu wopanda pake komanso woipa, amangoyendayenda nʼkumalankhula mabodza.+

13 Amatsinzinira ena diso lake,+ amachita zizindikiro ndi phazi lake ndiponso amachita zizindikiro ndi zala zake.

14 Popeza mtima wake ndi wachinyengo,

Nthawi zonse amakonza ziwembu+ komanso amakhalira kuyambanitsa anthu.+

15 Choncho tsoka lake lidzabwera mwadzidzidzi.

Adzathyoledwa modzidzimutsa moti sadzachira.+

16 Pali zinthu 6 zimene Yehova amadana nazo.

Zilipo zinthu 7 zimene amanyansidwa nazo:

17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja amene amakhetsa magazi a anthu osalakwa,+

18 Mtima umene umakonza ziwembu,+ mapazi othamangira kukachita zoipa,

19 Mboni yachinyengo imene nthawi zonse imanena mabodza,+

Komanso aliyense amene amayambitsa mikangano pakati pa abale.+

20 Mwana wanga, uzitsatira malamulo a bambo ako,

Ndipo usasiye kutsatira malangizo* a mayi ako.+

21 Uwamange pamtima pako nthawi zonse

Ndipo uwamange mʼkhosi mwako.

22 Ukamayenda adzakutsogolera.

Ukamagona adzakulondera.

Ndipo ukadzuka, adzakuuza zochita.*

23 Chifukwa lamulolo ndi nyale,+

Ndipo malangizo ndi kuwala,+

Komanso kudzudzula kumene kumathandiza munthu kusintha ndi njira yakumoyo.+

24 Zidzakuteteza kwa mkazi woipa,+

Komanso ku lilime lokopa la mkazi wachiwerewere.*+

25 Usasirire kukongola kwake mumtima mwako.+

Kapena kulola kuti ukopeke ndi maso ake achikoka,

26 Munthu amafika potsala ndi mkate umodzi wokha chifukwa cha hule,+

Koma mkazi wa mwini amasaka moyo wako wamtengo wapatali.

27 Kodi munthu anganyamule makala a moto pachifuwa pake, zovala zake osapsa?+

28 Kapena kodi munthu angayende pamakala a moto, mapazi ake osapsa?

29 Nʼchimodzimodzi ndi aliyense wogona ndi mkazi wa mnzake.

Aliyense wokhudza mkaziyo adzalangidwa.+

30 Anthu sanyoza munthu wakuba

Ngati waba kuti apeze chakudya pamene ali ndi njala.

31 Koma akapezeka, adzabweza zinthuzo kuwirikiza ka 7.

Adzapereka zinthu zonse zamtengo wapatali zamʼnyumba mwake.+

32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*

Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+

33 Adzangodzivulaza yekha ndipo anthu adzamunyoza,+

Moti kunyozeka kwake sikudzafufutika.+

34 Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.

Pomubwezera sadzamva chisoni.+

35 Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,*

Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.

7 Mwana wanga, usunge mawu anga

Ndipo uziona kuti malamulo anga ndi amtengo wapatali.+

 2 Usunge malamulo anga kuti upitirize kukhala ndi moyo.+

Uteteze malangizo* anga ngati mwana wa diso lako.

 3 Uwamange kuzala zako,

Ndipo uwalembe pamtima pako.+

 4 Nzeru uiuze kuti: “Ndiwe mchemwali wanga,”

Ndipo kumvetsa zinthu ukutche “mʼbale wanga,”

 5 Kuti zikuteteze kwa mkazi wamakhalidwe oipa,*+

Ndiponso kwa mkazi wachiwerewere* wolankhula mawu okopa.+

 6 Ndinayangʼana pansi

Kuchokera pawindo la nyumba yanga,

 7 Ndipo pamene ndinkayangʼanitsitsa anthu osadziwa zinthu,

Ndinazindikira kuti pakati pa achinyamata pali mnyamata wina wopanda nzeru.*+

 8 Iye ankadutsa mumsewu pafupi ndi mphambano,

Ndipo ankalowera kunyumba ya mkaziyo

 9 Pa nthawi yamadzulo kuli kachisisira,+

Kutatsala pangʼono kuda.

10 Kenako ndinaona mkazi akubwera kudzakumana naye,

Atavala ngati hule+ ndipo anali ndi mtima wachinyengo.

11 Ndi wolongolola ndiponso wamakani.+

Ndipo sakhala pakhomo.*

12 Pasanapite nthawi amapezeka kuti ali panja, kenako amapezeka mʼmabwalo a mzinda,

Amadikirira anthu pafupi ndi mphambano iliyonse.+

13 Iye wagwira mnyamatayo nʼkumupatsa kisi.

Mʼmaso muli gwaa! akumuuza kuti:

14 “Ndinayenera kupereka nsembe zamgwirizano.+

Lero ndakwaniritsa zimene ndinalonjeza.

15 Nʼchifukwa chake ndabwera kudzakumana nawe,

Kudzakufunafuna ndipo ndakupeza.

16 Ndayala zofunda zabwino pabedi panga,

Nsalu za ku Iguputo zokongola kwambiri.*+

17 Ndawaza pabedi panga zonunkhiritsa za mule, aloye ndi sinamoni.+

18 Bwera tisonyezane chikondi mpaka mʼmawa ndipo chitikwane.

Tiye tisangalatsane pochita zachikondi,

19 Chifukwa mwamuna wanga sali panyumba.

Iye wachoka, wapita kutali.

20 Wanyamula chikwama cha ndalama,

Ndipo adzabwera kunyumba tsiku limene mwezi udzaoneke wathunthu.”

21 Wasocheretsa mnyamatayo pochita zinthu zambiri zomukopa.+

Wamunyengerera ndi mawu okopa.

22 Mwadzidzidzi mnyamatayo akuyamba kulondola mkaziyo, ngati ngʼombe yamphongo imene ikupita kukaphedwa,

Ndiponso ngati munthu wopusa amene akuyenera kulangidwa pomuika mʼmatangadza.+

23 Iye akulondola mkaziyo mpaka muvi utaboola chiwindi chake,

Ngati mbalame imene ikuthamangira kumsampha ndipo sakudziwa kuti zichititsa kuti ataye moyo wake.+

24 Choncho ana anga, ndimvereni.

Mvetserani mawu amene ndikukuuzani.

25 Musalole kuti mtima wanu upatukire kunjira zake.

Musasochere nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zake,+

26 Chifukwa mkaziyo waphetsa anthu ambiri,+

Ndipo amene aphedwa ndi iyeyo ndi osawerengeka.+

27 Nyumba yake ndi njira yopita ku Manda.*

Imatsikira kuzipinda za imfa.

8 Nzerutu ikuitana,

Ndipo kuzindikira kukufuula.+

 2 Imaima pamalo okwera+ mʼmbali mwa msewu.

Imaima pamphambano za misewu.

 3 Pambali pa mageti, olowera mumzinda,

Pakhomo lolowera mumzindawo,

Ikungokhalira kufuula mokweza kuti:+

 4 “Ndikuitana anthu inu.

Ndikulankhula ndi nonsenu* mokweza.

 5 Inu osadziwa zinthu, phunzirani kukhala ochenjera.+

Opusa inu, khalani ndi mtima womvetsa zinthu.*

 6 Mvetserani, chifukwa zimene ndikulankhula ndi zofunika.

Pakamwa panga pamalankhula zinthu zabwino.

 7 Chifukwa pakamwa panga pamalankhula choonadi motsitsa,

Ndipo milomo yanga imanyansidwa ndi zoipa.

 8 Mawu onse otuluka pakamwa panga ndi olungama.

Pa mawu onsewo palibe abodza kapena achinyengo.

 9 Ndi osavuta kumva kwa munthu wozindikira

Komanso ndi olondola kwa anthu odziwa zinthu.

10 Landirani malangizo* anga osati siliva,

Komanso kudziwa zinthu mʼmalo mwa golide woyenga bwino kwambiri,+

11 Chifukwa nzeru ndi zabwino kwambiri kuposa miyala ya korali.*

Zinthu zina zonse zamtengo wapatali sizingafanane nazo.

12 Ine nzeru, ndimakhala pamodzi ndi kuchenjera.

Ndimadziwa zinthu ndiponso ndimatha kuganiza bwino.+

13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+

Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso mawu achinyengo.+

14 Ine ndili ndi malangizo abwino komanso nzeru zothandiza.+

Kumvetsa zinthu+ ndiponso mphamvu+ ndi zanga.

15 Chifukwa cha ine, mafumu amalamulira,

Ndipo akuluakulu a boma amakhazikitsa malamulo olungama.+

16 Chifukwa cha ine, akalonga amalamulira,

Ndipo anthu olemekezeka amaweruza mwachilungamo.

17 Ndimakonda amene amandikonda,

Ndipo amene akundifunafuna adzandipeza.+

18 Chuma ndi ulemerero zili ndi ine,

Ndili ndi chuma* chosatha komanso chilungamo.

19 Zimene munthu amapeza kwa ine nʼzabwino kuposa golide, ngakhale golide woyengedwa bwino kwambiri,

Ndipo mphatso zimene ndimapereka nʼzabwino kuposa siliva wabwino kwambiri.+

20 Ndimayenda mʼnjira yachilungamo,

Komanso pakati pa misewu yachilungamo.

21 Anthu amene amandikonda, ndimawapatsa cholowa chamtengo wapatali,

Ndipo ndimadzazitsa nyumba zawo zosungiramo zinthu.

22 Ine ndinali woyamba kulengedwa ndi Yehova,+

Ndinali woyambirira pa zinthu zonse zimene anapanga kalekale kwambiri.+

23 Ndinakhazikitsidwa kale kwambiri,*+

Kuyambira pachiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe.+

24 Ndinabadwa kulibe madzi akuya,*+

Kulibe akasupe osefukira madzi.

25 Mapiri asanaikidwe mʼmalo ake,

Komanso mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinabadwa,

26 Iye asanapange dziko lapansi ndi nthaka yake,

Kapena zibuma zoyamba za dothi lapadziko lapansi.

27 Pamene ankakonza kumwamba, ine ndinali pomwepo.+

Pamene ankaika malire pakati pa mlengalenga ndi nyanja,+

28 Pamene ankakhazikitsa* mitambo kumwamba,

Pamene ankakhazikitsa akasupe a madzi akuya,

29 Pamene ankaikira nyanja lamulo

Kuti madzi ake asapitirire pamene anawalamula,+

Pamene ankakhazikitsa maziko a dziko lapansi,

30 Pa nthawi imeneyo, ine ndinali pambali pake monga mmisiri waluso.+

Iye ankasangalala kwambiri ndi ine+ tsiku ndi tsiku.

Ndinkakhala wosangalala pamaso pake nthawi zonse.+

31 Ndinkasangalala ndi dziko lapansi limene anakonza kuti anthu azikhalamo,

Ndipo ana a anthu ndi amene ankandisangalatsa kwambiri.*

32 Tsopano ana anga, ndimvereni.

Ndithu, osangalala ndi amene amayenda mʼnjira zanga.

33 Mverani malangizo+ kuti mukhale anzeru,

Ndipo musamawanyalanyaze.

34 Wosangalala ndi munthu amene amandimvetsera

Pobwera mʼmamawa kwambiri pakhomo la nyumba yanga tsiku lililonse,*

Podikirira pafupi ndi khomo lolowera mʼnyumba mwanga.

35 Chifukwa wondipeza ine adzapeza moyo,+

Ndipo Yehova amasangalala naye.

36 Koma amene amandinyalanyaza amadzipweteka yekha,

Ndipo amene amadana ndi ine amakonda imfa.”+

9 Nzeru yeniyeni yamanga nyumba yake.

Yasema zipilala zake 7.

 2 Yakonza bwinobwino nyama yake,*

Yasakaniza vinyo wake.

Yayalanso patebulo pake.

 3 Yatuma antchito ake aakazi

Kuti apite pamalo okwera amumzinda kukaitana anthu kuti:+

 4 “Aliyense wosadziwa zinthu abwere kuno.”

Aliyense wopanda nzeru, nzeru ikumuuza kuti:

 5 “Bwera udzadye chakudya changa

Ndipo udzamwe nawo vinyo amene ndasakaniza.

 6 Leka kukhala munthu wosadziwa zinthu kuti upitirize kukhala ndi moyo.+

Lola kuti kumvetsa zinthu kukutsogolere.”+

 7 Amene amalangiza wonyoza amachititsidwa manyazi,+

Ndipo aliyense wodzudzula woipa adzavulazidwa.

 8 Usadzudzule wonyoza chifukwa angadane nawe.+

Dzudzula munthu wanzeru ndipo adzakukonda.+

 9 Pereka malangizo kwa munthu wanzeru ndipo adzawonjezera nzeru zake.+

Phunzitsa munthu wolungama ndipo adzapitiriza kuphunzira.

10 Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru,+

Ndipo ngati ungadziwe Mulungu, yemwe ndi Woyera Koposa,+ udzakhala womvetsa zinthu.

11 Chifukwa ine ndidzachulukitsa masiku a moyo wako,+

Ndipo ndidzawonjezera zaka za moyo wako.

12 Ukakhala wanzeru, iweyo ndi amene umapindula ndi nzeruzo,

Koma ngati ndiwe wonyoza, iweyo ndi amene udzavutike.

13 Mkazi wopusa amakhala wolongolola.+

Iye ndi woperewera nzeru ndipo sadziwa chilichonse.

14 Amakhala pampando pakhomo la nyumba yake

Pamalo okwera amumzinda,+

15 Nʼkumaitana anthu odutsa

Amene akungodziyendera panjira kuti:

16 “Aliyense amene ali wosadziwa zinthu abwere kuno.”

Aliyense wopanda nzeru, mkaziyo akumuuza kuti:+

17 “Madzi akuba amatsekemera,

Ndipo chakudya chodya mobisa chimakoma.”+

18 Koma mwamunayo sakudziwa kuti kumeneko kuli akufa,

Ndiponso kuti alendo a mkaziyo ali mʼdzenje la Manda.*+

10 Miyambi ya Solomo.+

Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+

Koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.

 2 Chuma chimene munthu wapeza chifukwa chochita zoipa chidzakhala chopanda phindu,

Koma chilungamo nʼchimene chimapulumutsa munthu ku imfa.+

 3 Yehova sadzachititsa kuti munthu wolungama akhale ndi njala,+

Koma anthu oipa sadzawapatsa zimene amalakalaka.

 4 Munthu waulesi adzakhala wosauka,+

Koma wogwira ntchito mwakhama adzalemera.+

 5 Mwana wochita zinthu mozindikira amatuta zokolola mʼchilimwe,

Koma mwana wochititsa manyazi amakhala ali mʼtulo tofa nato pa nthawi yokolola.+

 6 Madalitso amapita pamutu pa munthu wolungama,+

Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.

 7 Zabwino zimene munthu wolungama ankachita zikakumbukiridwa* amadalitsidwa,+

Koma dzina la anthu oipa lidzawola.+

 8 Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malangizo,*+

Koma wolankhula mopusa adzapeza mavuto.+

 9 Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzakhala wotetezeka,+

Koma munthu wochita zinthu mwachinyengo adzadziwika.+

10 Munthu amene amatsinzinira ena diso amachititsa ena kumva chisoni,+

Ndipo amene amalankhula mopusa adzapeza mavuto.+

11 Pakamwa pa wolungama pamachokera moyo,+

Koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+

12 Chidani nʼchimene chimayambitsa mikangano,

Koma chikondi chimaphimba machimo onse.+

13 Nzeru imapezeka pamilomo ya munthu wozindikira,+

Koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru.+

14 Anzeru ndi amene amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+

Koma pakamwa pa wopusa pamachititsa kuti awonongedwe.+

15 Munthu wolemera amaona kuti chuma chake chili* ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.

Koma anthu osauka amavutika chifukwa cha umphawi wawo.+

16 Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.

Koma zochita za woipa zimabweretsa tchimo.+

17 Amene amamvera malangizo* amathandiza ena kukapeza moyo,*

Koma amene amanyalanyaza chidzudzulo amasocheretsa ena.

18 Munthu amene amabisa chidani mumtima mwake amalankhula mabodza,+

Ndipo amene amafalitsa mphekesera zoipa ndi wopusa.

19 Mawu akachuluka sipalephera kukhala zolakwika,+

Koma amene amalamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+

20 Lilime la wolungama lili ngati siliva wabwino kwambiri,+

Koma mtima wa woipa ndi wopanda phindu.

21 Milomo ya wolungama imathandiza* anthu ambiri,+

Koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru.+

22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa munthu,+

Ndipo popereka madalitsowa Mulungu sawonjezerapo ululu.*

23 Kwa munthu wopusa, kuchita khalidwe lochititsa manyazi kuli ngati masewera,

Koma munthu wozindikira amakhala ndi nzeru.+

24 Chinthu chimene munthu woipa amaopa nʼchimene chidzamuchitikire,

Koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+

25 Mphepo yamkuntho ikawomba woipa amawonongedwa,+

Koma wolungama ali ngati maziko mpaka kalekale.+

26 Viniga* amachititsa kuti mano ayezimire ndipo utsi umapweteka mʼmaso,

Izi nʼzimene munthu waulesi amachita kwa munthu amene wamutuma.*

27 Kuopa Yehova kumatalikitsa moyo,+

Koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+

28 Zimene anthu olungama akuyembekezera zimasangalatsa,*+

Koma chiyembekezo cha anthu oipa sichidzakwaniritsidwa.+

29 Njira ya Yehova ndi malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+

Koma anthu ochita zoipa amawonongedwa mʼnjira imeneyi.+

30 Wolungama sadzagwetsedwa,+

Koma anthu oipa sadzakhalanso padziko lapansi.+

31 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula* zanzeru,

Koma lilime lolankhula zinthu zopotoka lidzadulidwa.

32 Milomo ya munthu wolungama imadziwa zinthu zosangalatsa,

Koma pakamwa pa anthu oipa mʼpachinyengo.

11 Yehova amanyasidwa ndi masikelo achinyengo,

Koma sikelo imene imayeza molondola imamusangalatsa.*+

 2 Kudzikweza kukafika manyazi amafikanso,+

Koma anthu odzichepetsa ndi amene ali ndi nzeru.+

 3 Kukhulupirika kwa anthu owongoka mtima nʼkumene kumawatsogolera,+

Koma wochita zinthu mwachinyengo adzawonongedwa chifukwa cha mabodza ake.+

 4 Chuma chidzakhala chopanda* phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+

Koma chilungamo nʼchimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+

 5 Chilungamo cha munthu wopanda cholakwa chimawongola njira yake,

Koma woipa adzagwa chifukwa cha kuipa kwake komwe.+

 6 Chilungamo cha anthu owongoka mtima chidzawapulumutsa,+

Koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+

 7 Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimathera pomwepo,

Ndipo zonse zimene amayembekezera kuchita ndi mphamvu zake zimalephereka.+

 8 Wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,

Ndipo mʼmalo mwake woipa ndi amene amakumana ndi mavutowo.+

 9 Wampatuko* amawononga mnzake ndi pakamwa pake,

Koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+

10 Mzinda umasangalala chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,

Ndipo anthu oipa akawonongedwa anthu amafuula mosangalala.+

11 Mzinda umakhala wapamwamba chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+

Koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+

12 Aliyense wopanda nzeru amasonyeza kuti akuipidwa ndi* mnzake,

Koma munthu amene alidi wozindikira amakhala chete.+

13 Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi za anzake,+

Koma munthu wokhulupirika* amasunga chinsinsi.*

14 Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.

Koma zinthu zimayenda bwino* ngati pali alangizi* ambiri.+

15 Munthu amene amalonjeza kuti adzapereka ngongole ya munthu wachilendo mwiniwakeyo akadzalephera kubweza, zinthu sizidzamuyendera bwino.+

Koma amene amapewa* kugwirana dzanja pochita mgwirizano adzakhala wotetezeka.

16 Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+

Koma anthu ankhanza amalanda chuma cha ena.

17 Munthu wokoma mtima* zinthu zimamuyendera bwino,*+

Koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.*+

18 Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+

Koma wofesa chilungamo amalandira mphoto yeniyeni.+

19 Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+

Koma munthu wofunafuna zoipa adzafa.

20 Anthu amtima wopotoka, Yehova amanyasidwa nawo,+

Koma amene amachita zinthu mosalakwitsa kanthu amamusangalatsa.+

21 Musakaikire mfundo yakuti:* Munthu woipa sadzalephera kulangidwa,+

Koma ana a anthu olungama adzapulumuka.

22 Mofanana ndi ndolo yagolide imene ili pamphuno ya nkhumba,

Ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola amene amakana nzeru.

23 Zimene munthu wolungama amalakalaka zimakhala ndi zotsatira zabwino.+

Koma zimene oipa amayembekezera zimabweretsa mkwiyo woopsa.

24 Munthu amapereka mowolowa manja* ndipo pamapeto pake amakhala ndi zinthu zochuluka.+

Munthu wina amaumira zimene amafunika kupatsa anthu ena, koma amasauka.+

25 Munthu wopereka mowolowa manja zinthu zidzamuyendera bwino,*+

Ndipo amene amatsitsimula ena* nayenso adzatsitsimulidwa.+

26 Wokana kugulitsa mbewu zake, anthu adzamʼtemberera.

Koma wolola kuzigulitsa adzamudalitsa.

27 Munthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino, adzakomeredwa mtima.+

Koma wofunitsitsa kuchita zoipa, zoipazo zidzamʼbwerera.+

28 Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto,+

Koma anthu olungama adzasangalala ngati mtengo wa masamba obiriwira.+

29 Aliyense wobweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake cholowa chake chidzakhala mphepo,+

Ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wanzeru.

30 Zotsatira za zimene munthu wolungama amachita zili ngati mtengo wa moyo,+

Ndipo munthu amene amalimbikitsa ena kuchita zabwino ndi wanzeru.+

31 Ngati wolungama padziko lapansi amapatsidwa mphoto,

Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+

12 Munthu amene amakonda malangizo* amakondanso kudziwa zinthu,+

Koma amene amadana ndi kudzudzulidwa ndi wosaganiza bwino.*+

 2 Yehova amasangalala ndi munthu wabwino,

Koma munthu amene amakonza mapulani ochita zinthu zoipa, Mulungu amamuweruza kuti ndi wolakwa.+

 3 Palibe munthu amene angakhale wotetezeka chifukwa chochita zoipa,+

Koma anthu olungama sadzazulidwa.

 4 Mkazi wamakhalidwe abwino ndi chisoti cha ulemu kwa mwamuna wake,+

Koma mkazi wochita zinthu zochititsa manyazi ali ngati matenda amene amawoletsa mafupa a mwamunayo.+

 5 Maganizo a anthu olungama ndi achilungamo,

Koma malangizo a anthu oipa ndi achinyengo.

 6 Mawu a anthu oipa ali ngati msampha wakupha,*+

Koma pakamwa pa anthu owongoka mtima pamawapulumutsa.+

 7 Anthu oipa akagonjetsedwa sakhalaponso,

Koma nyumba ya anthu olungama idzakhalapobe.+

 8 Munthu amatamandidwa chifukwa cholankhula zinthu zanzeru,+

Koma amene ali ndi mtima wopotoka adzanyozedwa.+

 9 Kuli bwino kukhala munthu wamba koma nʼkukhala ndi wantchito,

Kusiyana nʼkukhala wodzikuza koma wopanda chakudya.+

10 Wolungama amasamalira ziweto zake,+

Koma munthu woipa amaganiza kuti ndi wachifundo, pamene ali wankhanza.

11 Amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chokwanira,+

Koma amene amafunafuna zinthu zopanda pake ndi wopanda nzeru.

12 Munthu woipa amasirira nyama imene anthu ena oipa agwira,

Koma muzu wa anthu olungama umabala zipatso.

13 Munthu woipa amakodwa ndi zolankhula zake zochimwa,+

Koma wolungama amapulumuka pamavuto.

14 Munthu amasangalala ndi zinthu zabwino chifukwa cha mawu ake abwino,*+

Ndipo ntchito za manja ake zidzamupindulira.

15 Njira ya munthu wopusa imakhala yolondola mʼmaso mwake,+

Koma munthu wanzeru amalandira malangizo.*+

16 Munthu wopusa amasonyeza kuti wakhumudwa nthawi yomweyo,*+

Koma munthu wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.*

17 Munthu woona mtima akamapereka umboni amalankhula zoona,*

Koma mboni yonama imanena zachinyengo.

18 Mawu a munthu amene amalankhula asanaganize amalasa ngati lupanga,

Koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+

19 Milomo imene imalankhula zoona idzakhalapo mpaka kalekale,+

Koma lilime labodza lidzangokhalapo kwa kanthawi kochepa.+

20 Chinyengo chimakhala mumtima mwa anthu okonza chiwembu,

Koma amene amalimbikitsa mtendere* amasangalala.+

21 Palibe chopweteka chimene chidzagwere wolungama,+

Koma anthu oipa ndi amene adzakumane ndi mavuto ambiri.+

22 Yehova amanyansidwa ndi milomo yonama,+

Koma anthu amene amachita zinthu mokhulupirika amamusangalatsa.

23 Munthu wochenjera amabisa zimene akudziwa,

Koma mtima wa munthu wopusa umangolankhula zinthu zosonyeza kupusa kwake.+

24 Dzanja la anthu akhama lidzalamulira anthu,+

Koma manja aulesi adzagwira ntchito yokakamiza.+

25 Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauweramitsa,+

Koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.+

26 Wolungama amafufuza malo abwino odyetserako ziweto zake,

Koma njira ya anthu oipa imawasocheretsa.

27 Munthu waulesi akamasaka sathamangitsa nyama imene akufuna kupha,+

Koma khama ndi chuma chamtengo wapatali cha munthu.

28 Njira yachilungamo imathandiza munthu kuti akhale ndi moyo,+

Ndipo mʼnjira yake mulibe imfa.

13 Mwana wanzeru amalandira malangizo* ochokera kwa bambo ake,+

Koma wonyoza samvera akadzudzulidwa.*+

 2 Munthu adzadya zinthu zabwino kuchokera pa zipatso zapakamwa pake,+

Koma anthu achinyengo amalakalaka kuchita zachiwawa.

 3 Amene amayangʼanira pakamwa pake* amateteza moyo wake,+

Koma amene amatsegula kwambiri pakamwa pake adzawonongeka.+

 4 Waulesi amalakalaka zinthu, chonsecho alibe chilichonse.+

Koma munthu wakhama zinthu zidzamuyendera bwino.*+

 5 Wolungama amadana ndi mabodza,+

Koma zochita za munthu woipa zimabweretsa manyazi ndi kunyozeka.

 6 Chilungamo chimateteza munthu wosalakwa,+

Koma kuchita zoipa kumachititsa kuti wochimwa awonongeke.

 7 Pali munthu amene amadzionetsa ngati wolemera koma chonsecho alibe chilichonse.+

Pali munthu winanso amene amadzionetsa ngati wosauka koma ali ndi chuma chambiri.

 8 Chuma chimawombola moyo wa munthu,+

Koma anthu osauka saopsezedwa* nʼkomwe.+

 9 Kuwala kwa nyale ya anthu olungama kukuwonjezeka kwambiri.*+

Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+

10 Kudzikuza kumangoyambitsa mikangano basi,+

Koma anthu amene amapempha malangizo* amakhala ndi nzeru.+

11 Chuma chimene munthu amachipeza mofulumira* sichichedwa kutha,+

Koma chuma cha munthu amene wachipeza pangʼonopangʼono* chidzawonjezeka.

12 Chinthu chimene umayembekezera chikalephereka, mtima umadwala.+

Koma chomwe umalakalaka chikachitika, chimakhala ngati mtengo wa moyo.+

13 Aliyense amene safuna kutsatira malangizo, adzakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita zakezo,+

Koma munthu amene amamvera malamulo adzalandira mphoto.+

14 Zimene munthu wanzeru amaphunzitsa* zimapereka moyo,+

Chifukwa zimapulumutsa munthu kumisampha ya imfa.

15 Munthu wozindikira kwambiri, anthu amamukomera mtima,

Koma anthu achinyengo moyo wawo umakhala wodzaza ndi mavuto.

16 Munthu wochenjera amadziwa zimene akuchita,+

Koma wopusa amaonetsa uchitsiru wake wonse.+

17 Munthu woipa wobweretsa uthenga amakumana ndi mavuto,+

Koma nthumwi yokhulupirika imachiritsa.+

18 Aliyense amene amanyalanyaza malangizo* amasauka ndipo amanyozeka,

Koma amene amamvera akadzudzulidwa adzalemekezedwa.+

19 Zimene munthu amalakalaka zikakwaniritsidwa amasangalala.+

Koma opusa amadana ndi zoti asiye zinthu zoipa.+

20 Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru,+

Koma amene amachita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.+

21 Tsoka limatsatira ochimwa,+

Koma anthu olungama zinthu zimawayendera bwino.+

22 Munthu wabwino amasiyira cholowa zidzukulu zake,

Koma chuma cha munthu wochimwa chidzasungidwa kuti chidzakhale cha munthu wolungama.+

23 Munda wa munthu wosauka akaulima umatulutsa chakudya chochuluka,

Koma chingathe kutengedwa* ndi anthu opanda chilungamo.

24 Munthu amene sakwapula* mwana wake ndiye kuti akudana naye,+

Koma amene amamukonda salephera* kumupatsa chilango.+

25 Wolungama amadya nʼkukhuta,+

Koma mimba za anthu oipa zimakhala zopanda kanthu.+

14 Mkazi amene alidi wanzeru amamanga nyumba yake,+

Koma wopusa amaigwetsa ndi manja ake.

 2 Munthu amene amachita zabwino amaopa Yehova,

Koma amene amachita zinthu mwachinyengo* amanyoza Mulungu.

 3 Mawu odzikuza a munthu wopusa ali ngati chikwapu cholangira munthu,

Koma milomo ya anthu anzeru idzawateteza.

 4 Ngati palibe ngʼombe, chodyeramo chimakhala choyera.

Koma zokolola zimachuluka ngati pali ngʼombe yamphongo yamphamvu.

 5 Mboni yokhulupirika sinama,

Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.+

 6 Munthu wonyoza amafunafuna nzeru koma sazipeza,

Koma munthu womvetsa zinthu amaphunzira zinthu mosavuta.+

 7 Usayandikire munthu wopusa,

Chifukwa suphunzira chilichonse mʼmawu otuluka pakamwa pake.+

 8 Nzeru zimathandiza munthu wochenjera kuzindikira njira imene akuyenda,

Koma anthu opusa amapusitsika* ndi kupusa kwawo komwe.+

 9 Anthu opusa akapalamula mlandu amangoseka,*+

Koma anthu owongoka mtima amakhala ofunitsitsa kugwirizananso.

10 Ngati munthu mtima ukumupweteka amadziwa yekha,

Ndipo munthu wina sangamvetse mmene mnzake akusangalalira mumtima mwake.

11 Nyumba ya munthu woipa idzawonongedwa,+

Koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.*

12 Pali njira imene imaoneka ngati yabwino kwa munthu,+

Koma pamapeto pake imabweretsa imfa.+

13 Ngakhale pamene munthu akuseka, mtima wake ukhoza kumamupweteka.

Ndipo kusangalala kungathere mʼchisoni.

14 Munthu wa mtima wosakhulupirika adzakumana ndi zotsatira za zochita zake,+

Koma munthu wabwino amapeza mphoto chifukwa cha zochita zake.+

15 Munthu amene sadziwa zambiri amakhulupirira mawu alionse,

Koma wochenjera amaganizira zotsatira za zimene akufuna kuchita.+

16 Munthu wanzeru amachita zinthu mosamala ndipo amapewa zoipa,

Koma wopusa amachita zinthu mosasamala* ndipo amakhala wodzidalira.

17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+

Koma munthu amene amaganiza bwino amadedwa.

18 Anthu osadziwa zambiri adzakhala opusa,

Koma kwa ochenjera, kudziwa zinthu kudzakhala ngati chisoti chachifumu.+

19 Anthu oipa adzagwadira anthu abwino,

Ndipo oipa adzagwada pamageti a anthu olungama.

20 Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi anzake,+

Koma munthu wolemera amakhala ndi anzake ambiri.+

21 Munthu amene amanyoza mnzake ndiye kuti akuchimwa,

Koma wosangalala ndi munthu amene amakomera mtima anthu onyozeka.+

22 Anthu okonza chiwembu amasochera,

Koma amene ali ndi mtima wofunitsitsa kuchita zabwino amawachitira zinthu mokhulupirika komanso kuwasonyeza chikondi chokhulupirika.+

23 Kugwira ntchito iliyonse mwakhama kumapindulitsa,

Koma kungolankhula chabe kumasaukitsa.+

24 Chisoti chaulemu cha anthu anzeru ndi chuma chawo.

Koma kupusa kumapangitsa kuti anthu opusa apitirizebe kukhala opusa.+

25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo ya anthu,

Koma mboni yabodza imalankhula zabodza zokhazokha.

26 Munthu woopa Yehova amamukhulupirira pa chilichonse,+

Ndipo ana a munthu ameneyu adzapeza malo othawirako.+

27 Kuopa Yehova kuli ngati kasupe wa moyo,

Chifukwa kumateteza moyo kumisampha ya imfa.

28 Kuchuluka kwa anthu kumabweretsa ulemerero kwa mfumu,+

Koma wolamulira amene alibe anthu oti aziwalamulira ulamuliro wake umatha.

29 Munthu amene sakwiya msanga ndi wozindikira zinthu kwambiri,+

Koma wosaugwira mtima amasonyeza uchitsiru wake.+

30 Mtima wodekha umapangitsa kuti thupi likhale lathanzi,

Koma nsanje imawoletsa mafupa.+

31 Amene amabera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+

Koma amene amakomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+

32 Woipa adzagwetsedwa ndi kuipa kwakeko,

Koma kukhulupirika kwa munthu wolungama kudzakhala malo ake othawirako.+

33 Munthu womvetsa zinthu salankhula modzitama kuti ali ndi nzeru,+

Koma munthu wopusa, nthawi zonse amalengeza zimene akudziwa.

34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,+

Koma tchimo limachititsa manyazi mitundu ya anthu.

35 Mfumu imasangalala ndi wantchito amene amachita zinthu mozindikira,+

Koma imakwiya ndi wantchito wochita zinthu zochititsa manyazi.+

15 Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+

Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+

 2 Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+

Koma pakamwa pa zitsiru pamangolankhula mawu opusa.

 3 Maso a Yehova ali paliponse,

Amaona anthu oipa ndi abwino omwe.+

 4 Lilime lodekha* lili ngati mtengo wa moyo,+

Koma mawu achinyengo amachititsa kuti anthu ataye mtima.

 5 Munthu wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+

Koma munthu wochenjera amamvera ena akamudzudzula.+

 6 Mʼnyumba ya munthu wolungama muli chuma chambiri,

Koma zokolola za munthu woipa zimamubweretsera mavuto.+

 7 Milomo ya munthu wanzeru imafalitsa zimene akudziwa,+

Koma mtima wa munthu wopusa suchita zimenezo.+

 8 Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa kwa Yehova,+

Koma pemphero la munthu wowongoka mtima limamusangalatsa.+

 9 Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+

Koma amakonda munthu amene amachita chilungamo.+

10 Chilango chimaoneka choipa* kwa munthu amene wasiya njira yabwino,+

Koma aliyense amene amadana ndi kudzudzulidwa adzafa.+

11 Ngati Yehova amaona bwinobwino amene ali mʼManda* ndiponso malo achiwonongeko,*+

Ndiye kuli bwanji zimene zili mʼmitima ya anthu?+

12 Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akumudzudzula.+

Iye sadzapempha malangizo kwa anthu anzeru.+

13 Mtima wachimwemwe umapangitsa kuti nkhope izioneka yosangalala,

Koma munthu sasangalala ngati mtima ukumupweteka.+

14 Anthu anzeru* amayesetsa kuti adziwe zinthu,+

Koma pakamwa pa anthu opusa pamasangalala ndi zinthu zopusa.+

15 Masiku onse a munthu amene akukumana ndi mavuto amakhala oipa,+

Koma munthu amene ali ndi mtima wosangalala* amachita phwando nthawi zonse.+

16 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+

Kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri koma uli ndi nkhawa.*+

17 Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+

Kusiyana ndi kudya nyama ya ngʼombe yamphongo yonenepa* koma pali chidani.+

18 Munthu wosachedwa kupsa mtima amayambitsa mkangano,+

Koma munthu amene sakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+

19 Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+

Koma njira ya munthu wowongoka mtima ili ngati msewu wosalazidwa bwino.+

20 Mwana wanzeru amasangalatsa bambo ake,+

Koma munthu wopusa amanyoza mayi ake.+

21 Munthu wopanda nzeru amasangalala ndi uchitsiru,+

Koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+

22 Mapulani sakwaniritsidwa ngati anthu sakambirana,*

Koma alangizi akachuluka zinthu zimayenda bwino.+

23 Munthu amasangalala akapereka yankho labwino,*+

Ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+

24 Munthu amene ndi wozindikira ali panjira yokwezeka yopita kumoyo,+

Ndipo amapewa kuyenda mʼnjira yotsikira ku Manda.*+

25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+

Koma adzateteza malire a malo a mkazi wamasiye.+

26 Yehova amadana ndi ziwembu za munthu woipa,+

Koma mawu osangalatsa ndi oyera kwa iye.+

27 Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake,+

Koma amene amadana ndi ziphuphu adzakhalabe ndi moyo.+

28 Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+

Koma pakamwa pa anthu oipa pamangolankhula zoipa.

29 Yehova ali kutali ndi anthu oipa,

Koma amamva pemphero la anthu olungama.+

30 Maso owala amapangitsa* kuti mtima usangalale.

Uthenga wabwino umachititsa kuti mafupa akhale amphamvu.*+

31 Munthu amene amamvetsera chidzudzulo chopatsa moyo,

Amakhala pakati pa anthu anzeru.+

32 Aliyense amene amakana malangizo amanyoza moyo wake,+

Koma amene amamvetsera akadzudzulidwa amakhala wozindikira.+

33 Kuopa Yehova nʼkumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+

Ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+

16 Munthu amakonza maganizo amumtima mwake,*

Koma yankho limene amapereka* limachokera kwa Yehova.+

 2 Njira zonse za munthu zimaoneka zabwino* kwa iye,+

Koma Yehova amafufuza zolinga zake.+

 3 Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova,*+

Ndipo mapulani ako adzayenda bwino.

 4 Yehova amapangitsa kuti chilichonse chikwaniritse cholinga chake,

Ngakhalenso oipa amene adzalangidwe pa tsiku latsoka.+

 5 Yehova amanyansidwa ndi munthu aliyense wa mtima wonyada.+

Musakayikire mfundo yakuti* munthu wotero sadzalephera kulangidwa.

 6 Cholakwa chimaphimbika ndi kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika,+

Ndipo chifukwa choopa Yehova, munthu amapewa kuchita zoipa.+

 7 Yehova akasangalala ndi njira za munthu,

Amachititsa ngakhale adani a munthuyo kukhala naye pamtendere.+

 8 Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa koma uli wachilungamo+

Kusiyana nʼkupeza zinthu zambiri mopanda chilungamo.+

 9 Munthu angakhale ndi pulani ya zimene akufuna kuchita pa moyo wake,

Koma Yehova ndi amene amatsogolera mapazi ake.+

10 Chigamulo chilichonse chimene mfumu ikupereka chizikhala chogwirizana ndi malangizo ochokera kwa Mulungu.+

Mfumuyo isamakhotetse chilungamo.+

11 Miyezo komanso masikelo achilungamo ndi ochokera kwa Yehova.

Miyala yonse yoyezera imene ili mʼthumba anaipanga ndi iyeyo.+

12 Mafumu abwino amadana ndi kuchita zinthu zoipa,+

Chifukwa mpando wawo wachifumu umakhazikika akamalamulira mwachilungamo.+

13 Mawu achilungamo amasangalatsa mafumu.

Iwo amakonda munthu amene amalankhula moona mtima.+

14 Mkwiyo wa mfumu uli ngati mthenga wa imfa,+

Koma munthu wanzeru amauziziritsa.*+

15 Mfumu ikamukomera munthu mtima, munthuyo amakhala ndi moyo wabwino.

Kukoma mtima kwake kuli ngati mtambo wa mvula mʼnyengo ya chilimwe.+

16 Kupeza nzeru nʼkwabwino kwambiri kuposa kupeza golide.+

Ndipo ndi bwino kusankha kumvetsa zinthu kuposa siliva.+

17 Anthu owongoka mtima amapewa kuchita zinthu zoipa.

Aliyense amene amateteza njira yake, amasunga moyo wake.+

18 Kunyada kumachititsa kuti munthu awonongeke,

Ndipo mtima wodzikuza umachititsa kuti munthu apunthwe.+

19 Kuli bwino kukhala wodzichepetsa pakati pa anthu ofatsa,+

Kusiyana nʼkugawana katundu amene anthu odzikuza alanda.

20 Munthu wosonyeza kuzindikira pochita zinthu, zidzamuyendera bwino,

Ndipo wosangalala ndi munthu amene amadalira Yehova.

21 Munthu wa mtima wanzeru adzatchedwa wozindikira,+

Ndipo amene amalankhula mokoma mtima* amakopa ena ndi mawu akewo.+

22 Kuzindikira kuli ngati kasupe wa moyo kwa ozindikirawo,

Koma zitsiru zimalangidwa ndi kupusa kwawo komwe.

23 Munthu wanzeru amasankha mawu mwanzeru akamalankhula,+

Ndipo mawu ake amakopa anthu ena.

24 Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.

Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+

25 Pali njira imene imaoneka ngati yabwino kwa munthu,

Koma pamapeto pake imabweretsa imfa.+

26 Munthu amagwira ntchito mwakhama kuti apeze chakudya.

Chifukwa njala imamuchititsa* kuti apitirize kugwira ntchito.+

27 Munthu wopanda pake amafukula zinthu zoipa,+

Ndipo zimene amalankhula zili ngati moto umene ukuyaka.+

28 Munthu woyambitsa mavuto* amayambanitsa anthu,+

Ndipo wonenera anzake zoipa amalekanitsa mabwenzi apamtima.+

29 Munthu wachiwawa amakopa mnzake kuti achite zoipa,

Ndipo amamuchititsa kuti ayende mʼnjira yolakwika.

30 Akamakonza ziwembu, amatsinzinira maso ake.

Ndipo akamachita zinthu zosayenera amalumira milomo yake.

31 Imvi ndi chisoti chachifumu cha ulemerero+

Zikapezeka ndi munthu amene akuyenda mʼnjira yachilungamo.+

32 Munthu wosakwiya msanga+ ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu,

Ndipo munthu amene amalamulira mkwiyo wake amaposa munthu amene wagonjetsa mzinda.+

33 Maere amaponyedwa pachovala,+

Koma zonse zimene maerewo asonyeza zimachokera kwa Yehova.+

17 Ndi bwino kudya mkate wouma pali mtendere,*+

Kusiyana ndi kuchita maphwando ochuluka* mʼnyumba imene muli mikangano.+

 2 Wantchito wozindikira adzalamulira mwana wa mbuye wake amene amachita zinthu zochititsa manyazi.

Adzalandira nawo cholowa pamodzi ndi ana a mbuye wake.

 3 Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+

Koma Yehova ndi amene amayesa mitima.+

 4 Munthu woipa amakonda kumvetsera mawu opweteka.

Ndipo munthu wachinyengo amamvetsera lilime loyambitsa mavuto.+

 5 Wonyoza munthu wosauka amanyoza amene anamupanga.+

Ndipo amene amasangalala ndi tsoka la wina sadzalephera kulangidwa.+

 6 Zidzukulu zili ngati chisoti chaulemu kwa anthu okalamba,

Ndipo ana amalemekezeka chifukwa cha bambo awo.*

 7 Sitingayembekezere kuti munthu wopusa alankhule zinthu zanzeru.*+

Ndipo nʼzosayenera kuti wolamulira* azilankhula zabodza.+

 8 Mphatso ili ngati mwala wamtengo wapatali kwa mwiniwake.*+

Kulikonse kumene wapita, imachititsa kuti zinthu zimuyendere bwino.+

 9 Aliyense amene amakhululuka* zolakwa akufunafuna chikondi,+

Koma amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.+

10 Kudzudzula kumamufika pamtima munthu womvetsa zinthu,+

Kuposa kukwapula munthu wopusa zikwapu 100.+

11 Munthu woipa amangofuna kupanduka,

Koma munthu wankhanza adzatumidwa kuti akamulange.+

12 Ndi bwino kukumana ndi chimbalangondo chimene ana ake asowa,

Kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru chimene chimachita zopusa.+

13 Ngati munthu amabwezera zoipa pa zabwino,

Zoipa sizidzachoka panyumba yake.+

14 Kuyambitsa ndewu kuli ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo.*

Choncho mkangano usanabuke, chokapo.+

15 Aliyense wonena kuti munthu woipa alibe mlandu ndiponso aliyense wonena kuti munthu wolungama ndi wolakwa,+

Onsewa ndi onyansa kwa Yehova.

16 Kodi pali phindu lililonse ngati munthu wopusa ali ndi njira yopezera nzeru,

Pamene alibe cholinga chopeza nzeruzo?*+

17 Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse,+

Ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.+

18 Munthu wopanda nzeru amagwirana dzanja ndi munthu wina

Ndipo amalonjeza pamaso pa mnzake kuti iye akhala chikole.+

19 Aliyense amene amakonda mikangano amakonda zolakwa.+

Aliyense woika khomo la nyumba yake pamwamba akudziitanira mavuto.+

20 Munthu amene mtima wake ndi wopotoka zinthu sizidzamuyendera bwino,*+

Ndipo amene amalankhula mwachinyengo adzagwera mʼmavuto.

21 Bambo amene wabereka mwana wopusa adzamva chisoni.

Ndipo bambo wa mwana wopanda nzeru sasangalala.+

22 Mtima wosangalala uli ngati mankhwala amene amachiritsa,+

Koma munthu akakhumudwa mphamvu zake zimatha.*+

23 Munthu woipa amalandira chiphuphu mobisa,

Kuti akhotetse chilungamo.+

24 Munthu wozindikira amakhala ndi cholinga choti apeze nzeru,

Koma maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

25 Mwana wopusa amamvetsa chisoni bambo ake,

Komanso amapweteketsa mtima wa* mayi ake amene anamubereka.+

26 Si bwino kulanga* munthu wolungama,

Ndipo kukwapula anthu olemekezeka nʼkosayenera.

27 Munthu wodziwa zinthu amayamba waganiza asanalankhule,+

Ndipo munthu wozindikira amapitiriza kukhala wodekha.+

28 Ngakhale munthu wopusa amene wakhala chete adzaonedwa ngati wanzeru,

Ndipo amene watseka pakamwa pake adzaonedwa ngati wozindikira.

18 Munthu aliyense amene amadzipatula amangoganizira kuchita zimene amalakalaka.

Iye amakana* nzeru zonse zopindulitsa.

 2 Munthu wopusa sasangalala ndi kumvetsa zinthu.

Iye amangokonda kuulula zimene zili mumtima mwake.+

 3 Munthu woipa akabwera, pamabweranso kunyozeka,

Ndipo munthu akamachita zinthu zochititsa manyazi amanyozeka.+

 4 Mawu amʼkamwa mwa munthu ali ngati madzi akuya.+

Kasupe wa nzeru ali ngati mtsinje wosefukira.

 5 Si bwino kukondera munthu woipa+

Kapena kulephera kuchitira chilungamo munthu wolungama.+

 6 Zolankhula za munthu wopusa zimayambitsa mikangano,+

Ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+

 7 Pakamwa pa munthu wopusa mʼpamene pamamuchititsa kuti awonongedwe,+

Ndipo milomo yake ndi msampha wa moyo wake.

 8 Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma,*+

Akachimeza chimalowa mʼmimba.+

 9 Munthu waulesi pa ntchito yake

Ndi mʼbale wake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+

10 Dzina la Yehova ndi nsanja yolimba.+

Wolungama amathawira mmenemo ndipo amatetezedwa.*+

11 Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba.

Ndipo mʼmaganizo mwake chili ngati mpanda umene ukumuteteza.+

12 Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+

Ndipo akadzichepetsa amapeza ulemerero.+

13 Munthu akayankhira nkhani asanaimvetsetse,

Kumakhala kupusa ndipo amachita manyazi.+

14 Mtima wa munthu ukhoza kupirira matenda,+

Koma mtima wosweka ndi ndani angaupirire?+

15 Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu,+

Ndipo khutu la munthu wanzeru limafunitsitsa kudziwa zinthu.

16 Mphatso ya munthu imamʼtsegulira njira,+

Ndipo imamuthandiza kuti akafike kwa anthu olemekezeka.

17 Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola,+

Mpaka mnzake atabwera nʼkudzamufunsa mafunso.*+

18 Kuchita maere kumathetsa mikangano+

Ndipo kumathetsa nkhani pakati pa* anthu amphamvu.

19 Kusangalatsa mʼbale amene walakwiridwa nʼkovuta kwambiri kuposa kulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba,+

Ndipo mikangano ingathe kulekanitsa anthu ngati mageti otseka a mzinda wolimba.+

20 Mimba ya munthu imakhuta zipatso za mawu otuluka pakamwa pake.+

Iye amakhuta zokolola za milomo yake.

21 Imfa ndiponso moyo zili mumphamvu ya lilime,+

Ndipo amene amakonda kuligwiritsa ntchito adzadya zipatso zake.+

22 Munthu amene wapeza mkazi wabwino wapeza chinthu chabwino,+

Ndipo Yehova amamukomera mtima.*+

23 Munthu wosauka akamalankhula amachita kuchonderera,

Koma munthu wolemera amayankha mwaukali.

24 Pali anthu ogwirizana amene ndi okonzeka kuchitirana zoipa,+

Koma pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.+

19 Ndi bwino kukhala wosauka nʼkumachita zinthu mokhulupirika+

Kusiyana nʼkukhala munthu wopusa nʼkumalankhula mabodza.+

 2 Munthu wosadziwa zinthu si wabwino,+

Ndipo amene amachita zinthu mopupuluma* akuchimwa.

 3 Kupusa kwa munthu nʼkumene kumapotoza njira yake,

Ndipo mtima wake umakwiyira Yehova.

 4 Chuma chimachititsa kuti munthu akhale ndi anzake ambiri,

Koma munthu wosauka amasiyidwa ngakhale ndi mnzake weniweni.+

 5 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,+

Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha sadzathawa chilango.+

 6 Anthu ambiri amafuna kukondedwa ndi munthu wolemekezeka,*

Ndipo aliyense ndi bwenzi la munthu wopereka mphatso.

 7 Abale ake onse a munthu wosauka amadana naye,+

Kuwonjezera pamenepo anzake amamupewa,+

Iye amawachonderera kuti amuthandize, koma palibe amene amamuyankha.

 8 Munthu amene wapeza nzeru amakonda moyo wake.+

Amene amaona kuti kukhala wozindikira nʼkofunika kwambiri zinthu zidzamuyendera bwino.+

 9 Mboni yonama sidzalephera kulangidwa,

Ndipo amene amalankhula zabodza zokhazokha adzawonongedwa.+

10 Nʼzosayenera kuti munthu wopusa azikhala moyo wawofuwofu.

Chimodzimodzinso kuti munthu wantchito alamulire anthu audindo!+

11 Kuzindikira kumachititsa kuti munthu abweze mkwiyo wake,+

Ndipo kunyalanyaza cholakwa kumamʼchititsa kukhala wokongola.+

12 Mkwiyo wa mfumu uli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu,+

Koma kukoma mtima kwake kuli ngati mame pazomera.

13 Mwana wopusa amabweretsa mavuto kwa bambo ake,+

Ndipo mkazi wolongolola* ali ngati denga limene silisiya kudontha.+

14 Nyumba komanso chuma ndi cholowa chochokera kwa makolo,

Koma mkazi wanzeru amachokera kwa Yehova.+

15 Ulesi umabweretsa tulo tofa nato,

Ndipo munthu waulesi adzakhala ndi njala.+

16 Amene amasunga lamulo amasunga moyo wake.+

Amene amachita zinthu mosasamala adzafa.+

17 Amene amakomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova,+

Ndipo adzamʼbwezera* zimene anachitazo.+

18 Langa mwana wako padakali chiyembekezo,+

Ndipo usakhale ndi mlandu wochititsa* kuti afe.+

19 Munthu wosachedwa kupsa mtima ayenera kulipira,

Chifukwa ukayesa kumʼpulumutsa, uzichita zimenezi kawirikawiri.+

20 Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo*+

Kuti udzakhale wanzeru mʼtsogolo.+

21 Munthu amakhala ndi mapulani ambiri mumtima mwake,

Koma zolinga za Yehova nʼzimene zidzakwaniritsidwe.+

22 Chinthu chosiririka mwa munthu ndi chikondi chake chokhulupirika,+

Ndipo ndi bwino kukhala wosauka kusiyana nʼkukhala munthu wonama.

23 Kuopa Yehova kumathandiza munthu kuti apeze moyo.+

Munthu amene amachita zimenezi amagona tulo tokoma ndipo zoipa sizimugwera.+

24 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,

Koma nʼkulephera kulibweretsa pakamwa.+

25 Menya munthu wonyoza+ kuti wosadziwa zinthu achenjere,+

Ndipo dzudzula munthu womvetsa zinthu kuti awonjezere zimene akudziwa.+

26 Munthu amene amazunza bambo ake ndiponso kuthamangitsa mayi ake,

Ndi mwana wochititsa manyazi ndi wonyozetsa.+

27 Mwana wanga ukasiya kumvera malangizo,

Udzasochera nʼkusiya kutsatira mawu anzeru.

28 Mboni yopanda pake imanyoza chilungamo,+

Munthu woipa amasangalala kuchita zoipa ngati mmene amasangalalira ndi chakudya.+

29 Zilango amazisungira anthu onyoza,+

Ndipo zikwapu ndi zokwapulira msana wa anthu opusa.+

20 Munthu amene amamwa vinyo wambiri amayamba kunyoza+ ndipo amene amamwa mowa wambiri amachita zosokoneza.+

Aliyense amene amasochera ndi zinthu zimenezi alibe nzeru.+

 2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+

Aliyense woputa mkwiyo wake akuika moyo wake pangozi.+

 3 Munthu amalemekezeka akapewa mkangano,+

Koma aliyense wopusa amafulumira kuyambitsa mkangano.+

 4 Waulesi salima nthawi yozizira,

Choncho iye azidzapemphapempha nthawi yokolola chifukwa adzakhala alibe kanthu.*+

 5 Maganizo amumtima* mwa munthu ali ngati madzi akuya,

Koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.

 6 Anthu ambiri amanena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika,

Koma ndi ndani amene angapeze munthu wokhulupirika?

 7 Munthu wolungama amachita zinthu mokhulupirika.+

Ana ake ndi osangalala.+

 8 Mfumu ikakhala pampando wachifumu kuti iweruze,+

Maso ake amazindikira* anthu onse oipa.+

 9 Ndi ndani anganene kuti: “Ndayeretsa mtima wanga.+

Ndine woyera ku tchimo langa”?+

10 Miyala yachinyengo yoyezera komanso miyezo yachinyengo,*

Zonsezi nʼzonyansa kwa Yehova.+

11 Ngakhale mwana* amadziwika ndi zochita zake,

Ngati khalidwe lake lili loyera ndiponso labwino.+

12 Khutu lakumva ndiponso diso loona,

Zonsezi anazipanga ndi Yehova.+

13 Usamakonde tulo chifukwa ungasauke.+

Tsegula maso ako ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.+

14 Wogula amanena kuti, “chinthu ichi si chabwino, si chabwino chimenechi!”

Kenako amachoka ndipo amayamba kudzitama.+

15 Pali golide komanso miyala yambiri yamtengo wapatali ya korali,*

Koma milomo yodziwa zinthu ndi yamtengo wapatali.+

16 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.+

Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+

17 Chakudya chimene munthu wachipeza mwachinyengo chimamukomera,

Koma pambuyo pake mʼkamwa mwake mumadzaza miyala.+

18 Anthu akakambirana zolinga zawo zimakwaniritsidwa,*+

Ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+

19 Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi.+

Usamagwirizane ndi munthu amene amakonda kunena miseche.*

20 Aliyense amene amatemberera bambo ake komanso mayi ake,

Nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+

21 Munthu akapeza cholowa mwadyera,

Pamapeto pake Mulungu sadzamudalitsa.+

22 Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+

Yembekezera Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+

23 Miyala yachinyengo* yoyezera ndi yonyansa kwa Yehova,

Ndipo masikelo achinyengo si abwino.

24 Yehova ndi amene amatsogolera mapazi a munthu.+

Ndiye munthu payekha angadziwe bwanji njira yoyenera kuyenda?

25 Umakhala msampha munthu akathamangira kufuula kuti, “Nʼzoyera!”+

Koma pambuyo polonjeza nʼkuyamba kuganiziranso bwino zimene walonjezazo.+

26 Mfumu yanzeru imazindikira anthu oipa,+

Ndipo imawaponda ndi wilo lopunthira mbewu.+

27 Mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova.

Imafufuza zinthu zamkati mwa mtima wake.

28 Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+

Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+

29 Ulemerero wa anyamata ndi mphamvu zawo,+

Ndipo ulemerero wa anthu achikulire ndi imvi zawo.+

30 Mabala obwera chifukwa chopatsidwa chilango amachotsa zoipa,+

Ndipo zikwapu zimayeretsa mtima wa munthu.

21 Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi mʼdzanja la Yehova.+

Amaupititsa kulikonse kumene iye akufuna.+

 2 Njira zonse za munthu zimaoneka zabwino kwa iye,+

Koma Yehova amafufuza mitima.*+

 3 Kuchita zinthu zoyenera komanso zachilungamo

Kumasangalatsa kwambiri Yehova kuposa nsembe.+

 4 Maso odzikweza komanso mtima wonyada

Zili ngati nyale imene imatsogolera anthu oipa, koma zimenezi ndi tchimo.+

 5 Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino,*+

Koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.+

 6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama

Kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira komanso msampha wakupha.*+

 7 Zinthu zachiwawa zimene anthu oipa amachita nʼzimene zidzawawononge,+

Chifukwa amakana kuchita zinthu mwachilungamo.

 8 Njira ya munthu wochimwa imakhala yokhotakhota,

Koma zochita za munthu wolungama ndi zowongoka.+

 9 Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumba

Kusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+

10 Munthu woipa amalakalaka zoipa,+

Ndipo mnzake samukomera mtima.+

11 Munthu wonyoza akapatsidwa chilango, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru,

Ndipo munthu wanzeru akaphunzira zinthu zambiri, amadziwa zinthu.*+

12 Mulungu amene ndi wolungama amayangʼana nyumba ya munthu woipa.

Amagwetsa anthu oipa kuti akumane ndi tsoka.+

13 Aliyense amene amatseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,

Nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+

14 Mphatso yoperekedwa mwachinsinsi imathetsa mkwiyo,+

Ndipo chiphuphu choperekedwa mwamseri* chimathetsa ukali waukulu.

15 Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+

Koma anthu ochita zoipa amadana ndi chilungamo.

16 Munthu amene wasochera nʼkusiya kuchita zinthu mozindikira

Adzapumula mʼgulu la anthu akufa.+

17 Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka.+

Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18 Munthu woipa ndi dipo la munthu wolungama,

Ndipo munthu wochita zachinyengo adzatengedwa mʼmalo mwa anthu owongoka mtima.+

19 Ndi bwino kukhala mʼchipululu

Kusiyana ndi kukhala ndi mkazi wolongolola* komanso wosachedwa kukwiya.+

20 Chuma chamtengo wapatali komanso mafuta zimapezeka mʼnyumba ya munthu wanzeru,+

Koma munthu wopusa amasakaza* zinthu zimene ali nazo.+

21 Amene akufunafuna chilungamo ndiponso chikondi chokhulupirika

Adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+

22 Munthu wanzeru amagonjetsa* mzinda wa anthu amphamvu,

Ndipo amawononga mpanda wolimba umene amadalira.+

23 Amene amateteza pakamwa pake komanso lilime lake

Amapewa mavuto.+

24 Munthu wochita zinthu modzikuza amene saganizira zotsatira zake ndi amene mumamuti

Ndi munthu wonyada komanso amene amakonda kudzionetsera ndiponso kudzitamandira.+

25 Zinthu zimene munthu waulesi amalakalaka zidzamupha,

Chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+

26 Tsiku lonse amalakalaka chinachake mwadyera,

Koma munthu wolungama amapereka, saumira chilichonse.+

27 Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa.+

Ndiye kuli bwanji akaipereka ndi zolinga zoipa!*

28 Mboni yonena mabodza idzawonongedwa,+

Koma munthu amene amamvetsera adzapereka umboni wa zinthu zimene anamva ndipo zidzamuyendera bwino.*

29 Munthu woipa amadzionetsa ngati wolimba mtima,+

Koma wolungama amasankha njira yoyenera kuyenda.+

30 Palibe nzeru kapena kuzindikira, kapena malangizo amene angalepheretse zimene Yehova amafuna.+

31 Hatchi amaiphunzitsa pokonzekera tsiku la nkhondo,+

Koma Yehova ndi amene amapulumutsa.+

22 Ndi bwino kusankha dzina labwino* kusiyana ndi chuma chochuluka.+

Kulemekezedwa* nʼkwabwino kuposa siliva ndi golide.

 2 Anthu olemera ndiponso anthu osauka ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi:

Onsewo anapangidwa ndi Yehova.+

 3 Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala,

Koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.

 4 Zotsatira za kudzichepetsa komanso kuopa Yehova

Ndi chuma, ulemerero ndi moyo.+

 5 Minga ndi misampha zili mʼnjira ya munthu wochita zopotoka,

Koma aliyense amene amaona kuti moyo wake ndi wamtengo wapatali, amakhala nazo kutali.+

 6 Phunzitsa mwana kuti aziyenda mʼnjira imene akuyenera kuyendamo.+

Ngakhale akadzakalamba sadzachoka mʼnjira imeneyo.+

 7 Wolemera amalamulira anthu osauka,

Ndipo wobwereka amakhala kapolo wa wobwereketsa.+

 8 Wofesa zosalungama adzakolola mavuto,+

Ndipo ndodo ya ukali wake idzatha.+

 9 Munthu wowolowa manja* adzadalitsidwa,

Chifukwa amagawana chakudya chake ndi anthu osauka.+

10 Thamangitsa munthu wonyoza

Ndipo mikangano itha,

Komanso milandu ndi kunyozana zilekeka.

11 Munthu amene mtima wake ndi woyera ndipo amalankhula mokoma mtima,

Adzakhala bwenzi la mfumu.+

12 Maso a Yehova amateteza wodziwa zinthu,

Koma iye amawononga mawu a munthu wochita zachinyengo.+

13 Waulesi amanena kuti: “Panja pali mkango!

Ndithu undipha pakati pa bwalo la mzinda!”+

14 Pakamwa pa akazi amakhalidwe oipa* pali ngati dzenje lakuya.+

Amene waputa mkwiyo wa Yehova adzagweramo.

15 Uchitsiru umakhazikika mumtima mwa mwana.+

Koma ndodo yomulangira ndi imene imauthamangitsira kutali ndi iye.+

16 Amene amabera mwachinyengo munthu wosauka kuti awonjezere chuma chake+

Komanso wopereka mphatso kwa munthu wolemera,

Ndithu adzasauka.

17 Tchera khutu lako ndipo umvetsere mawu a anthu anzeru,+

Kuti ulandire ndi mtima wonse nzeru zochokera kwa ine.+

18 Chifukwa nʼzosangalatsa kuti uzisunge mumtima mwako,+

Ukatero zidzakhazikika pamilomo yako nthawi zonse.+

19 Lero ndakudziwitsa zinthu,

Nʼcholinga choti uzidalira Yehova.

20 Kodi sindinakulembere

Zinthu zoti zikupatse malangizo komanso kukuphunzitsa,

21 Nʼcholinga choti ndikuphunzitse mawu oona komanso odalirika,

Kuti ubwerere kwa amene wakutuma nʼkukamuuza lipoti lolondola?

22 Usabere munthu wosauka chifukwa choti ndi wosauka,+

Ndipo usapondereze munthu wonyozeka pageti la mzinda,+

23 Chifukwa Yehova adzawateteza pa mlandu wawo,+

Ndipo adzachotsa moyo wa anthu amene akuwabera mwachinyengo.

24 Usamagwirizane ndi munthu wosachedwa kupsa mtima

Kapena kuchita zinthu ndi munthu wosachedwa kukwiya,

25 Kuti usaphunzire njira zake

Nʼkudzitchera wekha msampha.+

26 Usakhale mʼgulu la anthu amene akugwirana dzanja pochita mgwirizano,

Amene amakhala chikole cha ngongole za anthu ena.+

27 Ukadzalephera kulipira,

Adzakulanda bedi limene umagonapo.

28 Usamasunthe chizindikiro chakalekale cha malire,

Chimene makolo anu anaika.+

29 Kodi wamuona munthu waluso pa ntchito yake?

Iye adzaima pamaso pa mafumu.+

Sadzaima pamaso pa anthu wamba.

23 Ukakhala pansi kuti udye ndi mfumu,

Uzionetsetsa zimene zili pamaso pako.

 2 Uzidziletsa*

Ngati umadya kwambiri.

 3 Usalakelake chakudya chake chokoma,

Chifukwa ndi chakudya chachinyengo.

 4 Usadzitopetse pofuna kupeza chuma.+

Leka kuchita zimenezi, mʼmalomwake uzisonyeza kuti ndiwe womvetsa zinthu.*

 5 Ukayangʼana pamene panali chumacho, umapeza kuti palibe,+

Chifukwa ndithu chimamera mapiko ngati chiwombankhanga nʼkuulukira mʼmwamba.+

 6 Usadye chakudya cha munthu womana.*

Usalakelake chakudya chake chokoma,

 7 Chifukwa iye ali ngati munthu amene amakuyangʼanitsitsa kuti adziwe kuchuluka kwa chakudya chimene wadya.

Iye amakuuza kuti: “Idya ndi kumwa,” koma salankhula zimenezo ndi mtima wonse.

 8 Mbamu imene wadya udzaisanza

Ndipo mawu ako oyamikira adzangopita pachabe.

 9 Usayese kuphunzitsa munthu wopusa,+

Chifukwa iye adzanyoza mawu ako anzeru.+

10 Usamasunthe chizindikiro chakalekale cha malire,+

Kapena kulowerera munda wa ana amasiye.

11 Chifukwa amene akuwateteza* ndi wamphamvu.

Iye adzawateteza pa mlandu wawo ndi iwe.+

12 Yesetsa ndi mtima wonse kumvetsera malangizo ndi kuwagwiritsa ntchito,

Ndipo khutu lako limvetsere mawu anzeru.

13 Mwana usalephere kumupatsa chilango.*+

Ngakhale utamukwapula ndi chikwapu, sangafe.

14 Umukwapule ndi chikwapu,

Kuti upulumutse moyo wake ku Manda.*

15 Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru,

Ndithu mtima wanga udzasangalala.+

16 Milomo yako ikamalankhula zinthu zabwino,

Ndidzasangalala kuchokera pansi pa mtima.*

17 Mtima wako usamasirire anthu ochimwa,+

Koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.+

18 Chifukwa ukatero udzakhala ndi tsogolo labwino,+

Ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.

19 Mwana wanga, mvera ndi kukhala wanzeru,

Ndipo tsogolera mtima wako panjira yabwino.

20 Usakhale mʼgulu la anthu amene amamwa vinyo wambiri.+

Usakhale mʼgulu la anthu amene amadya nyama mosusuka,+

21 Chifukwa chidakwa komanso munthu wosusuka adzasauka,+

Ndipo kuwodzera kudzaveka munthu nsanza.

22 Uzimvera bambo ako amene anakubereka,

Ndipo usanyoze mayi ako chifukwa chakuti akalamba.+

23 Gula* choonadi ndipo usachigulitse,+

Chimodzimodzinso nzeru, malangizo ndi kumvetsa zinthu.+

24 Bambo a munthu wolungama ndithu adzasangalala.

Aliyense amene anabereka mwana wanzeru adzakondwera naye.

25 Bambo ako ndi mayi ako adzasangalala,

Ndipo mayi amene anakubereka adzakondwera.

26 Mwana wanga, ndipatse mtima wako,

Ndipo maso ako asangalale ndi njira zanga.+

27 Chifukwa hule lili ngati dzenje lakuya,

Ndipo mkazi wachiwerewere* ali ngati chitsime chachingʼono.+

28 Iye amabisalira anthu panjira ngati wachifwamba.+

Amachititsa kuti chiwerengero cha amuna osakhulupirika chiwonjezereke.

29 Ndi ndani amene akuvutika? Ndi ndani amene ali ndi nkhawa?

Ndi ndani amene ali pa mikangano? Ndi ndani amene ali ndi madandaulo?

Ndi ndani amene ali ndi mabala popanda chifukwa? Ndi ndani amene ali ndi maso ofiira?

30 Ndi amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo,+

Amene amafunafuna* vinyo wosakaniza.

31 Usakopeke ndi kufiira kwa vinyo,

Pamene akunyezimira mʼkapu nʼkumatsetserekera kukhosi mwamyaa!

32 Chifukwa pamapeto pake amaluma ngati njoka,

Ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri.

33 Maso ako adzaona zinthu zachilendo,

Ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota.+

34 Udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja,

Komanso ngati munthu amene wagona pansonga ya mtengo* wa ngalawa.

35 Udzanena kuti: “Andimenya koma sindinamve kupweteka.

Andikuntha koma sindinadziwe chilichonse.

Kodi ndidzuka nthawi yanji?+

Ndikufuna ndikamwenso wina.”

24 Usamasirire anthu oipa,

Ndipo usamalakelake utakhala pagulu lawo,+

 2 Chifukwa mtima wawo umangoganizira zochita chiwawa,

Ndipo milomo yawo imangokhalira kulankhula zobweretsera ena mavuto.

 3 Nzeru zimamanga nyumba ya* munthu,+

Ndipo kuzindikira kumachititsa kuti ilimbe kwambiri.

 4 Kudziwa zinthu kumachititsa kuti zipinda za nyumbayo zidzaze

Ndi zinthu zonse zamtengo wapatali ndiponso zosangalatsa.+

 5 Munthu wanzeru ndi wamphamvu,+

Ndipo akakhala wodziwa zinthu amawonjezera mphamvu zake.

 6 Ukamatsatira malangizo anzeru udzatha kumenya nkhondo yako,+

Ndipo pakakhala alangizi* ambiri udzapambana.*+

 7 Kwa munthu wopusa nʼzosatheka kupeza nzeru zenizeni.+

Ndipo amakhala alibe chilichonse choti anganene pageti la mzinda.

 8 Aliyense wokonzera anzake ziwembu

Adzatchedwa katswiri wokonza ziwembu.+

 9 Mapulani a munthu* wopusa amamupangitsa kuti achite tchimo,

Ndipo anthu amanyansidwa ndi munthu wonyoza.+

10 Ukafooka pa nthawi imene ukukumana ndi mavuto,

Mphamvu zako zidzachepa.

11 Pulumutsa anthu amene atengedwa kuti akaphedwe,

Ndipo amene akuyenda modzandira popita kukaphedwa uwathandize.+

12 Ukanena kuti: “Ifetu zimenezi sitimazidziwa,”

Kodi amene amafufuza mitima sazindikira zimene zili mʼmaganizo mwako?+

Ndithudi, amene amakuyangʼanitsitsa adzadziwa

Ndipo adzabwezera munthu aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+

13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino.

Uchi wochokera pazisa za njuchi umatsekemera.

14 Mofanana ndi zimenezi, dziwa kuti nzeru ndi zabwino kwa iwe.*+

Ukazipeza, udzakhala ndi tsogolo labwino

Ndipo chiyembekezo chako sichidzawonongedwa.+

15 Mofanana ndi munthu woipa, usamabisalire munthu wolungama pafupi ndi nyumba yake kuti umuchitire chiwembu.

Usamawononge malo ake okhala.

16 Chifukwa munthu wolungama akhoza kugwa maulendo 7 ndipo adzadzukanso,+

Koma anthu oipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzagwa.+

17 Mdani wako akagwa usamasangalale,

Ndipo akapunthwa, mtima wako usamakondwere.+

18 Ukachita zimenezi Yehova adzaona ndipo zidzamuipira

Moti adzachotsa mkwiyo wake pa mdani wakoyo.+

19 Usamapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.

Usamasirire anthu oipa,

20 Chifukwa aliyense woipa alibe tsogolo,+

Ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.+

21 Mwana wanga uziopa Yehova komanso mfumu.+

Ndipo usamakhale pagulu la anthu ofuna kuti zinthu zisinthe,+

22 Chifukwa tsoka lawo lidzabwera modzidzimutsa.+

Ndipo ndi ndani amene angadziwe za tsoka limene onsewa* adzawabweretsere?+

23 Mawu awanso ndi a anthu anzeru:

Si bwino kukondera poweruza mlandu.+

24 Aliyense amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wolungama,”+

Anthu adzamutemberera ndipo mitundu ya anthu idzaitanira tsoka pa iye.

25 Koma anthu amene amamudzudzula zinthu zidzawayendera bwino.+

Adzalandira madalitso a zinthu zabwino.+

26 Anthu adzakisa milomo ya munthu amene amayankha moona mtima.*+

27 Konzekera ntchito yako yapanja, ndipo uonetsetse kuti ntchito yonse yatheka mʼmunda wako.

Ukatero ukamange nyumba yako.*

28 Usapereke umboni wotsutsana ndi mnzako ngati ulibe umboni weniweni.+

Usapusitse anthu ena ndi milomo yako.+

29 Usanene kuti: “Ndimuchitira zimene iye wandichitira.

Ndimubwezera zimene anandichitira.”+

30 Ndinadutsa pamunda pa munthu waulesi,+

Pamunda wa mpesa wa munthu wopanda nzeru.

31 Ndinaona kuti munali tchire lokhalokha.

Zitsamba zoyabwa zinali paliponse mʼmundamo,

Komanso mpanda wake wamiyala unali utagumuka.+

32 Nditaona zimenezi, ndinayamba kuziganizira mumtima mwanga,

Ndipo ndinaphunzirapo kuti:

33 Ukapitiriza kugona pangʼono, ukapitiriza katulo pangʼono,

Ukapitiriza kupinda manja pangʼono kuti upume,

34 Umphawi wako udzabwera ngati wachifwamba,

Ndipo kusauka kwako kudzabwera ngati munthu wokhala ndi zida.+

25 Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya+ mfumu ya Yuda anakopera ndi iyi:

 2 Kusunga chinsinsi ndi ulemerero wa Mulungu,+

Ndipo ulemerero wa mafumu ndi kufufuza bwino nkhani.

 3 Nʼzosatheka kufufuza kutalika kwa kumwamba komanso kuzama kwa dziko lapansi,

Nʼchimodzimodzinso mitima ya mafumu.

 4 Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,

Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+

 5 Chotsani woipa pamaso pa mfumu,

Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+

 6 Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+

Ndipo usakhale pakati pa anthu olemekezeka,+

 7 Chifukwa ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti, “Bwera udzakhale apa,”

Kusiyana nʼkuti ikuchititse manyazi pamaso pa munthu wolemekezeka.+

 8 Usamafulumire kupititsa mlandu kukhoti,

Chifukwa udzachita chiyani mnzako akadzapereka umboni wosonyeza kuti iweyo ndi wolakwa?+

 9 Thetsa nkhaniyo pokambirana ndi mnzakoyo,+

Koma usaulule nkhani zachinsinsi zimene unauzidwa,*+

10 Kuti amene akumvetsera asakuchititse manyazi

Komanso kuti usafalitse nkhani yoipa* imene sungathe kuithetsa kuti isapitirize kufalikira.

11 Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera+

Ali ngati zipatso za maapozi agolide mʼmbale zasiliva.

12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera+

Amakhala ngati ndolo yagolide ndiponso ngati chokongoletsera chagolide woyenga bwino.

13 Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aituma

Ili ngati kuzizira kwa sinowo* pa tsiku lokolola,

Chifukwa imatsitsimula moyo wa abwana ake.+

14 Munthu wodzitama kuti apereka mphatso koma nʼkulephera kupereka,+

Ali ngati mitambo komanso mphepo yosabweretsa mvula.

15 Chifukwa cha kuleza mtima munthu angathe kunyengerera munthu waudindo,

Ndipo mawu okoma akhoza* kuthyola fupa.+

16 Ukapeza uchi udye umene ungakukwane,

Chifukwa ukadya wambiri ungathe kuusanza.+

17 Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako,

Kuti angatope nawe nʼkuyamba kudana nawe.

18 Munthu wopereka umboni wabodza pa mlandu wa mnzake+

Ali ngati chibonga chakunkhondo, lupanga, komanso muvi wakuthwa.

19 Kukhulupirira munthu wosadalirika* pa nthawi yamavuto

Kuli ngati dzino lothyoka komanso phazi lotsimphina.

20 Amene amaimbira nyimbo munthu amene ali ndi chisoni mumtima mwake+

Ali ngati munthu amene amavula chovala pa tsiku lozizira,

Komanso ngati viniga* amene wathiridwa musoda

21 Ngati mdani wako* ali ndi njala, umʼpatse chakudya.

Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse madzi akumwa,+

22 Ukachita zimenezi ndiye kuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,*+

Ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.

23 Mphepo yakumpoto imabweretsa mvula yambiri

Ndipo lilime lonena miseche limachititsa kuti anthu akhale ndi nkhope zolusa.+

24 Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumba

Kusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+

25 Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+

Ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.

26 Munthu wolungama amene amagonja* nʼkuchita zofuna za munthu woipa

Amakhala ngati kasupe wamatope komanso chitsime chimene chawonongedwa.

27 Si bwino kudya uchi wambiri,+

Komanso si bwino kuti munthu adzifunire yekha ulemerero.+

28 Munthu wosaugwira mtima+

Ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa.

26 Sinowo sayenera kugwa mʼchilimwe ndiponso mvula siyenera kugwa pa nthawi yokolola,

Chimodzimodzinso munthu wopusa, iye sayenera kulemekezedwa.+

 2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira ndiponso namzeze amakhala ndi chifukwa choulukira.

Nalonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.*

 3 Chikwapu nʼchokwapulira hatchi, zingwe nʼzomangira pakamwa pa bulu,+

Ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.+

 4 Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake,

Kuti iweyo usafanane naye.

 5 Ukamayankha munthu wopusa uziganizira uchitsiru wake,

Kuti asaganize kuti ndi wanzeru.+

 6 Munthu amene amasiya ntchito yake mʼmanja mwa munthu wopusa

Ali ngati munthu amene wapundula mapazi ake nʼkudzivulaza yekha.*

 7 Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusa+

Uli ngati miyendo* ya munthu wolumala amene akuyenda motsimphina.

 8 Kupereka ulemerero kwa munthu wopusa,+

Kuli ngati kumanga mwala pagulaye.*

 9 Mwambi wamʼkamwa mwa anthu opusa

Uli ngati chitsamba chaminga chimene chili mʼmanja mwa munthu woledzera.

10 Wolemba ntchito munthu wopusa kapena anthu ongodutsa mʼnjira,

Ali ngati woponya muvi ndi uta amene amangolasa mwachisawawa nʼkuvulaza anthu.

11 Wopusa amabwereza zochita zake zopusa+

Mofanana ndi galu amene amabwerera kumasanzi ake.

12 Kodi waona munthu amene amaganiza kuti ndi wanzeru?+

Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa iyeyo.

13 Waulesi amanena kuti: “Mumsewu muli mkango wamphamvu,

Mʼbwalo la mzinda mukuyendayenda mkango.”+

14 Mofanana ndi chitseko chimene chimangozungulira pamene anachimangirira,

Waulesi nayenso amangotembenukatembenuka pabedi pake.+

15 Munthu waulesi amapisa dzanja lake mʼmbale ya chakudya,

Koma amalephera kulibweretsa pakamwa pake chifukwa chotopa kwambiri.+

16 Munthu waulesi amaganiza kuti ndi wanzeru kwambiri

Kuposa anthu 7 amene ayankha zanzeru.

17 Munthu wongodutsa amene amakwiya chifukwa cha mkangano* womwe si wake,+

Ali ngati munthu wogwira makutu a galu.

18 Munthu wamisala amene akuponya mivi yoyaka moto komanso mivi yakupha,

19 Akufanana ndi munthu amene amapusitsa mnzake nʼkunena kuti, “Inetu ndimangochita zocheza.”+

20 Ngati palibe nkhuni moto umazima,

Ndipo ngati palibe munthu wonenera anzake zoipa, mikangano imatha.+

21 Makala komanso nkhuni zimachititsa kuti moto uziyaka,

Mofanana ndi zimenezi munthu wokonda kuyambana ndi anthu amakolezera mikangano.+

22 Mawu a munthu wonenera ena zoipa ali ngati chakudya chokoma,*

Akachimeza chimalowa mʼmimba.+

23 Mawu achikondi ochokera pakamwa pa munthu wa mtima woipa,+

Ali ngati siliva wokutira phale.

24 Munthu amene amadana ndi ena amabisa chidanicho ndi milomo yake,

Koma mumtima mwake mumakhala chinyengo.

25 Ngakhale azilankhula mawu okoma, usamukhulupirire,

Chifukwa mumtima mwake muli zinthu 7 zonyansa.*

26 Ngakhale chidani chake chitaphimbika ndi chinyengo,

Zoipa zake zidzaululika mumpingo.

27 Amene akukumba dzenje adzagweramo yekha,

Ndipo amene akugubuduza mwala udzabwerera kwa iye nʼkumupsinja.+

28 Lilime lonama limadana ndi amene lamʼpweteka,

Ndipo pakamwa polankhula mwachiphamaso pamabweretsa chiwonongeko.+

27 Usadzitame ndi zimene udzachite mawa

Chifukwa sukudziwa zimene zidzachitike mawa.*+

 2 Munthu wina* akutamande, osati pakamwa pako.

Anthu ena* akutamande, osati milomo yako.+

 3 Mwala umalemera ndiponso mchenga umalemera,

Koma mavuto ochititsidwa ndi munthu wopusa amalemera kwambiri kuposa zonsezi.+

 4 Mkwiyo ndi wankhanza ndipo umawononga ngati madzi osefukira,

Koma nsanje ndi ndani angaipirire?+

 5 Kudzudzula munthu mosabisa mawu nʼkwabwino kusiyana ndi kumukonda koma osamusonyeza chikondicho.+

 6 Mabala ovulazidwa ndi mnzako amakhala okhulupirika,+

Koma makisi a munthu* amene amadana nawe amakhala ambiri.*

 7 Munthu akakhuta amakana kudya* uchi wakuchisa,

Koma kwa munthu wanjala, ngakhale chinthu chowawa chimatsekemera.

 8 Mofanana ndi mbalame imene yasochera* pachisa pake,

Ndi mmenenso alili munthu amene wasochera kunyumba kwake.

 9 Mafuta ndi zofukiza zonunkhira nʼzimene zimasangalatsa mtima.

Chimodzimodzinso kukhala ndi mnzako wabwino amene amakupatsa malangizo mosapita mʼmbali.+

10 Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako,

Ndipo usalowe mʼnyumba ya mchimwene wako pa tsiku limene tsoka lakugwera.

Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa mchimwene wako amene ali kutali.+

11 Mwana wanga, khala wanzeru ndipo usangalatse mtima wanga,+

Kuti ndimuyankhe amene amanditonza.+

12 Munthu wochenjera akaona tsoka amabisala,+

Koma wosadziwa zinthu amangopitabe ndipo amakumana ndi mavuto.

13 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.

Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+

14 Munthu akapereka moni kwa mnzake* mokuwa mʼmamawa kwambiri,

Mnzakeyo sangasangalale nazo.*

15 Mkazi wolongolola* ali ngati denga limene limadontha nthawi zonse pa tsiku la mvula.+

16 Amene angakwanitse kumuletsa angathenso kuimitsa mphepo

Ndipo angathe kugwira mafuta ndi dzanja lake lamanja.

17 Chitsulo chimanola chitsulo chinzake.

Chimodzimodzinso munthu amanola munthu mnzake.*+

18 Amene amasamalira mtengo wa mkuyu adzadya zipatso zake,+

Ndipo amene amasamalira mbuye wake adzalemekezedwa.+

19 Chithunzi cha nkhope ya munthu chimaonekera mʼmadzi,

Mofanana ndi zimenezi, mtima wa munthu umaonekera mumtima wa munthu wina.

20 Manda ndiponso malo achiwonongeko* sakhuta,+

Nawonso maso a munthu sakhuta.

21 Siliva amamuyengera mʼmbiya yoyengera ndipo golide amamuyengera mungʼanjo,+

Mofanana ndi zimenezi munthu amayesedwa ndi zimene anthu akunena pomutamanda.*

22 Ngakhale utasinja chitsiru ndi musi

Ngati mmene umasinjira mbewu mumtondo,

Uchitsiru wake sungachichokere.

23 Uyenera kudziwa bwino maonekedwe a ziweto zako.

Uzisamalira bwino* nkhosa zako,+

24 Chifukwa chuma sichidzakhalapo mpaka kalekale+

Komanso chisoti chachifumu sichidzakhalapo ku mibadwo yonse.

25 Udzu wobiriwira umapita ndipo udzu watsopano umaonekera,

Komanso zomera zamʼmapiri zimasonkhanitsidwa.

26 Nkhosa zamphongo zazingʼono zimakupezetsa zovala,

Ndipo mbuzi zamphongo ndi malipiro ogulira munda.

27 Udzakhala ndi mkaka wa mbuzi wokwanira woti udye,

Woti udyetse banja lako komanso atsikana ako antchito.

28 Anthu oipa amathawa popanda wowathamangitsa,

Koma olungama amakhala olimba mtima ngati mkango.*+

 2 Anthu okhala mʼdziko akamachimwa,* dzikolo limasintha akalonga pafupipafupi,+

Koma kalonga akamathandizidwa ndi munthu wozindikira komanso wodziwa zinthu, amakhala nthawi yaitali.+

 3 Munthu wosauka amene amabera mwachinyengo anthu onyozeka,+

Ali ngati mvula imene imakokolola chakudya chonse.

 4 Anthu amene asiya chilamulo amatamanda munthu woipa,

Koma amene amasunga chilamulo amakwiyira anthu amene asiya chilamulowo.+

 5 Anthu oipa sangamvetse chilungamo,

Koma amene akufunafuna Yehova angathe kumvetsa chilichonse.+

 6 Munthu wosauka amene amachita zinthu mokhulupirika,

Ali bwino kuposa munthu wolemera amene amachita zachinyengo.+

 7 Mwana womvetsa zinthu amatsatira malamulo,

Koma amene amakonda kucheza ndi anthu osusuka amachititsa manyazi bambo ake.+

 8 Munthu amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja+ ndi katapira,

Chuma chakecho chidzapita kwa munthu amene amakomera mtima anthu osauka.+

 9 Munthu amene amakana kumvera chilamulo,

Ngakhale pemphero lake limakhala lonyansa.+

10 Munthu amene amasocheretsa anthu owongoka mtima kuti azichita zinthu zoipa, adzagwera mʼdzenje lake lomwe,+

Koma anthu osalakwa adzalandira zinthu zabwino.+

11 Munthu wolemera amadziona ngati wanzeru,+

Koma munthu wosauka amene ndi wozindikira amamufufuza nʼkudziwa zoona zake.+

12 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, anthu amasangalala kwambiri,*

Koma anthu oipa akayamba kulamulira, anthu amabisala.+

13 Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino,+

Koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.+

14 Wosangalala ndi munthu amene nthawi zonse amasamala zochita zake,*

Koma amene amaumitsa mtima wake adzakumana ndi tsoka.+

15 Mtsogoleri woipa amene akulamulira anthu onyozeka+

Ali ngati mkango wobangula komanso chimbalangondo chimene chakonzekera kugwira nyama.

16 Mtsogoleri wosazindikira amagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika,+

Koma amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo adzatalikitsa moyo wake.+

17 Munthu amene ali ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu, adzakhala wothawathawa mpaka kumanda.*+

Aliyense asamuthandize.

18 Amene amayenda mosalakwitsa kanthu adzapulumutsidwa,+

Koma amene njira zake ndi zokhotakhota adzagwa mwadzidzidzi.+

19 Munthu amene amalima munda wake adzakhala ndi chakudya chambiri,

Koma amene akutanganidwa ndi zinthu zopanda phindu adzakhala pa umphawi waukulu.+

20 Munthu wokhulupirika adzalandira madalitso ambiri,+

Koma amene akufuna kulemera mofulumira, sadzapitiriza kukhala wosalakwa.+

21 Si bwino kukondera.+

Koma munthu akhoza kuchita zinthu zolakwika pofuna kupeza kachidutswa ka chakudya.

22 Munthu wadyera amayesetsa kuti apeze chuma,

Osadziwa kuti umphawi udzamugwira.

23 Amene amadzudzula munthu,+ pambuyo pake adzakondedwa kwambiri+

Kuposa munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamaso.

24 Wobera bambo ake ndi mayi ake nʼkumanena kuti, “Si kulakwa,”+

Amakhala ngati mnzake wa munthu wobweretsa chiwonongeko.+

25 Munthu wadyera amayambitsa mikangano,

Koma aliyense amene amadalira Yehova zinthu zidzamuyendera bwino.*+

26 Aliyense amene amadalira mtima wake ndi wopusa,+

Koma amene amachita zinthu mwanzeru adzapulumuka.+

27 Aliyense amene amapereka zinthu zake kwa anthu osauka sadzasowa kanthu,+

Koma amene amatseka maso ake kuti asaone osaukawo adzalandira matemberero ambiri.

28 Munthu woipa akayamba kulamulira, munthu amabisala,

Koma oipawo akatha anthu olungama amachuluka.+

29 Munthu amene amaumitsa khosi lake* pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza+

Adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.+

 2 Olungama akachuluka, anthu amasangalala,

Koma munthu woipa akamalamulira, anthu amabuula.+

 3 Munthu amene amakonda nzeru amasangalatsa bambo ake,+

Koma woyenda ndi mahule amawononga chuma chake.+

 4 Mfumu ikamachita zinthu zachilungamo dziko limalimba,+

Koma munthu wokonda ziphuphu amaligwetsa.

 5 Munthu amene amayamikira mnzake mwachiphamaso

Akuyalira ukonde mapazi ake.+

 6 Tchimo la munthu woipa limamutchera msampha,+

Koma munthu wolungama amafuula mokondwera ndipo amasangalala.+

 7 Wolungama amafunitsitsa kuti anthu osauka aziweruzidwa mwachilungamo,+

Koma woipa safuna kuchita zimenezi.+

 8 Anthu odzitama ali ngati anthu amene amayatsa tauni,+

Koma anthu anzeru amaletsa mkwiyo.+

 9 Munthu wanzeru akayamba kukangana ndi chitsiru,

Pamangokhala phokoso ndi kunyozana, ndipo munthu wanzeruyo sapindula chilichonse.+

10 Anthu okonda kukhetsa magazi amadana ndi munthu aliyense wosalakwa,+

Ndipo amafuna kuchotsa moyo wa anthu owongoka mtima.*

11 Munthu wopusa amatulutsa mkwiyo wake wonse,+

Koma wanzeru amakhala wodekha ndipo amalamulira mkwiyo wake.+

12 Wolamulira akamamvera mabodza,

Antchito ake onse adzakhala oipa.+

13 Munthu wosauka komanso munthu wopondereza ena ndi ofanana* pa chinthu chimodzi ichi:

Yehova amachititsa kuti maso a onsewa aziona kuwala.*

14 Mfumu ikamaweruza anthu osauka mwachilungamo,+

Idzapitiriza kulamulira mpaka kalekale.+

15 Chikwapu* komanso kudzudzula nʼzimene zimapereka nzeru,+

Koma mwana womulekerera amachititsa manyazi mayi ake.

16 Oipa akachuluka, machimo amachuluka,

Koma olungama adzaona oipawo akugwa.+

17 Langa mwana wako ndipo adzakupatsa mpumulo

Komanso adzakusangalatsa kwambiri.+

18 Ngati anthu sakutsogoleredwa ndi Mulungu, amachita zinthu motayirira,+

Koma osangalala ndi amene amatsatira chilamulo.+

19 Wantchito safuna kusintha ndi mawu okha,

Chifukwa ngakhale atamvetsa mawuwo, safuna kuwatsatira.+

20 Kodi waona munthu amene amafulumira kulankhula asanaganize?+

Munthu wopusa ali ndi chiyembekezo chachikulu kuposa munthu ameneyu.+

21 Ngati munthu akusasatitsa kapolo wake kuyambira ali mwana,

Mʼtsogolo adzakhala wosayamika.

22 Munthu wosachedwa kukwiya amayambitsa mkangano.+

Aliyense amene sachedwa kupsa mtima amakhala ndi machimo ambiri.+

23 Kudzikuza kwa munthu kudzamutsitsa,+

Koma amene ali ndi mtima wodzichepetsa adzapeza ulemerero.+

24 Amene amathandiza munthu wakuba amadzibweretsera mavuto.

Iye angamve kuitana kuti akapereke umboni,* koma osakanena chilichonse.+

25 Kuopa anthu ndi msampha,*+

Koma amene amakhulupirira Yehova adzatetezedwa.+

26 Anthu ambiri amafunitsitsa kuonana ndi wolamulira,*

Koma kwa Yehova nʼkumene munthu amapeza chilungamo.+

27 Munthu wopanda chilungamo ndi wonyansa kwa anthu olungama,+

Koma munthu amene amachita zabwino ndi wonyansa kwa munthu woipa.+

30 Uwu ndi uthenga wamphamvu womwe Aguri mwana wa Yake analankhula ndi Itiyeli komanso Ukali.

 2 Ine sindidziwa zambiri poyerekeza ndi anthu ena onse,+

Ndipo sinditha kumvetsa zinthu ngati mmene anthu ena amachitira.

 3 Ine sindinaphunzire zinthu zanzeru,

Ndipo sindidziwa zinthu zimene Woyera Koposa amadziwa.

 4 Ndi ndani amene anakwerapo kumwamba kenako nʼkutsika?+

Ndi ndani amene anasonkhanitsapo mphepo mʼmanja mwake?

Ndi ndani amene anamangapo madzi pachovala chake?+

Ndi ndani amene anaika malire a dziko lapansi?+

Dzina lake ndi ndani, nanga mwana wake dzina lake ndi ndani? Ndiuzeni ngati mukudziwa.

 5 Mawu onse a Mulungu ndi oyengeka.+

Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.+

 6 Usawonjezere kanthu pa mawu ake+

Kuti angakudzudzule,

Nʼkuoneka kuti ndiwe wabodza.

 7 Ndikukupemphani zinthu ziwiri.

Mundipatse zinthu zimenezi ndisanafe.

 8 Zinthu zabodza komanso mawu onama muziike kutali ndi ine.+

Musandipatse umphawi kapena chuma.

Mungondipatsa chakudya chokwanira,+

 9 Kuti ndisakhute kwambiri nʼkukukanani kuti: “Kodi Yehova ndi ndani?”+

Ndiponso kuti ndisasauke nʼkukaba ndi kuchititsa kuti dzina la Mulungu wanga linyozedwe.

10 Usanenere wantchito zoipa kwa bwana wake,

Kuti angakutemberere ndipo ungapezeke wolakwa.+

11 Pali mʼbadwo umene umatemberera bambo awo

Komanso umene sudalitsa mayi awo.+

12 Pali mʼbadwo umene umadziona kuti ndi woyera+

Koma sunayeretsedwe ku zonyansa zake.*

13 Pali mʼbadwo umene maso ake ndi onyada

Ndiponso umene maso ake amayangʼana modzikweza.+

14 Pali mʼbadwo umene mano ake ndi malupanga

Ndiponso umene nsagwada zake ndi mipeni yophera nyama.

Mʼbadwowo umapondereza anthu ovutika apadziko lapansi

Komanso osauka pakati pa anthu.+

15 Misundu* ili ndi ana aakazi awiri amene amafuula kuti, “Tipatseni! Tipatseni!”

Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta

Ndiponso zinthu 4 zimene sizinena kuti, “Ndakhuta!” Zinthu zake ndi izi:

16 Manda,*+ mimba yosabereka,

Nthaka yopanda madzi

Komanso moto umene sunena kuti, “Ndakhuta!”

17 Munthu amene amanyoza bambo ake ndiponso amene samvera mayi ake,+

Akhwangwala akuchigwa* adzakolowola diso lake

Ndipo ana a chiwombankhanga adzalidya.+

18 Pali zinthu zitatu zimene nʼzodabwitsa kwambiri kwa ine,

Ndiponso zinthu 4 zimene sindizimvetsa. Zinthu zake ndi izi:

19 Njira ya chiwombankhanga mumlengalenga,

Njira ya njoka pamwala,

Njira ya sitima pakatikati pa nyanja,

Ndiponso njira ya mwamuna ndi mtsikana.

20 Zimene mkazi wachigololo amachita ndi izi:

Iye amadya nʼkupukuta pakamwa pake

Kenako amanena kuti, “Sindinachite cholakwa chilichonse.”+

21 Pali zinthu zitatu zimene zimagwedeza dziko lapansi

Ndiponso zinthu 4 zimene dziko lapansi silitha kuzipirira. Zinthu zake ndi izi:

22 Kapolo akamalamulira monga mfumu,+

Munthu wopusa akamadya kwambiri,

23 Mkazi amene amadedwa* akakwatiwa,

Komanso mtsikana wantchito akatenga malo a abwana ake aakazi.+

24 Pali zinthu 4 zomwe zili mʼgulu la zinthu zingʼonozingʼono kwambiri padziko lapansi

Koma ndi zanzeru mwachibadwa.* Zinthu zake ndi izi:+

25 Nyerere si zamphamvu,

Koma zimasonkhanitsa chakudya chawo mʼchilimwe.+

26 Mbira+ si nyama zamphamvu

Koma zimamanga nyumba zawo pathanthwe.+

27 Dzombe+ lilibe mfumu

Koma limauluka lonse litagawikana mʼmagulumagulu.+

28 Nalimata+ amagwira zinthu ndi mapazi ake

Ndipo amalowa mʼnyumba yachifumu.

29 Pali zinthu zitatu zimene zimayenda mochititsa chidwi

Ndiponso zinthu 4 zimene zimasangalatsa zikamayenda. Zinthu zake ndi izi:

30 Mkango umene ndi wamphamvu kwambiri panyama zonse zakutchire

Ndiponso umene suopa chilichonse nʼkubwerera mʼmbuyo,+

31 Galu wosaka kapena mbuzi yamphongo,

Ndiponso mfumu imene ili limodzi ndi asilikali ake.

32 Ngati wachita zinthu zopusa nʼkudzikweza,+

Kapena ngati ukufuna kuchita zimenezo,

Gwira pakamwa pako.+

33 Chifukwa mkaka ukaukhutchumula umatulutsa mafuta,

Mphuno ukaifinya imatulutsa magazi,

Ndipo kukolezera mkwiyo kumayambitsa mkangano.+

31 Mawu a Mfumu Lemueli, uwu ndi uthenga wamphamvu umene mayi ake anamupatsa pomulangiza:+

 2 Kodi ndikuuze chiyani mwana wanga?

Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wochokera mʼmimba mwanga?

Kodi ndikuuze mawu otani iwe mwana wa malonjezo anga?+

 3 Usamapereke mphamvu zako kwa akazi,+

Kapena kutsatira njira zimene zimachititsa kuti mafumu awonongedwe.+

 4 Nʼkosayenera kuti mafumu azimwa vinyo,

Nʼkosayenera kuti mafumu azichita zimenezi, iwe Lemueli,

Kapena kuti olamulira azinena kuti: “Kodi chakumwa changa chili kuti?”+

 5 Chifukwa angamwe nʼkuiwala malamulo

Ndiponso kupondereza ufulu wa anthu onyozeka.

 6 Pereka mowa kwa anthu amene akuwonongedwa+

Komanso vinyo kwa anthu amene ali ndi nkhawa.*+

 7 Asiyeni amwe kuti aiwale umphawi wawo,

Ndipo asakumbukirenso mavuto awo.

 8 Lankhula poteteza anthu amene sangathe kudziteteza okha.

Teteza ufulu wa anthu onse amene akuwonongedwa.+

 9 Lankhula ndipo uweruze mwachilungamo.

Teteza ufulu wa anthu onyozeka komanso osauka.*+

א [Aleph]

10 Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino?*+

Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya korali.*

ב [Beth]

11 Mwamuna wake amamudalira ndi mtima wonse,

Ndipo mwamunayo amapeza chilichonse chimene akufunikira.

ג [Gimel]

12 Masiku onse a moyo wake,

Mkaziyo amachitira mwamuna wakeyo zinthu zabwino osati zoipa.

ד [Daleth]

13 Amatenga ulusi ndi nsalu,

Ndipo amasangalala kugwira ntchito ndi manja ake.+

ה [He]

14 Iye ali ngati sitima zapamadzi za munthu wamalonda,+

Amabweretsa chakudya chake kuchokera kutali.

ו [Waw]

15 Amadzukanso kudakali usiku,

Nʼkupereka chakudya kwa banja lake

Ndipo atsikana ake antchito amawapatsa gawo lawo.+

ז [Zayin]

16 Amaganizira zogula munda ndipo amauguladi.

Amalima munda wa mpesa chifukwa cha khama lake.*

ח [Heth]

17 Amakonzekera kugwira ntchito yovuta,*+

Ndipo amalimbitsa manja ake.

ט [Teth]

18 Amaonetsetsa kuti akupeza phindu pa malonda ake.

Nyale yake simazima usiku.

י [Yod]

19 Manja ake amagwira ndodo yokulungako ulusi,

Ndipo zala zake zimagwira ndodo yopotera chingwe.+

כ [Kaph]

20 Amatambasula dzanja lake nʼkuthandiza munthu wonyozeka,

Ndipo amatambasula manja ake kuti athandize wosauka.+

ל [Lamed]

21 Kukamazizira, iye sadera nkhawa za banja lake

Chifukwa anthu onse a mʼbanja lake amavala zovala zotentha.*

מ [Mem]

22 Iye amapanga yekha zoyala pabedi.

Zovala zake zimakhala za nsalu zabwino ndiponso za ubweya wa nkhosa wapepo.

נ [Nun]

23 Mwamuna wake amadziwika bwino pamageti a mzinda,+

Pamene amakhala pamodzi ndi akulu amʼdzikolo.

ס [Samekh]

24 Iye amapanga zovala* nʼkuzigulitsa,

Ndipo amapanga malamba nʼkuwapereka kwa amalonda.

ע [Ayin]

25 Iye amavala mphamvu ndi ulemerero ngati chovala,

Ndipo sada nkhawa akamaganizira zamʼtsogolo.

פ [Pe]

26 Amatsegula pakamwa pake mwanzeru,+

Ndipo lamulo la kukoma mtima lili* palilime lake.

צ [Tsade]

27 Iye amayangʼanira ntchito zapabanja pake,

Ndipo sadya chakudya cha ulesi.+

ק [Qoph]

28 Ana ake amaimirira nʼkumutchula kuti ndi wosangalala.

Mwamuna wake amaimirira nʼkumutamanda kuti:

ר [Resh]

29 “Pali akazi ambiri amakhalidwe abwino,*

Koma iweyo umaposa onsewo.”

ש [Shin]

30 Munthu akhoza kuoneka ngati wabwino koma zisali choncho ndipo kukongola sikungachedwe kutha,*+

Koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.+

ת [Taw]

31 Mʼpatseni mphoto chifukwa cha zimene amachita,*+

Ndipo ntchito zake zimutamande mʼmageti a mzinda.+

Mʼchilankhulo choyambirira, “adziwe.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Kapena kuti, “zachilungamo.”

Kapena kuti, “komanso ziningʼa.”

Kapena kuti, “malamulo.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Tiye tichitire limodzi maere.”

Kapena kuti, “Tonse tikagwiritsa ntchito chikwama chimodzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamutu wa.”

Kapena kuti, “Ndikakudzudzulani, mubwerere.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzadya zipatso.”

Kapena kuti, “zolinga zawo zidzawabweretsera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.” Kutanthauza munthu amene amachita makhalidwe amene sasangalatsa Mulungu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.” Kutanthauza munthu amene ndi wotalikirana ndi Mulungu chifukwa cha makhalidwe ake oipa.

Kapena kuti, “amasiya mwamuna wake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amapita kwa iye.”

Kapena kuti, “amene amachita zinthu mokhulupirika.”

Kapena kuti, “usaiwale malamulo anga.”

Kapena kuti, “choonadi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “usatsamire.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mchombo wako.”

Kapena kuti, “Ndiponso ndi zinthu zabwino kwambiri pa zokolola zako.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Zikuoneka kuti akutanthauza makhalidwe a Mulungu amene atchulidwa mʼmavesi amʼmbuyomu.

Kapena kuti, “silidzawomba chilichonse.”

Kapena kuti, “amene akufunikira.”

Kapena kuti, “Ngati dzanja lako lingathe kuchita zimenezo.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Kapena kuti, “lamulo langa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tchera khutu lako ku.”

Kapena kuti, “maso ako owala aziyangʼanitsitsa.”

Mabaibulo ena amati, “Sinkhasinkha bwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti usapereke zaka zako ku zinthu zankhanza.”

Kapena kuti, “mphamvu zako.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa msonkhano komanso mpingo.”

Kapena kuti, “Pamene umatunga madzi ako pakhale podalitsidwa.”

Kapena kuti, “azikusangalatsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Kapena kuti, “malamulo.”

Kapena kuti, “adzakupatsa malangizo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Kapena kuti, “ali ndi zolinga zoipa.”

Kapena kuti, “sadzavomera dipo lililonse.”

Kapena kuti, “malamulo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachilendo.”

Kapena kuti, “mnyamata wina amene ali ndi zolinga zoipa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo mapazi ake sakhala pakhomo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zamitundu yosiyanasiyana.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi ana a anthu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “muumvetse mtima.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “cholowa chamtengo wapatali.”

Kapena kuti, “kuyambira nthawi yosakumbukirika.”

Kapena kuti, “Ndinabadwa ndi ululu wapobereka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ankalimbitsa.”

Kapena kuti, “mtundu wa anthu ndi umene unkandisangalatsa kwambiri.”

Kapena kuti, “Pokhala maso pakhomo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Yapha nyama yake.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Mbiri yake ikakumbukiridwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “malamulo.”

Kapena kuti, “amaona kuti zinthu zake zamtengo wapatali zili.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Mabaibulo ena amati, “akuyenda panjira ya kumoyo.”

Kapena kuti, “imatsogolera.”

Kapena kuti, “chisoni; mavuto.”

“Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.

Kapena kuti, “kwa amene anamulemba ntchito.”

Kapena kuti, “Chiyembekezo cha anthu olungama chimasangalatsa.”

Kapena kuti, “pamabereka zipatso.”

Kapena kuti, “mwala woyezera wolemera mokwanira umamusangalatsa.”

Kapena kuti, “Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda.”

Kapena kuti, “Munthu wosaopa Mulungu.”

Kapena kuti, “amanyoza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wa mzimu wokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amabisa nkhani.”

Kapena kuti, “Koma munthu amapulumuka.”

Kapena kuti, “aphungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amadana ndi.”

Kapena kuti, “wachikondi chokhulupirika.”

Kapena kuti, “amachitira zabwino moyo wake.”

Kapena kuti, “manyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amamwaza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepetsedwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amathirira ena mosaumira.”

Kapena kuti, “manyazi.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Kapena kuti, “wopanda nzeru.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene amadikirira kuti akhetse magazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pake.”

Kapena kuti, “uphungu.”

Kapena kuti, “tsiku lomwelo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amangoziphimba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zachilungamo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “alangizi a mtendere.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Kapena kuti, “akalangizidwa.”

Kapena kuti, “zimene amalankhula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzudzulidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kukusangalala.”

Kapena kuti, “amene amakhala pamodzi nʼkumakambirana.”

Kapena kuti, “mʼnjira zachinyengo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachisonkhanitsa ndi manja ake.”

Kapena kuti, “Chilamulo cha munthu wanzeru.”

Kapena kuti, “akadzudzulidwa.”

Kapena kuti, “angathe kuwonongedwa.”

Kapena kuti, “sapereka chilango kwa.”

Mabaibulo ena amati, “sazengereza.”

Kapena kuti, “zopotoka.”

Mabaibulo ena amati, “anthu opusa amapusitsa anzawo.”

Kapena kuti, “Anthu opusa akapalamula mlandu zoti akonze zinthu zimangowaseketsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “idzalemera.”

Kapena kuti, “amakhala wokwiya.”

Kapena kuti, “moleza mtima.”

Kapena kuti, “Lilime lochiritsa.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Kapena kuti, “chowawa kwambiri.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndiponso Abadoni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”

Kapena kuti, “wabwino.”

Kapena kuti, “koma uli wosokonezeka maganizo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “yodyetsedwa bwino.”

Kapena kuti, “sakambirana moona mtima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “manyazi.”

Kapena kuti, “Kuyangʼana munthu ndi nkhope yachimwemwe kumapangitsa.”

Kapena kuti, “umanenepetsa mafupa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Munthu ndi amene amaika maganizo amumtima mwake mwadongosolo.”

Kapena kuti, “yankho lolondola.” Mʼchilankhulo choyambirira, “yankho la lilime.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zoyera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Pereka ntchito zako kwa Yehova.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake.”

Kapena kuti, “amaupewa.”

Kapena kuti, “mawu osangalatsa.” Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi milomo yotsekemera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pamamuchititsa.”

Kapena kuti, “wokonza ziwembu.”

Kapena kuti, “popanda phokoso.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nsembe zochuluka.”

Kapena kuti, “makolo awo.”

Kapena kuti, “mawu abwino.”

Kapena kuti, “wolemekezeka.”

Kapena kuti, “Mphatso ndi mwala umene umachititsa kuti mwiniwake akomeredwe mtima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amaphimba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kutsegulira madzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Pamene ali wopanda nzeru?”

Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzapeza zabwino.”

Kapena kuti, “mafupa ake amauma.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakwiyitsa.”

Kapena kuti, “kulipiritsa chindapusa.”

Kapena kuti, “Amanyansidwa ndi.”

Kapena kuti, “ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakwezedwa mʼmwamba,” kutanthauza kuti amaikidwa mʼmalo otetezeka.

Kapena kuti, “kudzamufufuza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumalekanitsa.”

Kapena kuti, “amamufunira zabwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amayenda mofulumira ndi mapazi ake.”

Kapena kuti, “wowolowa manja.”

Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”

Kapena kuti, “adzamʼpatsa mphoto pa.”

Kapena kuti, “Ndipo usalakelake.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Mabaibulo ena amati, “Pa nthawi yokolola adzafunafuna zinthu koma sadzazipeza.”

Kapena kuti, “Zolinga zamumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Malangizo amumtima.”

Kapena kuti, “amapeta.”

Kapena kuti, “Miyala iwiri yosiyana yoyezera ndiponso zinthu ziwiri zosiyana zoyezera.”

Kapena kuti, “mnyamata.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “zimakhazikika.”

Kapena kuti, “amene amakonda kukopa ena ndi milomo yake.”

Kapena kuti, “miyala iwiri yosiyana yoyezera.”

Kapena kuti, “zolinga.”

Kapena kuti, “zinthu zimupindulire.”

Mabaibulo ena amati, “mofulumira kwa amene akufunafuna imfa.”

Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”

Kapena kuti, “amadziwa zoyenera kuchita.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chiphuphu chobisidwa pachovala.”

Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amameza.”

Kapena kuti, “amakwera mpanda wa.”

Kapena kuti, “limodzi ndi khalidwe lochititsa manyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzalankhula kwamuyaya.”

Kapena kuti, “mbiri yabwino.” Mʼchilankhulo choyambirira, “dzina.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Kukomeredwa mtima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Amene ali ndi diso labwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “achilendo.” Onani Miy. 2:16.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Uziika mpeni pakhosi pako.”

Mabaibulo ena amati, “Leka kudzidalira kuti ndiwe womvetsa zinthu.”

Kapena kuti, “cha aliyense amene diso lake ndi loipa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Wowawombola.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Impso zanga zidzasangalala.”

Kapena kuti, “Peza.”

Kapena kuti, “wachilendo.” Onani Miy. 2:16.

Kapena kuti, “Amene amasonkhana kuti alawe.”

Kapena kuti, “mlongoti.”

Kapena kuti, “banja la.”

Kapena kuti, “aphungu.”

Kapena kuti, “zinthu zidzakuyendera bwino; udzapulumuka.”

Kapena kuti, “Ziwembu za munthu.”

Kapena kuti, “nʼzotsekemera kwa iwe.”

Kutanthauza Yehova komanso mfumu.

Mabaibulo ena amati, “Kuyankha mosapita mʼmbali kuli ngati kukisa munthu.”

Kapena kuti, “ukalimbitse banja lako.”

Kapena kuti, “usaulule zinsinsi za ena.”

Kapena kuti, “mphekesera zoipa.”

Kapena kuti, “chipale chofewa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “lilime lofewa likhoza.”

Mabaibulo ena amati, “munthu amene amachita zachinyengo.”

“Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene amadana nawe.”

Kutanthauza kufewetsa mtima wake komanso kumuchititsa kuti azichita zinthu zabwino.

Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amanjenjemera pamaso pa munthu woipa.”

Mabaibulo ena amati, “Ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ali ngati munthu amene amamwa chiwawa.”

Kapena kuti, “miyendo yalendelende.”

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.

Mabaibulo ena amati, “amene amalowerera mkangano.”

Kapena kuti, “ngati zinthu zofunika kuzimeza msangamsanga.”

Kapena kuti, “Chifukwa mtima wake ndi wonyansa kwambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “sukudziwa kuti tsiku libala chiyani.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anthu ochokera kudziko lina.”

Kapena kuti, “kupsompsona kwa munthu.”

Mabaibulo ena amati, “osachokera pansi pa mtima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amapondaponda.”

Kapena kuti, “ikuthawa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akadalitsa mnzake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “angaone ngati akumutemberera.”

Kapena kuti, “wokonda kudandaula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope ya mnzake.”

Kapena kuti, “Abadoni.”

Kapena kuti, “munthu amasonyeza mmene alili anthu akamamutamanda.”

Kapena kuti, “Uziika mtima wako pa; Uziyangʼanira.”

Kapena kuti, “mkango wamphamvu.”

Kapena kuti, “akamachita zinthu zoukira.”

Kapena kuti, “pamakhala ulemerero wochuluka.”

Kapena kuti, “amene sachita mantha.”

Kapena kuti, “mʼdzenje.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzanenepa.”

Kapena kuti, “amene safuna kusintha.”

Mabaibulo ena amati, “Koma anthu owongoka mtima amasamalira moyo wa anthu opanda cholakwawo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakumana pamodzi.”

Kutanthauza kuti amawapatsa moyo.

Kapena kuti, “Chilango.”

Kapena kuti, “lumbiro limene linalinso ndi mawu otemberera.”

Kapena kuti, “kumatchera msampha.”

Mabaibulo ena amati, “amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ku ndowe zake.”

“Msundu” ndi mtundu wa nyongolotsi zimene zimakhala mʼmadzi ndipo zimaluma anthu kapena zinyama nʼkumayamwa magazi.

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “akukhwawa.”

Kapena kuti, “sakondedwa.”

Kapena kuti, “ndi zanzeru kwambiri.”

Kapena kuti, “amene mtima wawo ukuwawa.”

Kapena kuti, “Teteza anthu onyozeka komanso osauka pa mlandu wawo.”

Kapena kuti, “wabwino kwambiri.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “pogwiritsa ntchito ndalama zimene wapeza.” Mʼchilankhulo choyambirira, “pogwiritsa ntchito zipatso za manja ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Amamangirira mphamvu mchiuno mwake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zovala ziwiri.”

Kapena kuti, “zovala zamkati.”

Kapena kuti, “Malangizo achikondi ali; Lamulo la chikondi chokhulupirika lili.”

Kapena kuti, “abwino kwambiri.”

Kapena kuti, “kukhoza kukhala kopanda phindu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mupatseni kuchokera pa zipatso za manja ake.”

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani