Kodi Mungatani Kuti Mupirire Mavuto a M’Dzikoli?
Na. 1 2022
© 2022 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira, pitani pa donate.jw.org. Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kupatulako ngati tasonyeza Baibulo lina.
Mawu Oyamba
Pamene zinthu m’dzikoli zikuipiraipira, anthufe tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana obwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe komanso oyambitsidwa ndi anthu. Onani zimene mungachite kuti mupirire mavutowa komanso kuti mudziteteze ndi kuteteza okondedwa anu