Kodi Mukufuna Kudziwa Zambiri?
Kabuku kano kangofotokoza mwachidule kwambiri nkhani zosangalatsa zimene zikupezeka m’Baibulo. Koma kabukuka sikanafotokoze mwatsatanetsatane zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani iliyonse.
Mwachitsanzo, mwina mumafuna mutadziwa mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso monga awa: Kodi Mulungu amasamala za ine ngati munthu pandekha? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi moyo wosangalala?
Mungapeze mayankho a mafunso amenewa komanso ena opatsa chidwi m’buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Bukuli lakonzedwa kuti litithandize kuphunzira nkhani za m’Baibulo imodzi ndi imodzi. Kuphunzira mwa njira imeneyi kungatithandize kupeza mosavuta malemba a m’Baibulo amene akugwirizana ndi nkhani imene tikuphunzirayo.
Mukhoza kuwerenga kapena dowunilodi kabukuka kapenanso kupempha munthu woti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere pawebusaiti yathu ya www.pr418.com/ny.