Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lfb 45
  • Ufumu Unagawikana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu Unagawikana
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Zili Mʼbuku la 1 Mafumu
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb 45
Ahiya akung’amba chovala chake zidutswa zokwana 12 Yerobowamu akuona

MUTU 45

Ufumu Unagawikana

Pamene Solomo ankalambira Yehova, ku Isiraeli kunali mtendere. Koma kenako anakwatira akazi ambiri a mitundu ina ndipo akaziwa ankalambira mafano. Pang’ono ndi pang’ono, Solomo anasintha ndipo nayenso anayamba kulambira mafano. Yehova anakwiya kwambiri ndi zimenezi. Ndiyeno anauza Solomo kuti: ‘Ufumu wa Isiraeli uchotsedwa ku banja lako ndipo ugawikana pawiri. Ndidzapereka mbali yaikulu ya ufumuwu kwa mtumiki wako ndipo banja lako lidzatsala ndi mbali yochepa.’

Yehova anachitanso zinthu zina posonyeza kuti zimenezi zidzachitikadi. Tsiku lina, mtumiki wina wa Solomo dzina lake Yerobowamu anali pa ulendo ndipo anakumana ndi mneneri Ahiya. Ahiya anang’amba chovala chake zidutswa zokwana 12. Atatero anauza Yerobowamu kuti: ‘Yehova achotsa ufumu wa Isiraeli ku banja la Solomo ndipo augawa pawiri. Tenga zidutswa 10 izi chifukwa iweyo udzakhala mfumu ya mafuko 10.’ Mfumu Solomo atamva zimenezi, ankafuna kupha Yerobowamu. Choncho Yerobowamu anathawira ku Iguputo. Patapita nthawi, Solomo anamwalira ndipo mwana wake Rehobowamu anakhala mfumu. Zitatero Yerobowamu anaona kuti akhoza kubwerera ku Isiraeli.

Aisiraeli ambiri akupereka nsembe kwa fano la mwana wa ng’ombe amene Yerobowamu waimika

Akuluakulu a ku Isiraeli anauza Rehobowamu kuti: ‘Mukamawalamulira bwino anthuwa, akhala okhulupirika kwa inu.’ Koma achinyamata anzake anamuuza kuti: ‘Anthuwa musamawalamulire mowanyengerera. Muziwagwiritsa ntchito zolemetsa kuposa zimene bambo anu ankawagwiritsa.’ Rehobowamu anamvera malangizo amenewa. Choncho ankalamulira anthuwo mwankhanza ndipo iwo anamuukira. Anthuwo anasankha Yerobowamu kuti akhale mfumu ya mafuko 10, omwe ankadziwika kuti ufumu wa Isiraeli. Mafuko awiri okha ndi amene anakhalabe okhulupirika kwa Rehobowamu ndipo ankadziwika kuti ufumu wa Yuda. Apa ndiye kuti mafuko 12 a Aisiraeli anagawikana.

Yerobowamu sankafuna kuti anthu ake azipita kukalambira ku Yerusalemu kumene mfumu yake anali Rehobowamu. Kodi ukudziwa chifukwa chake? Yerobowamu ankaopa kuti anthuwo akhoza kumuukira n’kupita kumbali ya Rehobowamu. Choncho anapanga mafano awiri a ana a ng’ombe n’kuuza anthuwo kuti: ‘Muzilambirira konkuno, chifukwatu ku Yerusalemu n’kutali.’ Ndiye anthuwo anayambadi kulambira ana a ng’ombewo ndipo anaiwala Yehova.

“Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana. Pali mgwirizano wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?  . . . Nanga munthu wokhulupirira ndi wosakhulupirira angafanane pa zinthu ziti?”—2 Akorinto 6:14, 15

Mafunso: N’chifukwa chiyani ufumu wa Isiraeli unagawikana? Kodi Mfumu Rehobowamu komanso Mfumu Yerobowamu anachita zoipa zotani?

1 Mafumu 11:1-13, 26-43; 12:1-33

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani