Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA JULY 31, 2017–AUGUST 6, 2017
4 Yehova Amatitonthoza M’masautso Athu Onse
Tonsefe timakumana ndi mavuto koma Yehova amatilimbikitsa. Nkhaniyi ikufotokoza zinthu zimene Yehova watipatsa zomwe zingatilimbikitse panopa komanso m’tsogolo.
MLUNGU WA AUGUST 7-13, 2017
9 Tizikonda ndi Mtima Wonse Chuma Chimene Mulungu Watipatsa
Nkhaniyi ikufotokoza zimene tingachite potsatira mfundo zimene tikuphunzira mufanizo la Yesu la wamalonda amene ankafunafuna ngale. Itithandizanso kudzifufuza pa nkhani ya mmene timaonera utumiki wathu ndiponso mfundo za m’Baibulo zimene taphunzira.
MLUNGU WA AUGUST 14-20, 2017
22 Musamaiwale Nkhani Yofunika Kwambiri
MLUNGU WA AUGUST 21-27, 2017
27 Muzikhala Kumbali ya Ulamuliro wa Yehova
Chifukwa chotanganidwa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku tikhoza kuiwala zinthu zofunika. Nkhanizi zitithandiza kuzindikira kuti nkhani ya ulamuliro wa Yehova ndi yofunika kwambiri. Zitithandizanso kudziwa mmene tingasonyezere kuti tili kumbali ya ulamulirowo