Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA FEBRUARY 26, 2018–MARCH 4, 2018
7 “Iye Amapereka Mphamvu kwa Munthu Wotopa”
Kodi tingatani tikamapanikizika ndi mavuto? Munkhaniyi tikambirana lemba la chaka cha 2018. Tionanso chifukwa chake tiyenera kudalira Yehova kuti azitipatsa mphamvu komanso mmene amatipatsira mphamvuzo.
MLUNGU WA MARCH 5-11, 2018
12 Chikumbutso Chimatithandiza Kukhala Ogwirizana
Chaka chino, Chikumbutso cha imfa ya Khristu chidzachitika Loweruka pa 31 March 2018. Kodi tingakonzekere bwanji mwambo umenewu? Nanga tingapindule bwanji ngati titapezekapo? Kodi mwambowu umathandiza bwanji anthu a Mulungu padziko lonse kuti azigwirizana? Nkhaniyi iyankha mafunso amenewa.
MLUNGU WA MARCH 12-18, 2018
17 N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kupereka kwa Amene Ali ndi Chilichonse?
Chilichonse chimene tili nacho chimachokera kwa Yehova. Koma iye amayembekezerabe kuti tizigwiritsa ntchito ndalama zathu pothandiza pa ntchito ya gulu lake. Nkhaniyi ikufotokoza ubwino wogwiritsa ntchito zinthu zathu zamtengo wapatali kuti tizilemekeza Yehova.
MLUNGU WA MARCH 19-25, 2018
22 Kodi Tiyenera Kukonda Ndani Kuti Tikhale Osangalala?
MLUNGU WA MARCH 26, 2018–APRIL 1, 2018
27 Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoli
Nkhani yoyamba ikusonyeza kuti kukonda Yehova n’kumene kumatithandiza kukhala osangalala, osati kukonda zinthu zopanda pake zimene anthu ambiri amazikonda ‘m’masiku otsiriza’ ano. (2 Tim. 3:1) Nkhani yachiwiri ikusonyeza kuti makhalidwe a anthu a m’dzikoli amasiyana kwambiri ndi a anthu a Mulungu.