Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA JUNE 4-10, 2018
3 Kodi Tingapeze Bwanji Ufulu Weniweni?
MLUNGU WA JUNE 11-17, 2018
8 Tizitumikira Yehova Mulungu Amene Amapereka Ufulu
Anthu ambiri masiku ano amamenyera ufulu wawo. Koma kodi Akhristu ayenera kukhala ndi maganizo otani pa nkhani ya ufulu? Nkhani ziwirizi zikufotokoza tanthauzo la ufulu weniweni komanso zimene tingachite kuti tiupeze. Zikusonyezanso mmene tingagwiritsire ntchito mwanzeru ufulu wathu kuti zinthu zitiyendere bwino komanso kuti tithandize anthu ena. Koma chofunika kwambiri n’chakuti tiona mmene tingagwiritsire ntchito ufulu wathu polemekeza Yehova amene amapereka ufulu weniweni.
MLUNGU WA JUNE 18-24, 2018
15 Tizitsanzira Yehova pa Nkhani Yolimbikitsa Ena
MLUNGU WA JUNE 25, 2018–JULY 1, 2018
20 Tizilimbikitsana Ndipo “Tiwonjezere Kuchita Zimenezi”
Nkhanizi zikusonyeza kuti Yehova wakhala akulimbikitsa atumiki ake ndipo atumiki akewo amamutsanzira n’kumalimbikitsana. Tionanso chifukwa chake tiyenera kulimbikitsana kwambiri masiku ano kuposa kale lonse
MLUNGU WA JULY 2-8, 2018
25 Achinyamata, Kodi Mukuyesetsa Kukwaniritsa Zolinga Zauzimu?
Achinyamata mumpingo zimawayendera bwino ngati ali ndi cholinga chosangalatsa Yehova. Nkhaniyi ikufotokoza chifukwa chake achinyamata ayenera kukhala ndi zolinga zauzimu adakali aang’ono. Ikufotokozanso ubwino woika patsogolo ntchito yolalikira.