Magazini Yophunzira
JUNE 2018
NKHANI ZOPHUNZIRA KUYAMBIRA: AUGUST 6–SEPTEMBER 2, 2018
© 2018 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
PATSAMBA LOYAMBA:
URUGUAY
Alongo awiri akufotokoza uthenga wofunika kwa mwini shopu mumzinda wa Montevideo, womwe ndi likulu la Uruguay
KULI OFALITSA
11,711
MAPHUNZIRO A BAIBULO
9,001
OPEZEKA PA CHIKUMBUTSO (2017)
23,426
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.
Ngati mukufuna kupereka pitani pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.