Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA OCTOBER 1-7, 2018
3 Kodi Mukudziwa Nkhani Yonse?
MLUNGU WA OCTOBER 8-14, 2018
8 Tisamaweruze Poona Maonekedwe Akunja
Nkhani yoyamba ikufotokoza zinthu zimene zingatilepheretse kudziwa mfundo zonse zokhudza nkhani inayake. Ikufotokozanso mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize kuganizira bwino zimene timadziwa pa nkhani inayake kuti tizindikire zoona zake. Munkhani yachiwiri tikambirana zinthu zitatu zimene zimachititsa munthu kuti aweruze anthu potengera maonekedwe akunja. Ikufotokozanso zimene tingachite kuti tiziweruza anthu mopanda tsankho.
MLUNGU WA OCTOBER 15-21, 2018
18 Anthu Opatsa Amakhala Osangalala
MLUNGU WA OCTOBER 22-28, 2018
23 Tizigwira Ntchito ndi Yehova Tsiku Lililonse
Yehova analenga anthu n’cholinga choti akhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala. Ngati tsiku lililonse mumachita zinthu zimene zingathandize kuti zolinga za Yehova zikwaniritsidwe ndiye kuti mudzakhala osangalala. Nkhanizi zikufotokozanso ubwino wokhala anthu opatsa m’njira zosiyanasiyana.