Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA DECEMBER 31, 2018–JANUARY 6, 2019
3 “Gula Choonadi Ndipo Usachigulitse”
MLUNGU WA JANUARY 7-13, 2019
8 “Ndidzayenda M’choonadi Chanu”
Nkhani ziwirizi zitithandiza kuona kuti choonadi ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Choonadi ndi chamtengo wapatali kwambiri kuposa chinthu chilichonse chimene timalolera kusiya kuti tipeze choonadicho. Nkhanizi zitithandizanso kuti tisasiye kuona kuti choonadi ndi chamtengo wapatali komanso kuti tisayerekeze n’komwe kugulitsa mfundo ya choonadi iliyonse imene Yehova watiphunzitsa.
MLUNGU WA JANUARY 14-20, 2019
13 Muzikhulupirira Yehova Kuti Mukhale ndi Moyo
Buku la Habakuku lili ndi mfundo zotithandiza kuti tizikhulupirira Yehova pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto. Nkhaniyi itithandiza kudziwa kuti tikamakhulupirira Yehova pa nthawi imene tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana iye adzatipulumutsa.
MLUNGU WA JANUARY 21-27, 2019
18 Kodi Mumayendera Maganizo a Ndani?
MLUNGU WA JANUARY 28, 2019–FEBRUARY 3, 2019
23 Tiziyendera Maganizo a Yehova
Munthu akamakula mwauzimu amazindikira kuti maganizo a Yehova ndi apamwamba kwambiri. Nkhani ziwirizi zitithandiza kuti tisamayendere maganizo a anthu a m’dzikoli koma tiziyendera maganizo a Yehova.