Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb18.12 4
  • December 17-23

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • December 17-23
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18.12 4

December 17-23

MACHITIDWE 15-16

  • Nyimbo Na. 96 ndi Pemphero

  • Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • “Anasankha Zochita Pogwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu”: (10 min.)

    • Mac. 15:1, 2​—Nkhani yamdulidwe inkafuna kugawanitsa mpingo wachikhristu womwe unangoyamba kumene (bt 102-103 ¶8)

    • Mac. 15:13-20​—Bungwe lolamulira linasankha zochita pa nkhaniyi pogwiritsa ntchito Malemba (w12 1/15 5 ¶6-7)

    • Mac. 15:28, 29; 16:4, 5​—Zimene bungwe lolamulira linasankha pa nkhaniyi zinachititsa kuti mipingo ikhale yolimba (bt 123 ¶18)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Mac. 16:6-9​—Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yowonjezera utumiki wathu? (w12 1/15 10 ¶8)

    • Mac. 16:37​—Kodi mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito bwanji ufulu wake wokhala nzika ya Roma popititsa patsogolo uthenga wabwino? (“ndife Aroma” mfundo zimene ndikuphunzira pa Mac. 16:37, nwtsty)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Mac. 16:25-40

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

  • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Musonyezeni ndi kukambirana mfundo za m’vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (koma musaonetse vidiyoyi)

  • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 74

  • “Tizitamanda Yehova Mosangalala Poimba Nyimbo”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Ana Anatamanda Yehova Poimba Nyimbo. Pomaliza nkhaniyi, pemphani onse kuti aimirire n’kuimbira limodzi vidiyo ya Nyimbo 084 Timadzipereka.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 18

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)

  • Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani