June 24-30
AFILIPI 1-4
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Afilipi.]
Afil. 4:6—Mukakhala ndi nkhawa muzipemphera kwa Yehova (w17.08 10 ¶10)
Afil. 4:7—Muzilola kuti “mtendere wa Mulungu” uzikutetezani (w17.08 10 ¶7; 12 ¶16)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Afil. 2:17—Kodi mtumwi Paulo ‘anadzipereka ngati nsembe yachakumwa’ m’njira yotani? (it-2 528 ¶5)
Afil. 3:11—Kodi “kuuka koyambirira” kumatanthauza chiyani? (w07 1/1 26-27 ¶5)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Afil. 4:10-17 (5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (4)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) fg phunziro 6 ¶3-4 (8)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Zipangizo Zanu Zamakono Zimakulamulirani?: (5 min.) Onerani vidiyoyi. Kenako kambiranani mafunso awa: Kodi zipangizo zamakono ndi zothandiza bwanji? Kodi tingakumane ndi mavuto otani ngati nthawi zonse timangokhalira kugwiritsa ntchito zipangizozi? Nanga mungadziwe bwanji ngati muli ndi vutoli? N’chiyani chingakuthandizeni kuti nthawi zonse muzichita “zinthu zofunika kwambiri”? (Afil. 1:10)
“Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?”: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kodi Ndiyenera Kusankha Zosangalatsa Zotani?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs 6:16-23 ndi mfundo zakumapeto
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero