CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AHEBERI 12-13
Chilango Chimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda
M’Baibulo mawu akuti chilango angatanthauze kudzudzula, kulangiza komanso kuphunzitsa. Monga mmene bambo wachikondi amachitira, nayenso Yehova amatipatsa chilango. Amatilangiza kapena kutipatsa chilangochi:
Tikamawerenga Baibulo, kuphunzira patokha, tikakhala pamisonkhano komanso tikamasinkhasinkha
Tikamalandira uphungu kapena malangizo kuchokera kwa Akhristu anzathu
Polola kuti tikumane ndi zotsatirapo za zimene talakwitsa
Tikadzudzulidwa kapena kuchotsedwa mumpingo
Polola kuti tikumane ndi mayesero kapena chizunzo.—w15 9/15 21 ¶13; it-1 629