February 10-16
GENESIS 15-17
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“N’chifukwa Chiyani Yehova Anasintha Dzina la Abulamu ndi Sarai?”: (10 min.)
Gen. 17:1—Ngakhale kuti Abulamu anali wopanda ungwiro, ankayesetsa kuchita zabwino (it-1 817)
Gen. 17:3-5—Dzina la Abulamu linasinthidwa kukhala Abulahamu (it-1 31 ¶1)
Gen. 17:15, 16—Dzina la Sarai linasinthidwa kukhala Sara (w09 2/1 13)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 15:13, 14—Kodi zaka 400 zomwe mbadwa za Abulahamu zinasautsidwa zinayamba liti, nanga zinatha liti? (it-1 460-461)
Gen. 15:16—Kodi “m’badwo wachinayi” wa Abulahamu unabwerera bwanji ku Kanani? (it-1 778 ¶4)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 15:1-21 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi wofalitsayu anagwiritsa ntchito bwanji mafunso? Nanga anagwiritsira ntchito bwanji chitsanzo pophunzitsa?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako mugawireni kabuku ka Uthenga Wabwino, ndipo sonyezani mmene mungayambitsire phunziro pokambirana naye phunziro 3. (th phunziro 6)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Zimene Mungachite Kuti Mulimbitse Chikondi M’banja Lanu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 16 ndime 17-22
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 125 ndi Pemphero