MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki-Kulalikira Pogwiritsa Ntchito Foni
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Kulalikira pogwiritsa ntchito foni ndi njira yofunika pochitira “umboni mokwanira za uthenga wabwino.” (Mac 20:24)a Imatithandiza kulalikira kwa munthu pamene zingakhale zovuta kumulalikira pamasom’pamaso.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Tizikonzekera. Tizisankha nkhani yoyenera. Kenako tizilemba autilaini ya zimene tikufuna kunena. Mwina mungalembenso kauthenga kakafupi kamene munganene ngati munthu sanayankhe foni koma foniyo ikulola kuti musiye uthenga. Zimathandiza kukhala patebulo muli ndi autilaini ndi zinthu zina zofunika pafupi monga chipangizo chomwe mwatsegula JW Library® kapena jw.org®
Tizikhala omasuka. Tizilankhula mwachibadwa, kumwetulira ndiponso kugwiritsa ntchito manja ngati kuti tikulankhula ndi munthu pamasom’pamaso. Tizipewanso kuimaima polankhula. Komanso zimathandiza kuchita utumikiwu ndi anthu ena. Mwininyumba akafunsa mafunso, tizibwereza mokweza mafunsowo kuti mnzathu azitithandiza kupeza mayankho
Tizisiya funso loti tidzayankhe pa ulendo wobwereza. Munthu akasonyeza chidwi tingamusiyire funso loti tidzayankhe tikadzaimbanso. Tinganenenso kuti tikhoza kukamusiyira buku kapena magazini, kutumiza pa imelo kapena m’njira ina. Apo ayi, tinganene kuti tikhoza kumutumizira vidiyo kapena nkhani inayake pa foni kapena pogwiritsa ntchito chipangizo china. Ngati n’zotheka, tingamuuze zinthu zina zimene angapeze pawebusaiti yathu.
a Ngati n’zololeka kulalikira pogwiritsa ntchito foni m’dera lanu, muzitsatira malamulo okhudza kusunga chinsinsi cha anthu ena.