Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • wp23.1 3
  • Mulungu Amasamala za Inu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mulungu Amasamala za Inu
  • sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Mulungu Akulonjeza Kuti Kuvutika Maganizo Kudzatheratu
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • Matenda Ovutika Maganizo Ndi Vuto la Padziko Lonse
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
  • 2 | ‘Malemba Angakulimbikitseni’
    sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
Onani Zambiri
sanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2023
wp23.1 3
Mnyamata wakhala pansi pafupi ndi bedi lake, akuwerenga Baibulo.

Mulungu Amasamala za Inu

M’BAIBULO muli malangizo abwino kwambiri amene angakuthandizeni chifukwa ndi buku lochokera kwa Mulungu. Ngakhale zili choncho, si buku la zachipatala. Komabe lingakuthandizeni kuthana ndi mavuto osiyanasiyana pa moyo wanu monga kuvutika ndi nkhawa, kumva kupweteka m’thupi komanso ngati mukudwala matenda ovutika maganizo.

Chofunika kwambiri n’chakuti Baibulo limatitsimikizira kuti mlengi wathu Yehova Mulungu,a amadziwa bwino mmene timaganizira komanso mmene timamvera kuposa wina aliyense. Iye ndi wofunitsitsa kutithandiza kuthana ndi mavuto aliwonse amene tikukumana nawo. Mwachitsanzo, taonani malemba awiri a m’Baibulo otsatirawa amene angakulimbikitseni:

“Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.”​—SALIMO 34:18.

“Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’”—YESAYA 41:13.

Koma kodi Yehova amatithandiza bwanji kuthana ndi mavuto obwera chifukwa cha matenda ovutika maganizo? Monga mmene muonere munkhani zotsatirazi, muona zimene Yehova amachita posonyeza kuti amasamaladi za ife komanso mmene amatithandizira m’njira zosiyanasiyana.

a Yehova ndi dzina la Mulungu.​—Salimo 83:18.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani