Magazini Yophunzira
NOVEMBER 2023
NKHANI ZOPHUNZIRA KUYAMBIRA: JANUARY 8–FEBRUARY 4, 2024
© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka pitani pa donate.jw.org.
Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika lolembedwa m’Chichewa chamakono, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina.
CHITHUNZI CHAPACHIKUTO:
Ezara ali kukachisi ndipo akulira komanso kupemphera chifukwa cha machimo a anthu. Gulu nalonso likulira. Kenako Sekaniya akulimbikitsa Ezara pomuuza kuti: “Aisiraeli ali ndi chiyembekezo . . . ndipo ife tili nawe.”—Ezara 10:2, 4 (Onani nkhani yophunzira 48, ndime 17)