Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • w24.02 104
  • Kodi Mukudziwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukudziwa?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mukusamalira ‘Chishango Chanu Chachikulu Chachikhulupiriro’?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Muziona Kuti Moyo Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kulankhula Zomveka
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24.02 104
Ezara watenga mpukutu ndipo waima patsogolo pa anthu n’kumatamanda Yehova.

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani mawu ena m’Baibulo amanenedwa mobwerezabwereza?

NTHAWI zina olemba Baibulo ankabwereza ndendende mawu omweomwewo. Tiyeni tione mfundo zitatu zomwe ziyenera kuti zinkawachititsa kuchita zimenezi.

Nthawi yomwe zinthuzo zinalembedwa. M’nthawi ya Aisiraeli, anthu ambiri analibe mabuku awoawo a Chilamulo. Ankangomvetsera Chilamulo chikamawerengedwa akasonkhana kuchihema. (Deut. 31:10-12) N’zoonekeratu kuti pankakhala zosokoneza akamamvetsera ataimirira kwa maola angapo pagulu lalikulu. (Neh. 8:2, 3, 7) Pa nthawi ngati zimenezi, kubwereza mawu kunali kofunika kwambiri chifukwa kukanathandiza anthuwo kuti azikumbukira mosavuta malemba n’kumawagwiritsa ntchito. Komanso kubwerezako kukanawathandiza kuti azikumbukira mfundo zonse zokhudza malamulo omwe Mulungu anawapatsa.​—Lev. 18:4-22; Deut. 5:1.

Mmene zinalembedwera. Mabuku ena m’Baibulo analembedwa ngati nyimbo, mwachitsanzo buku la Masalimo, Nyimbo ya Solomo komanso la Maliro. Nthawi zina mawu a nyimbo ankabwerezedwa pofuna kutsindika mutu wa nyimboyo komanso kuthandiza omvetsera kuti aloweze mawu ake. Chitsanzo ndi mawu opezeka pa Salimo 115:9-11, pomwe amati: “Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu nyumba ya Aroni, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu. Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova, iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.” Kodi mwaona mmene kubwereza mawuwa kukanathandizira oimbawo, kuti mfundo zamtengo wapatali zachoonadizi zikhazikike m’mitima mwawo?

Kuti atsindike mfundo zofunika. Nthawi zina olemba Baibulo ankabwereza mawu ofunika. Mwachitsanzo, Yehova atalamula Aisiraeli kuti asamadye magazi, anauza Mose kuti abwereze chifukwa chake kwa maulendo angapo. Mulungu ankafuna kutsindika kuti moyo wa chamoyo chilichonse uli m’magazi, kapena kuti magazi amaimira moyo. (Lev. 17:11, 14) Pambuyo pake, pamene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu ankatchula zinthu zoyenera kupewa kuti munthu asangalatse Mulungu, anabwerezanso kufunika kopewa magazi.​—Mac. 15:20, 29.

Sikuti Yehova amafuna kuti tikhale ndi chizolowezi chomangobwerezabwereza mawu a m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Ukamapemphera, usamanene mawu omweomwewo mobwerezabwereza.” (Mat. 6:7) Kenako anatchula zinthu zomwe tiyenera kupempherera, zomwe ndi zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Mat. 6:9-13) Koma ngakhale kuti sitiyenera kubwerezabwereza mawu m’mapemphero athu, n’zololeka kupempherera nkhani ina yake mobwerezabwereza.​—Mat. 7:7-11.

Pa chifukwa chabwino, Mulungu analola kuti mawu kapena ziganizo zinazake m’Baibulo zibwerezedwe. Imeneyi ndi njira imodzi imene Mlangizi wathu wamkulu amatiphunzitsira kuti zinthu zizitiyendera bwino.​—Yes. 48:17, 18.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani