Mawu Oyamba
Anthu amakhala ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mmene chilengedwe komanso moyo unayambira padzikoli. Magazini ya Galamukani! ino ikuthandizani kufufuza maumboni amene alipo pankhaniyi ndipo kenako muona kuti zolondola ndi ziti. Kodi chilengedwechi chinangokhalapo chokha kapena chinachita kulengedwa ndi Mlengi? Kudziwa yankho la funsoli kungakuthandizeni kwambiri.