Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • ll section 3
  • Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?
    Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Adamu ndi Hava Sanamvere Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Mulungu Analenga Anthu Awiri Oyamba
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Anataya Mwayi Wokhala M’Paradaiso
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll section 3

CHIGAWO 3

Kodi Moyo Unali Wotani M’Paradaiso?

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zambiri zabwino. Genesis 1:28

Yehova anapanga Hava n’kumupereka kwa Adamu

Yehova anapanga mkazi woyamba, Hava, ndipo anam’pereka kwa Adamu kuti akhale mkazi wake.​—Genesis 2:21, 22.

Yehova anawalenga ndi thupi ndiponso maganizo angwiro.

Adamu ndi Hava akuyang’ana Paradaiso

Iwo ankakhala m’Paradaiso m’munda wa Edeni umene unali wokongola kwambiri. M’mundawu munali mtsinje, mitengo ya zipatso ndi nyama.

Yehova ankalankhula nawo ndiponso ankawaphunzitsa. Iwo akanamvera Mulungu, akanakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.

Mulungu anawauza kuti asadye zipatso za mtengo umodzi m’mundamo. Genesis 2:16, 17

Mtengo wa chipatso chimene Yehova analetsa Adamu ndi Hava

Yehova anasonyeza Adamu ndi Hava mtengo umodzi wa zipatso m’mundamo ndipo anawauza kuti akadzadya zipatso za mtengo umenewo, adzafa.

Mngelo woipa dzina lake Satana Mdyerekezi anagwiritsa ntchito njoka polankhula ndi Hava

Mngelo mmodzi anagalukira Mulungu. Mngelo woipa ameneyu ndi Satana Mdyerekezi.

Satana sanafune kuti Adamu ndi Hava amvere Yehova. Choncho, kudzera mwa njoka anauza Hava kuti iwo akadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anawauza kuti asadye, sadzafa, koma adzafanana ndi Mulungu. Limenelitu linali bodza lenileni.​—Genesis 3:1-5.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani