MUTU 4
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama
“Zolinga zimakhazikika anthu akakambirana.”—Miyambo 20:18
Tonsefe timafuna ndalama zogulira zinthu zofunika m’banja lathu. (Miyambo 30:8) Paja “ndalama zimatetezera.” (Mlaliki 7:12) Mabanja ambiri amavutika kuti akambirane nkhani za ndalama. Koma musalole kuti ndalama zisokoneze banja lanu. (Aefeso 4:32) Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhulupirirana ndiponso kukambirana mmene angagwiritsire ntchito ndalama zawo.
1 MUZIKHALA NDI BAJETI
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi ndi kuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo?” (Luka 14:28) N’zofunika kwambiri kuti muzigwirizana mmene mudzagwiritsira ntchito ndalama zanu. (Amosi 3:3) Muyenera kusankha zinthu zofunika kugula komanso kuchuluka kwa ndalama zimene mungawononge. (Miyambo 31:16) Komanso ngati muli ndi ndalama zokwanira kuti mugule chinachake sikuti muyenera kuchigula basi. Yesetsani kupewa ngongole. Muzingogwiritsa ntchito ndalama zimene muli nazo.—Miyambo 21:5; 22:7.
ZIMENE MUNGACHITE:
Mukatsala ndi ndalama pa mapeto pa mwezi, muzikambirana zimene mungachite nazo
Ngati ndalama zanu zimakhala zoperewera, kambiranani zimene mungachite kuti musamawononge zambiri. Mwachitsanzo, m’malo mophika chakudya chambiri n’kutaya chotsala, muzingophika chokwanira bwinobwino banja lanulo
2 MUZIKAMBIRANA MOMASUKA
ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Timasamalira zinthu zonse moona mtima, osati pamaso pa Yehova pokha ayi, komanso pamaso pa anthu.” (2 Akorinto 8:21) Muziuza mwamuna kapena mkazi wanu ndalama zonse zimene mumalandira komanso mmene mumazigwiritsira ntchito.
Muzikambirana kaye musanagwiritse ntchito ndalama zambiri. (Miyambo 13:10) Kukambirana bwinobwino nkhani za ndalama kungathandize kuti muzikhala mwamtendere. Muzionanso kuti ndalama zimene mumapeza ndi za banja lonse osati zanokha.—1 Timoteyo 5:8.
ZIMENE MUNGACHITE:
Muzikambirana n’kuona kuchuluka kwa ndalama zimene aliyense angagwiritse ntchito popanda kuuza mnzake
Musamadikire kuti pakhale vuto kaye kuti mukambirane za ndalama