Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • hf section 7
  • Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 ATHANDIZENI KUTI AZIMASUKA NANU
  • 2 MUZIYESETSA KUMVETSA MAGANIZO AWO
  • 3 MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA
  • 4 MUZIGWIRIZANA MMENE MUNGAWAPHUNZITSIRE
  • Mungatani Kuti Banja Lanu Likhale Losangalala?​—Mbali Yachiwiri
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Makolo, Muzithandiza Ana Anu Kuti Azikonda Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf section 7
Bambo ndi mwana wake akukonza njinga limodzi

MUTU 7

Zimene Mungachite Pophunzitsa Mwana Wanu

“Mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako, ndi kuwakhomereza mwa ana ako.”—Deuteronomo 6:6, 7

Yehova amafuna kuti makolo azitsogolera ana awo. (Akolose 3:20) Choncho makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo kuti azikonda Yehova komanso kuti adzakhale anthu odalirika. (2 Timoteyo 1:5; 3:15) Makolo ayeneranso kudziwa zimene zili mumtima mwa ana awo. Musaiwale kuti ana amatsatira zimene mumachita. Choncho Mawu a Yehova ayenera kukhala mumtima mwanu choyamba kuti muphunzitse bwino ana anu.—Salimo 40:8.

1 ATHANDIZENI KUTI AZIMASUKA NANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Muzithandiza ana anu kuti azimasuka kulankhula nanu. Ana ayenera kudziwa kuti mukhoza kuwamvetsera nthawi iliyonse imene akufuna kukuuzani zinazake. Mukamakhala mwamtendere m’banja mwanu, ana amamasuka kufotokoza maganizo awo. (Yakobo 3:18) Koma sangamasuke akaona kuti mukhoza kukwiya kapena kuwadzudzula akakuuzani zinazake. Muyenera kuwalezera mtima ndipo muziwatsimikizira kuti mumawakonda.—Mateyu 3:17; 1 Akorinto 8:1.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzimvetsera ana anu akafuna kulankhula nanu

  • Muzilankhulana ndi ana anu nthawi zonse osati pakakhala vuto basi

2 MUZIYESETSA KUMVETSA MAGANIZO AWO

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Munthu wosonyeza kuzindikira pa zinthu adzapeza zabwino.” (Miyambo 16:20) Nthawi zina mwana akalankhula musamaganizire zimene wanena koma zimene akutanthauza komanso mmene akumvera mumtima mwake. Achinyamata amakonda kukokomeza zinthu kapena kulankhula zina koma akutanthauza zina. Paja Baibulo limati: “Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa.” (Miyambo 18:13) Choncho musamafulumire kukwiya.—Miyambo 19:11.

Mayi akukalipira mwana wake chifukwa cha zimene mwanayo wangowauza

ZIMENE MUNGACHITE:

  • aya mwana wanu alankhule zotani, yesetsani kuti musamudule mawu kapena kumupsera mtima

  • Muzikumbukira mmene munkamvera muli msinkhu wakewo komanso zimene munkaona kuti n’zofunika

3 MUZICHITA ZINTHU MOGWIRIZANA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.” (Miyambo 1:8) Yehova wapereka udindo wolera ana kwa bambo komanso mayi. Muyenera kuphunzitsa ana anu kuti azikulemekezani ndiponso kukumverani. (Aefeso 6:1-3) Ana amadziwa ngati makolo awo ‘sagwirizana.’ (1 Akorinto 1:10) Ngati simunagwirizane pa nkhani inayake, muziyesetsa kuti ana anu asaone zimenezi chifukwa angasiye kukulemekezani.

Bambo watengera pambali mwana wake kuti amulangize pomwe ana ena ali m’chipinda china

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muyenera kugwirizana zimene muzichita polangiza ana anu

  • Ngati mukusiyana maganizo pa nkhaniyi, yesetsani kumvetsa zimene mnzanuyo akufuna

4 MUZIGWIRIZANA MMENE MUNGAWAPHUNZITSIRE

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera.” (Miyambo 22:6) Sikuti kuphunzitsa bwino ana anu kumangochitika kokha. Koma muyenera kugwirizana zimene muzichita powaphunzitsa ndiponso kuwalangiza. (Salimo 127:4; Miyambo 29:17) Muyenera kuthandiza ana kumvetsa ubwino wa malamulo anu komanso zifukwa zimene mumawalangira. (Miyambo 28:7) Muziwaphunzitsanso kukonda Mawu a Yehova ndiponso kumvetsa mfundo zake. (Salimo 1:2) Zimenezi zingawathandize kukhala ndi chikumbumtima chabwino.—Aheberi 5:14.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muziyesetsa kuthandiza ana anu kuti adziwe bwino Mulungu n’kumamudalira

  • Muziwathandiza kuzindikira ndiponso kupewa zinthu zoipa zimene zimapezeka pa Intaneti. Muziwaphunzitsanso mmene angapewere ogwirira ana

Makolo akuphunzitsa mwana wawo kuyambira ali wamng’ono mpaka kubatizidwa

“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera”

YEHOVA ADZAKUDALITSANI MUKAMACHITA KHAMA

Makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana kaganizidwe ka Yehova. (Aefeso 6:4) Koma Yehova amadziwa kuti zimenezi si zapafupi. Ngakhale zili choncho, dziwani kuti zotsatira zake zidzakhala zosangalatsa ndipo zingalemekeze Mulungu.—Miyambo 23:24.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndingathandize bwanji mwana wanga kuti azimasuka kundiuza chilichonse?

  • Kodi ndingaphunzire chiyani pa zimene makolo ena amachita polera ana awo?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani