Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • hf section 8
  • Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi
  • Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1 MUZIDALIRA YEHOVA
  • 2 MUZIDZISAMALIRA KOMANSO KUSAMALIRA BANJA LANU
  • 3 LOLANI KUTI ENA AKUTHANDIZENI
  • Yehova Amayang’anira Anthu Ake
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kodi Baibulo Lingandithandize Ngati Ndili ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Yehova Amatithandiza Tikamakumana ndi Mayesero
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
hf section 8
Mwamuna ndi mkazi wake akulilira mwana wawo yemwe wamwalira

MUTU 8

Mukakumana ndi Mavuto Amwadzidzidzi

“Mukusangalala kwambiri ngakhale kuti padakali pano n’koyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana amene akukuchititsani chisoni.”—1 Petulo 1:6

Ngakhale mutayesetsa kwambiri kuti mukhale ndi banja losangalala, mukhoza kukumana ndi mavuto amwadzidzidzi. (Mlaliki 9:11) Koma Yehova amatikonda ndipo amatithandiza tikakumana ndi mavuto. Kutsatira mfundo zimene zili m’mutu umenewu kungathandize inuyo ndi banja lanu kuti mupirire mavuto ngakhale atakhala aakulu kwambiri.

1 MUZIDALIRA YEHOVA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ‘Muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Nthawi zonse muzikumbukira kuti Mulungu si amene amayambitsa mavuto anu. (Yakobo 1:13) Mukamayesetsa kukhala naye pa ubwenzi wabwino, adzakuthandizani kwambiri. (Yesaya 41:10) “Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”—Salimo 62:8.

Kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo tsiku lililonse kungakulimbikitseninso. Mukatero mudzaona umboni wakuti Yehova “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akorinto 1:3, 4; Aroma 15:4) Iye amalonjeza kuti adzakupatsani “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.”—Afilipi 4:6, 7, 13.

Bambo ali m’chipatala ndipo akupemphera limodzi ndi banja lake

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuupeza mtima komanso kuganiza bwinobwino

  • Ganizirani njira zonse zimene mungatsatire ndiyeno n’kusankhapo imene ingakuthandizeni

2 MUZIDZISAMALIRA KOMANSO KUSAMALIRA BANJA LANU

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mtima wa munthu womvetsa zinthu umadziwa zinthu, ndipo khutu la anzeru limafunafuna kudziwa zinthu.” (Miyambo 18:15) Muzikambirana ndi aliyense m’banjamo ndiponso kumvetsera bwino akamalankhula kuti mudziwe zimene angafunike.—Miyambo 20:5.

Kodi mungatani ngati wina m’banjamo kapena wachibale wamwalira? Musamachite manyazi kulira. Kumbukirani kuti ngakhale Yesu “anagwetsa misozi.” (Yohane 11:35; Mlaliki 3:4) Muyeneranso kupuma ndiponso kugona mokwanira. (Mlaliki 4:6) Zimenezi zingakuthandizeni kwambiri kuti mupirire.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikambirana nthawi ndi nthawi ndi banja lanu. Mukatero, simudzavutika kukambirana momasuka mukakumana ndi mavuto amwadzidzidzi.

  • Muzilankhula ndi anthu ena amene akumana ndi vuto lofanana ndi lanu

3 LOLANI KUTI ENA AKUTHANDIZENI

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Anzanu angafune kukuthandizani koma mwina sangadziwe zoti achite. Musachite manyazi kuwauza zimene mukufuna. (Miyambo 12:25) Muyeneranso kupempha anthu amene amadziwa bwino Baibulo kuti akupatseni malangizo chifukwa malangizowo angakuthandizeni kwambiri.—Yakobo 5:14.

Mukamakonda kucheza ndi anthu amene amakhulupirira Mulungu komanso malonjezo ake iwo adzakulimbikitsani kwambiri. Mudzalimbikitsidwanso mukamathandiza anthu ena amene akuvutikanso. Muziwauza zimene zimakuchititsani kukhulupirira Yehova ndiponso malonjezo ake. Muzilimbikira kuthandiza anthu ena komanso musasiye kucheza ndi anthu amene amakukondani.—Miyambo 18:1; 1 Akorinto 15:58.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzikambirana ndi mnzanu amene mumamudalira n’kulola kuti akuthandizeni

  • Musamubisire zimene mukufuna

MUZIGANIZIRA KWAMBIRI ZA YEHOVA

Ngakhale vutolo litakusowetsani mtendere kwambiri muziyesetsa kuganizira za Mulungu. Yobu atapanikizika ndi mavuto ananena kuti: “Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.” (Yobu 1:21, 22) Tsanzirani Yobu n’kumaona kuti nkhani zokhudza dzina la Yehova komanso cholinga chake n’zofunika kwambiri kuposa mavuto anu. Zinthu zikachitika m’njira imene simunkayembekezera, musataye mtima. Muzikhulupirira Mulungu ndi mtima wanu wonse. Paja iye anati: “Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.”—Yeremiya 29:11.

DZIFUNSENI KUTI . . .

  • Kodi ndimakhulupirira kwambiri Yehova ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono?

  • Kodi Yehova wandipatsa zinthu zabwino ziti zimene ndingamuthokozere tsiku lililonse?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani