Mawu Oyamba Gawo 2
N’chifukwa chiyani Yehova anabweretsa chigumula chimene chinawononga zamoyo zonse? Kale kwambiri anthu asanachuluke padzikoli, Satana anachititsa kuti anthu asamamvere Yehova. Anthu ena monga Adamu, Hava ndi mwana wawo Kaini anasankha kuchita zofuna za Satana. Koma panalinso anthu ena ochepa monga Abele ndi Nowa omwe anasankha kuchita zimene Yehova amafuna. Pofika nthawi ya Nowa anthu ambiri ankachita zoipa, n’chifukwa chake Yehova anawononga dziko loipalo. Chigawochi chitithandiza kudziwa kuti Yehova amaona ngati tasankha kukhala kumbali yake kapena kukhala kumbali ya Satana, ndipo sadzalola kuti Satana alepheretse zolinga zake.