Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lfb sect. 9
  • Mawu Oyamba Gawo 9

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Oyamba Gawo 9
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yehoyada Anali Wolimba Mtima
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuopa Yehova?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Achinyamata, Kodi Mudzachita Chiyani pa Moyo Wanu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb sect. 9
Kamtsikana ka ku Isiraeli kakulankhula ndi mkazi wa Namani wakhate

Mawu Oyamba Gawo 9

Chigawochi chikufotokoza za achinyamata, aneneri komanso mafumu amene anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Ku Siriya kunali kamtsikana kena ka ku Isiraeli komwe kankakhulupirira kuti mneneri wa Yehova angathe kuchiritsa Namani. Mneneri Elisa ankakhulupirira kuti Yehova angamupulumutse kwa adani ake. Mkulu wa Ansembe dzina lake Yehoyada anaika moyo wake pangozi kuti apulumutse Yehoasi amene agogo ake a Ataliya ankafuna kumupha. Mfumu Hezekiya inkakhulupirira kuti Yehova apulumutsa Yerusalemu ndipo sanagonjere zimene Asuri ankafuna. Mfumu Yosiya inachotsa mafano, kumanganso kachisi n’kuthandiza anthu kuti ayambirenso kulambira koona.

ZIMENE TIPHUNZIRE M’CHIGAWOCHI

  • Musamadzione kuti ndinu aang’ono moti simungauze ena za Yehova

  • Yehova analonjeza kuti adzakhala nafe tikamachita zinthu zabwino

  • Mofanana ndi Yona, tiphunzire kutsatira malangizo a Yehova ndipo tisamadandaule zinthu zikakhala kuti sizinayende mmene timafunira

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani