NYIMBO 2
Dzina Lanu Ndinu Yehova
zosindikizidwa
1. Mulungu woona—
Mlengi wa zinthu zonse
Mulungu wamuyaya—
Ndinudi Yehova.
Ndifetu amwayi
Kukhala anthu anu.
Tilengeza za inu,
Ku mitundu yonse.
(KOLASI)
Yehova, Yehova,
M’lungu ndinu nokha.
Kumwambako ndi padziko
Palibenso wina.
Ndinudi Wamphamvuyonse
Onsetu adziwe.
Yehova, Yehova,
M’lungu wathu ndinu nokha.
2. Tingathe kukhala
Chilichonse mwafuna.
Tigwire ntchito yanu—
Ndinudi Yehova.
Mwatipatsa dzina
Tikhale Mboni zanu.
Uwu ndi mwayi wathu—
Tikutamandani.
(KOLASI)
Yehova, Yehova,
M’lungu ndinu nokha.
Kumwambako ndi padziko
Palibenso wina.
Ndinudi Wamphamvuyonse
Onsetu adziwe.
Yehova, Yehova,
M’lungu wathu ndinu nokha.
(Onaninso 2 Mbiri 6:14; Sal. 72:19; Yes. 42:8.)