NYIMBO 29
Tizichita Zinthu Zogwirizana ndi Dzina Lathu
zosindikizidwa
1. Yehova, wamphamvuyonse wam’yaya,
Wamphamvu, chilungamo, n’chikondi.
Mwini choonadi komanso nzeru,
Mukulamulira monga Mfumu.
Timasangalala potumikira,
Ndi kulengeza Ufumu wanu.
(KOLASI)
Ndi mwayidi kukhala Mboni zanu.
Tichite monga mwa dzina lathu.
2. Tikamatumikira ndi abale
Timakhaladi ogwirizana.
Pophunzitsa anthu cho’nadi chanu,
Timakhalanso osangalala.
Timadziwikanso ndi dzina lanu,
Ndi mwayi wathu kulitchukitsa.
(KOLASI)
Ndi mwayidi kukhala Mboni zanu.
Tichite monga mwa dzina lathu.
(Onaninso Deut. 32:4; Sal. 43:3; Dan. 2:20, 21.)