NYIMBO 34
Kuchita Zinthu Mokhulupirika
zosindikizidwa
1. Mulungu wanga mundiweruze,
Muone ngati ndimakudalirani.
Ndifufuzeni ndi kundiyesa.
Konzani mtima wanga, mundidalitse.
(KOLASI)
Koma ine ndatsimikizadi
Kumachita zinthu mokhulupirika.
2. Sindicheza ndi anthu oipa.
Ndimadana ndi onyoza choonadi.
Chonde musachotse moyo wanga
Limodzi ndi anthu okonda zoipa.
(KOLASI)
Koma ine ndatsimikizadi
Kumachita zinthu mokhulupirika.
3. Ndimakonda nyumba yanu M’lungu.
Ndimasangalala kukulambirani.
Ndidzayendadi kuguwa lanu
Pokutamandani mokweza kwambiri.
(KOLASI)
Koma ine ndatsimikizadi
Kumachita zinthu mokhulupirika.
(Onaninso Sal. 25:2.)