NYIMBO 35
“Muzitsimikizira Kuti Zinthu Zofunika Kwambiri Ndi Ziti”
zosindikizidwa
1. Kuzindikira kudzatithandiza,
Kudziwa zoona,
Kudziwa zomwe ndi zofunika,
Kuti tizizichita.
(KOLASI)
Uzidana ndi choipa.
Sangalatsa;
Mtima wa Mulungu,
Madalitso tidzapeza,
Tikamachita zofunika.
2. Palibe chofunika kuposa
Kulengeza uthenga,
Kufufuza a njala ya choonadi
N’kuwaphunzitsa.
(KOLASI)
Uzidana ndi choipa.
Sangalatsa;
Mtima wa Mulungu,
Madalitso tidzapeza,
Tikamachita zofunika.
3. Tikamachita zofunika,
Tidzakhala okhutira.
Mtendere wa Mulungu
Udzatetezatu maganizo.
(KOLASI)
Uzidana ndi choipa.
Sangalatsa;
Mtima wa Mulungu,
Madalitso tidzapeza,
Tikamachita zofunika.
(Onaninso Sal. 97:10; Yoh. 21:15-17; Afil. 4:7.)