NYIMBO 53
Kukonzekera Kupita Kolalikira
zosindikizidwa
1. Tsopano
Kunja kwacha,
Tikalalikiretu.
Komano mvula,
Yayambanso kugwa.
N’zosavuta kupitiriza
Kugona.
(KOLASI)
Tisafo’ke tikonzekere,
Tipemphe Yehova,
Iye angatilimbikitse
N’zofunika.
Tipezenso woyenda naye
Wotilimbikitsa.
Angelo amatithandiza
Osafo’ka.
2. Chimwemwe
Tidzapeza,
Ngati sitingafo’ke.
Ndipo Yehova
Amaona zonse
Sangaiwalenso chikondi
chathuchi.
(KOLASI)
Tisafo’ke tikonzekere,
Tipemphe Yehova,
Iye angatilimbikitse
N’zofunika.
Tipezenso woyenda naye
Wotilimbikitsa.
Angelo amatithandiza
Osafo’ka.
(Onaninso Mlal. 11:4; Mat. 10:5, 7; Luka 10:1; Tito 2:14.)