NYIMBO 111
Tili Ndi Zifukwa Zambiri Zokhalira Osangalala
1. Tili ndi zifukwa zambiri,
Zakuti tisangalale.
Anthu a mumitundu yonse
Akusangalala nafe.
Chisangalalo n’chachikulu,
Mawu a M’lungu tidziwa.
Timawaphunzira mwakhama;
Amatilimbikitsadi.
Zotisangalatsa n’zambiri,
Mumtimamu zikuyaka.
Tikakumana ndi mavuto,
Yehova amathandiza.
(KOLASI)
Amatisangalatsadi,
Yehova Mulungu wathu.
Ndi wabwinodi ndi ntchito zake,
N’zazikulu ndi zamphamvu.
2. Timasangalala kuona,
Kumwamba, nyanja ndi dziko.
Yehova analenga zonse,
Ife timayamikira.
Timachitiratu umboni,
Ndi kulengeza Ufumu.
Madalitso a Ufumuwo,
Tilengeza kulikonse.
Kusangalala kwamuyaya,
Kwayandikira tsopano.
Zimene anatilonjeza
Tidzasangalala nazo.
(KOLASI)
Amatisangalatsadi,
Yehova Mulungu wathu.
Ndi wabwinodi ndi ntchito zake,
N’zazikulu ndi zamphamvu.
(Onaninso Deut. 16:15; Yes. 12:6; Yoh. 15:11.)