NYIMBO 113
Yehova Amatipatsa Mtendere
zosindikizidwa
1. Tamandani Yehova,
Wamtendereyo.
Nkhondo adzazithetsa,
Mwa Mwana wake.
Adzapambana nkhondo,
Yachilungamo.
Mtendere udzabwera,
Padziko lonse.
2. Tasiya kulankhula
Zokhumudwitsa.
Malupanga, mikondo,
Zonse tataya.
Tisungabe mtendere
Tikhululuke.
Monga nkhosa za Yesu,
Zamtenderedi.
3. Mtendere ndi umboni
wa madalitso.
Tasunga malamulo
a M’lungu wathu.
Timakonda mtendere,
Tiusonyeza
Mpaka M’paradaiso
Wamtendereyo.
(Onaninso Sal. 46:9; Yes. 2:4; Yak. 3:17, 18.)