NYIMBO 117
Khalidwe la Ubwino
zosindikizidwa
1. Yehova M’lungu wabwino
Mumatidalitsadi.
Ndinu wokhulupirika,
Mumachita zabwino.
Mumasonyeza chifundo
Kwa anthu ochimwafe.
Tilambire inu nokha.
Tikutumikireni.
2. Taona ubwino wanu
Mwa atumiki anu.
Khalidwe lawo labwino
Limatilimbikitsa.
Mwatipatsa Mawu anu
Ndi abusa abwino.
Mutipatse mzimu wanu
Tizichita zabwino.
3. Chonde muzitidalitsa
Tikachita zabwino.
Tikhale okoma mtima
Kwa munthu aliyense.
M’mabanja ndi mumipingo
Ndiponso kulikonse,
Muzitithandiza kuti
Tizichita zabwino.
(Onaninso Sal. 103:10; Maliko 10:18; Agal. 5:22; Aef. 5:9.)