NYIMBO 119
Tiyenera Kukhala Ndi Chikhulupiriro
zosindikizidwa
1. Kale Mulungu ankalankhula
Kudzera mwa aneneri.
Lero kudzera mwa Mwana wake,
Akuti, ‘lapanitu.’
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni,
M’pamene tingadzapulumuke.
2. Mosangalala timvera Yesu,
Tilalikira Ufumu.
Tilengezabe molimba mtima;
Anthu amve uthenga.
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni,
M’pamene tingadzapulumuke.
3. Talimbatu m’chikhulupiriro;
Sitidzabwerera m’mbuyo.
Tidziwa Yehova M’lungu wathu
Adzatipulumutsa.
(KOLASI)
Kodi chikhulupiriro
Chathu ndi cholimba ndithu?
Chikakhala chenicheni,
M’pamene tingadzapulumuke.
(Onaninso Aroma 10:10; Aef. 3:12; Aheb. 11:6; 1 Yoh. 5:4.)