NYIMBO 124
Tizikhulupirika Nthawi Zonse
zosindikizidwa
1. Tikhulupirike zedi,
Kwa M’lungu ndi kum’konda.
Malamulo ake onse,
Tifuna kuwadziwa.
Timapindula kwambiri,
Tikamamvera iye.
Ndi wokhulupirikadi,
Ndipo sitingam’siye.
2. Tikhulupirike zedi,
Kwa abale mumpingo.
Nthawi zonse pamavuto,
Amatisamalira.
Tiziwalemekezatu
Kuchokera mumtima.
Tiwamvere nthawi zonse,
Ndipo tisawasiye.
3. Tikhulupirike zedi
Tikamalangizidwa.
Ndi abale amumpingo,
Tifunika kumvera.
Ndipo Yehova Mulungu
Adzatidalitsatu,
Tikakhulupirikadi,
Iye adzatikonda.
(Onaninso Sal. 149:1; 1 Tim. 2:8; Aheb. 13:17.)