NYIMBO 137
Akazi Achikhristu Okhulupirika
zosindikizidwa
1. Sara, Esitere, Rute, ndi ena—
Onsewa ’nali akazi abwino,
Anali odzipereka kwa M’lungu.
Timawadziwa ndi mayina awo.
Panali ena sanatchulidwe,
Iwotu Yehova ankawakondanso.
2. Akaziwatu amatikumbutsa
Makhalidwe omwe tifunikira.
Monga ubwino ndi kulimba mtima.
Ndi zitsanzo zotilimbikitsadi.
Alongo a masiku anonso,
Khalani zitsanzo kwa ena tonsefe.
3. Achemwali, amayi, amasiye
Mumachita khama pogwira ntchito
Mumagonjera, mumadzichepetsa.
Musaope Mulungu ali nanu.
Ndipo iye akulimbitseni,
Musafooketu, mudzadalitsidwa.
(Onaninso Afil. 4:3; 1 Tim. 2:9, 10; 1 Pet. 3:4, 5.)