Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lmd 10
  • Kudzipereka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudzipereka
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Afike Poyamba Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd 10

KUPHUNZITSA ANTHU

Yesu ndi Nikodemo akukambirana usiku pamalo ochezera.

Yohane 3:1, 2

PHUNZIRO 10

Kudzipereka

Mfundo yaikulu: “Tinkafunitsitsa kukuuzani uthenga wabwino wa Mulungu komanso kupereka miyoyo yathu yeniyeniyo kuti tikuthandizeni.”​—1 Ates. 2:8.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu ndi Nikodemo akukambirana usiku pamalo ochezera.

VIDIYO: Yesu Anaphunzitsa Nikodemo

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 3:1, 2. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. N’kutheka kuti n’chiyani chomwe chinachititsa kuti Nikodemo apite kwa Yesu usiku?​—Onani Yohane 12:42, 43.

  2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wofunitsitsa kuphunzitsa anthu pomwe analolera kucheza ndi Nikodemo usiku?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Timasonyeza kuti timakonda anthu tikamawaphunzitsa modzipereka kuti akhale ophunzira a Yesu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muziphunzira pamalo komanso nthawi yabwino kwa iyeyo. Mwina angakonde kuti muziphunzira naye tsiku linalake pamlungu kapena nthawi inayake pa tsiku. Kodi angakonde kuti muziphunzira naye komwe amagwira ntchito, kunyumba kwake kapena malo ena? Ngati n’zotheka, sinthani zina ndi zina kuti muziphunzira naye pa nthawi ndi malo omwe angakonde.

4. Muziphunzira naye nthawi zonse. Ngati mutachokapo, musamalephere kuphunzira naye. Yesani njira izi:

  1. Kodi mungaphunzire naye nthawi ina mlungu womwewo?

  2. Kodi mungaphunzire naye pa foni kapena pa vidiyokomfelensi?

  3. Kodi mungapemphe wofalitsa wina kuti akaphunzire naye?

5. Muzipemphera kuti muziona zinthu moyenera. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuti musamachite ulesi pophunzira ndi munthuyo ngakhale kuti nthawi zina sapezekapezeka paphunziro kapenanso amavutika kugwiritsa ntchito zomwe akuphunzira. (Afil. 2:13) N’zachidziwikire kuti ali ndi makhalidwe ambiri abwino. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kuganizira makhalidwe amenewo.

ONANINSO MALEMBA AWA

Miy. 3:27; Mac. 20:35; 2 Akor. 12:15

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani