MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mwana Wolowerera
ONERANI VIDIYO YAKUTI MWANA WOLOWERERA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi ndi zinthu ziti zimene zikusonyeza kuti David anali atayamba kuyenda m’njira yolakwika, nanga akulu komanso anthu a m’banja lake anachita chiyani poyesetsa kumuthandiza?
N’chifukwa chiyani M’bale ndi Mlongo Barker ali chitsanzo chabwino kwa makolo?
Kodi taphunzira chiyani m’vidiyoyi pa nkhani ya . . .
kudzipereka kwambiri pa ntchito yathu?
kucheza ndi anthu oipa?
kumvera malangizo?
kukhululukira anthu amene alapa?