CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 19-20
“Mukhale Tcheru ndi Kuyang’anira Gulu Lonse la Nkhosa”
Akulu amadyetsa, kuteteza ndi kusamalira nkhosa chifukwa amadziwa kuti nkhosazo zinagulidwa ndi magazi a mtengo wapatali a Yesu. Abale ndi alongo amayamikira kwambiri akulu omwe ali ngati Paulo, amene amadzipereka posamalira nkhosa.