CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 ATESALONIKA 1-5
“Pitirizani Kutonthozana ndi Kulimbikitsana”
Mkhristu aliyense akhoza kulimbikitsa ena. Mwachitsanzo, timalimbikitsa Akhristu anzathu ngati nthawi zonse timapezeka pamisonkhano komanso kulalikira. Tingawalimbikitse ngakhale zitakhala kuti tikuchita zimenezi “movutikira kwambiri” chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. (1 Ates. 2:2) Komanso tikamaganizira zimene tinganene, mwinanso kufufuza mfundo zina m’mabuku athu, tikhoza kumatonthoza ndiponso kulimbikitsa abale athu.
Kodi mungapeze kuti mfundo zimene mungagwiritse ntchito polimbikitsa munthu amene ali ndi vuto linalake?
Kodi ndi ndani mumpingo wanu amene mukufuna kumulimbikitsa?